Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza ndi Kuteteza Atsikana

Kuthandiza ndi Kuteteza Atsikana

Kuthandiza ndi Kuteteza Atsikana

ZIMAMVETSA chisoni kwambiri mtsikana wamng’ono, amene akadali mwana, akatenga mimba asanakwatiwe. Komabe, atsikana amene amatenga mimba akadali aang’ono ndi ambiri, ndipo zimenezi zimakhudza aliyense m’njira inayake. Vuto la atsikana otenga mimba akadali aang’ono ndi umboni umodzi chabe wosonyeza kuipa kosamvera lamulo la Mulungu loti: “Thaŵani dama.”—1 Akorinto 6:18.

Ngakhale zili choncho, nthaŵi zina mtsikana amene waphunzitsidwa njira za Mulungu amasankha kunyalanyaza kapena kusamvera zimene waphunzitsidwazo. Amachita dama n’kupezeka kuti watenga mimba. Kodi Akristu oona amatani zimenezi zikachitika? Mtsikana woloŵerera woteroyo akasonyeza umboni woti walapa, makolo ake ndi Akristu ena mumpingo ayenera kumuthandiza ndi kumuchirikiza mwachikondi.

Taganiziraninso za Nicole. Makolo ake anali kumuphunzitsa kuti adzakhale wa Mboni za Yehova. Choncho zinali zopweteka kwambiri pamene anatenga mimba asanakwatiwe. Komabe, Nicole akukumbukira kuti, “Akristu anzanga ankabwera kunyumba kwathu n’kumandilimbikitsa kuti ndiphunzire Baibulo ndiponso kuti ndikhale woyandikana ndi Yehova.”

Sikuti Mboni za Yehova zimasangalala ndi chiwerewere. Koma zimadziŵa kuti mwa kutsatira mfundo za m’Baibulo, ochita zolakwa ‘angasandulike.’ (Aroma 12:2) Zili ndi chikhulupiriro cholimba kuti Mulungu amakhululukira anthu ochimwa amene alapa. (Aefeso 1:7) Zimadziŵanso kuti ngakhale mwana akhale wapatchire, mwanayo amakhala kuti sanalakwe chilichonse. Choncho, m’malo momusankha mwana woteroyo, Akristu mu mpingo amamusonyeza chikondi ndi kukoma mtima kofanana ndi kumene angasonyeze mwana wina aliyense mu mpingomo.—Akolose 3:12.

Mzimayi wina wosakwatiwa amene anali ndi ana anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Pasanapite nthaŵi yaitali anayamba kutsatira zimene anaphunzira m’Baibulo ndipo anasintha kwambiri pamoyo wake. Ponena za anthu a Mboni, iye anati: “Onse anandisonyeza chidwi chenicheni, ndiponso anali ndi chidwi ndi ana anga. Anandipatsa chakudya ndi zovala pamene ndinafunikira thandizo ndiponso anandipatsa ndalama. Nditavomerezedwa kuti ndiyambe kulalikira mu utumiki wa kumunda ndi Mboni za Yehova, ankayang’anira ana anga ine ndikachokapo. Anachita zonse zomwe akanatha kundithandiza kuti ndiyambe kukonda Yehova kuchokera pansi pa mtima.”

Kupeŵa

Komabe, ndi bwino kuthandiza atsikana kupeŵa mavuto amenewo poyambirira pomwe. Choncho Mboni za Yehova zimayesetsa kukhala ndi mabanja achikondi ndiponso ogwirizana kuti ana awo azikula bwino. M’malo mongowaopseza anawo, kumawauza za kuopsa kwa Edzi kapena kuopsa kotenga mimba, Mboni zimayesetsa kuphunzitsa ana awo kukonda Yehova Mulungu ndi malamulo ake kuchokera pansi pa mtima. (Salmo 119:97) Zimakhulupirira kuti ana amafunika kuuzidwa zinthu zolondola pankhani ya kugonana. Ndipo chofunika kwambiri kuposa pamenepo, zimakhulupirira kuti kuyambira ali makanda, ana amafunika kuwaphunzitsa mfundo za makhalidwe abwino zopezeka m’Baibulo. (2 Timoteo 3:15) Ku Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova, anthu amaphunzirako zinthu zosiyanasiyana. Komabe, makolo a Mboni amalimbikitsidwanso kuphunzira Baibulo ndi ana awo paokha. Mabuku osiyanasiyana, monga buku loti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, anakonzedwa kuti athandize makolo kuphunzitsa ana awo makhalidwe abwino. *

Kutsatira mfundo za makhalidwe abwino zapamwamba kwambiri za m’Baibulo n’kosemphana ndi khalidwe lachiwerewere limene lafala m’dzikoli masiku ano. Koma kutsatira mfundo zimenezo pamoyo kungateteze atsikana ambiri kuti apeŵe vuto lotenga mimba akadali aang’ono.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 12]

Akristu oona amakomera mtima azimayi osakwatiwa amene ali ndi ana, ndiponso amachita zinthu mowaganizira