Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Okalamba Tiyenera Kuwachitira Zinthu Motani?

Kodi Anthu Okalamba Tiyenera Kuwachitira Zinthu Motani?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Anthu Okalamba Tiyenera Kuwachitira Zinthu Motani?

MU CHILIMWE cha mu 2003, anthu masauzande ambiri anafa ku Ulaya chifukwa chakuti kunatentha moipa kwambiri, zimene sizinachitikeponso pa zaka 60 zapitazi. Anthu ambiri amene anafa anali okalamba. Ena anasiyidwa okha ndi achibale awo amene anapita ku tchuthi. Ena akuti ananyalanyazidwa kapena kuiwalidwa ndi anthu ogwira ntchito m’zipatala ndi m’nyumba zosamalira anthu okalamba, amene anachulukidwa ntchito. Nyuzipepala ya Le Parisien inati, ku Paris kokha, mitembo 450 sinadzatengedwe ndi achibale. “Kodi tikukhala moyo wamtundu wanji woti timaiwala azibambo, azimayi, ndi azigogo athu?” inafunsa choncho nyuzipepalayo ponena za anthu amene anafa ali okha ndipo palibe amene anadzawatenga.

M’dzikoli, limene anthu a zaka zopitirira 65 akuwonjezeka ndi anthu 795,000 pa mwezi, kusamalira okalamba tsopano ndi imodzi mwa nkhani zimene zikudetsa nkhaŵa kwambiri masiku ano. Nancy Gordon, amene ndi wothandizira kwa mkulu woyang’anira ntchito zokhudza chiŵerengero cha anthu, m’bungwe loona za kalembera la U.S. Census Bureau, anati: “Padziko lonse lapansi, anthu akukalamba kwambiri kuposa kale lonse ndipo tifunika kuganizira zimene mayiko angachite kuti athane ndi mavuto amene ukalamba umabweretsa ndiponso kuti agwiritse ntchito mpata umenewo kuthandiza okalamba.”

Mlengi wathunso ali ndi chidwi ndi anthu okalamba. Ndipo Mawu ake, Baibulo, amatipatsa malangizo a mmene tiyenera kuchitira ndi okalamba.

Kulemekeza Okalamba

Chilamulo cha Mulungu, chimene anachipereka kwa Mose, chinalimbikitsa kulemekeza okalamba. Chilamulocho chinati: “Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba.” (Levitiko 19:32) Olambira Mulungu omvera anayenera ‘kugwada’ pamene pali aimvi pa zifukwa ziŵiri. (1) Kusonyeza ulemu kwa munthu wachikulireyo. (2) Monga umboni woti munthuyo amaopa Mulungu. Choncho, okalamba anayenera kulemekezedwa ndi kuonedwa monga anthu ofunika kwambiri.—Miyambo 16:31; 23:22.

Ngakhale kuti Akristu masiku ano sayendera Chilamulo cha Mose, mfundo zake zimasonyeza mmene Yehova amaganizira ndi zinthu zimene amaziona kuti n’zofunika, ndipo zimasonyeza bwino kwambiri kuti amaona anthu okalamba monga anthu ofunika kwambiri. Anthu a mu mpingo wachikristu woyambirira ankazimvetsa bwino mfundo zimenezi. Umboni wakale kwambiri wa zimenezi umapezeka m’buku la m’Baibulo la Machitidwe. Panthaŵi imeneyo, pakati pa Akristu a ku Yerusalemu panali akazi amasiye aumphaŵi. Mosakayikira ena a iwo anali okalamba. Atumwi anasankha amuna seveni “a mbiri yabwino” kuti aonetsetse kuti akazi ameneŵa azilandira chakudya tsiku lililonse mwadongosolo, ndipo anaona kuti kusamalira akazi ameneŵa kunali “ntchito” yofunika ya mpingo.—Machitidwe 6:1-7.

Mtumwi Paulo anasonyeza kuti mfundo ‘yogwadira aimvi’ imagwiranso ntchito mu mpingo wachikristu. Anauza Timoteo, amene anali woyang’anira wachikristu wocheperapo msinkhu kuti: “Mkulu usam’dzudzule, komatu um’dandaulire ngati atate; . . . akazi aakulu ngati amayi.” (1 Timoteo 5:1, 2) Ngakhale kuti Timoteo wocheperapoyo anali ndi udindo pa Akristu achikulire, sanayenera kunyoza mwamuna wachikulire. M’malo mwake, anayenera kumudandaulira mwaulemu ngati mmene akanachitira ndi bambo ake. Ndipo anayenera kusonyeza ulemu womwewo kwa akazi achikulire mu mpingo. Pomulangiza zimenezi, mtumwi Paulo anali kulimbikitsa Timoteo, ndipo tingati analinso kulimbikitsa anthu onse mu mpingo wachikristu, kuti ‘pali aimvi azigwada.’

Koma anthu oopa Mulungu sachita kufunikira lamulo kuti achitire ulemu anthu achikulire. Taganizirani chitsanzo cha m’Baibulo cha Yosefe, amene sananyinyirike koma anabweretsa abambo ake achikulire a Yakobo ku Igupto, zimene zinachititsa kuti bambo akewo, amene panthaŵiyo anali ndi zaka 130, asavutike ndi njala imene inali ponseponse nthaŵi imeneyo. Ataona bambo ake kwa nthaŵi yoyamba patatha zaka zopitirira 20, Yosefe ‘anagwera pakhosi pake nakhala m’kulira pakhosi pake.’ (Genesis 46:29) Zaka zambirimbiri Aisrayeli asanapatsidwe lamulo loti azikonda ndi kulemekeza kwambiri okalamba, Yosefe anachita zinthu mogwirizana ndi maganizo a Mulungu.

Panthaŵi ya utumiki wake, Yesu nayenso anasonyeza kuti anali kuganizira okalamba. Anadzudzula mwamphamvu atsogoleri achipembedzo amene ankaona ngati anali ololedwa kunyalanyaza makolo awo okalamba chifukwa cha miyambo yawo yachipembedzo. (Mateyu 15:3-9) Yesu anasamaliranso mayi ake mwachikondi. Akuvutika ndi ululu woopsa pamtengo wozunzirapo, Yesu anakonza zoti mayi ake azisamalidwa ndi mtumwi wake wokondedwa Yohane.—Yohane 19:26, 27.

Mulungu Sataya Anthu Ake Okhulupirika

Wamasalmo anapemphera kuti: “Musanditaye mu ukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga.” (Salmo 71:9) Mulungu ‘sataya’ atumiki ake okhulupirika, ngakhale iwowo aziona ngati atha ntchito. Wamasalmo sanaone ngati Yehova anamutaya, m’malo mwake, anazindikira kuti afunika kudalira Mlengi wake, makamaka pamene anali kukalamba. Yehova akaona munthu wokhulupirika, kapena kuti wachifundo woteroyo, amamuthandiza moyo wake wonse. (Salmo 18:25) Nthaŵi zambiri chithandizo chimenecho chimachokera kwa Akristu anzathu.

Kuchokera pa zimene zanenedwa pamwambapa, n’zachionekere kuti onse amene akufuna kulemekeza Mulungu ayeneranso kulemekeza okalamba. Anthu okalamba ndi a mtengo wapatalidi m’maso mwa Mlengi wathu. Popeza tinalengedwa m’chifanizo chake, tiyeni nthaŵi zonse tiziona anthu a “imvi” monga momwe Mlengi wathu amawaonera.—Salmo 71:18.

[Chithunzi patsamba 17]

Akristu amalemekeza okalamba