Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kumwa Moŵa Wambiri Nthaŵi Imodzi Kuli ndi Vuto Lanji?

Kodi Kumwa Moŵa Wambiri Nthaŵi Imodzi Kuli ndi Vuto Lanji?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Kumwa Moŵa Wambiri Nthaŵi Imodzi Kuli ndi Vuto Lanji?

“Ngakhale kuti tinakhala tikumwa kwa maola angapo, mmene ine ndi mnzanga timachoka kuphwandoko nthaŵi ya 1 koloko m’maŵa tinanyamula botolo la moŵa. Tinayamba kupita kunyumba, kumamwa uku tikuyenda. Kenaka ndinadzidzimuka kuona dzuwa likutuluka ndipo ndinazindikira kuti timaloŵera njira yolakwika. Ndipo tinali kuyenda pakati pa msewu waukulu. Ndi mwayi kuti sitinagundidwe ndi galimoto.”—Anatero Clay. *

KUMWA MOŴA WAMBIRI NTHAŴI IMODZI. Ena amati kumeneku n’kumwa n’cholinga chofuna kuledzera. Lipoti la bungwe loona za kumwa mwauchidakwa lotchedwa U.S. National Institute on Alcohol Abuse and Alcoholism linachita kutchula kuchuluka kwake kwa moŵawo. Linati kumwa moŵa wambiri nthaŵi imodzi “nthaŵi zambiri kumatanthauza kumwa mabotolo asanu kapena kuposa pamenepo nthaŵi imodzi ngati ndinu mwamuna, ndi mabotolo anayi kapena kuposa pamenepo nthaŵi imodzi ngati ndinu mkazi.”

Akuluakulu oona zaumoyo ku United States akuti kumwa moŵa wambiri nthaŵi imodzi ndi “vuto lalikulu limene likuika pangozi umoyo wa anthu.” Malinga ndi kafukufuku amene anachitika pakati pa ophunzira akusekondale ku England, ku Scotland, ndi ku Wales, “ophunzira okwana 25 mwa ophunzira 100 alionse a zaka 13 ndi 14 anati anamwapo mabotolo asanu a moŵa nthaŵi imodzi.” Pafupifupi theka la ophunzira onse a zaka 15 ndi 16 amene anafunsidwa anati anachita chimodzimodzi.

M’kafukufuku wina amene anachitika ku United States, ophunzira akukoleji aŵiri mwa ophunzira 5 alionse anati anamwapo moŵa wambiri nthaŵi imodzi m’milungu iŵiri yam’mbuyomo kafukufukuyo asanachitike. Malinga n’zimene ananena a Unduna wa Zaumoyo ku United States, “achinyamata pafupifupi 10,400,000 a zaka zapakati pa 12 ndi 20 anati anamwapo moŵa. Pa achinyamata amenewo, achinyamata 5,100,000 amamwa moŵa wambiri nthawi imodzi ndipo 2,300,000 amamwa moŵa mwauchidakwa ndipo amamwa moŵa wambiri kasanu pamwezi.” Kafukufuku amene anachitika ku Australia anasonyeza kuti m’dziko limenelo, atsikana ambiri kuposa anyamata amamwa moŵa wambiri nthaŵi imodzi, ndipo amamwa mabotolo 13 mpaka 30 nthaŵi imodzi!

Achinyamata ambiri amene amamwa moŵa chonchi amatero chifukwa chokakamizidwa ndi anzawo. Munthu wina wochita kafukufuku dzina lake Carol Falkowski anati: “Masiku ano kuli maseŵera atsopano ndiponso odzithemba omwera moŵa, monga kukhala pagulu n’cholinga chomwa moŵa mpaka kuledzera. Maseŵera ena ndi oti anthu onse amayenera kumaliza katoti ka kachaso panthaŵi imene pa TV akuonetsa zinazake kapena pamene pagulupo akunena nkhani inayake.”

Kuipa Komwa Moŵa Wambiri Nthaŵi Imodzi

Ngakhale kuti ena angaone kuti kumwa moŵa wambiri ndi maseŵera chabe, ameneŵa ndi maseŵera oopsa kwambiri. Moŵa ukachuluka m’thupi mpweya supita wokwanira ku ubongo, ndipo ziwalo zimene zimagwira ntchito zofunika m’thupi zimayamba kusiya. Zizindikiro zake zingakhale kusanza, kukomoka, ndi kupuma pang’onopangono kapena mwaphuma. Nthaŵi zina munthu amafa. Patatha pafupifupi mwezi umodzi Kim wa zaka 17 atamaliza sukulu ya sekondale, anapita ku phwando kumene aliyense anali ndi ufulu womwa mmene angathere. Kim anamwa mabotolo 17 kenaka n’kukomoka. Ndiyeno mkulu wake anabwera kudzamutenga n’kupita naye kunyumba. M’maŵa wake, mayi ake anamupeza atafa.

Kumwa mwauchidakwa nthaŵi zambiri sikupha munthu mwachindunji, koma kumawonongabe thanzi. Katswiri wa zamaganizo dzina lake Jerome Levin anati: “Moŵa ungawononge chiwalo chilichonse m’thupi mwanu. Ziwalo zimene umakonda kuwononga ndi ubongo, chiwindi, ndi mtima.” Nkhani inayake m’magazini yotchedwa Discover inati: “Kafukufuku watsopano akusonyeza kuti anthu amene amamwa moŵa ali ana amadzipweteka kwambiri. Chifukwa chakuti ubongo wa achinyamata umakhala ukukulabe mpaka kufika zaka za m’ma 20, achinyamata amene amamwa mwauchidakwa akhoza kuwononga mbali yaikulu ya ubongo wawo.” Kumwa moŵa kwambiri akutinso kumachititsa munthu kukhala ndi ziphuphu zambiri, kukhala ndi makwinya asanakalambe, kunenepa kwambiri, kuwonongeka ziwalo zam’kati, kusanduka chidakwa, ndi kuyamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.

Palinso kuopsa kwina komwa moŵa mwauchidakwa. Mukaledzera, ena akhoza kupezerapo mpata wokuchitani chipongwe. Akhoza kukupwetekani kapena ngakhale kukugwirirani kumene. Kuwonjezera apo, inuyo mukhoza kupweteka anthu ena chifukwa chochita zinthu zachiwawa zimene mutakhala kuti simunaledzere simungaganize n’komwe zozichita. Baibulo limachenjeza kuti ukaledzera, “maso ako adzaona zachilendo, mtima wako udzalankhula zokhota.” (Miyambo 23:33) Zotsatirapo zoipa za kuledzera koteroko ndi monga kudana ndi anzanu, kulephera kusukulu ndi kuntchito, kumangidwapo ndi apolisi, ndiponso kukhala mphaŵi. *Miyambo 23:21.

Kukakamizidwa Kumwa

Ngakhale kuti pali zoopsa zoterozo, moŵa umatsatsidwa kwambiri malonda ndipo m’mayiko ambiri umapezeka mosavuta. Ndipo potsatsa malonda pa TV ndi m’manyuzipepala, kumwa moŵa amakuonetsa ngati kotsogola. Koma nthaŵi zambiri achinyamata amayamba kumwa moŵa wambiri nthaŵi imodzi chifukwa chokakamizidwa ndi anzawo.

M’kafukufuku amene cholinga chake chinali kuphunzitsa anthu zinthu zokhudza moŵa ku Australia, achinyamata 36 mwa achinyamata 100 alionse amene anafunsidwa mafunso anati amamwa moŵa “kuti afanane ndi anzawo akamacheza.” Anthu akayamba kuledzera pa “phwando la moŵa,” munthu wamanyazi angayambe kuchita zinthu zoseketsa anthu pamene anzake akumulimbikitsa kumwa mabotolo ambirimbiri a moŵa motsatizana. Mtsikana wina dzina lake Katie anamubweretsa kunyumba kwawo atakomoka chifukwa chochita zimenezo. Akuti “mnzake” anamupatsa moŵa n’kumuuza kuti: “Katie, wakula tsopano. Uyenerano kuphunzira kupapira.”

Chilakolako chofuna kusangalala ndiponso kufanana ndi anzake a munthu n’chachikulu kwambiri moti ngakhale kuti pali umboni wochuluka wosonyeza kuti kumwa moŵa wambiri nthaŵi imodzi n’koopsa, anthu ambiri amamwabe choncho.

Kodi Musankha Kuchita Chiyani?

Ndiye mafunso amene alipo ndi oti: Kodi inuyo musankha kuchita chiyani pankhani yomwa moŵa? Kodi mungotsatira zimene anzanu akuchita? Kumbukirani zimene Baibulo limanena pa Aroma 6:16, zoti: “Kodi inu simudziŵa kuti pamene mudzipereka kwa wina wake kumumvera iye ngati akapolo, ndinu akapolo a iye amene mumumvera?” (Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Mukamangotengera zonse zimene anzanu akuchita, mumasanduka kapolo wawo. Baibulo limakulimbikitsani kuganiza panokha. (Miyambo 1:4) Lili ndi malangizo amene angakuthandizeni kupeŵa kuchita zinthu zoipa kwambiri. Taganizirani zimene limanena pa nkhani ya moŵa.

Baibulo sililetsa kumwa moŵa, ndipo silinena kuti achinyamata asamasangalale. Koma limaletsa kumwa mwauchidakwa. Lemba la Miyambo 20:1 limati: “Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru.” Zoonadi, moŵa ungachititse munthu kuchita zinthu zoseketsa ndiponso zaphokoso. N’zoona kuti mukhoza kusangalala nawo kwa kanthaŵi, koma mukaumwetsa ‘umaluma ngati njoka,’ ndipo umakusiyani mutapweteka kwambiri m’thupi ndiponso m’maganizo.—Miyambo 23:32.

Chinanso chofunika kuchiganizira n’choti m’mayiko ambiri muli lamulo loletsa anthu osakwana zaka zinazake kumwa moŵa. Akristu amamvera malamulo oterowo. (Tito 3:1) Cholinga cha malamuloŵa n’choti akutetezeni.

Chinthu chomaliza, ndiponso chofunika kwambiri, n’choti muyenera kuganizira mmene kumwa mwauchidakwa kungawonongere moyo wanu wauzimu. Yehova Mulungu akufuna kuti muzimutumikira ‘ndi nzeru zanu zonse,’ osati ndi nzeru zopereŵera chifukwa choti zinawonongeka ndi moŵa! (Mateyu 22:37) Mawu a Mulungu amaletsa “maledzero” ndiponso “mamwaimwa.” (1 Petro 4:3) Choncho kumwa moŵa wambiri nthaŵi imodzi n’kosemphana ndi zimene Mlengi wathu amafuna. Kumwa mwauchidakwa koteroko kungalepheretse munthu kukhala paubwenzi wabwino ndi Mulungu.

Kodi muyenera kutani ngati muli ndi vuto lomwa moŵa wambiri nthaŵi imodzi? Musachedwe, pezani thandizo msanga polankhula ndi kholo lanu kapena Mkristu wokhwima maganizo. * Pempherani kwa Yehova Mulungu ndipo m’pempheni kuti akuthandizeni, chifukwa iye ndi “thandizo lopezekeratu m’masautso.” (Salmo 46:1) Kaŵirikaŵiri munthu amayamba kumwa moŵa wambiri nthaŵi imodzi ndiponso asanakwanitse zaka zovomerezeka mwa lamulo chifukwa chokakamizidwa ndi anzake, choncho mungafunike kusintha anthu amene mumacheza nawo ndiponso zosangalatsa zimene mumakonda. Kusintha koteroko sikuti n’kophweka, koma ndi thandizo la Yehova zinthu zingakuyendereni bwino.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 11 Malinga ndi kafukufuku wina amene anachitika ku United States, “anthu amene nthaŵi zambiri amamwa moŵa wambiri nthaŵi imodzi ndi amenenso kaŵirikaŵiri sapita ku sukulu masiku ena, sakhoza kusukulu, amavulazidwa, ndipo amawononga katundu, kuposa anthu amene samwa moŵa wambiri nthaŵi imodzi.”

^ ndime 21 Nthaŵi zina munthu angafunike kuthandizidwa ndi dokotala wodziŵa kuthandiza anthu amene ali ndi vuto limeneli.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 31]

Zotsatirapo Zoipa za Kumwa Moŵa Wambiri Nthaŵi Imodzi

Ziŵerengero zotsatirazi zikusonyeza zotsatirapo zomvetsa chisoni za kumwa moŵa wambiri nthaŵi imodzi pakati pa ophunzira a kukoleji ku United States:

Kufa: Chaka chilichonse, ophunzira akukoleji 1,400 a zaka zapakati pa 18 ndi 24 amafa atavulala chifukwa choledzera, kuphatikizapo kuvulala pa ngozi za galimoto

Kuvulala: Ophunzira 500,000 a zaka zapakati pa 18 ndi 24 amavulala pamene sanayenera kuvulala chifukwa choledzera

Kupwetekedwa: Ophunzira opitirira 600,000 a zaka zapakati pa 18 ndi 24 amapwetekedwa ndi wophunzira mnzawo amene wamwa moŵa

Kugwiriridwa: Ophunzira opitirira 70,000 a zaka zapakati pa 18 ndi 24 amagwiriridwa chifukwa choti iwowo anali ataledzera kapena munthu amene anali naye anali ataledzera

[Mawu a Chithunzi]

Source: The U.S. National Institute on Alcohol Abuse and Alcoholism

[Chithunzi patsamba 29]

Anzanu angakulimbikitseni kumwa moŵa wambiri nthaŵi imodzi