Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulimbana ndi Mavuto Amene Amakhalapo Munthu Akakhala Mayi Akadali Wamng’ono

Kulimbana ndi Mavuto Amene Amakhalapo Munthu Akakhala Mayi Akadali Wamng’ono

Kulimbana ndi Mavuto Amene Amakhalapo Munthu Akakhala Mayi Akadali Wamng’ono

MTSIKANA akakhala ndi mimba akadali wamng’ono amakumana ndi mavuto oyenera anthu akuluakulu. Mtsikana wina amene ali ndi mwana anati: “Ndimamva ngati ndili ndi zaka 40. Ndinayamba kulimbana ndi mavuto a anthu akuluakulu ndili mwana.” Zoonadi, mtsikana akazindikira kuti ali ndi mimba, akhoza kuzunguzika maganizo ndipo amakhala ndi mantha komanso nkhaŵa.

Ngati ndinu mtsikana wamng’ono ndipo muli ndi mimba, nanunso mungamve choncho. Koma kungokhala osachitapo kanthu chifukwa choganiza zinthu zolefula sikungakuthandizeni. Baibulo limati: “Woyang’ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.” (Mlaliki 7:8; 11:4) Mlimi amene amangokhala osachitapo kanthu chifukwa choda nkhaŵa ndi nyengo, sangaphule kanthu kalikonse. Inunso musangokhala osachitapo kanthu. Pakapita nthaŵi, muyenera kuyamba kukwaniritsa udindo umene muli nawo.—Agalatiya 6:5.

Kodi mungachite chiyani? Ena angakuuzeni kuti muchotse mimbayo. Koma anthu amene akufuna kuyambiranso kusangalatsa Mulungu sangachite zimenezo, chifukwa Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti kuchotsa mimba n’kuphwanya lamulo la Mulungu. (Eksodo 20:13; 21:22, 23; Salmo 139:14-16) M’maso mwa Mulungu, moyo wa mwana aliyense wosabadwa, kuphatikizapo mwana wapatchire, ndi wamtengo wapatali.

Nanga bwanji kukwatiwa ndi bambo ake a mwanayo n’kulerera limodzi mwana wanuyo? Mungaganize kuti kukwatiwa kungakuchotseni manyazi. Ngakhale pamene bambo wachinyamata akuona kuti ndi udindo wake kuthandiza nawo kulera mwana wake, si ndiye kuti kukwatiwa naye kumakhala chinthu chanzeru nthaŵi zonse. * Mnyamata akakhala woti akhoza kupatsa mtsikana pathupi sizitanthauza kuti ndi wokhwima maganizo mokwanira kapena ali ndi nzeru zokwanira kuti akhale mwamuna ndi bambo wabwino. Ndiponso sizitanthauza kuti akhoza kupeza ndalama zokwanira zosamalira mkazi ndi mwana. Kuwonjezera apo, ngati mnyamatayo ali wa chipembedzo china, kukwatiwa naye n’kusemphana ndi malangizo a m’Baibulo oti mukwatiwe “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39) Zimene zachitikirapo ena zasonyeza kuti kuthamangira ukwati musanakhwime, umene ungangokhala wa kanthaŵi kochepa basi, kungangokuwonjezerani mavuto.

Nanga bwanji kumupereka mwanayo ku bungwe limene limapereka ana kwa anthu ena kuti akhale ana awo? Ngakhale kuti zimenezi n’zabwinoko kusiyana ndi kuchotsa mimba, muyenera kuganizira mfundo yoti ngakhale kuti zinthu pa moyo wanu zingaoneke ngati zasokonekera, mungathebe kusamala ndi kulera mwana wanuyo nokha.

Kulimbana ndi Mavutowo

N’zoona kuti kulera mwana popanda mwamuna si kophweka. Komabe, mwa kuyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo ndi kudalira Mulungu kuti akupatseni mphamvu ndi kukutsogolerani, mukhoza kulimbana ndi mavuto anuwo bwinobwino. Pansipa pali zinthu zina zimene mungachite zomwe zingakuthandizeni.

Yesetsani kukhalanso pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Zindikirani kuti kugonana musanaloŵe m’banja ndi kuchimwira Mulungu, kusemphana ndi mfundo zake zapamwamba za makhalidwe abwino. (Agalatiya 5:19-21; 1 Atesalonika 4:3, 4) Choncho, chinthu chofunika kwambiri kuchita ndicho kulapa ndi kupempha Mulungu kuti akukhululukireni. (Salmo 32:5; 1 Yohane 2:1, 2) N’zoona kuti mungaone kuti siinu woyenera kuthandizidwa ndi Mulungu. Komabe, Yehova akulonjeza kuti adzatikhululukira tikalapa ndipo amathandiza anthu amene amasiya zolakwa zawo. (Yesaya 55:6, 7) Pa Yesaya 1:18, Yehova anati: “Ngakhale zoipa zanu zili zofiira [zazikulu, zoipa kwambiri], zidzayera ngati matalala [zidzayereratu].” Baibulo limalimbikitsanso anthu ochimwa kupeza thandizo lauzimu limene akulu oikidwa mu mpingo amapereka.—Yakobo 5:14, 15.

Lekani kugonana musanaloŵe m’banja. Zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kuthetsa chibwenzi chanu ndi bambo a mwanayo. Kupitiriza chibwenzicho musanakwatirane kungangokuikani pachiyeso chopitiriza kuchita zinthu zosasangalatsa Mulungu. Musaiwale kuti malamulo a Mulungu cholinga chake n’choti atiteteze, ngakhale kuti amaoneka okhwima. Nicole, amene tinamutchula mu nkhani zina zija, anati: “Ndinazindikira kuti Mulungu amanena zoona. Amafuna kutithandiza.”—Yesaya 48:17, 18.

Uzani makolo anu. Mwina mukhoza kukhala ndi mantha kuti makolo anu akukwiyirani. N’zoona kuti adzakwiya ndiponso adzada nkhaŵa akamva zoti muli ndi mimba. Mwina akhozanso kuona ngati alephera pa ntchito yawo yaukholo ndipo angamaone ngati ndi iwowo achititsa kuti mukhale ndi khalidwe loipa. Komabe, ngati makolo anu amaopadi Mulungu, mkwiyowo udzatha pakapita nthaŵi. Iwowo ndi makolo anu, ndipo ngakhale mwachita zinthu zolakwa, amakukondanibe. Poona mtima wanu wolapa, mosakayikira adzamva ngati mmene anamvera tate wa mwana woloŵerera wa mu fanizo la Yesu, ndipo adzakukhululukirani.—Luka 15:11-32.

Sonyezani kuti mumayamikira. Makolo, achibale, ndi anzanu nthaŵi zambiri angakuthandizeni ndi kukulimbikitsani. Mwachitsanzo, makolo anu angakulipirireni kuchipatala kuti mupeze chithandizo. Mwana wanu akabadwa, angakusonyezeni mmene mungamusamalire; ndipo akhoza kumakhala ndi mwanayo nthaŵi zina inu mukachokapo. Ponena za mayi ake, Nicole anati: “Ngakhale kuti mwanayo anali wanga, mayi anga anandithandiza kwambiri.” Anzanunso angakuthandizeni, mwina kukupatsani zovala za mwana ndi zinthu zina zimene mungafunikire, mosachita kuulutsa poyera. (Miyambo 17:17) Anthu akamakuthandizani, muzitsatira langizo la m’Baibulo, loti ‘muziyamika.’ (Akolose 3:15) Kuwauza kuti mukuthokoza kwambiri kungawathandize anthu amene akukuthandizaniwo kuti asaone ngati simukuyamikira zimene akukuchitiranizo.

Phunzirani luso lolerera mwana. Simungafune kuti muzingodalira anthu a m’banja lanu ndi anzanu mpaka kalekale. Choncho yambani kuphunzira luso limene lidzakuthandizani kusamala bwino mwana wanu ndi kuyendetsa bwino banja lanu. Kuphunzira kusamalira mwana, amene amakhala woti sangathe n’komwe kudzichitira kalikonse, n’kovuta. Pali zinthu zambiri zimene mufunika kuphunzira zokhudza kadyedwe, kusamala thanzi, ndi zinthu zina zofunika posamala mwana. N’zochititsa chidwi kuti Baibulo limalimbikitsa akazi achikulire achikristu kuti azilimbikitsa akazi aang’ono kukhala “osamala bwino mabanja awo.” (Tito 2:5, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Mosakayikira mayi anu, ndiponso mwina Akristu ena achikulire a mu mpingo mwanu, angakuthandizeni kwambiri pankhani imeneyi.

Muzigwiritsa ntchito ndalama mosamala. Baibulo limati, “ndalama zitchinjiriza.” (Mlaliki 7:12) Mwana akabadwa pamafunika ndalama zambiri zogulira zinthu zofunika.

Choyamba, zingakhale bwino kukatenga ndalama zilizonse zimene boma likuyenera kukupatsani. Koma nthaŵi zambiri mtsikana amafunikirabe kudalira makolo ake kuti azimupatsa ndalama. Ngati zimenezo n’zimene mukuchita, n’chinthu chanzeru ndiponso n’kuwaganizira makolo anuwo kuchepetsa kwambiri ndalama zimene mumawononga. Ngakhale kuti mungakonde kumugulira mwana wanu zinthu zatsopano, mungasungeko ndalama mutamagula zinthu pakaunjika.

Yesetsani kuchita maphunziro enaake. Lemba la Miyambo 10:14 limati: “Anzeru akundika zomwe adziŵa.” Ngakhale kuti zimenezi zikukhudza makamaka kudziŵa zinthu za m’Baibulo, zikukhudzanso maphunziro a kusukulu. Muyenera kukhala ndi luso lokwanira kuti mudzathe kupeza ntchito n’kumadzisamala nokha.

N’zoona kuti n’zovuta kumapita kusukulu kwinaku mukulera mwana. Komabe, ngati simumaliza sukulu, inuyo ndi mwana wanu mungadzakhale ndi moyo waumphaŵi, wodalira kuthandizidwa ndi boma, wopeza tindalama tochepa, wokhala m’nyumba zoipa, kapena kukhala ndi matenda osoŵa zakudya m’thupi, mpaka kalekale. Choncho, ngati zingatheke, pitirizani sukulu. Mayi ake a Nicole anaonetsetsa kuti Nicole amalize sukulu, ndipo chifukwa chochita zimenezo, anatha kuchita maphunziro ena ophunzitsa ntchito, ndipo panopa amagwira ntchito yothandiza loya.

Bwanji osachita kafukufuku kuti muone maphunziro amene mungathe kuchita? Ngati zingakuvuteni kumapita kusukulu, mwina mungafufuze kuti muone ngati mungathe kumaphunzirira kunyumba. Mwinanso zingakuyendereni bwino mutamachita sukulu imene amakutumizirani zoŵerenga kunyumba.

Zinthu Zingakuyendereni Bwino

Kwa mtsikana amene sali pabanja, kulera mwana n’kovuta. Koma n’zotheka kuti zinthu zikuyendereni bwino! Mwa kuleza mtima, kuchita khama, ndi kudalira thandizo la Yehova Mulungu, mungasanduke kholo lachikondi, lodziŵa bwino kulera mwana. Ndipo ana a azimayi osakwatiwa angakule bwinobwino n’kudzakhala achikulire oima paokha. Mwina mpaka mungadzasangalale kuona mwana wanu atamvera malangizo amene mwakhala mukum’patsa n’kusanduka munthu wokonda Mulungu.—Aefeso 6:4.

Nicole anafotokoza zimenezi motere: “Ndi thandizo la Mulungu, ngakhale kuti zinkaoneka ngati zosatheka poyamba, ndinasangalala kuthandiza kamtsikana kanga kusanduka munthu wachikulire wokoma mtima, waulemu, ndi wodziimira payekha. Masiku ano ndikamamuyang’ana, ndimakumbukira masiku ambiri amene sindinkagona tulo chifukwa chochulukidwa mavuto, komanso ndimasangalala.”

Koma kodi achikulire ayenera kutani akamachita zinthu ndi atsikana amene anabereka ana akadali aang’ono ndiponso ana awowo? Kodi pali njira iliyonse yothandizira atsikana kuti asatenge mimba akadali aang’ono kuti apeŵe mavuto amene tawafotokozaŵa?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Nkhani yofotokoza udindo ndi mavuto amene anyamata osakwatira amene ali ndi ana amakhala nawo mungaipeze mu nkhani ya “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . ” ya mu Galamukani! ya May 8, 2000, ndi ya June 8, 2000.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Atsikana amene amakhala ndi ana akadali aang’ono amakumana ndi mavuto ambiri akamalera ana awo

[Chithunzi patsamba 10]

Kuthamangira kukwatiwa musanakhwime si chinthu chanzeru

[Chithunzi patsamba 10]

Akulu achikristu angathandize achinyamata amene akuchita zolakwa kuyesetsa kukhalanso pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu

[Chithunzi patsamba 11]

Ndi bwino kuti azimayi osakwatiwa amalize sukulu