Atate Amene Ana Amafunikira
Atate Amene Ana Amafunikira
ANA amafunikira tate amene amawakonda, amene ali bwenzi lawo loti lingawathandize nthaŵi iliyonse, ndiponso amene amachita chilichonse chomwe angathe kuti awathandize kukula bwino kuti adzakhale akuluakulu odalirika. Koma zoti ana amafunika tate wotereyu sizinagogomezeredwe mokwanira.
N’zoona kuti mayi ndi amene amabereka ana, ndipo kufunika kokhala mayi wabwino n’kodziŵika bwino. Koma posonyeza kuti bambonso ali ndi udindo wofunika ngati wa mayi, magazini yotchedwa The Wilson Quarterly inati: “Kuchepa kwa chisamaliro chimene atate amapatsa ana awo n’kumene kwabweretsa mavuto ambiri amene anthu a ku America akuvutika nawo,” ndipo tingawonjezere kuti, n’kumene kwabweretsanso mavuto amene anthu padziko lonse akuvutika nawo.
Nyuzipepala ya ku Brazil yotchedwa Jornal da Tarde inafotokoza za kafukufuku amene anasonyeza kuti mavuto ambiri okhudza khalidwe la achinyamata, monga ndewu, kupulupudza, kulephera kusukulu, ndi kusachita chidwi ndi zinthu, nthaŵi zambiri “amabwera chifukwa chosakhala ndi bambo.” Ndipo buku la Chitaliyana lotchedwa Gli imperfetti genitori (Makolo Osadziŵa Zonse), lolembedwa ndi Marcello Bernardi, linatsindika kuti ana amafunika kukhala ndi makolo onse aŵiri kuti akule bwino.
Moyo wa Banja Ungasinthe N’kukhala Wabwinopo
Ngakhale pamene tate wonyalanyaza banja lake wachititsa kuti mavuto a m’banjamo achuluke, kapena ndi iyeyo amene wayambitsa mavutowo, sizikutanthauza kuti zinthu sizingasinthe moti moyo wa banjalo n’kukhala wabwinopo. Kodi zinthu zingasinthe bwanji? Kodi tate ayenera kuchita chiyani?
N’zachionekere kuti ana amafunika kukhala ndi banja lolinganizidwa bwino, ndipo amafuna kumaona kuti pali winawake amene amawafunira zabwino amene akutsogolera zinthu. Ngati palibe zimenezo, monga momwe zimakhalira nthaŵi zambiri masiku ano, ana sakula bwino. Komabe sikuti zinthu sizingasinthe, kaya atate akhale alipo kapena palibe. Pa Salmo 68:5, Baibulo limati: “Mulungu, mokhala mwake moyera, ndiye Atate wa ana amasiye.” *
Mmene Mungapezere Thandizo
Umboni woti thandizo la Mulungu ndi lofunika kwambiri kuti zinthu ziyende bwino ndiponso kuti munthu angathe kupeza thandizo limeneli, unaoneka pa zimene anafotokoza Lidia, mtsikana wa ku Poland amene tinamutchula mu nkhani yoyamba uja. Kodi moyo wa banja lake unali wotani? Kodi banjalo linalandira bwanji thandizo la Mulungu?
Franciszek, bambo wake wa Lidia, anavomereza kuti pamene ana ake anali aang’ono, iye ananyalanyaza banja lake, monga momwe mwana wake ananenera. Iye anati: “Zimene zinkachitikira ana anga ndinalibe nazo ntchito. Sindinawasonyeze chikondi chilichonse, ndipo analibe ubwenzi uliwonse ndi ine.” Choncho sanadziŵe kuti pamene Lidia anali ndi zaka 14, iye ndi mchimwene wake wamng’ono ndi mchemwali wake wamng’ono anali atayamba kale kumapita ku mapwando aphokoso, kusuta fodya, kumwa moŵa, ndi kuchita ndewu ndi anzawo.
Kenaka Franciszek anazindikira mavuto amene ana ake anali nawo, ndipo zinamudzidzimutsa kwambiri mpaka anaganiza zochitapo kanthu. Iye akuti: “Ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize.” N’zochititsa chidwi kuti patangopita nthaŵi yochepa Mboni za Yehova zinabwera kunyumba kwawo, ndipo iye ndi mkazi wake anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Kenaka makolowo anayamba kugwiritsa ntchito zimene amaphunzirazo pamoyo wawo. Kodi zimenezi zinakhudza bwanji ana awo?
Franciszek akufotokoza kuti: “Anawo anaona kuti ndinasiya kumwa moŵa ndipo ndinakhala tate wabwino kuposa kale. Iwo ataona zimenezi, anafuna kuzidziŵa bwino Mboni za Yehova. Nawonso anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anasiya kucheza ndi anzawo a makhalidwe oipa.” Rafał, mwana wake wamwamuna, anati: “Ndinayamba kuwakonda bambo anga ngati kuti anali mnzanga.” Iye akupitiriza kuti: “Gulu la zigaŵenga limene ndimayenda nalo mwadzidzidzi linakhala losafunikanso. Tinali ndi zinthu zambiri zauzimu zochita.”
Franciszek tsopano ndi mkulu wachikristu mu mpingo wa Mboni za Yehova, ndipo amachitabe chidwi kwambiri ndi banja lake ndi kupita patsogolo kwauzimu kwa aliyense m’banjamo. Mkazi wake ndi Lidia ndi apainiya, olalikira uthenga wabwino nthaŵi zonse. Rafał ndi mchemwali wake wamng’ono, Sylwia, amachita nawo phunziro la Baibulo, amayankha pa misonkhano yachikristu, ndipo amauza ena chikhulupiriro chawo, ndipo amachita zonsezi ndi mtima wonse.
Anachita Zimene Ankaphunzitsa
Taganiziraninso zimene zinachitikira Luis, bambo ake a Macarena. Paja ameneyu ndi mtsikana wa zaka 21 wa ku Spain amene tinamutchula mu nkhani yoyamba uja. Luis anatengera moyo wa bambo ake, omwe anali achidakwa. Monga momwe Macarena ananenera, bambo akewo ankachoka ndi anzawo, nthaŵi zina kwa masiku angapo. Kuwonjezera apo, akazi awo ankawaona ngati wantchito, osati mnzawo woti azimukonda. Ukwati wawo unali utatsala pang’ono kutha, ndipo Macarena ndi azibale ake aang’ono anali ovutika maganizo kwambiri.
Koma patapita nthaŵi Luis anavomera kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iye akufotokoza kuti: “Ndinayamba kumacheza ndi mkazi wanga ndi ana anga. Tinkachezera limodzi, kudyera limodzi, ndi kuphunzira Baibulo limodzi. Tinkathandizananso kugwira ntchito zapakhomo ndipo tikafuna kusangalala tinkasangalalira limodzi.” Macarena akuti: “Ndinayamba kuona kuti ndili ndi bambo achikondi amene amasamaladi banja lawo.”
Kuwonjezera apo, sikuti Luis anangolimbikitsa banja lake kutumikira Mulungu basi, koma iye anachita zimene ankaphunzitsa. Macarena akufotokoza kuti bambo akewo “anasiya bizinesi yabwino kwambiri, chifukwa choti inkawadyera nthaŵi yambiri koma iwo ankafuna kuthera nthaŵi yambiri pa banja lawo.” Zotsatirapo zake zinali zabwino kwambiri. Macarena akuti: “Chitsanzo chawo chandiphunzitsa kukhala ndi moyo wosalira zambiri ndiponso kuika zinthu zauzimu patsogolo.” Tsopano Macarena ndi mpainiya, ndipo mayi ake ndi azibale ake aang’ono amalimbikira kwambiri mu mpingo wachikristu.
Zimene Anasankha Bwana wa pa Kampani ya Sitima Uja
N’zachionekere kuti tate amene ana amafunikira ndi amene amasankha zinthu moganizira ana akewo. Mwana wachinyamata wa Takeshi Tamura, bwana wa ku Japan amene tinamutchula mu nkhani yapita uja, anali ndi anzake a makhalidwe oipa kwambiri, zimene zikanamubweretsera mavuto aakulu. M’menemo munali mu 1986, chaka chimene Takeshi anaganiza zosiya ntchito yake pa kampani ya Japanese National Railways. Kodi panopa, patatha zaka zopitirira 18, Takeshi amaganiza chiyani za zimene anasankhazo?
Iye ananena posachedwapa kuti: “Ndikuganiza kuti palibenso chinthu china chabwino chimene ndinachita choposa zomwe ndinasankha kuchitazi. Kucheza ndi mwana wanga mokwanira ndi kuchitira naye zinthu limodzi, kuphatikizapo kuphunzira naye Baibulo, kunali ndi zotsatirapo zabwino kwambiri. Tinasanduka mabwenzi, ndipo anasiya kucheza ndi anzake oipa ndiponso anasiya khalidwe lake loipa.”
Mkazi wa Takeshi anakhala wa Mboni za Yehova zaka zingapo m’mbuyomo, ndipo khalidwe lake labwino n’limene linachititsa mwamuna wake kuganiza zophunzira Baibulo ndiponso zosamalira banja lake. Pamapeto pake Takeshi, mwana wake wamwamuna, ndi mwana wake wamkazi onse anakhala Mboni. Tsopano Takeshi ndi mwana wake wamwamuna onse ndi akulu m’mipingo mwawo
ndipo mkazi wake ndi mwana wake wamkazi ndi apainiya.Atate Amafunika Thandizo
Atate ambiri, ngakhale adziŵe kuti akunyalanyaza ana awo, sadziŵa choti awachitire. Nyuzipepala ya ku Spain yotchedwa La Vanguardia tsiku linalake inali ndi mutu wakuti: “Makolo 42 pa makolo 100 Alionse [a ku Spain] Anavomereza Kuti Sadziŵa Mmene Angalerere Ana Awo Achinyamata.” Koma tinganenenso zomwezo zokhudza atate a ana osafika zaka 13 ndi ana amene akungophunzira kumene kuyenda. Mosiyana ndi zimene anthu ambiri amaganiza, ana aang’onoŵa nawonso amafunika kuti atate awo azicheza nawo ndiponso aziwasamalira.
Kodi tingaphunzirenso zina zotani za mmene munthu angakhalire tate wabwino? Kodi ndani amene ali zitsanzo zabwino kwambiri zoti atate angatengere, ndipo tingaphunzire chiyani kwa iwo? Nkhani yathu yomaliza iyankha mafunso ameneŵa.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Onani mutu wakuti “Mabanja a Kholo Limodzi Akhoza Kupambana!” m’buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Zithunzi patsamba 23]
Atate amene anapatsa ana awo zomwe anawo ankafunikira
Franciszek ndi banja lake
Luis ndi banja lake
Takeshi ndi banja lake