Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhaŵa Imene Munthu Ali Nayo pa Maonekedwe Ake Ikasanduka Matenda

Nkhaŵa Imene Munthu Ali Nayo pa Maonekedwe Ake Ikasanduka Matenda

Nkhaŵa Imene Munthu Ali Nayo pa Maonekedwe Ake Ikasanduka Matenda

AMBIRI a ife tikadziyang’ana pagalasi, timaona zinthu zina n’zina zimene tikhoza kuzisintha kuti tionekeko bwino. Choncho timasintha zovala zathu kapena kupesanso tsitsi lathu, kapena timadzola zodzoladzola kenako n’kuchoka kumakachita zinthu zina. Palibe cholakwika ndi kudera nkhaŵa maonekedwe athu koteroko ndiponso kuchita zimenezo n’koyenera. Koma anthu ena amada nkhaŵa ndi maonekedwe awo monyanyira ndipo amayamba kuchita zinthu zimene madokotala amati ndi matenda.

Buku la zamankhwala lotchedwa The Merck Manual of Diagnosis and Therapy limafotokoza kuti munthu akamadwala matenda ameneŵa “amada nkhaŵa kwambiri ndi cholakwika chinachake pa maonekedwe ake, zimene zimamuvutitsa maganizo ndipo amalephera kucheza bwino ndi anthu ena, kugwira bwino ntchito, kapena kuchita zinthu zina zofunika pa moyo wake.” * Chifukwa chakuti anthu odwala matenda ameneŵa amaganiza kuti chinachake pa thupi lawo n’cholakwika kapena amakokomeza kachinthu kenakake kolakwika kochepa, amayamba kudziona ngati onyansa.

Pulofesa J. Kevin Thompson wa pa yunivesite ya South Florida, ku United States anati matenda ameneŵa si ofala kwambiri ndipo “mwina amagwira munthu mmodzi kapena anthu aŵiri mwa anthu 100 alionse abwinobwino, kapena anthu 10 mpaka 15 mwa anthu 100 alionse amene amapita kukaonana ndi dokotala chifukwa cha matenda a maganizo.” Koma ananenanso kuti: “Anthu ena ochita kafukufuku akuganiza kuti anthu odwala matendaŵa akuchulukirachulukira chifukwa njira zotulukirira matendaŵa zapita patsogolo ndiponso anthu ambiri masiku ano ayamba kumada nkhaŵa ndi maonekedwe awo.” Ngakhale kuti matendaŵa angagwire anthu a misinkhu yonse, nthaŵi zambiri amayamba munthu akakhala ndi zaka 13 mpaka 19. Pakati pa anthu achikulire, nthendayi imagwira amuna ndi akazi ochuluka mofanana. Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi matenda ovutika kudya, amene nthaŵi zambiri amagwira akazi.

Chifukwa anthu odwala nthendayi amada nkhaŵa kwambiri ndi maonekedwe awo, amangokhalira kudziyang’ana pagalasi ndipo amalephera kudziletsa kuchita zimenezi, ndiponso nthaŵi zina safuna kucheza ndi anthu ena. Kuwonjezera apo, “chifukwa anthu odwala matendaŵa amavutika maganizo ndiponso amalephera kuchita zinthu bwinobwino, angamagonekedwe m’chipatala kambirimbiri ndiponso angamafune kudzipha,” limatero buku la zamankhwala tinalitchula kale lija la The Merck Manual of Diagnosis and Therapy. Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ena odwala matendaŵa amafuna kuti achitidwe opaleshoni yowakongoletsa. Dokotala wina dzina lake Katharine Phillips, amene analemba buku linalake lonena za matendaŵa anati: “Nthaŵi zambiri ndimauza anthu odwala matendaŵa kuti asachititse opaleshoni yowakongoletsa. Munthu akachita opaleshoniyi sangathenso kudzisintha kuti akhale ngati mmene analili kale, ndipo anthu ambiri odwala matenda ameneŵa nthaŵi zambiri amaona kuti opaleshoniyo sinagwire ntchito.” *

Nthaŵi zina matendaŵa amayamba munthu ali wamng’ono kwambiri. Magazini yotchedwa George Street Journal * inafotokoza nkhani ya mnyamata wa zaka sikisi “amene ankaganiza kuti mano ake anali achikasu, mimba yake inali ‘yonenepa,’ ndiponso kuti tsitsi lake silinkaoneka bwino. ‘Zolakwika’ zonsezi palibe munthu wina amene ankaziona. Ankapesa tsitsi lake kwa pafupifupi ola lathunthu m’maŵa uliwonse, ndipo akaona kuti silikuonekabe ‘bwino’ ankaviika mutu wake m’madzi n’kuyambiranso kupesako, ndipo nthaŵi zambiri anali kuchedwa kusukulu.” Tsiku lina atafika m’chipinda cha adokotala, mpaka anagwada pansi kuti adziyang’anire pa mpando umene chitsulo chake chinali chonyezimira.

Musalole Dzikoli Kulamulira Maganizo Anu

M’magazini okhala ndi zikuto zonyezimira, m’manyuzipepala, ndi pa TV pamakhala zithunzi zambirimbiri zimene zimasonyeza anthu mmene munthu wokongola ayenera kuonekera. Maganizo a otsatsa malondawo ndi osavuta kuwatsatira. Iwo amati: Mukasonyeza anthu zithunzi zosonyeza mmene thupi labwino liyenera kuonekera, adzayamba kuwononga ndalama zawo zimene anachita kuzivutikira pogula zinthu zowathandiza kuti nawonso ayambe kuoneka choncho. Kuwonjezera apo, akamafuna kuti achite zinthu zofanana ndi zimene anzawo akuchita ndiponso anthu a m’banja mwawo kapena anzawo akamawanyoza ngati sakuoneka bwino, n’zosadabwitsa kuti anthu ena amayamba kuganiza molakwika za maonekedwe awo. * Komabe, kuganiza molakwika za maonekedwe a munthu n’kosiyana kwambiri ndi matenda a maganizo oda nkhaŵa kwambiri ndi maonekedwe.

Si zoona, ndiponso si mmene zimakhalira kuti ngati munthu si wokongola ndiye kuti anthu ena sazichita naye chidwi. Nthaŵi zambiri anthu sasankha anthu ocheza nawo chifukwa cha mmene anthuwo akuonekera. N’zoona kuti mwina poyamba maonekedwe angakope munthu koma khalidwe la munthuyo, ndi zimene amayendera pamoyo wake n’zimene zimalimbitsa ubwenzi. M’njira zina, aliyense wa ife ali ngati buku. Likhoza kukhala ndi chikuto chokongola, koma ngati nkhani yake ili yosasangalatsa, anthu sachedwa kusiya kuliŵerenga. Koma ngati lili losangalatsa, ngakhale litakhala ndi chikuto chonyansa, anthu amapitirizabe kuliŵerenga. Choncho, m’malo moganizira kwambiri za maonekedwe anu, bwanji osamaganizira kwambiri za makhalidwe anu? Zimenezo n’zimene Mawu a Mulungu, Baibulo, limakulimbikitsani kuchita.—Miyambo 11:22; Akolose 3:8; 1 Petro 3:3, 4.

Ndipo zoona zake n’zakuti, maonekedwe athu amasintha tikamakula. Zikanakhala kuti moyo wathu, mabwenzi athu, ndi chimwemwe chathu zimadalira maonekedwe okongola amene timakhala nawo tili anyamata, tonsefe tikanakhala ndi tsogolo lomvetsa chisoni kwambiri! Koma tsogolo lathu likhoza kukhala losiyana ndi limenelo. Kodi zimenezi zingatheke bwanji?

Kukongola Kumene Sikutha

Lemba la Miyambo 16:31 limati: ‘Imvi ndiyo korona wa ulemu, ikapezedwa m’njira ya chilungamo.’ M’maso mwa Yehova Mulungu, ndiponso m’maso mwa anthu amene amaona zinthu ngati mmene Yehova Mulungu amazionera, kukongola kwa anthu amene amakalamba akutumikira Mulungu sikutha. M’malo mwake, chifukwa cha mbiri yawo yochita zinthu mwakhama ndiponso modzipereka kwa Mulungu, akachita imvi amakhala ngati alandira korona waulemu. Anthu amtengo wapatali oterowo amafunika kuti tiziwakonda ndi kuwalemekeza kwambiri.—Levitiko 19:32.

Kuwonjezera apo, m’dziko latsopano limene Yehova walonjeza, adzachotsa zinthu zoipa zimene zachitikira anthu onse okhulupirika, achikulire ndi achinyamata omwe, chifukwa cha uchimo umene tinatengera kwa makolo athu. Tsiku lililonse azidzaona ndi kumva kuti thupi lawo likusintha kukhala labwinopo, mpaka lidzafika pokhala langwiro. (Yobu 33:25; Chivumbulutso 21:3, 4) Zimenezo ndi zinthu zosangalatsadi kuziyembekezera! Kodi mungakonde kudzakhala mmodzi wa anthu amenewo? Ngati mungakonde kutero, yesetsani kuganizira kukongola kumene kulidi kwaphindu, ndipo musalole kuti maganizo opereŵera amene nthaŵi zina amakhala ankhanza a dzikoli alamulire maganizo anu. Mukatero mudzakhala munthu wosangalala ndiponso wokongola.—Miyambo 31:30.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Buku lotchedwa The Medical Journal of Australia limati “kuda nkhaŵa ndi maonekedwe ako ndi chizindikiro chofala cha matenda angapo a maganizo.” Matendaŵa ndi monga kuvutika maganizo, kulephera kudziletsa kuchita zinthu zinazake, ndi kuvutika kudya poopa kunenepa. Choncho matenda oda nkhaŵa kwambiri ndi maonekedwe a munthu angakhale ovuta kuwatulukira.

^ ndime 5 Onani nkhani yakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi Ndichititse Opaleshoni Kuti Ndikhale Wokongola?” mu Galamukani! ya September 8, 2002. Komabe, munthu amene ali ndi matenda aakulu a maganizo angafunike kukaonana ndi dokotala wa maganizo.

^ ndime 6 Yofalitsidwa ndi yunivesite ya Brown, ku Rhode Island, ku United States.

^ ndime 8 Kuti mumve zambiri, onani mutu wakuti “Kodi Mawonekedwe Ngofunika Motani?” m’buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.