Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mapeto a Tsankho

Mapeto a Tsankho

Mapeto a Tsankho

KODI ifeyo patokha tikuona kuti tili ndi tsankho? Mwachitsanzo, kodi timaganiza kuti munthu ali ndi khalidwe linalake pongoona mtundu wa khungu lake, dziko lake, kapena fuko lake, ngakhale kuti munthuyo sitikumudziŵa? Kapena kodi timaona zabwino za munthu aliyense payekha poona makhalidwe amene ali nawo?

Panthaŵi ya Yesu, anthu ambiri amene ankakhala ku Yudeya ndi Galileya ‘sanali kuyenderana nawo Asamariya.’ (Yohane 4:9) Mawu amene analembedwa m’buku la miyambo ya Ayuda lotchedwa Talmud mosakayikira anasonyeza mmene Ayuda ambiri ankamvera. Mawuwo amati: “Chonde ndisaonane ndi Msamariya.”

Ngakhale atumwi a Yesu ayenera kuti ankasonyeza tsankho ndithu kwa Asamariya. Panthaŵi inayake, Asamariya a m’mudzi winawake sanawalandire bwino atumwiwo. Yakobo ndi Yohane anapempha kuti aitanitse moto kuchokera kumwamba kuti unyeketse anthu osafuna kumvawo. Yesu anawadzudzula powasonyeza kuti khalidwe lawolo linali loipa.—Luka 9:52-56.

Kenaka Yesu anafotokoza fanizo la munthu amene anaukiridwa ndi achifwamba akuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko. Ayuda aŵiri opembedza amene anamudutsa sanafune kumuthandiza. Koma Msamariya wina anaima n’kumanga mabala a munthuyo. Kenaka anakonza zoti munthuyo asamalidwe mpaka mabala akewo atapola. Msamariya ameneyo anasonyeza kuti analidi mnansi weniweni. (Luka 10:29-37) Fanizo la Yesulo liyenera kuti linathandiza omvetsera ake kuzindikira kuti anatsekeka m’maso ndi tsankho lawolo moti sankatha kuona makhalidwe abwino a ena. Zaka zingapo izi zitachitika, Yohane anabwereranso ku Samariya ndipo analalikira m’midzi yambiri kumeneko, mwina kuphatikizapo mudzi umene ankafuna kuti uwonongedwe uja.—Machitidwe 8:14-17, 25.

Mtumwi Petro nayenso anafunika kuchita zinthu mopanda tsankho pamene mngelo anamuuza kuti akalankhule za Yesu kwa Korneliyo, kazembe wankhondo wachiroma. Petro anali asanazolowere kuchita zinthu ndi anthu amene sanali Ayuda, ndipo Ayuda ambiri sankakonda asilikali achiroma. (Machitidwe 10:28) Koma Petro atazindikira kuti ndi Mulungu amene anali kumutsogolera, anati: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”—Machitidwe 10:34, 35.

Chifukwa Cholimbanirana ndi Tsankho

Tsankho limaphwanya mfundo yofunika kwambiri imene Yesu anaphunzitsa, yoti: “Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Ndani angafune kudedwa chifukwa cha kumene anabadwira, mtundu wa khungu lake, kapena mmene anakulira basi? Tsankho limaphwanyanso mfundo ya Mulungu yoti anthu onse ndi ofanana. Baibulo limaphunzitsa kuti mwa munthu mmodzi, Yehova “analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi.” (Machitidwe 17:26) Choncho anthu onse ndi apachibale.

Kuwonjezera apo, Mulungu amaweruza munthu aliyense payekha. Mulungu salanga munthu chifukwa cha zimene makolo ake anachita. (Ezekieli 18:20; Aroma 2:6) Ngakhale titakhala kuti tinazunzidwa ndi dziko linalake, chimenecho si chifukwa chokwanira chodana ndi anthu onse ochokera dziko limenelo, amene mwina sanachite nawo n’komwe zinthu zoipazo. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti ‘akonde adani awo, ndi kupempherera iwo akuwazunza.’—Mateyu 5:44, 45.

Chifukwa cha ziphunzitso ngati zimenezi, Akristu a m’zaka 100 zoyambirira anatha kugonjetsa tsankho n’kukhala abale apadziko lonse. Ankaitanana kuti mbale ndi mlongo, ndipo ankachitirana zinthu ngati analidi apachibale, ngakhale kuti anali ochokera m’mitundu yosiyanasiyana. (Akolose 3:9-11; Yakobo 2:5; 4:11) Mfundo zimene zinabweretsa kusintha kumeneko zingathandizenso masiku ano.

Kulimbana ndi Tsankho Masiku Ano

Pafupifupi tonsefe timakhala ndi maganizo olakwika a mmene timaonera ena, koma maganizo ameneŵa sayenera kuyambitsa tsankho. Buku lakuti The Nature of Prejudice limati: “Kuganiza molakwika kumasanduka tsankho kokha ngati munthu sakufuna kusintha atadziŵa zinthu zatsopano.” Nthaŵi zambiri tsankho likhoza kutha anthu akadziŵana bwino. Komabe, buku lomwelo limati, “kucheza kokhako kumene kumathandiza anthu kuchitira zinthu limodzi n’kumene kungachititse anthu kusintha maganizo awo.”

Mmenemu ndi mmene John wa ku Nigeria wa fuko la Ibo anathetsera tsankho lake kwa anthu a fuko la Hausa. Iye anati: “Ndili kuyunivesite ndinakumana ndi ophunzira ena a fuko la Hausa amene anakhala anzanga, ndipo ndinazindikira kuti anali ndi makhalidwe abwino kwambiri. Ndinachita ntchito inayake ya kusukulu ndi wophunzira winawake wa fuko la Hausa, ndipo tinachita zinthu mogwirizana kwambiri, pamene mnzanga amene ndinkagwira naye ntchitoyo kale, amene anali wa fuko la Ibo, ankangochita zaulesi.”

Chida Cholimbanirana ndi Tsankho

Malinga ndi lipoti lotchedwa UNESCO Against Racism, “maphunziro angakhale chida chamtengo wapatali cholimbanirana ndi mitundu yatsopano ya tsankho, kusalana, ndi kupatulana.” Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti maphunziro a m’Baibulo ndi amene amathandiza kwambiri pankhani imeneyi. (Yesaya 48:17, 18) Anthu akamatsatira zimene Baibulo limanena, amasiya kukayikirana n’kumalemekezana ndipo chidani chimatha chifukwa cha chikondi.

Mboni za Yehova zaona kuti Baibulo limathandiza pothetsa tsankho. Ndipo Baibulo limawapatsa chifukwa choti alimbanirane ndi tsankho ndiponso mwayi wochita zinthu ndi anthu a mafuko osiyanasiyana. Christina, amene mawu ake akupezeka mu nkhani yoyambirira ya nkhani zino, ndi wa Mboni za Yehova. Iye anati: “Misonkhano yathu ku Nyumba ya Ufumu imandichititsa kumva kuti ndine munthu wofunika. Ndimamva kuti ndine wotetezeka ndikakhala kumeneko chifukwa ndimaona kuti palibe amene akundichitira tsankho.”

Jasmin, amene alinso wa Mboni, akukumbukira kuti anayamba kuchitiridwa tsankho ali ndi zaka nayini. Iye anati: “Lachinayi ndi tsiku limene nthaŵi zonse limakhala losangalatsa kwa ine chifukwa madzulo ake ndimapita ku Nyumba ya Ufumu. Kumeneko anthu amandikonda ndipo ndimamva kuti ndine munthu wapadera, osati wosafunika.”

Ntchito zogwira mongodzipereka zimene Mboni za Yehova zimakonza zimagwirizanitsa anthu osiyanasiyana. Simon anabadwira ku Britain, ngakhale kuti banja lake kwawo ndi kuzilumba za ku Caribbean. Anthu akhala akumuchitira tsankho kwambiri pamene anali kugwira ntchito yomanga nyumba ku makampani osiyanasiyana. Koma zimenezi sizinachitike panthaŵi imene anali kugwirira ntchito limodzi ndi abale ake ofanana naye chikhulupiriro. Simon anafotokoza kuti: “Ndagwira ntchito ndi Mboni zambiri zochokera m’mayiko osiyanasiyana, koma tinaphunzira kugwirira ntchito limodzi bwinobwino. Anzanga ena apamtima kwambiri ndi anthu ochokera m’mayiko ena oti anakula mosiyana kwambiri ndi ineyo.”

N’zoona kuti Mboni za Yehova ndi anthu opanda ungwiro. Choncho angafunike kuti apitirizebe kulimbana ndi maganizo a tsankho. Koma kudziŵa kuti Mulungu alibe tsankho kumawalimbikitsa kuti apitirizebe kuchita zimenezo.—Aefeso 5:1, 2.

Phindu limene limabwera chifukwa cholimbana ndi tsankho n’lalikulu. Tikamacheza ndi anthu osiyanasiyana, timadziŵa zambiri. Kuwonjezera apo, pogwiritsa ntchito Ufumu wake, Mulungu posachedwapa adzakhazikitsa dziko limene anthu ake adzakhala okonda chilungamo. (2 Petro 3:13) Panthaŵi imeneyo, tsankho lidzatheratu mpaka muyaya.

[Bokosi patsamba 11]

Kodi Ndili ndi Maganizo a Tsankho?

Dzifunseni mafunso otsatiraŵa kuti muone ngati mwina mosadziŵa muli ndi tsankho la mtundu winawake:

1. Kodi ndimaganiza kuti anthu a fuko, dera, kapena dziko linalake ali ndi makhalidwe oipa, monga kupusa, ulesi, kapena kuumira? (Nthabwala zambiri zimalimbikitsa tsankho la mtundu umenewu.)

2. Kodi ndimaona kuti alendo amene anadzakhazikika m’dziko mwathu kapena anthu a fuko lina ndi amene akuchititsa kuti ndizikhala ndi mavuto azachuma kapena mavuto ena amene ndimakumana nawo kumene ndimakhala?

3. Kodi ndalolera kuti chidani chimene dera lathu lakhala nacho kuyambira kalekale ndi dziko lina chindichititse kudana ndi anthu ochokera dziko limenelo?

4. Kodi ndimatha kuona munthu aliyense amene ndimakumana naye monga munthu payekha, osayang’ana mtundu wa khungu lake, chikhalidwe chake, kapena fuko lake?

5. Kodi ndimasangalala ndikapeza mpata wodziŵana ndi anthu a chikhalidwe chosiyana ndi changa? Kodi ndimachita khama kuti ndiadziŵe?

[Chithunzi patsamba 8]

Mu fanizo lake la Msamariya wachifundo, Yesu anatiphunzitsa mmene tingathetsere tsankho

[Chithunzi patsamba 8]

Kunyumba ya Korneliyo, Petro anati: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu”

[Chithunzi patsamba 9]

Zimene Baibulo limaphunzitsa zimagwirizanitsa anthu osiyanasiyana

[Chithunzi patsamba 9]

Mboni za Yehova zimatsatira zinthu zimene zaphunzira

[Chithunzi patsamba 10]

Christina​—“Misonkhano ya ku Nyumba ya Ufumu imandichititsa kumva kuti ndine munthu wofunika”

[Chithunzi patsamba 10]

Jasmin​—“Anthu amandikonda ndipo ndimamva kuti ndine munthu wapadera, osati wosafunika”

[Zithunzi patsamba 10]

Simon, amene amagwira ntchito yongodzipereka​—“Tinaphunzira kugwirira ntchito limodzi bwinobwino”