Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunika Kolimbikitsa Mwana Wanu Kuphunzira

Kufunika Kolimbikitsa Mwana Wanu Kuphunzira

Kufunika Kolimbikitsa Mwana Wanu Kuphunzira

ZIMENE munthu amaphunzira kapena saphunzira ali mwana zingakhudze zimene angadzathe kuchita m’tsogolo. Choncho, kodi ana amafunikira chiyani kuchokera kwa makolo awo kuti adzakhale achikulire olongosoka, oti zinthu zidzawayendere bwino? Taonani zimene anthu ena anena malinga ndi kafukufuku amene wachitika zaka zaposachedwapa.

Ntchito ya Timitsempha ta mu Ubongo

Kupita patsogolo kwa zida zotha kuonera zimene zikuchitika mu ubongo kwathandiza asayansi kuphunzira zinthu zambiri zokhudza kakulidwe ka ubongo zimene kale samazidziŵa. Maphunziro oterowo asonyeza kuti zaka zoyambirira za moyo wa mwana ndi nthaŵi yofunika kwambiri yoti ubongo ukule bwino kuti munthu azidzatha kudziŵa zinthu, kusonyeza bwinobwino mmene akumvera mu mtima, ndi kulankhula bwino chinenero. Magazini ya Nation inati: “Timitsempha ta mu ubongo timalumikizana mwamsanga kwambiri pa zaka zoyambirira za moyo wa munthu popeza ubongo umakhala ukusintha nthaŵi zonse chifukwa cha zinthu zobadwa nazo ndiponso zimene zikuchitikira munthuyo.”

Asayansi akukhulupirira kuti timitsempha tambiri timalumikizana pa zaka zoyambirira za moyo wa munthu. Nthaŵi imeneyi ndi imene “ubongo wa mwana umayala maziko oti m’tsogolo udzathe kulumikiza timitsempha tokhudzana ndi nzeru, kutha kuzindikira kuti iyeyo ndi ndani, kutha kudalira anthu ena, ndi kufuna kuphunzira,” malinga n’zimene ananena katswiri wa kakulidwe ka ana, Dr. T. Berry Brazelton.

Pa zaka zoyambirira za moyo wa mwana, ubongo wake umakula kwambiri, timitsempha ta mu ubongowo timalumikizana kwambiri, ndipo umagwira ntchito kwambiri. Mwana akakhala kuti akulimbikitsidwa kuphunzira ndi kuchita zinthu zosiyanasiyana, timitsempha timalumikizana tambiri mu ubongo wake, ndipo timapanga tinjira tambirimbiri ta mauthenga. Tinjira timeneti n’timene timapangitsa kuti munthu azitha kuganiza ndi kuphunzira.

Zikuoneka kuti mukamalimbikitsa mwana kuchita zinthu zosiyanasiyana, timitsempha tambiri mu ubongo wake timayamba kugwira ntchito ndipo timalumikizananso kwambiri. N’zochititsa chidwi kuti zimenezi sikuti zimangokhudza kulimbikitsa mwana kukhala ndi nzeru chabe, zomwe angazipeze mwa kudziŵa zinthu, manambala, ndi chinenero. Asayansi apeza kuti maganizo akenso amafunika kulimbikitsidwa. Kafukufuku wasonyeza kuti ana amene sakupatilidwa, sasisitidwa ndiponso amene anthu saseŵera nawo kapena kuwalimbikitsa kuganiza, amakhala ndi timitsempha tochepa tolumikizana mu ubongo wawo.

Kodi Kulimbikitsa Mwana Kuphunzira Kungamuthandize Kuchita Zonse Zomwe Angathe?

Zikuoneka kuti mwana akamakula, thupi lake limasiya kugwiritsa ntchito timitsempha tina ta mu ubongo timene tinalumikizana, timene tsopano tikuoneka kuti tilibe ntchito. Zimenezi zingakhudze kwambiri zimene mwana angathe kuchita. Katswiri wofufuza ubongo dzina lake Max Cynader anati: “Ngati mwana salimbikitsidwa kuchita zinthu zinazake pa nthaŵi yoyenera, tinjira ta timitsempha ta mu ubongo sitiyalana bwinobwino.” Malinga n’zimene ananena Dr. J. Fraser Mustard, zotsatirapo zake n’zoti mwana akhoza kukhala wopereŵera nzeru, wosatha kulankhula bwinobwino ndiponso wosatha masamu, akhoza kudzakhala ndi thanzi lofooka akadzakula, ndipo akhoza kudzakhala ndi khalidwe loipa.

Choncho zikuoneka kuti zinthu zimene munthu amakumana nazo ali mwana zingadzakhudzedi moyo wake akadzakula. Kaya munthuyo adzakhala wosakhumudwa msanga kapena wokhumudwa mofulumira, kaya azidzatha kuganiza kwambiri kapena azidzaganiza mopereŵera, ndipo kaya adzakhala munthu wachifundo kapena ayi, zikhoza kudalira zimene anakumana nazo ali mwana. Choncho ntchito ya makolo ndi yofunika kwambiri. Dokotala wina wa ana anati: “Chinthu chimodzi chofunika kwambiri mwana akamakula ndicho kukhala ndi munthu womulera wozindikira bwino zimene mwanayo amafunikira.”

Zimenezo zikuoneka ngati zophweka ndithu. Mukawalimbikitsa ana anu kuphunzira ndi kuwasamalira, zinthu zidzawayendera bwino. Koma makolo amadziŵa kuti kudziŵa mmene angasamalire ana awo bwinobwino si chinthu chophweka. Munthu sabadwa akudziŵa kale mmene angalerere bwino ana.

Malinga ndi kafukufuku winawake, makolo 25 mwa makolo 100 alionse amene anafunsidwa sanadziŵe kuti zimene amachita ndi mwana wawo zingamulimbikitse kapena kumulepheretsa kukhala ndi nzeru, kuchita zinthu modzidalira, ndiponso kukonda kuphunzira. Zimenezi zikudzutsa funso loti: Kodi njira yabwino kwambiri yolimbikitsira mwana kukwanitsa zinthu zimene angathe kuchita ndi yotani? Ndipo kodi mungatani kuti mulimbikitse mwana wanu kuchita zimenezi? Tiyeni tione.

[Chithunzi patsamba 6]

Ana amene amangokhala okhaokha popanda wowalimbikitsa kuchita zinthu zosiyanasiyana sangakule bwino ngati ana ena