Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Izi N’zomwe Achinyamata Amafunikira

Izi N’zomwe Achinyamata Amafunikira

Izi N’zomwe Achinyamata Amafunikira

Kwa zaka zambiri, oŵerenga ambiri, achinyamata ndi achikulire omwe, akhala akunena kuti buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, lili ndi zimene achinyamata amafunikira kudziŵa. Mtsikana wina wa zaka za pakati pa 15 ndi 19 wa ku Sinaloa ku Mexico, anapempha mabuku ameneŵa khumi kuti akapatse anzake. Anafotokoza kuti ngakhale kuti iye si wa Mboni za Yehova, amalikonda kwambiri buku limeneli, ndipo anati: “Ndimakulemekezani kwambiri anthu inu.”

Iye anati: “Ndili ndi anzanga ambiri amene ali ndi mafunso ochuluka okhudza moyo wawo masiku ano. Ndinawaonetsa bukuli, ndipo analikonda kwambiri. Buku limeneli ndi labwino kwambiri, ndipo lili ndi zonse zimene wachinyamata angafune kudziŵa.” Iye anafunsa ngati zingatheke kuti alandire mabukuwo asanatsekere sukulu.

Buku la Achichepere Akufunsa lili ndi mitu 39. Ina mwa mitu imeneyi ndi monga: “Kodi Ndingachititse Motani Makolo Anga Kundipatsa Ufulu Wowonjezereka?” “Kodi Ndingapange Motani Mabwenzi Enieni?” “Bwanji Ponena za Kugonana Ukwati Usanachitike?” ndi “Kodi Ndingadziŵe Motani Ngati Chili Chikondi Chenicheni?” Mungathe kuitanitsa buku la masamba 320 limeneli polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.