‘Limandithandiza Kupirira Mavuto’
‘Limandithandiza Kupirira Mavuto’
Zimenezo n’zimene mayi wina wa ku Connecticut, ku United States, ananena ataŵerenga buku lakuti Yandikirani kwa Yehova. Iye anati: “Ndikuliŵerenga pang’onopang’ono tsiku lililonse. Pa masiku amene kuvutika maganizo kumandichititsa kuti ndizivutika ngakhale kupuma, ndikaŵerenga pang’ono buku limeneli mofatsirira limandithandiza kupirira zovutazo.”
Iye anapitiriza kuti: “Chithunzi cha mbusa wachikondi chimene chili pa tsamba 69 chinandikhudza mtima kwambiri. Ndipo ndinayamikira mfundo imene ili pa tsamba 28, pa ndime 8, yonena za Mose ali pachitsamba choyaka moto kuti ‘malo ozungulira chitsambacho anakhala oyera chifukwa chakuti Yehova anali kulankhulira pamenepo!’ Ngati Yehova angachititse dothi kukhala loyera, ndiye kuti ngakhale nanenso zinthu zikhoza kundiyendera bwino. Mfundo imeneyi yandithandiza kwambiri chifukwa ndimavutika maganizo nthaŵi ndi nthaŵi.”
Tikukhulupirira kuti mupindula kwambiri mukaŵerenga buku lamasamba 320 limeneli lakuti Yandikirani kwa Yehova. Mungathe kuitanitsa buku limeneli polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.
□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire buku lakuti Yandikirani kwa Yehova.
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.