Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungalimbikitsire Ana Kuti Azikonda Kuphunzira

Mmene Mungalimbikitsire Ana Kuti Azikonda Kuphunzira

Mmene Mungalimbikitsire Ana Kuti Azikonda Kuphunzira

“Uphunzitse mwana njira yomwe ayenera kuitsata, ndipo atadzakalamba, sadzaisiya.”—MIYAMBO 22:6, MALEMBO OYERA.

KODI munayeserapo kuuza ana kuti agone pamene chinachake chosangalatsa chinali kuchitika? Ngakhale akhale atatopa, akulira, ndiponso akuvuta, amayesetsa kukhalabe maso kuti zinthu zisawapite. Mlembi wina dzina lake John Holt analemba kuti: “Chilakolako cha ana chofuna kumvetsetsa zimene zikuchitika ndi kuphunzira kuchita zinthu mwaluso n’chofanana ndi mmene amafunira kudya, kupuma, kapena kugona. Nthaŵi zina chimakhala chachikulu kwambiri kuposa zinthu zimenezi.”

Vuto limene ana amakhala nalo n’loti akhalebe ndi chilakolako chawo chofuna kuphunzira moyo wawo wonse, kuphatikizapo nthaŵi imene ali pasukulu. Ngakhale kuti palibe njira inayake yapadera imene ingawathandize kuchita zimenezi, pali njira zina zoti anthu ena anayeserapo ndipo zinawathandiza zimene makolo, aphunzitsi, ndi ana angatsatire. Koma chofunika kwambiri kuposa njira ina iliyonse ndi chikondi.

Akondeni Ana Anu Kuti Athe Kuchita Zonse Zomwe Angathe

Ana amafunitsitsa kuti makolo awo aziwakonda. Makolo akamawakonda, ana amamva kuti ndi otetezeka, ndipo amakhala omasuka kulankhula, kufunsa mafunso, ndi kufufuza zinthu. Chikondi chimachititsa makolo kulankhula nthaŵi zonse ndi ana awo ndi kukhala ndi chidwi ndi maphunziro awo. Kafukufuku wasonyeza kuti “zikuoneka kuti makolo ndiwo angathandize kwambiri kuti ana akhale ndi mtima wokonda kuphunzira,” malinga n’zimene limanena buku lotchedwa Eager to Learn—Helping Children Become Motivated and Love Learning. Makolo angathandize kwambiri ana kukhala ndi mtima wokonda kuphunzira akamachita zinthu mogwirizana ndi aphunzitsi. “Chimene chimathandiza kwambiri kuti mwana akhale ndi mtima wokonda kuphunzira ndicho makolo ndi aphunzitsi akamachita zinthu mogwirizana,” limatero bukulo.

Makolo angathandizenso ana awo kukhala anzeru. M’kafukufuku amene anachitika kwa nthaŵi yaitali wa mabanja 43, amene analembedwa m’buku lotchedwa Inside the Brain, ochita kafukufukuyo “anapeza kuti ana amene makolo awo ankawalankhula kwambiri [m’zaka zitatu zoyambirira za moyo wawo] anali anzeru kwambiri poyerekezera ndi ana amene makolo awo sankawalankhula kwambiri.” Bukulo linapitiriza kuti “makolo amene amalankhula ndi ana awo kwambiri amawayamikira anawo akachita bwino zinthu, amawayankha mafunso awo, amawatsogolera m’malo mongowalamulira, ndipo amagwiritsa ntchito mawu osiyanasiyana polankhula nawo.” Ngati ndinu kholo, kodi mumalankhula nthaŵi zonse ndi ana anu m’njira imene ingawathandize?

Pamene Pali Chikondi Pamakhala Kukoma Mtima ndi Kumvetsetsana

Ana amasiyana luso lawo ndi zimene angathe kuchita. Makolo sayenera kukonda anawo mosiyana chifukwa cha kusiyana kumeneku. Koma masiku ano, kuti munthu aoneke kuti ndi waphindu anthu amaona zimene munthuyo angathe kuchita, ndipo zimenezi zingachititse ana ena “kuganiza kuti phindu lawo monga munthu limadalira kuchita zinthu mopambana ena,” malinga ndi zimene limanena buku lotchedwa Thinking and Learning Skills. Kuwonjezera pa kuchititsa ana ameneŵa “kuchita mantha akaganiza zoti alephera,” kuona zinthu m’njira yoteroyo kungawachititsenso kumada nkhaŵa kwambiri. Magazini yotchedwa India Today inanena kuti nkhaŵa imene achinyamata amakhala nayo chifukwa choti anthu amawayembekezera kuti azikhoza kwambiri kusukulu ndiponso chifukwa chakuti mabanja awo sawathandiza, akuti ndi imene yachititsa kwambiri kuti chiŵerengero cha achinyamata amene amadzipha ku India chikwere kuwonjezereka katatu m’zaka 25 zapitazi.

Ana angapwetekedwenso maganizo mukamawanena kuti ndi “opusa” kapena “opepera.” Mawu ankhanza oterowo amagwetsa ulesi mwana akamaphunzira m’malo momulimbikitsa. Koma kholo lachikondi liyenera kukhala lokoma mtima nthaŵi zonse, ndipo liyenera kulimbikitsa chilakolako chachibadwa chimene mwana amakhala nacho chofuna kuphunzira, ndipo mwanayo ayenera kuphunzira malinga ndi mmene angathere, popanda kuchita mantha kapena kunyozedwa. (1 Akorinto 13:4) Ngati mwana ali ndi vuto loti satha kuphunzira zinthu msanga, makolo achikondi amayesera kumuthandiza, osamuchititsa kumva kuti ndi wopusa kapena wopanda phindu. N’zoona kuti zimenezi zingafune kuti makolo akhale oleza mtima ndiponso azichita zinthu momuganizira mwanayo, koma kuchita zimenezi n’kothandiza kwambiri. Kodi munthu angatani kuti akhale ndi chikondi choterocho? Kuona zinthu mwauzimu ndicho chinthu choyamba chofunika kwambiri.

Kuona Zinthu Mwauzimu Kumathandiza Munthu Kuika Maphunziro Pamalo Oyenera

Kuona zinthu mwauzimu mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena n’kofunika kwambiri pa zifukwa zingapo. Choyamba, kumatithandiza kuika maphunziro pamalo oyenera, kuwaona kuti ndi ofunika koma osawaona kuti ndi ofunika kuposa zonse. Mwachitsanzo, kudziŵa masamu kungathandize munthu m’njira zosiyanasiyana, koma sikungamuchititse kukhala ndi makhalidwe abwino.

Baibulo limatilimbikitsanso kusathera nthaŵi yochulukitsitsa pa maphunziro, ndipo limati: “Saleka kulemba mabuku ambiri; ndipo kuphunzira kwambiri kutopetsa thupi.” (Mlaliki 12:12) N’zoona kuti ana amafunika kuphunzira bwino, koma zimenezi siziyenera kuwathera nthaŵi yawo yonse. Amafunikanso kukhala ndi nthaŵi yochita zinthu zina zothandiza, makamaka zinthu zauzimu, zimene zimaphunzitsa mtima wa munthu.

Mbali yachiŵiri yoona zinthu mwauzimu mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena ndiyo kudzichepetsa. (Mika 6:8) Anthu odzichepetsa amadziŵa zofooka zawo, ndipo safuna kukhala patsogolo pa onse kapena kuchita mpikisano mosaganizira ena, makhalidwe amene akuoneka m’masukulu ambiri masiku ano. Makhalidwe oipa ameneŵa “angachititse munthu kuvutika maganizo kwambiri,” inatero magazini ya India Today. Kaya ndife achinyamata kapena achikulire, zinthu zimatiyendera bwino tikatsatira malangizo ouziridwa a m’Baibulo akuti: “Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.” “Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.”—Agalatiya 5:26; 6:4.

Kodi makolo angatsatire bwanji mfundo zimenezi pa maphunziro a ana awo? Njira imodzi ndiyo kulimbikitsa mwana aliyense kukhala ndi zolinga zoti azikwaniritse ndi kuona mmene akuchitira zinthu panopa poyerekezera ndi m’mbuyomu. Mwachitsanzo, ngati mwana wanu posachedwapa analemba mayeso a masamu kapena a masipelo, muuzeni kuti ayerekezere mmene wakhozera panopa ndi mmene anakhozera mayeso a m’mbuyomu. Ndiyeno muyamikireni kapena mulimbikitseni. Mukamachita zimenezi, mumamuthandiza kukhala ndi zolinga zimene angathe kuzikwaniritsa, kuona mmene akuchitira, ndi kuthetsa zofooka zilizonse zimene angakhale nazo, popanda kumuyerekezera ndi anthu ena.

Koma masiku ano, achinyamata ena anzeru bwinobwino safuna kumakhoza kusukulu poopa kusekedwa. Achinyamata ena amati: “Kukhoza kusukulu n’kwachikale.” Kodi kuona zinthu mwauzimu kungathandize pamenepa? Inde, kungathandize. Taganizirani zimene limanena lemba la Akolose 3:23, zoti: “Chilichonse muchita, muchichite ndi mtima wanu wonse, monga m’mene mungagwirire ntchito ya Ambuye osati ya anthu.” (Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Kodi pangakhalenso chifukwa china chabwino chochitira khama choposa kufuna kusangalatsa Mulungu? Kukhala ndi maganizo oyenera ameneŵa kumathandiza munthu kupeŵa kukopeka ndi zimene anzake akuchita.

Phunzitsani Ana Kukonda Kuŵerenga

Kuŵerenga ndi kulemba n’zofunika kwambiri pamaphunziro, a kusukulu ndi auzimu omwe. Makolo angathandize ana awo kukonda mabuku mwa kuwaŵerengera mokweza kuyambira akadali makanda. Daphne, amene amagwira ntchito yoŵerenga zimene anthu ena alemba kuti aone ngati pali zolakwika, akuyamikira makolo ake chifukwa ankamuŵerengera nthaŵi zonse ali mwana. Iye akufotokoza kuti: “Makolo anga anandithandiza kuti ndizikonda mabuku. Chifukwa cha zimenezo, ndinaphunzira kuŵerenga ndisanayambe sukulu. Makolo anga anandiphunzitsanso kufufuza zinthu kuti ndizitha kupeza mayankho a mafunso anga. Zimene anandiphunzitsazi zandithandiza kwambiri, mpaka panopa.”

Komabe, Holt, amene tinamutchula koyambirira uja, akuchenjeza kuti kuŵerengera ana “sikuli ngati mankhwala a zonse.” Iye akuwonjezera kuti: “Ngati kuŵerengako sikukusangalatsa kholo ndi mwana yemweyo, kungakhale ndi zotsatirapo zoipa osati zabwino. . . . Ngakhale ana amene amakonda kuwaŵerengera . . . sasangalala ngati makolowo sakusangalala nazo.” Choncho Holt akulangiza makolo kuti azisankha mabuku amene iwowo amasangalala nawonso, chifukwa anawo angafune kuti aziwaŵerengera mabuku amenewo mobwerezabwereza! Mabuku aŵiri amene makolo ambiri padziko lonse amakonda kuŵerengera ana awo ndi Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Chifukwa chakuti mabuku ameneŵa anakonzedwa mwapadera kuti akhale mabuku a ana, ali ndi zithunzi zambiri, amathandiza ana kuganiza, ndiponso amaphunzitsa mfundo za Mulungu.

Timoteo, Mkristu amene anakhalapo m’zaka 100 zoyambirira, anali ndi mwayi wokhala ndi amayi ndi agogo aakazi amene anali ndi chidwi chomuphunzitsa, makamaka kumuphunzitsa zinthu zauzimu. (2 Timoteo 1:5; 3:15) Timoteo atakula anakhala munthu wodalirika kwambiri, khalidwe limene munthu sangakhale nalo chifukwa cha maphunziro a kusukulu okha. (Afilipi 2:19, 20; 1 Timoteo 4:12-15) Masiku ano m’mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse lapansi muli achinyamata ambiri a khalidwe labwino ngati Timoteo, amuna ndi akazi omwe, chifukwa chakuti ali ndi makolo achikondi, okonda zinthu zauzimu.

Phunzitsani Mwansangala!

Ngati mphunzitsi akufuna kuti ophunzira ake azikonda kuphunzira, “pali liwu limodzi limene limafotokoza mmene ayenera kuphunzitsira—mwansangala,” limatero buku lotchedwa Eager to Learn. “Ngakhale asanalankhule n’komwe, aphunzitsi ansangala amasonyeza ophunzira awo kuti ali ndi chidwi kwambiri ndi zimene akuphunzitsanzo, ndipo akamaphunzitsa amaonekadi kuti akusangalala kwambiri ndi zimene akuphunzitsazo.”

Koma zoona zake n’zakuti si kholo lililonse kapena mphunzitsi aliyense amene amaphunzitsa mwansangala. Choncho ophunzira anzeru amayesetsa okha kukhala ndi mtima wofuna kuphunzira, kuona kuphunzira ngati udindo wawo. Zimenezi n’zofunika, chifukwa buku talitchula kale lija limati “palibe amene adzakhala limodzi ndi ana athu moyo wawo wonse kuwathandiza kuti aziphunzira, azigwira ntchito yochititsa kaso, aziganiza, ndi kuwathandiza kuti azichita khama limene limafunika kuti munthu akhale ndi luso labwino.”

Pamenepanso zikuoneka kuti kunyumba, osati kusukulu, n’kumene ana amafunika kuphunzira mfundo zabwino zoyenera kutsatira. Makolo, kodi mumakhala ndi chidwi ndi maphunziro? Kodi panyumba panu ndi malo abwino ophunzirirapo, malo amene amasonyeza kufunika kotsatira mfundo zauzimu? (Aefeso 6:4) Kumbukirani kuti chitsanzo chanu ndiponso zimene mumaphunzitsa zidzakhudza ana anu kwa nthaŵi yaitali atamaliza sukulu ndiponso atachoka panyumbapo.—Onani bokosi lakuti “Mabanja Amene Amatha Kuphunzitsa Bwino Ana,” patsamba 7.

Zindikirani Kuti Anthu Amaphunzira M’njira Zosiyana

Palibe anthu aŵiri amene ali ndi ubongo wofanana, aliyense ali ndi njira yake yophunzirira. Zimene zimathandiza munthu mmodzi zikhoza kusathandiza munthu wina. Choncho, Dr. Mel Levine analemba m’buku lake lotchedwa A Mind at a Time kuti: “Si chilungamo kumawatenga ana onse mofanana. Ana osiyana amaphunziranso mosiyanasiyana; mwana aliyense ali ndi ufulu woti aziphunzitsidwa m’njira yomuyenera iyeyo.”

Mwachitsanzo, anthu ena amamvetsa bwino zinthu akaona zithunzi. Ena amamvetsa bwino zinthu zolembedwa kapena zonenedwa pakamwa, kapena kuphatikiza njira ziŵiri zonsezi. Levine anati: “Njira yabwino kwambiri yokumbukirira chinachake ndiyo kuchisintha, kusintha zinthuzo mwa njira inayake. Ngati ndi chithunzi, chifotokozeni m’mawu, ngati ali mawu, asandutseni chithunzi m’maganizo mwanu.” Kuphunzira mwanjira imeneyi kumathandiza kuti maphunziro akhale aphindu komanso osangalatsa.

N’zoona kuti mungafunike kuyesa njira zosiyanasiyana kuti mupeze njira imene mumaphunzirira bwino kwambiri. Hans, mtumiki wachikristu wa nthaŵi zonse, ankaphunzira Baibulo ndi George, mwamuna wachikulire wosaphunzira kwambiri. George ankavutika kumvetsetsa zinthu ndi kuzikumbukira. Choncho Hans anayesera kujambula pa pepala zithunzi zosonyeza mfundo zofunika kwambiri. Hans anati: “Pamenepo m’pamene George anasinthira. Ndipo anayamba kumvetsetsa ndi kukumbukira mfundo bwino kwambiri moti ngakhale mwiniwakeyo anadabwa! Nditatulukira mmene amaganizira, ndinazindikira kuti anali wanzeru kwambiri kuposa mmene ndinkaganizira poyamba. Pasanapite nthaŵi yaitali anasiya kudzikayikira, ndipo anayamba kusangalala kwambiri ndi maphunziro athu kuposa kale.”

Ngakhale Munthu Akalambe Angathebe Kuphunzira

Buku lakuti Inside the Brain limati: “Zimene ubongo ungachite zimadalira ngati ukugwiritsidwa ntchito kapena ayi. Ndi chiwalo choti ngati suchigwiritsa ntchito chimawonongeka, ndipo chimafunitsitsa kuphunzira luso latsopano.” Bukulo limanenanso kuti: “Mofanana ndi mmene kuchita maseŵera olimbitsa thupi kumathandizira kuti anthu akhalebe amphamvu ngakhale afike zaka za m’ma 70 kapena 80, ochita kafukufuku akusonyeza kuti kugwiritsa ntchito ubongo kungauthandizenso chimodzimodzi ukamakalamba. Kwa nthaŵi yaitali, anthu akhala akukhulupirira kuti akamakalamba amayamba kupereŵera nzeru. Koma kafukufuku watsopanoyu wasonyeza kuti zimenezi zinkakhala choncho chifukwa n’zimene anthuwo ankakhulupirira ndipo sankagwiritsa nchito ubongo wawo. Kuwonjezera pamenepo, anthu akamakalamba sikuti mbali zambiri za ubongo wawo zimawonongeka, ngati mmene tinkaganizira kale.” Kuchepa mphamvu kwambiri kwa ubongo nthaŵi zambiri kumakhala chizindikiro cha matenda, monga matenda a mtima.

N’zoona kuti ubongo ungachepeko mphamvu pa ukalamba koma suchepa mphamvu modetsa nkhaŵa kwambiri. Ubongo ukamagwira ntchito kwambiri suchepa mphamvu, makamaka ngati munthuyo amachitanso maseŵera olimbitsa thupi nthaŵi zonse. Buku lotchedwa Elderlearning—New Frontier in an Aging Society limati: “Munthu akamaphunzira zinthu zatsopano zambiri, m’pamenenso savutika kuphunzira zinthu zina. Anthu amene sasiya kuphunzira savutika kuphunzira zinthu zatsopano.”

Zimenezi zinaoneka ku Australia mu kafukufuku amene anatenga zaka 20 wa anthu a zaka zapakati pa 60 ndi 98. Nzeru za anthu ambiri amene anali nawo m’kafukufukuyo zinachepa pang’ono chabe pachaka. Komabe, “nzeru za anthu ena, kuphatikizapo anthu a zaka za m’ma 90, sizinachepe n’komwe,” linatero lipotilo. “Ameneŵa nthaŵi zambiri anali anthu amene anachitapo maphunziro ovuta monga kuphunzira chinenero chakunja kapena kuphunzira kuimba nyimbo ndi chida chinachake.”

George, amene tinamutchula kale uja, anali ndi zaka za m’ma 70 pamene anayamba kuphunzira Mawu a Mulungu. Chimodzimodzinso Virginia, amene tsopano ali ndi zaka za m’ma 80, ndi mwamuna wake amene panopa anamwalira, Robert, nawonso anayamba kuphunzira Baibulo ali nkhalamba. Virginia akuti: “Ngakhale kuti Robert anali wosaona kwenikweni, ankakamba nkhani zazifupi zochokera m’Baibulo m’Nyumba ya Ufumu zimene anali ataziloŵeza pamtima. Ineyo kale kuŵerenga sikunkandisangalatsa, koma masiku ano ndimakonda kuŵerenga kwambiri. Ndipo lero m’maŵa uno ndaŵerenga Galamukani! yathunthu.”

George, Robert, ndi Virginia ndi zitsanzo zitatu zokha za anthu ambiri okalamba amene amachita zinthu zosiyana ndi zimene ambiri amakhulupirira kuti okalamba amachita, ndipo amagwiritsa ntchito ubongo wawo kwambiri. Kafukufuku wasonyeza kuti kwa ubongo, kuphunzira zinthu kwa zaka 70 kapena 80 kuli ngati dontho lamadzi mukaliyerekezera ndi m’golo wodzaza ndi madzi, chifukwa ubongowo umakhala usanayambe n’komwe kudzaza. N’chifukwa chiyani ubongo uli ndi mphamvu zazikulu choncho zomwe sizigwiritsidwa ntchito?

[Bokosi pamasamba 20, 21]

Intaneti ndi TV—Kodi Zimathandiza Kapena Zimalepheretsa Kuphunzira?

“Kugwiritsa ntchito Intaneti kuli ndi ubwino ndi kuipa kwake,” limatero buku lotchedwa A Mind at a Time. Kuphunzira kupeza zimene munthu akufuna kudziŵa n’kofunika kwambiri, koma bukulo linati ophunzira ena, “amangotenga zinthu pa Intaneti popanda kuzimvetsa kapena kuziyerekezera ndi zimene akudziŵa kale. Choncho kutenga zinthu pa Intaneti kungasanduke njira yatsopano yophunzirira zinthu popanda kuchita chilichonse kapena njira yopezera luso lobera maganizo a anthu ena.”

Ochita kafukufuku anena kuti kuthera nthaŵi yaitali mukuonera TV kungabwezere m’mbuyo luso lanu lotha kulimbana ndi zothetsa nzeru ndiponso kumvetsera munthu wina akamalankhula, kungachepetse luso loganiza, ndipo sikuthandiza munthu kukulitsa khalidwe labwino. Buku lotchedwa Eager to Learn limati: “Ma TV ayenera kulembedwa mawu ochenjeza anthu kuti akhoza kuwononga thanzi lawo, monga momwe amalembera pa ndudu za fodya.”

Buku lina linati zimene ana amafunikira kwambiri ndi “kumva anthu akulankhula (poŵerenga kapena pocheza), chikondi, ndi kuwakupatira mwachikondi nthaŵi zonse.”

[Bokosi/Zithunzi patsamba 23]

Mabanja Amene Amatha Kuphunzitsa Bwino Ana

Kuchita zinthu zotsatirazi kungathandize banja lanu kuphunzira bwino:

▪ Kuuza ana mwachikondi ndiponso pafupipafupi kuti mumawayembekezera kukwanitsa zinthu zimene angathedi kukwanitsa

▪ Kuona kuti kugwira ntchito mwakhama ndiyo njira yothandiza kuti zinthu zikuyendereni bwino

▪ Kukhala ndi moyo wotakataka, osangokhala phwii

▪ Kuphunzitsa ana pakhomo mlungu uliwonse ndi kuchita zinthu monga homuweki, kuŵerenga mabuku pongofuna kusangalala, kuchita zimene aliyense amakonda kuchita akakhala ndi mpata, kugwirira ntchito limodzi monga banja, ndi kuphunzitsa ana ntchito zapakhomo

▪ Kuona banja monga malo olimbikitsirana ndi kuthandizana pakagwa mavuto

▪ Kukhala ndi malamulo apabanjapo omveka bwino, amene makolo amaonetsetsa kuti akutsatiridwa

▪ Kulankhulana pafupipafupi ndi aphunzitsi

▪ Kulimbikitsana kukula mwauzimu

[Chithunzi]

Makolo, kodi mumaphunzitsa ana anu kukonda kuŵerenga?

[Mawu a Chithunzi]

Zachokera m’buku lakuti Eager to Learn—Helping Children Become Motivated and Love Learning.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 24]

Zimene Mungachite Kuti Kuphunzira Kwanu Kukhale Kwaphindu ndi Kosangalatsa

Khalani ndi Chidwi Mukakhala ndi chidwi ndi chinthu chinachake, mumachiphunzira msanga. Buku lakuti Motivated Minds—Raising Children to Love Learning linanena kuti: “Ochita kafukufuku asonyeza mosapita m’mbali kuti ana akamaphunzira chifukwa chakuti amasangalala ndi kuphunzirako, amamvetsa kwambiri, amapindula kwambiri, ndipo saiwala msanga. Amakhalanso olimbikira, amakhala ndi luso lotha kupeza njira zatsopano, ndipo amafunitsitsa kuchita zinthu zovuta.”

Onani Kugwirizana kwa Zimene Mukuphunzirazo ndi Zochitika pa Moyo Wanu Mlembi ndiponso mphunzitsi wina dzina lake Richard L. Weaver II analemba kuti: “Mukaona kugwirizana kwa zimene mukuphunzira m’kalasi ndi zimene zimachitikadi pa moyo wanu, zimakhala ngati mwayatsa getsi limene limakuthandizani kumvetsa zinthu.”

Yesetsani Kumvetsa Anthu akamayesetsa kumvetsa chinachake, zimakhudza maganizo awo ndipo sachedwa kukumbukira zimene akuphunzirazo. Kuloŵeza pamtima n’kofunika nthaŵi zina, koma sikungalowe m’malo mwa kumvetsa zinthu. Lemba la Miyambo 4:7, 8 limati: “M’kutenga kwako konseko utenge luntha. Uilemekeze, ndipo idzakukweza.”

Ikani Maganizo Onse pa Zimene Mukuphunzirazo Buku lakuti Teaching Your Child Concentration limati: “Kuika maganizo onse pa zimene munthu akuphunzira n’kofunika kwambiri pa maphunziro.” Bukulo limafotokoza kuti: “N’kofunika kwambiri moti ena amati ndiko chiyambi cha nzeru ndipo ena amati ndiko nzeru zenizenizo.” Mungathe kuphunzitsa munthu kuti aziika maganizo ake onse pa zimene akuphunzira. Chinsinsi chake chagona pa kuyamba ndi kuphunzira kwa kanthaŵi kochepa, kenako n’kumawonjezera nthaŵi yophunzirirayo pang’onopang’no.

Zineneni M’mawu Anu “Ophunzira anzeru kwambiri ndi amene amadziŵa bwino kunena zinthu m’mawu awo,” anatero Dr. Mel Levine m’buku lake lotchedwa A Mind at a Time. Mukamanena zinthu m’mawu anu mumazigawa m’mbali zing’onozing’ono zimene mungathe kuzikumbukira mosavuta. Anthu odziŵa bwino kulemba notsi amatsatira mfundo imeneyi posalemba notsi ndendende ngati mmene munthu akulankhulira.

Gwirizanitsani Zimene Mukuphunzirazo ndi Zam’mbuyomu M’buku lotchedwa The Brain Book, Peter Russell anati zinthu zimene timakumbukira zimakhala ngati zakolowekedwa pa zinthu zimene tikudziŵa kale. Mwachidule, mumakumbukira bwino zinthu ngati muzigwirizanitsa ndi zimene mukudziŵa kale. Mukagwirizanitsa zinthu zambiri, m’pamenenso mumakumbukira bwino zinthu.

Khalani ndi Zithunzi M’maganizo Mwanu Zithunzi zokhudza mtima siziiwalika. Choncho, muzikhala ndi chithunzi cha zinthuzo m’maganizo mwanu ngati mungathe kutero. Akatswiri odziŵa za kukumbukira amagwiritsa ntchito njira imeneyi, ndipo nthaŵi zambiri amapanga zithunzi zokokomeza kapena zoseketsa m’maganizo mwawo kuti ziwathandize kukumbukira.

Bwerezani Pomatha maola 24, tingaiwale pafupifupi zonse zimene taphunzira. Mwa kubwereza mwachidule mukatha kuphunzira, kenaka kubwerezanso pakatha tsiku limodzi, mlungu umodzi, mwezi umodzi, ndipo ngakhale miyezi sikisi, tingathe kukumbukira zinthu bwino kwambiri, mwina ngakhale kukumbukira zonse bwinobwino.

[Zithunzi patsamba 24]

Makolo ndi aphunzitsi ayenera kuchita zinthu mogwirizana kuti athandize ana kuphunzira

[Zithunzi patsamba 26]

Ukalamba suyenera kulepheretsa munthu kuphunzira