Matenda Osintha Mtundu wa Khungu
Matenda Osintha Mtundu wa Khungu
Yolembedwa ndi wolemba Galamukani! ku South Africa
▪ Nthaŵi zina Sibongile amanena zinthu zanthabwala zokhudza matenda a khungu lake. Amanena akumwetulira kuti, “Ndinabadwa munthu wakuda, ndinasanduka mzungu, ndipo tsopano ndangosokonezeka mutu.” Iye ali ndi matenda osintha mtundu wa khungu.
Nthendayi imayamba chifukwa cha kutha kwa maselo amene amachititsa khungu kukhala ndi mtundu wake. Zimenezi zimachititsa kuti pakhungu pakhale mawangamawanga oyera. Anthu ena amangokhala ndi banga limodzi lokha ndipo vutoli silipitirira pamenepo. Koma kwa anthu ena, mawangaŵa amakuta thupi lonse mofulumira. Ndipo ena mawanga awo amafalikira pang’onopang’ono kwa zaka zambiri. Matendaŵa sapweteka ndipo si opatsirana.
Sikuti anthu onse okhala ndi matendaŵa amachita kuonekeratu ngati mmene alili Sibongile, chifukwa vutoli limaoneka kwambiri munthu akakhala ndi khungu lakuda. Koma anthu amene ali ndi vuto limeneli ndi ambiri. Ena ali ndi mawanga ochepa chabe pamene ena ali nawo ambiri. Ziŵerengero zikusonyeza kuti pafupifupi munthu mmodzi kapena anthu aŵiri pa anthu 100 alionse ali ndi vuto limeneli. Matendaŵa amagwira anthu a mtundu uliwonse ndipo amagwira amuna ndi akazi mofanana. Chimene chimayambitsa matenda ameneŵa sichikudziŵikabe.
Ngakhale kuti matendaŵa alibe mankhwala, pali zinthu zosiyanasiyana zimene munthu angachite kuti adzithandize. Mwachitsanzo, ngati munthu ali ndi khungu loyera, vutoli limaonekera kwambiri khungu limene lilibe matendaŵa likapsa ndi dzuwa. Choncho kupeŵa kukhala pa dzuwa kungathandize kuti vutoli lisamaonekere kwambiri. Kwa anthu a khungu lakuda, pali mankhwala odzola apadera amene angabise mawanga oyera kuti khungu lizioneka la mtundu umodzi. Odwala ena athandizidwa atagwiritsa ntchito njira inayake yobwezeretsa mtundu pa khungu. Potsatira njira imeneyi, munthu amamwa mankhwala miyezi yambiri ndipo amagwiritsa ntchito kuwala kwinakwake kwapadera. Njira imeneyi yathandiza anthu ena kuti khungu limene linali ndi vutoli likhalenso ndi mtundu wake wakale. Odwala ena amagwiritsa ntchito njira yochotsa mtundu umene watsalira pakhungu. Cholinga cha njira imeneyi ndi kuwononga maselo obweretsa mtundu pakhungu amene atsala kuti thupi lonse lizioneka la mtundu wofanana, pogwiritsa ntchito mankhwala.
Matendaŵa angachititse munthu wodwalayo kuvutika maganizo, makamaka ngati afalikira mpaka kumaso. Sibongile anafotokoza kuti: “Posachedwapa, ana aŵiri anandiyang’ana n’kuthaŵa, kwinaku akukuwa. Ena safuna kundilankhula, poganiza kuti mwina ndili ndi nthenda yopatsirana kapena ndinatembereredwa. Ngati pali chinthu chimodzi chimene ndingafune kuti anthu amvetsetse, n’choti sayenera kuopa anthu amene ali ndi vuto limeneli. Sangatenge matendaŵa pomukhudza munthuyo kapena kudzera mu mpweya.”
Sibongile salola kuti vuto lakeli limulepheretse kugwira ntchito yophunzitsa anthu Baibulo imene amaikonda kwambiri monga wa Mboni za Yehova. Pogwira ntchito imeneyi, munthu amafunika kupita kumakomo kwa anthu n’kumakalankhula nawo pamaso m’pamaso. Iye akuti: “Ndazoloŵera mmene ndimaonekera. Sindiona chovuta kukhala mmene ndililimu, ndipo ndikuyembekezera kwambiri nthaŵi imene khungu langa lidzakhalenso ndi mtundu wake wakale m’dziko lapansi laparadaiso limene Yehova Mulungu walonjeza.”—Chivumbulutso 21:3-5.
[Chithunzi patsamba 28]
Mu 1967, matendaŵa asanayambe