Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mudzaŵerenga Liti Zonsezi?”

“Mudzaŵerenga Liti Zonsezi?”

“Mudzaŵerenga Liti Zonsezi?”

Mu July 2001, mwamuna wina wokhala mu mzinda wa Khabarovsk, kum’maŵa kwa Russia, anapeza magazini a Galamukani! okwana 34 mu laibulale ya mumzindawo. Anabwereka magaziniwo, ndipo tsiku loti awabweze litakwana mu August, sanafune kuwabweza. Choncho anawabwerekanso kachiŵiri mpaka mu September. Anawakonda kwambiri magaziniwo moti anawabwerekanso mu November, limodzi ndi magazini ena sikisi atsopano a Galamukani!

Izi zisanachitike, mwamunayo nthaŵi zonse ankapeŵa mabuku achipembedzo. Koma n’chifukwa chiyani anayamba kuŵerenga Galamukani!? “Chifukwa chakuti nkhani zambiri m’magazini imeneyi zimakhala zokhudza mavuto amene anthu amakumana nawo ndipo zimakhala zosangalatsa ndiponso zokhudza munthu aliyense,” iye analemba choncho.

“Nthaŵi zambiri mumakhala nkhani zolembedwa bwino kwambiri zokhudza mizinda yamakono ndi mayiko, kuphatikizapo nkhani zonena za miyambo ya anthu,” anapitiriza choncho mwamunayo. Iye amasangalalanso ndi nkhani za anthu amene zinthu zawayendera bwino pamoyo wawo, amene sanagonje koma anapitirizabe kutsatira mfundo zawo zauzimu, ndipo anathandiza ena kupirira mavuto ndi masoka. Kodi maganizo ake ndi otani pa magazini imeneyi? “Tinganene kuti palibe magazini ina yonena za nkhani zimene zikuchitika panopa, za sayansi, malo osiyanasiyana, ndi chikhalidwe cha anthu osiyanasiyana padziko lonse lapansi, imene ingapose Galamukani!”

Mwamunayo anapempha magazini akale a Galamukani! a m’chinenero cha ku Russia kuyambira a mu 1995 mpaka aposachedwapa. Kuwonjezera pa Galamukani! anapemphanso mabuku ena osiyanasiyana ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Iye analemba kuti: “Mwina mungandifunse kuti ‘mudzaŵerenga liti zonsezi?’” Iye anadziyankha yekha funso lakelo ponena kuti ali ndi nthaŵi yoŵerengera mabuku othandiza chifukwa sawononga nthaŵi yambiri kuonerera TV kapena kugwiritsa ntchito Intaneti.

Magazini ya Galamukani! imakhala ndi nkhani zambiri zochititsa chidwi zimene zikuchitika panopa komanso imasonyeza mmene mavuto amene alipo masiku ano adzathere. Bwanji osapempha Mboni za Yehova kuti zizikubweretserani magazini atsopano a Galamukani! mwezi uliwonse?

[Chithunzi patsamba 31]

Kumvetsetsa Matenda a Maganizo

[Chithunzi patsamba 31]

Kodi Mulungu Mumamudziŵa Dzina Lake?

[Chithunzi patsamba 31]

Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Ingachitikedi?

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Nuclear explosion: U.S. Department of Energy photograph