Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Landisintha Kwambiri”

“Landisintha Kwambiri”

“Landisintha Kwambiri”

Zimenezo ndi zimene mnyamata wa zaka 12 wa ku Virginia, ku United States, analemba zokhudza buku latsopano lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Iye anati linamuphunzitsa zinthu zimene sankazidziŵa ndipo anali asanazimvepo. Anafotokoza kuti:

“Buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso landiphunzitsa kuti ndizikonda Mulungu nthaŵi zonse, ndizilankhula za iye kwa munthu aliyense, ndipo ndizilankhula naye m’pemphero. Landiphunzitsanso kuti ndizipempha Mulungu kuti andithandize ndi kunditeteza. Ndinaphunzira kuti aliyense amene amakonda Mulungu ndi kuchita zimene Mulunguyo amalamula adzakhala m’Paradaiso.

“Landisintha kwambiri. Ndinkanena bodza nthaŵi zonse, koma nditayamba kuŵerenga buku limeneli ndinasiya kunama. Zinthu zimene ndaphunzira m’buku limeneli zandichititsa kufuna kuŵerenga mabuku ena okhala ngati ameneŵa. Choncho ndingasangalale kuŵerenga mabuku ena ndi kudziŵa zambiri za Mulungu.”

Mwina nanunso mudzamva chimodzimodzi mukaŵerenga buku lokhala ndi zithunzi zokongola limeneli la masamba 256 amene kukula kwake n’chimodzimodzi ndi masamba a magazini ino. Nanunso mungasangalale kuŵerenga mitu monga yakuti, “Yesu Atiphunzitsa Kupemphera,” “Phunziro la Kukhala Wokoma Mtima,” “Mmene Tingakhalire Osangalala,” ndi “Chifukwa Chake Tiyenera Kupewa Bodza.” Mungathe kuitanitsa buku limeneli polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.

[Chithunzi patsamba 32]

Kuphunzitsa mwana kuti asamaname