Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusanduka Azimayi Akadali Ana

Kusanduka Azimayi Akadali Ana

Kusanduka Azimayi Akadali Ana

“Mnyamata amene anali chibwenzi changa anali wokongola. Anali ndi ndalama zambiri ndipo tinkapita ku malo osiyanasiyana osangalatsa. Mwezi wina nditaona kuti sindinasambe, ndinadziŵa kuti zinthu sizili bwino ayi. Sindinadziŵe kuti ndiwauza bwanji mayi anga. Ndipo sindinakhulupirire kuti zimenezi zandichitikiradi. Ndinali ndi zaka 16 zokha, ndipo sindinadziŵe chochita.”—Anatero Nicole.

MASIKU ano Nicole, * amene ali ndi zaka za m’ma 30, ndi mzimayi wa ana atatu wa nyonga zake amene zinthu zikumuyendera bwino. Mwana wake woyamba ali ndi zaka 20. Koma zaka zingapo zapitazo anali mmodzi wa atsikana mamiliyoni ambiri osakwatiwa amene amatenga mimba akadali aang’ono. Mofanana ndi atsikana ena amene amasanduka azimayi akadali ana, anakumana ndi mavuto aakulu, anafunika kusankha zinthu zovuta, ndipo sanali kudziŵa chomwe chimuchitikire m’tsogolo.

Nicole nthaŵi zambiri safuna kulankhula za zimene zinamuchitikira ali mtsikana wamng’ono. Panthaŵi imeneyo, anasokonezeka maganizo, sanakhulupirire zinthu zomwe zinali kumuchitikira, anali ndi mantha, anali wokwiya, ndipo anataya mtima, pamene anzake panthaŵi imeneyo ankangoganiza za zovala zawo ndi mmene akukhozera kusukulu. Komabe, sikuti Nicole analibiretu pogwira. Iye anachokera ku banja lachikondi limene linayesetsa kumuphunzitsa mfundo zapamwamba kwambiri za makhalidwe. Ngakhale kuti kwakanthaŵi iye sanatsatire mfundo zimenezo ndipo zotsatirapo zake zinali zopweteka, kenaka mfundo zomwezo n’zimene zinamuthandiza kukhala ndi moyo waphindu ndiponso watanthauzo. Iye anayamba kuyendera mfundo yoti: “Zinthu zikhoza kusintha.”

Koma n’zomvetsa chisoni kuti si atsikana onse amene amakhala ndi ana akadali aang’ono omwe amakhala ndi banja lothandiza loterolo, kapena amene amakhala ndi maganizo oti zinthu zikhoza kusintha. Ambiri amapezeka kuti ali paumphaŵi umene umaoneka ngati sudzatha. Ena amakhala akupwetekedwabe mumtima chifukwa chogwiriridwa kapena kuchitiridwa chiwawa.

Zonsezi zikutanthauza kuti ana a atsikana aang’ono zinthu siziwayendera bwino. Buku lonena za atsikana amene amabereka akadali aang’ono lotchedwa Teen Moms—The Pain and the Promise, limati ana a atsikana aang’ono “nthaŵi zambiri amabadwa osalemera mokwanira, amadwaladwala, ambiri a iwo amamwalira, salandira chithandizo chokwanira cha mankhwala, amavutika kwambiri ndi njala ndi kupereŵera kwa zakudya m’thupi; amachitiridwa chiwawa kwambiri, ndipo amakula mochedwa poyerekezera ndi ana a azimayi achikulire.” Ndipo n’zosavuta kuti ana aakazi amene mayi awo anawabereka akadali mtsikana wamng’ono nawonso adzabereke akadali aang’ono, kusiyana ndi ana amene mayi awo anali achikulire.

Kodi atsikana amene amatenga mimba akadali aang’ono ndi ochuluka motani? Kodi atsikana amene amasanduka azimayi akadali ana angatani kuti zinthu ziwayendere bwino pamene akuyesetsa kulimbana ndi mavuto amene amakhalapo polera ana awo? Kodi pali njira iliyonse yothandizira atsikana kuti asatenge mimba akadali aang’ono kuti asadzakumane ndi mavuto ngati ameneŵa? Nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso ameneŵa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina ena mu nkhani zino asinthidwa.