Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chinthu Chabwino Kuposa Kutchuka

Chinthu Chabwino Kuposa Kutchuka

Chinthu Chabwino Kuposa Kutchuka

YOSIMBIDWA NDI CHARLES SINUTKO

M’chaka cha 1957 ndinapatsidwa mwayi wa ntchito yoimba ku Las Vegas, Nevada, ku United States, yoti azindilipira madola 1,000 pa mlungu, ndiponso panali mwayi woti ndikanatha kuimba kwa milungu ina 50 ngati anthu akanakonda nyimbo zangazo. Zimenezo zinatanthauza kuti ndikanapeza ndalama zina zokwana madola 50,000, zimene zinali ndalama zambiri pa nthaŵi imeneyo. Ndikufuna ndikufotokozereni chimene chinachititsa kuti ndipeze ntchito yabwino ngati imeneyo, ndi chimene chinachititsa kuti kuvomera kapena kukana ntchito imeneyi kukhale kovuta kwambiri.

BAMBO anga, omwe kwawo kunali ku Ukraine, anabadwira kum’maŵa kwa Ulaya mu 1910. Mu 1913 mayi awo anabwera nawo ku United States, kumene amuna awo anali kukhala. Bambo anakwatira mu 1935 ndipo ine ndinabadwa chaka chotsatiracho m’tawuni ya Ambridge, ku Pennsylvania. Chapanthaŵi imeneyo, azikulu awo aŵiri a Bambo anakhala Mboni za Yehova.

Ine ndi azing’ono anga atatu tili ana, banja lathu linkakhala pafupi ndi mzinda wa New Castle, ku Pennsylvania, ndipo mayi athu anaphunzira Baibulo kwa nthaŵi yochepa ndi Mboni. Makolo anga onse aŵiri sanakhale Mboni panthaŵi imeneyo, koma Bambo ankakhulupirira kuti azikulu awo anali ndi ufulu wokhulupirira zimene ankafuna kukhulupirira. Ngakhale kuti Bambo anatilera kuti tizinyadira dziko lathu, nthaŵi zonse ankanena kuti anthu ali ndi ufulu wolambira monga momwe akufunira.

Ntchito Yoimba

Makolo anga ankakhulupirira kuti ndinabadwa ndi mawu abwino oimbira, choncho anachita zonse zomwe akanatha kuti andithandize kupititsa patsogolo luso langalo. Pamene ndinali ndi zaka sikisi kapena seveni, Bambo ankandiimiritsa pa kauntala ya kumalo omwera moŵa kuti ndiimbe nyimbo ndi gitala yanga. Ndinkaimba nyimbo yakuti “Mayi.” Nyimboyo inkafotokoza makhalidwe a mayi wachikondi ndipo inkatha ndi mawu okwera okhudza mtima kwambiri. Anthu amene anali m’nyumba yomwera moŵayo, amene nthaŵi zambiri ankakhala ataledzera, ankagwetsa misozi n’kumaponya ndalama mu chipeŵa cha Bambo chimene ankachiyendetsa pakati pa anthuwo.

Ndinakhala ndi pulogalamu yanga yoyamba ya pawailesi kunyumba yamphepo ya WKST ku New Castle mu 1945, ndipo ndinkaimba nyimbo za chamba cha country. Kenaka ndinasintha n’kuyamba kuimba nyimbo zotchuka zimene zinkaimbidwa pa pulogalamu ya pawailesi yotchedwa Hit Parade, yomwe ankaimbapo nyimbo teni zotchuka kwambiri mlungu umenewo. Ndinaoneka pa TV koyamba mu 1950 pa pulogalamu ya Paul Whiteman. Nyimbo imene Paul Whiteman anaimba yakuti “Rhapsody in Blue” yolembedwa ndi George Gershwin ikadali yotchuka mpaka pano. Patapita nthaŵi yochepa Bambo anagulitsa nyumba yathu ya ku Pennsylvania ndipo tinasamukira ku Los Angeles, ku California, n’cholinga chofuna kupititsa patsogolo ntchito yanga yoimba.

Chifukwa cha khama la Bambo, pasanapite nthaŵi yaitali ndinakhala ndi pulogalamu yangayanga ya mlungu uliwonse ya pawailesi ku Pasadena ndi pulogalamu ina ya mphindi 30 mlungu uliwonse pa TV ku Hollywood. Ndinakajambulitsa nyimbo zanga ku situdiyo yotchedwa Capitol Records ndi bandi ya anthu 100 ya Ted Dale ndiponso ndinayamba kuimba pawailesi ya CBS. Mu 1955 ndinapita ku Lake Tahoe ku California kukaonetsa seŵero langa lophatikizana n’kuimba. Ndili kumeneko, zinthu zofunika pamoyo wanga zinasintha kwambiri.

Kuyamba Kuona Zinthu Zina Kukhala Zofunika

Chapanthaŵi imeneyo, Bambo aakulu, a John, amene analinso atasamukira ku California kuchoka ku Pennsylvania, anandipatsa buku lotchedwa “Mulungu Akhale Woona.” * * Ndinapita nalo ku Lake Tahoe. Seŵero lathu lomaliza litatha, chapakati pa usiku, ndinayamba kuŵerenga bukulo ndisanagone. Ndinasangalala kwambiri kupeza mayankho a m’Baibulo a mafunso amene ndinakhala ndikudzifunsa kwa nthaŵi yaitali.

Pasanathe nthaŵi yaitali, ndinayamba kumatsalira m’nyumba yomwera moŵa tikamaliza ntchito yathu n’kumacheza ndi asangalatsi anzanga, ndipo nthaŵi zambiri tinkacheza mpaka mbandakucha. Tinkakambirana nkhani monga zoti munthu akafa amapita kuti, chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti tizivutika, ndiponso kaya anthu pamapeto pake adzadziwononga okha ndi dziko lapansili. Patapita miyezi yochepa, pa July 9, 1955, ndinabatizidwa posonyeza kudzipatulira kwanga kuti nditumikire Yehova Mulungu, pamsonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova umene unachitikira pabwalo la maseŵero la Wrigley Field, ku Los Angeles.

Pasanathe miyezi sikisi, m’maŵa wa pa Khirisimasi mu 1955, wa Mboni mnzanga dzina lake Henry Russell, anandipempha kuti ndipite naye kukachezera Jack McCoy, amene analinso msangalatsi wa anthu. Henry anali woyang’anira za nyimbo ku wailesi ya NBC. Titafika, Jack anauza ana ake atatu ndi mkazi wake kuti akhale pansi amvetsere, ngakhale kuti tinawapeza akutsegula mphatso zawo za Khirisimasi. Iye ndi banja lake anakhala Mboni pasanapite nthaŵi yaitali.

Chapanthaŵi imeneyi ndinaphunzira ndi Mayi, ndipo anagwiritsadi choonadi cha m’Baibulo. Kenaka anakhala wa Mboni za Yehova ndiponso mpainiya, wolengeza ufumu nthaŵi zonse. Ndiyeno azing’ono anga atatu nawonso anabatizidwa ndipo anachita utumiki waupainiya kwakanthaŵi. Mu September 1956, ndili ndi zaka 20, ndinakhala mpainiya.

Zosankha Zokhudza Ntchito

Chapanthaŵi imeneyi George Murphy, mnzake wa bwana wanga, anayamba kukhala ndi chidwi chofuna kupititsa ntchito yanga patsogolo. George anachita nawo mafilimu ambiri m’zaka za m’ma 1930 ndi 1940. Mu December 1956, chifukwa cha anthu amene George anali kudziŵana nawo, ndinaoneka pa TV pa pulogalamu ya Jackie Gleason mu mzinda wa New York pa TV ya CBS. Zimenezi zinali zofunika kwambiri popititsa patsogolo ntchito yanga chifukwa pulogalamu imeneyo inkaonedwa ndi anthu pafupifupi 20,000,000. Ndili ku New York, ndinakayendera likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn kwa nthaŵi yoyamba.

Nditaoneka pa pulogalamu ya Jackie Gleason, ndinavomera kugwira ntchito yopanga mafilimu ku situdiyo ya MGM kwa zaka seveni. Ndinapatsidwa ntchito yoti ndizioneka nthaŵi zonse pa pulogalamu inayake ya pa TV. Koma patapita nthaŵi chikumbumtima changa chinayamba kundivutitsa chifukwa ndinayenera kuchita mbali ya munthu wotchova juga ndiponso katswiri woombera mfuti, ndipo mbali zimenezi zinkasonyeza chiwerewere ndi makhalidwe ena osemphana ndi Chikristu ngati zinthu zabwino. Choncho ndinasiya ntchito imeneyo. Asangalatsi anzanga anaganiza kuti ndapenga.

Zimenezi zikutibweretsa ku ntchito yabwino kwambiri imene ndinapatsidwa ku Las Vegas, yomwe ndinaitchula koyambirira ija. Ndinayenera kuyamba ntchitoyo mlungu umene woyang’anira woyendayenda amadzachezera mpingo wathu. Ngati sindikanavomera kuyamba ntchitoyo panthaŵi imeneyo, sakanandilembanso n’komwe. Sindinkadziŵa kuti ndichite chiyani, chifukwa Bambo anakhala akuyembekezera kwa nthaŵi yaitali kuti ndipange ndalama zambiri. Ndinaganiza kuti ndinafunika kuwabwezera kenakake chifukwa cha ntchito yonse yomwe anachita popititsa patsogolo ntchito yanga.

Choncho ndinalankhula ndi Carl Park, woyang’anira wotsogolera wathu yemwe anali woimba ndipo panthaŵi ina ankaimba bangwe pawailesi ya WBBR ku New York m’ma 1920. Ndinamufotokozera kuti ndikavomera ntchito imeneyi, nditha kuchita upainiya moyo wanga wonse osadandaulanso za ndalama. Iye anati: “Sindingakuuze chochita, koma ndingakuthandize kuganiza.” Ndiyeno anandifunsa kuti, “Kodi mtumwi Paulo akanakhala kuti akudzayendera mpingo wathu mlungu uno ukanachoka?” Ndipo anawonjezera kuti, “Kodi ukuganiza kuti Yesu angafune kuti uchite chiyani?”

Ndinaganiza kuti zimenezo zinali zomveka kwabasi. Nditawauza Bambo kuti ndaganiza zokana ntchito ya ku Las Vegas ija, ananena kuti ndikuwasokonezera moyo wawo. Madzulo ake anandidikirira kuti ndibwere atanyamula mfuti. Ankafuna kuti andiphe, koma anagwidwa ndi tulo, mwachionekere chifukwa choledzera. Kenaka anayesera kudzipha mu galaja ndi utsi wa galimoto. Ndinaitana opulumutsa anthu, ndipo anatha kuwatsitsimutsa.

Podziŵa zoti Bambo sankachedwa kupsa mtima, anthu ambiri mu mpingo mwathu ankawaopa, koma woyang’anira dera wathu, Roy Dowell sanachite nawo mantha. Roy atapita kukawaona, Bambo anamuuza kuti pamene ineyo ndinabadwa, zinkaoneka ngati mwina sindikhala ndi moyo. Bambo analonjeza kwa Mulungu kuti ngati ndipulumuka, adzandipereka kwa iye kuti ndimutumikire. Roy anawafunsa ngati anaganizapo zoti mwina Mulungu amafuna kuti akwaniritse lonjezo lawolo. Zimenezo zinawadabwitsa kwambiri Bambo. Kenaka Roy anawafunsa kuti: “Ngati panalibe cholakwika chilichonse kuti Mwana wa Mulungu achite utumiki wa nthaŵi zonse, n’chifukwa chiyani mukuona ngati m’polakwika kuti mwana wanu achite zomwezo?” Ndi funso limenelo, Bambo anandisiya kuti ndichite zomwe ndikufuna.

Kenaka, mu January 1957, mtsikana winawake dzina lake Shirley Large anabwera kuchokera ku Canada ndi mnzake amene anali kuchita naye upainiya kudzachezera anzake. Ine ndi Shirley tinadziŵana pamene tinapitira limodzi mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba limodzi ndi mnzake amene anali kuchita naye upainiya uja. Patapita nthaŵi yochepa, Shirley anandiperekeza ku Hollywood Bowl, kumene ndinakaimba ndi Pearl Bailey.

Kuchita Zimene Ndinasankha

Mu September 1957, ndinapatsidwa ntchito yokatumikira monga mpainiya wapadera ku chigawo cha Iowa. Nditawauza Bambo kuti ndavomera ntchito imeneyo, iwo analira. Sanali kumvetsa kaonedwe kanga katsopano ka zinthu zimene zinalidi zofunika. Ndinapita ku Hollywood ndipo ndinakafufutitsa ntchito zanga zonse. Mtsogoleri wotchuka wa bandi ndi kwaya dzina lake Fred Waring anali mmodzi wa anthu amene ndinayenera kuwagwirira ntchito. Anandiuza kuti sindidzagwiranso ntchito yoimba ngati sindikwaniritsa zimene ndinalonjezazo. Choncho ndinamufotokozera kuti ndinali kusiya ntchito yanga yoimba kuti ndizitha kuchita zambiri potumikira Yehova Mulungu.

A Waring anamvetsera mwatcheru nthaŵi yonse imene ndinali kulankhula, ndiyeno anandidabwitsa poyankha modekha kuti: “Mwanawe, ndikumva chisoni kuti ukusiya ntchito yabwino chonchi yoimba, koma ndakhala ndikugwira ntchito yoimba moyo wanga wonse ndipo ndaphunzira kuti pali zinthu zinanso zofunika pamoyo kuposa nyimbo. Mulungu adalitse zimene ukufuna kukachitazo.” Ndikukumbukirabe kuti ndinali ndi chimwemwe chodzadza tsaya mpaka ndinagwetsa misozi pamene ndinali kuyendetsa galimoto kubwerera kunyumba, pozindikira kuti tsopano ndinali womasuka kugwiritsa ntchito moyo wanga kutumikira Yehova.

“Kodi Chikhulupiriro Chako Chili Kuti?”

Ndinayamba kutumikira m’tawuni ya Strawberry Point, ku Iowa, ya anthu mwina 1,200 ndi mnzanga Joe Triff. Shirley anabwera kudzandichezera, ndipo tinakambirana za ukwati. Ndinalibe ndalama zilizonse zimene ndinasunga, ndipo iyenso analibe. Ndalama zonse zimene ndinali nditapanga ankaziyendetsa ndi bambo anga. Choncho ndinamufotokozera kuti: “Ndikufuna kukukwatira, koma kodi tizidzakhala bwanji? Ndalama zimene ndili nazo ndi zimene apainiya apadera amapatsidwa, madola 40 pamwezi basi.” Akulankhula modekha, koma mosapita m’mbali, monga momwe amachitira nthaŵi zonse, Shirley anandiyankha kuti: “Koma, Charles, kodi chikhulupiriro chako chili kuti? Yesu anati ngati tifunafuna choyamba Ufumu ndi chilungamo chake, adzatiwonjezera zonse zimene tikufunikira.” (Mateyu 6:33) Basi, tinadziŵa chochita. Tinakwatirana pa November 16, 1957.

Ndinkaphunzira Baibulo ndi mlimi winawake kufupi ndi Strawberry Point. Pakhomo pa mlimiyu panali nyumba ina yaing’ono kwambiri yamatabwa. Nyumbayo inalibe magetsi kapena madzi, ndiponso inali ndi chimbudzi chapanja. Koma ngati tikanafuna, tikanatha kukhala m’nyumba imeneyo kwaulere. Inali yachikale kwambiri, koma tinaganiza kuti popeza tsiku lonse tizikhala tili mu utumiki, timangofunikira malo ogona basi.

Ndinkakatunga madzi pa chitsime chapafupi. Tinkatenthetsa m’nyumbamo ndi moto wa nkhuni ndipo tinkaŵerengera nyali ya palafini. Shirley ankaphikira sitovu ya palafini. Posamba tinkagwiritsa ntchito bafa lakalekale lochapira zovala. Tinkamva kulira kwa nkhandwe usiku ndipo tinkaona kuti tinali amwayi kwambiri chifukwa chokhalira limodzi ndiponso chifukwa chotumikira Yehova limodzi kumalo kumene kumafunika kwambiri atumiki achikristu. Bill Malenfant ndi mkazi wake Sandra, amene tsopano akutumikira kulikulu la padziko lonse ku Brooklyn, anali apainiya apadera ku Decorah, ku Iowa, womwe unali mtunda wa makilomita pafupifupi 100 kuchoka komwe ife tinali. Nthaŵi ndi nthaŵi ankabwera kudzationa ndipo tinkapitira limodzi mu utumiki wa kumunda tsiku lonse. Patapita nthaŵi, tinakhala ndi kampingo kakang’ono ka anthu pafupifupi 25 ku Strawberry Point.

Kuyamba Ntchito Yoyendayenda

Mu May 1960 anatipempha kuti tiyambe utumiki woyang’anira dera. Dera lathu loyamba linali ku North Carolina, ndipo linaphatikizapo mizinda ya Raleigh, Greensboro, ndi Durham, ndi timatawuni tina tating’ono tambirimbiri. Tinayamba kukhala m’malo abwinopo chifukwa mabanja ambiri amene tinkakhala nawo anali kukhala m’nyumba za magetsi ndiponso anali ndi zimbudzi za m’nyumba. Koma zimene anali kutiuza anthu amene anali ndi zimbudzi zapanja zinali zochititsa mantha. Ankatichenjeza kuti tisamale kuti tisaponde mphiri ndi njoka zina tikamapita ku chimbudzi!

Kumayambiriro kwa 1963 anatisintha kutisamutsira ku dera la ku Florida, kumene ndinadwala matenda aakulu otupitsa minofu ya mtima ndipo ndinatsala pang’ono kufa. Mwina ndikanafa pakanapanda Bob ndi Ginny Mackey a ku Tampa. * Iwowa anandipititsa kwa dokotala wawo mpaka anandilipirira ndalama zonse kuchipatalako.

Kugwiritsa Ntchito Zimene Ndinaphunzira Ndili Wamng’ono

M’chilimwe cha mu 1963, anandipempha kuti ndikagwire ntchito ku New York yokhudzana ndi msonkhano waukulu wa Mboni za Yehova umene unali kudzachitikira kumeneko. Ndinapita limodzi ndi Milton Henschel, woimira Mboni za Yehova, ku pulogalamu yocheza ndi anthu pawailesi yomwe ankachititsa ndi Larry King. Mpaka pano a King akadali munthu wotchuka wochititsa pulogalamu yocheza ndi anthu pa TV. Anatilandira mwaulemu kwambiri, ndipo kwa pafupifupi ola lathunthu pulogalamuyo itatha, anatifunsa mafunso ambiri okhudza ntchito yathu.

Chilimwe chomwecho, Harold King, mmishonale amene anali atangotuluka kumene kundende ku China, dziko lachikomyunizimu, anabwera kudzacheza kulikulu lapadziko lonse la Mboni. Madzulo enaake analankhula kwa anthu pafupifupi 700, ndipo anafotokoza zimene anakumana nazo ndiponso kuti zaka zopitirira zinayi zimene anakhala m’ndende m’chipinda chayekhayekha zinalimbitsa chikhulupiriro chake. Ali m’ndende, analemba nyimbo zokhala ndi nkhani zokhudza Baibulo ndi utumiki wachikristu.

Madzulo osaiwalika amenewo, ine limodzi ndi Audrey Knorr, Karl Klein, ndi Fred Franz, amene anakhala Mboni kwa nthaŵi yaitali ndiponso amene anali ndi mawu ophunzitsidwa bwino oimbira, tinaimba limodzi nyimbo yakuti “Kumka Kunyumba ndi Nyumba,” imene kenaka inadzaikidwa m’buku la nyimbo limene Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito. Nathan Knorr, amene kenaka anadzatsogolera ntchito ya Mboni, anandipempha kuti ndikaimbe nyimbo imeneyo mlungu wotsatira pamsonkhano wa “Uthenga Wabwino Wosatha” ku Yankee Stadium, ndipo ndinakaimbadi.

Zokumana Nazo mu Ntchito Yoyendayenda

Panthaŵi imene tinali kutumikira ku Chicago, Illinois, panachitika zinthu ziŵiri zosaiwalika. Choyamba, pamsonkhano wadera, Shirley anakumana ndi Vera Stewart, amene analalikira kwa Shirley ndi mayi ake ku Canada chapakati pa m’ma 1940. Shirley, amene anali ndi zaka 11 panthaŵiyo, anasangalala kwambiri kumva malonjezo a Mulungu a m’Baibulo. Anafunsa Vera kuti, “Kodi mukuganiza kuti ineyo ndingathe kudzakhala m’dziko latsopano limenelo?” Vera anayankha kuti, “Sindikuona chifukwa chilichonse chimene sungadzakhaliremo, Shirley.” Aŵiri onseŵa sanaiwale mawu amenewo, ndipo ankawakumbukira ndendende. Kungoyambira pa kukumana kwawo koyambako, Shirley anadziŵa kuti chimene ankafuna kuchita ndicho kutumikira Yehova.

Chachiŵiri, Mboni inayake inandifunsa ngati ndinkakumbukira kuti ndinapeza thumba la mbatata lolemera makilogalamu pafupifupi 22 pakhonde pa nyumba yathu m’nyengo yachisanu mu 1958. Indedi, ndinakumbukira. Tinalipeza titavutika kuti tikafike kunyumba kwathu chifukwa cha chipale chofewa chambiri chimene chinali kugwa madzulo amenewo. Ngakhale sitinadziŵe kumene mbatatayo inachokera, tinayamikira Yehova chifukwa chotipatsa mphatso imeneyo. Tinalephera kutuluka m’nyumbamo kwa mlungu wathunthu chifukwa cha kuchuluka kwa chipale chofewa, koma tinasangalala kudya makeke a mbatata, mbatata yowotcha, tchipisi, futali wa mbatata ya kachewere, ndi supu wa mbatata! Tinalibenso chakudya china. Mboniyo sinkatidziŵa ndiponso sinkadziŵa kumene tinali kukhala, koma inali itamva kuti apainiya enaake chapafupipo anali kuvutika. Iye anati chinachake chinamuchititsa kuyamba kufunsa kumene banja lachinyamata limeneli linali kukhala. Alimi amadziŵa zonse zokhudza anthu okhala nawo pafupi, choncho sanachedwe kumulozera ku nyumba yathu ndipo ananyamula thumba la mbatatalo chipale chofewa chili m’kati kugwa.

Ndikuthokoza Kuti Ndinasankha Bwino

Pofika mu 1993, nditatha zaka 33 ndili mu ntchito yoyendayenda, thanzi langa linali lofooka kwambiri moti ndinayenera kusiya mwayi wa utumiki umenewo. Ine ndi Shirley tinakhala apainiya apadera opereka maola ochepa chifukwa cha thanzi lofooka, ndipo tikadali choncho mpaka pano. Ngakhale ndimamva chisoni kuti ndilibenso mphamvu zochitira ntchito yoyendayenda, ndimasangalala kuti ndinagwiritsa ntchito mphamvu zanga m’njira imeneyo.

Azing’ono anga atatu anasankha zinthu zosiyana ndi zimenezo. Aliyense wa iwo pomalizira pake anaganiza zopanga chuma, ndipo panopa palibe aliyense wa iwo amene akutumikira Yehova. Mu 1958, Bambo anabatizidwa. Iwo ndi Mayi anathandiza anthu ambiri kudziŵa Yehova, kudzipatulira kwa Iye, ndi kubatizidwa. Onse aŵiri anamwalira mu 1999. Choncho zimene ndinasankha, zosiya kutchuka kwa m’dzikoli ndi chuma zinachititsa kuti Bambo, komanso anthu ambiri amene iwo ndi Mayi anawaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo, akhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Nthaŵi zambiri ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi ndikanatha kupitirizabe kutumikira Yehova ndikanakhala kuti sindinasankhe zinthu motere pamoyo wanga?’

Patatha zaka zisanu chisiyireni ntchito ya dera, thanzi langa linawongokerako, ndipo ndinatha kuwonjezera utumiki wanga. Tsopano ndine woyang’anira wotsogolera mu mpingo wina ku Desert Hot Springs, ku California. Ndimakhalanso ndi mwayi wotumikira monga wothandizira pa ntchito yadera, kutumikira pa makomiti apadera, ndipo nthaŵi zina, kuphunzitsa pa Sukulu ya Utumiki Waupainiya.

Mpaka lero, Shirley ndiye bwenzi langa lapamtima. Palibenso wina amene ndimakonda kucheza naye kwambiri kuposa Shirley. Nthaŵi zambiri timakambirana zinthu zauzimu zolimbikitsa, ndipo tonsefe timasangalala ndi mfundo za choonadi cha m’Baibulo zimene timakambirana. Ndimakumbukirabe funso lake lodekha limene anandifunsa zaka zopitirira 47 zapitazo, ndipo ndimaliyamikira kwambiri, loti, “Koma, Charles, kodi chikhulupiriro chako chili kuti?” Akristu okwatirana achinyamata akanati azifunsana funso limenelo, ndikukhulupirira kuti ambiri a iwo angakhalenso ndi chimwemwe ndi madalitso ngati amene takhala nawo mu utumiki wa nthaŵi zonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 John Sinutko anakhalabe Mboni yokhulupirika ya Yehova mpaka imfa yake mu 1996 ali ndi zaka 92.

^ ndime 11 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano anasiya kulisindikiza.

^ ndime 32 Mu Galamukani! yachingelezi ya February 22, 1975, pa masamba 12 mpaka 16, muli nkhani imene Bob Mackey anasimba ya mmene anavutikira atafa ziwalo.

[Chithunzi patsamba 16]

Bambo aakulu, a John mu 1935, chaka chimene anabatizidwa

[Chithunzi patsamba 17]

Nyumba yathu yamatabwa

[Chithunzi patsamba 18]

Chithunzi cha mu 1975 cha makolo anga, amene anakhala okhulupirika mpaka imfa yawo

[Chithunzi patsamba 18]

Ine ndi Shirley masiku ano