Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Angatonthoze Anamalira

Angatonthoze Anamalira

Angatonthoze Anamalira

Mzimayi wina wa ku Jalisco, ku Mexico, analembera kalata ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico. Anapempha kuti: “Munditumizireko timabuku tingapo takuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Sindine wa Mboni za Yehova, koma ndimakhulupirira zinthu zambiri zimene inunso mumakhulupirira.”

Mzimayiyo anafotokoza chifukwa chimene ankafunira timabukuto. Anati: “Ndikufuna timabukuti chifukwa ndikuganiza kuti tingakhale tabwino kupatsa ena mwa anthu amene amabwera kudzagula maluwa m’sitolo mwathu. Ndikunena anthu amene amabwera kudzagula nkhata za maliro, omwe nthaŵi zina amakhala mkazi wake, ana ake, kapena mwamuna wake, wa munthu amene wamwalirayo. Ndikuganiza kuti timabuku timeneti tingawathandize kwambiri.”

Mwina inuyo kapena munthu wina amene mukumudziŵa angalimbikitsidwenso ataŵerenga kabuku ka masamba 32 kameneka. Kamayankha mafunso monga akuti: Kodi ndingakhale motani ndi chisoni changa? Kodi ena angathandize motani? Kodi pali chiyembekezo chotani cha anthu amene amwalira?

Mungathe kuitanitsa kabuku kameneka polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.