Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Yehova, Mwandipeza!”

“Yehova, Mwandipeza!”

“Yehova, Mwandipeza!”

Yosimbidwa ndi Nelly Lenz

“Kodi ndinu a Mboni za Yehova?” Ndinafunsa azibambo aŵiriwo, amene anali atabwera kunyumba kwathu. “Inde,” anayankha choncho. “Inenso!” ndinawauza mokweza mawu. Ndinali ndi zaka 13 zokha ndipo sindinkapita ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Makolo anga sanali Mboni za Yehova. Choncho, n’chifukwa chiyani ndinawauza kuti ndinali wa Mboni za Yehova?

PAKANAPANDA Mboni za Yehova, mwina sindikanabadwa. Mayi anga anakhala ndi pathupi panga akukhala ku Montreal, ku Quebec, Canada. Anali ndi zaka 17 zokha. Makolo awo anawakakamiza kuti achotse mimbayo, ndipo pamapeto pake anavomera.

Amayi anapempha kuti asagwire ntchito tsiku linalake n’cholinga choti akachotse mimbayo. Abwana awo, amene anali a Mboni za Yehova, zikuoneka kuti anadziŵa chifukwa chimene mayi angawo anapemphera kuti asagwire ntchito tsiku limenelo. Anawafotokozera Amayi mwachidule zifukwa zosonyeza kuti mphatso ya moyo ndi yamtengo wapatali. (Salmo 139:13-16) Akupita ku chipatalako, Amayi anaganizira zimene abwana awo anawauza zija. Anaganiza zoti sachotsa mimbayo. Nditabadwa mu 1964, mayi anga anandiika kumalo osungirako ana amasiye.

Kuyamba Kumva Choonadi cha M’Baibulo

Ndili ndi zaka pafupifupi ziŵiri, mayi anga ndi amuna awo amene anali atangokwatirana nawo kumene, anandichotsa kumalo osungirako ana amasiye kuja. Akukhala m’tawuni ya Sainte-Marguerite-du-Lac-Masson, anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo ankapita ku misonkhano ya mpingo. Koma pasanapite nthaŵi yaitali tinasamukira ku tawuni ya Boisbriand ndipo makolo anga anasiya kuphunzira Baibulo.

Zaka zingapo izi zitachitika, anayambiranso kuphunzira. Ndinkatchera khutu akamakambirana kuti ndimve zimene ankanena zokhudza dziko lapansi laparadaiso zopezeka m’Baibulo. (Luka 23:43) Ndinayamba kukonda Yehova kwambiri.

Koma tsiku lina Amayi anandiuza kuti asiya kuphunzira ndi Mboni ndipo sitizipitanso ku Nyumba ya Ufumu. Poyamba, ndinasangalala kwambiri kumva zimenezi. Popeza ndinali mwana wa zaka eyiti zokha, nthaŵi zina ndinkaona kuti misonkhanoyo inkatalika kwambiri. Koma madzulo amenewo pamene ndinafuna kulankhula ndi Yehova m’pemphero, ndinada nkhaŵa kuti mwina sandimvera.

Lamlungu lotsatira masana, ndinaona anthu oyandikana nafe nyumba, amene anali a Mboni za Yehova, akupita ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Ndinayamba kulira ndipo ndinafunsa Mulungu kuti, “N’chifukwa chiyani ana awo akupita ku misonkhano pamene ine sindingathe kupita?” Komabe, zimene Salmo 33:18 limanena zinandichitikira ineyo. Lemba limenelo limati: “Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake.”

Kuyambiranso Kupita ku Nyumba ya Ufumu

Patatha milungu itatu ndinapita kunyumba yoyandikana ndi yathuyo ndipo ndinauza amayi a kumeneko, a Lilianne, kuti ndikufuna ndizipita nawo ku misonkhano. A Lilianne anandifotokozera kuti zimenezo sizingatheke chifukwa mayi anga sankafuna kuyanjananso ndi Mboni za Yehova. Koma ndinalimbikirabe. Choncho anapita nane limodzi kunyumba kwathu ndipo anafunsa mayi anga ngati angalole kuti ndizipita nawo limodzi ku misonkhano. Ndinadabwa kuona kuti Amayi anavomera. Anati misonkhanoyo idzandiphunzitsa khalidwe labwino. Choncho ndinayamba kumapita ku misonkhano Lamlungu lililonse.

Kwa zaka pafupifupi zitatu ndinkapita ku misonkhano ya mpingo. Koma nditakwanitsa zaka 11, ukwati wa makolo anga unatha, ndipo ine ndi mayi anga tinasamuka. Kachiŵirinso, ndinasiya kuonana ndi Mboni za Yehova.

Zochitika Zosayembekezeka

Tsiku linalake nditakhala pamasitepe a kumaso kwa nyumba yathu, kunabwera Mboni ziŵiri, Eddie Besson ndi Don Fisher, ndipo anafunsa ngati makolo anga analipo. Nditawauza kuti kulibe, azibambowo ananyamuka kuti azipita. Koma ndinawathamangira, ndipo tinakambirana zimene zili koyambirira kwa nkhani ino zija.

M’pomveka kuti azibambo aŵiriwo anali odabwa kumva ndikunena kuti ndine wa Mboni za Yehova. Ndinawafotokozera mmene zinthu zinalili ndipo ndinawachonderera kuti abwerenso madzulo. Nditawafotokozera Amayi kuti kubwera a Mboni, anakwiya kwambiri ndipo anati sadzawalowetsa m’nyumba. Ndipo anakonza zochokapo anthuwo asanabwere. Misozi ili chuchuchu, ndinawapempha kuti asachokepo. Ali m’kati mokonzeka kuti azichoka, belu lapachitseko linalira, ndipo pakhomopo panali Eddie Besson. Tangoganizirani mmene ndinasangalalira pamene Amayi anavomera kuphunzira Baibulo!

Tsopano ndinatha kuyambiranso kumapita ku misonkhano! Koma chaka chimodzi chisanathe, Amayi anasiyanso kuphunzira Baibulo. Ulendo uno, anandiletsa kuonana ndi wa Mboni aliyense ndipo anataya mabuku a Mboni za Yehova onse amene anatha kupeza. Koma ndinatha kubisa Baibulo, nyimbo, mavoliyumu aŵiri a magazini a Nsanja ya Olonda, ma Yearbook of Jehovah’s Witnesses aŵiri, ndi buku lotchedwa Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. * Paphunziro lathu lomaliza, ndinafunsa Eddie Besson kuti ndichite chiyani, chifukwa ndinkakonda Yehova kwambiri. Anandilimbikitsa kuphunzira pandekha ndi kupemphera pafupipafupi. Ananditsimikizira kuti Yehova adzandisamalira. Ndinali ndi zaka 14 zokha.

Kuchita “Misonkhano” Yandekha

Kuyambira nthaŵi imeneyo, Lamlungu lililonse ndinkaloŵa m’chipinda mwanga n’kumayerekezera kuti ndili pamsonkhano wa mpingo. Poyamba ndi pomaliza, ndinkaimba nyimbo yoti “Yang’ananibe Maso Anu Pamphotho!” chifukwa nyimbo ya Ufumu yomwe ndinkakumbukira inali yomweyo basi. Mpaka pano, sinditha kuimba nyimbo imeneyi osagwetsa misozi. Ndinkaphunziranso nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yochokera m’mavoliyumu amene ndinali nawo aja. Ndinkamaliza “msonkhano” wanga ndi pemphero. Choncho, ngakhale kuti sindinali kukumana ndi anthu a Mboni, ndinkaona kuti Yehova anali nane pafupi.

Nditakwanitsa zaka 17, ine ndi Amayi tinasamukira ku Montreal. Zaka zimenezo zinali zovuta, chifukwa m’banja mwathu munalibe chikondi.

Yehova Anandipeza!

Tsika lina Amayi analandira buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi kwa Mboni za Yehova. Nditabwera kunyumba, ndinaliona lili pathebulo ndipo ndinayamba kuliŵerenga. Nditaona kuti limagwiritsa ntchito dzina la Mulungu, Yehova, ndinayamba kulira ndipo ndinapemphera chamumtima kuti, “Yehova, mwandipeza!”

Ndinafunika kuonana ndi abale ndi alongo anga achikristu. Koma ndikanachita bwanji zimenezi? Amayi anandiuza kuti munthu wina woyandikana naye nyumba mwina angakhale wa Mboni za Yehova. Choncho ndikupita kuntchito, ndinaima panyumba ya munthuyo n’kuimba belu lapachitseko. Mzibambo wina, amene anali akadali ndi tulo, anayankha. Anadabwa kwambiri nditamuuza kuti ndine wa Mboni za Yehova ndipo ndimafuna kubatizidwa! Anakonza zoti mlongo wina dzina lake Josée Miron aziphunzira nane Baibulo. Koma ulendo unonso, Amayi anayamba kundiletsa kuphunzira Baibulo. Anandiuza kuti ndiyenera kudikira mpaka n’takwanitsa zaka 18 ngati ndimafuna kukhala wa Mboni.

Kodi Ndivomere Kukhala ndi Banja Lina?

Abwana anga anaona kuti zinthu kunyumba kwathu zinali kuipiraipira. Nthaŵi zambiri Loweruka ndi Lamlungu ankandiitana kuti ndipite kunyumba kwawo ndikacheze ndi iwowo ndi akazi awo. Popeza ndimakonda mahatchi, nthaŵi zambiri tinkakwera mahatchi n’kumapita koyenda limodzi. Ndinkamva ngati anali makolo anga enieni.

Tsiku lina abwana anga anandiuza kuti iwowo ndi akazi awo amandikonda kwambiri ndipo angakonde kuti ndizikakhala nawo limodzi kunyumba kwawo. Zimene ankandiuzazi n’zimene ndinakhala ndikufuna moyo wanga wonse—kukhala m’banja lachikondi. Koma anandiuza kuti ndinafunika kuchita chinthu chimodzi. Ndinafunika kusiya kusonkhana ndi Mboni za Yehova. Anandipatsa mlungu umodzi kuti ndiganizire zimene anandiuzazo, koma sindinafunikire ngakhale tsiku limodzi kuti ndipeze yankho. Ndinawayankha nthaŵi yomweyo. Yehova anali asanandisiyepo, ndipo sindikanatha kumusiya.

Kutumikira Mulungu

Chifukwa cha mavuto amene ndinali kukumana nawo kunyumba, ndinasamuka n’kuyamba kukhala ndi bambo anga ondipeza. Anandilimbikitsa kuti ndipitirize kuphunzira Baibulo, ndipo pa December 17, 1983, ndili ndi zaka 19, ndinabatizidwa. Ndinali wokondwa kwambiri kuona Eddie Besson pa tsiku la ubatizo wanga. Tsopano sanakayikirenso zoti ndinali wa Mboni za Yehova!

Komabe, khalidwe la bambo anga ondipeza aja linasintha nditabatizidwa. Akandiona ndikupemphera, ankalankhula mokweza mawu kwambiri ndipo mwina ankatenga zinthu n’kumandigenda nazo! Ndiponso ankandikakamiza kuti ndichite maphunziro owonjezereka, amene akanasokoneza cholinga changa chokhala mpainiya, kapena kuti mlaliki wa nthaŵi zonse. Pamapeto pake anandiuza kuti ndisamuke. Anandipatsa cheke cha ndalama zokwana madola 100 ndipo anandiuza kuti nthaŵi imene ndidzafunike kukatenga ndalama ndi cheke chimenecho ndidzazindikira kuti Yehova sandisamala.

Ndinayamba upainiya pa September 1, 1986, ndipo mpaka lero ndikadali nachobe cheke chimenecho chifukwa sindinakatengebe ndalama zake! Nthaŵi zina zinali zovuta kuchita upainiya kumadera a kumudzi opanda galimoto. Koma anthu a mu mpingo wa kumeneko anandithandiza kwambiri.

Patapita nthaŵi ndinakumana ndi mwamuna wachikristu wokoma mtima, dzina lake Ruben Lenz. Tinakwatirana mu 1989. Panopa Ruben ndi mkulu mu mpingo wina m’tawuni ya Milton ku Ontario, ku Canada, kumene takhalako kuyambira mu 2002. Ukwati wathu ndi umodzi mwa mphatso zabwino kwambiri zimene Yehova wandipatsa. Ndinapitiriza utumiki wa nthaŵi zonse mpaka pamene tinakhala ndi mwana wathu woyamba, Erika, mu 1993. Zaka zopitirira pang’ono zitatu kuchokera pamenepo, tinakhala ndi mwana wamwamuna dzina lake Mika. Nditakhala zaka zambirimbiri ndili wosungulumwa, Yehova Mulungu wandidalitsa kwambiri pondipatsa banja limene limamukonda mofanana ndi mmene ineyo ndimamukondera.

Ngakhale kuti nthaŵi ndi nthaŵi ndinkasiyana ndi anthu a Yehova pamene ndinali kukula, sindinasiye kukhulupirira Mulungu ndi kuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso. (Yohane 3:36) Ndikuyamikira kwambiri kuti Yehova “anandipeza!”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 15]

Nditakwera hatchi ya abwana anga

[Chithunzi patsamba 15]

Nelly Lenz ndi mwamuna wake, Ruben, ndi ana awo, Erika ndi Mika