Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kunenepa Kwambiri Ndi Vutodi?

Kodi Kunenepa Kwambiri Ndi Vutodi?

Kodi Kunenepa Kwambiri Ndi Vutodi?

“Vuto loti achinyamata akunenepa kwambiri lasanduka mliri tsopano.”—Anatero S. K. Wangnoo, dokotala wamkulu wodziŵa za kagayidwe ka zakudya m’thupi pa chipatala cha Indraprastha Apollo, ku Delhi, ku India.

MONGA momwe mawu ameneŵa akusonyezera, mabanja ambiri opeza bwino ku India ayamba kukhala moyo umene ukuchititsa achinyamata ambiri kukhala onenepa kwambiri. Mliri umenewu ukufalikira m’mayiko ambiri chifukwa anthu ambiri sakuchita zinthu zambiri zolimbitsa thupi ndipo ayamba kudya zakudya zonenepetsa kwambiri. Dokotala wina wodziŵa za matenda a achinyamata anati: “Mbadwo wotsatira [ku Britain] udzakhala . . . mbadwo wonenepa kwambiri m’mbiri yonse ya anthu.” Nyuzipepala yotchedwa Guardian Weekly inati: “Kale, kunenepa kwambiri kunali kwenikweni vuto la anthu achikulire. Masiku ano ku Britain kuli achinyamata amene kadyedwe kawo ndiponso moyo wawo wosachita zinthu zolimbitsa thupi, zikuwachititsa kukhala ndi mavuto amene anayambira ku United States. Kukhala onenepa kwambiri kwa nthaŵi yaitali kudzawachititsa kuti adzakhale ndi matenda osiyanasiyana monga matenda a shuga, matenda a mtima, ndi khansa.”

Alembi a buku linalake lofotokoza za kunenepa kwambiri ndi mavuto amene kunenepako kumabweretsa, lotchedwa Food Fight anati: “Kudya kwambiri kwasanduka vuto lalikulu kwambiri lokhudza zakudya padziko lonse ndipo kwalowa m’malo mwa kudya mopereŵera.” Don Peck, m’nkhani inayake imene analemba m’magazini yotchedwa The Atlantic Monthly, anati: “Anthu a ku United States okwana pafupifupi nayini miliyoni tsopano ndi ‘onenepa kwambiri moti akudwala nako kunenepako,’ kutanthauza kuti apitirira kulemera kwabwino ndi makilogalamu 45 kapena kuposa pamenepo.” Anthu pafupifupi 300,000 amafa msanga chifukwa cha mavuto obwera ndi kunenepa kwambiri m’dziko limenelo, kutanthauza kuti, kuchotsapo kusuta fodya, kunenepa kwambiri kumapha anthu ambiri “kuposa chinthu china chilichonse.” Peck anamaliza nkhani yake ndi mawu akuti: “Kunenepa kwambiri posachedwapa kungapose njala ndi matenda opatsirana n’kukhala vuto lalikulu kwambiri padziko lonse lokhudza thanzi la anthu.” Choncho, kodi alipo amene angangokankhira kunkhongo vuto la kunenepa kwambiri limeneli? Dr. Walter C. Willett analemba m’buku lake lotchedwa Eat, Drink, and Be Healthy (Idyani, Imwani, Ndipo Khalani Athanzi) kuti “kupatulapo nkhani yakuti kaya mumasuta fodya kapena simusuta, chinthu chachiŵiri chabwino kwambiri chimene chingakuuzeni mmene thanzi lanu lidzakhalire m’tsogolo ndi nambala imene mumaona mukakwera sikelo.” Mawu ofunika kwambiri pamenepa ndi mmene thanzi lanu lidzakhalire m’tsogolo.

Kodi Munthu Wonenepa Kwambiri ndi Wonenepa Motani?

Kodi tikati munthu wanenepa modetsa nkhaŵa osati wangonenepa kwambiri chabe ndiye kuti wanenepa kufika pati? A chipatala cha Mayo ku Rochester, ku Minnesota, ku United States, anati: “M’mawu osavuta, munthu wonenepa modetsa nkhaŵa ndi amene amalemera kwambiri chifukwa chochuluka mafuta m’thupi.” Koma kodi mungadziŵe bwanji kuti munthu akafika apa ndiye kuti walemera kwambiri? Matchati osonyeza kutalika kwa munthu ndi mmene ayenera kulemerera angakusonyezeni moyerekezera chabe ngati munthu akulemera kwambiri, kapena ngati akulemera monkitsa. (Onani tchati pa tsamba 13.) Komabe, manambala ameneŵa satengera kusiyana kwa matupi a anthu. A chipatala cha Mayo anati: “Mafuta amene ali m’thupi mwa munthu, osati kulemera kwa munthu, ndi amene ali chizindikiro chabwino cha thanzi la munthu.” Mwachitsanzo, munthu amene amachita maseŵera osiyanasiyana angakhale wolemera kwambiri chifukwa cha kulemera kwa minofu yake kapena kukula kwa mafupa ake. Kodi n’chiyani chimene nthaŵi zambiri chimachititsa munthu kunenepa kwambiri kapena kunenepa modetsa nkhaŵa? Nkhani yotsatira iyankha funso limeneli.