Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinaphunzitsidwa Kukonda Mulungu Kuyambira Ndili Mwana

Ndinaphunzitsidwa Kukonda Mulungu Kuyambira Ndili Mwana

Ndinaphunzitsidwa Kukonda Mulungu Kuyambira Ndili Mwana

YOSIMBIDWA NDI ANATOLY MELNIK

Anthu ambiri amandiitana mwachikondi kuti Agogo. Mawu oti agogo amandikhudza mtima kwambiri chifukwa amandikumbutsa agogo anga aamuna, amene ndinkawakonda kwambiri ndipo ndimawathokoza kwambiri chifukwa cha zimene anandichitira. Ndikufuna ndikufotokozereni za agogo anga aamuna ndi aakazi ndi mmene anasinthira kwambiri moyo wa anthu a m’banja mwawo ndiponso wa anthu ena ambiri.

NDINABADWA m’mudzi wa Hlina, kumpoto kwa dziko limene masiku ano limatchedwa Moldova. * M’zaka za m’ma 1920, atumiki oyendayenda, amene ankatchedwa aulendo wachipembedzo, anabwera kuchokera ku dziko loyandikana nalo la Romania n’kufika ku dera la kwathu lamapiri okongola. Makolo a mayi anga anakhulupirira nthaŵi yomweyo uthenga wabwino umene anaumva ukulalikidwa kuchokera m’Baibulo. Mu 1927, anakhala Ophunzira Baibulo, monga momwe Mboni za Yehova zinkadziŵikira masiku amenewo. Pamene nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inkayamba mu 1939, m’mudzi wathu waung’onowo munali kale mpingo wa Mboni za Yehova.

Pamene ine ndinabadwa m’chaka cha 1936, azibale anga onse anali Mboni za Yehova kupatulapo bambo anga, amene anali akadali m’Tchalitchi cha Orthodox. Panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse, anayamba kuganizira mofatsa cholinga cha moyo ndipo pamapeto pake anadzipatulira kwa Mlengi wathu, Yehova Mulungu, ndipo anasonyeza zimenezi mwa kubatizidwa m’madzi. Agogo anga aamuna anathandiza kwambiri banja lathu kupita patsogolo mwauzimu. Ankakonda kwambiri Baibulo ndipo ankadziŵa mavesi ambirimbiri pamtima. Ankatha kusintha nkhani iliyonse n’kuiloŵetsa m’Baibulo.

Nthaŵi zambiri ndinkakhala pamwendo pa Agogo aamuna n’kumawamvetsera akundiuza nkhani za m’Baibulo. Anandiphunzitsa kukonda kwambiri Mulungu. Ndimawathokoza kwambiri chifukwa chochita zimenezo. Pamene ndinali ndi zaka eyiti, ndinapita kolalikira koyamba ndi Agogo aamuna. Pogwiritsa ntchito Baibulo, tinafotokozera anthu a m’mudzi mwathu kuti Yehova ndi ndani ndiponso mmene angayandikirane naye.

Kuzunzidwa ndi Anthu Achikomyunizimu

Mu 1947, potsatira malamulo a Chikomyunizimu ndiponso zonena za Tchalitchi cha Orthodox, akuluakulu a boma anayamba kuzunza Mboni za Yehova ku Moldova. Apolisi a gulu limene linadzayamba kutchedwa kuti KGB ndiponso apolisi wamba ankabwera ku nyumba zathu n’kumatifunsa kuti tiwauze amene anali kutsogolera ntchito yathu yolalikira, kumene mabuku athu anali kuchokera, ndi kumene tinali kukumana polambira. Anati adzaletsa ntchito ya Mboni za Yehova, chifukwa ankati “zimalepheretsa kupita patsogolo kwa Chikomyunizimu m’dzikomo.”

Panthaŵi imeneyi, Bambo, amene anali munthu wophunzira kwambiri, analinso atayamba kukonda kwambiri choonadi cha m’Baibulo. Iwo ndi Agogo aamuna ankatha kuyankha mwanzeru anthu akamawafunsa mafunso n’cholinga choti asaike pamavuto abale ndi alongo athu achikristu. Aŵiri onseŵa anali amuna olimba mtima ndi achikondi amene ankafunira zabwino okhulupirira anzawo. Mofanana ndi iwowo, Amayi nthaŵi zonse ankayankha modekha.

Mu 1948, Bambo anamangidwa n’kutengedwa. Sitinauzidwe kuti anawapeza ndi mlandu wotani. Anawalamula kuti akakhale zaka seveni m’ndende yokhala ndi chitetezo chokhwima kwambiri ndi zaka zina ziŵiri kunja kwa dziko lathu. Pomalizira pake anawatumiza ku dera la Magadan kumpoto chakum’maŵa kwa Russia, umene unali pamtunda wa makilomita opitirira 7,000 kuchokera kwathu. Sitinaonane kwa zaka nayini. Zinali zovuta kukhala wopanda bambo, koma Agogo aamuna anandithandiza kwambiri.

Kusamutsidwira ku Dziko Lina

Usiku wa pa June 6, 1949, asilikali aŵiri ndi wapolisi mmodzi anatiloŵera m’nyumba mwathu. Anatipatsa maola aŵiri okha kuti tichoke m’nyumbamo n’kuloŵa m’galimoto yawo. Sanatilongosolerenso china chilichonse. Anangotiuza kuti tinali kusamutsidwira ku dziko lina ndipo sitidzabwereranso. Choncho ndinasamutsidwira ku Siberia limodzi ndi Amayi, Agogo aamuna, Agogo aakazi, ndi anzathu ena okhulupirira. Ndinali ndi zaka 13 zokha. Patatha milungu ingapo tinafika ku dambo linalake, lokhala ndi nkhalango za mitengo yothithikana kwambiri. Dera limeneli linali losiyana kwambiri ndi kumudzi kwathu, kumene ndinkakukonda kwambiri. Nthaŵi zina tinkalira. Komabe, tinkakhulupirira kuti Yehova sadzatitaya.

Kamudzi kakang’ono kamene anatipititsako kanali ndi tinyumba ting’onoting’ono tokwana teni tomangidwa ndi mitengo. Mboni zina zinatumizidwa ku midzi ina m’dera limeneli. Pofuna kuopseza anthu okhala m’derali, komanso pofuna kuwalimbikitsa kudana nafe, akuluakulu a boma anawauza kuti a Mboni amadya anthu anzawo. Koma pasanapite nthaŵi yaitali anthuwo anazindikira kuti limeneli linali bodza ndipo panalibe chifukwa choti azitiopera.

Miyezi iŵiri yoyambirira titafika ku derako tinakhala m’kanyumba kenakake kakalekale. Koma tinafunika kumanga nyumba yoyenerera, nyengo yozizira kwambiri isanafike. Agogo aamuna ndi Agogo aakazi anathandiza ine ndi Amayi kumanga kanyumba kosavuta kumanga, kamene theka lake linali pamwamba pa nthaka ndipo theka lina linali pansi pa nthaka. Tinakhala m’kanyumba kameneko kwa zaka zopitirira zitatu. Sitinkaloledwa kuchoka m’mudzimo opanda chilolezo, komanso chilolezocho sichinkaperekedwa n’komwe.

Patapita nthaŵi ndinaloledwa kumapita ku sukulu. Popeza chipembedzo changa chinali chosiyana ndi cha anthu ena kusukuluko, aziphunzitsi ndi ana asukulu anzanga nthaŵi zambiri ankandifunsa mafunso. Agogo aamuna ankasangalala kwambiri ndikabwera kunyumba n’kuwauza mmene ndinafotokozera zinthu zimene timakhulupirira kwa anthu ena.

Tinapezako Kaufulu

M’tsogoleri wopondereza anthu Stalin atamwalira mu 1953, zinthu zinasinthako pang’ono ndipo moyo wathu unakhala wabwinoko. Tinayamba kuloledwa kutuluka m’mudzimo. Choncho tinatha kuyamba kukumana ndi okhulupirira anzathu ndi kupita ku misonkhano m’midzi imene kunatumizidwa Mboni zina. Kuti tisadabwitse anthu, tinkakumana m’timagulu ting’onoting’ono. Kuti tikafike kumeneko, tinkayenda pafupifupi makilomita 30. Nthaŵi zina tinkayenda m’chipale chofewa chomwe chinkafika mpaka m’mawondo, kunja kukuzizira koopsa. Tsiku lotsatira tinkayenda ulendo wautali wobwerera kunyumba. M’njiramo tinkadya tinkhaka ting’onoting’ono ndi timibulu tingapo ta shuga. Komabe tinali osangalala kwambiri, monga mmene anachitira Davide wakale!—Salmo 122:1.

Mu 1955, ndinabatizidwa posonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova. Nthaŵi yochepa izi zisanachitike, pamsonkhano wampingo kumudzi wapafupi, ndinakumana ndi Lidiya, mtsikana waulemu, wooneka bwino, watsitsi lakuda. Mofanana ndi ifeyo, iye ndi banja lake anali Mboni zimene zinasamutsidwa ku Moldova. Ankaimba bwino kwambiri ndipo analoweza pafupifupi nyimbo zonse 337 zimene zinali mu buku lathu lanyimbo limene tinkagwiritsa ntchito panthaŵi imeneyo. Zimenezi zinandisangalatsa kwambiri chifukwa nanenso ndinkakonda kwambiri nyimbo zathu. Mu 1956, tinagwirizana zokwatirana.

Ndinalembera Bambo kalata, chifukwa tinali titamva kuti anasamutsidwira ku Magadan, ndipo tinadikirira kuti ativomereze kaye tisanakwatirane. Pasanapite nthaŵi yaitali Bambo anamasulidwa ndipo anabwera kudzakhala nafe kumene tinali kukhala. Anatifotokozera mmene iwo ndi Akristu ena anapulumukira mavuto oipa kwambiri ku ndende zozunzirako anthu pothandizidwa ndi Mulungu. Nkhani ngati zimenezo zinalimbikitsa chikhulupiriro chathu.

Patangopita nthaŵi yochepa Bambo atabwera, tsiku lina pamene Amayi anali kukonza mafuta enaake amene tinkasakaniza mu penti ndi mu vanishi, panachitika ngozi yoopsa. Chimphika chachikulu cha mafuta owira chinapendekeka mwangozi, ndipo mafutawo anawakhuthukira Amayiwo. Anamwalira kuchipatala. Tinali ndi chisoni chosaneneka. Kenaka chisoni cha Bambo chinachepako, ndipo patapita nthaŵi anakwatira a Tatyana, Mboni ya m’mudzi wapafupi ndi wathu.

Kuwonjezera Utumiki Wathu

Mu 1958, ine ndi Lidiya tinasamuka m’mudzi womwe tinali kukhala wa Kizak, n’kupita ku mudzi wokulirapo wa Lebyaie, womwe unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 100. Tinali titaŵerenga kuti m’mayiko ena Akristu amalalikira ku nyumba ndi nyumba. Choncho tinayesera kuchita zimenezi ku dera lathu latsopanolo. Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! anali oletsedwa, koma tinkalandira magaziniŵa mwakabisira kuchokera ku madera kwina. Kenaka anatiuza kuti tizilandira magazini a m’chinenero cha Chilasha chokha. Nthaŵi yonseyi mpaka nthaŵi imeneyo, tinkalandiranso magazini a m’chinenero cha Chimodova. Choncho tinaphunzira mwakhama kuti tidziŵe bwino chinenero cha Chilasha. Mpaka lero ndimakumbukirabe mitu ya nkhani zimenezo, ngakhale mfundo zake zina.

Kuti tizipeza zofunika pamoyo wathu, Lidiya ankagwira ntchito pa chikepe chonyamula tirigu, ndipo ine ndinkagwira ntchito yotsitsa matabwa m’ngolo. Ntchito yake inali yolemetsa, komanso malipiro ake anali ochepa kwambiri. Ngakhale kuti anthu a Mboni ankadziŵika kuti amagwira ntchito mwakhama, sitinkapatsidwa chithandizo chilichonse cha ndalama kapena mabonasi. Akuluakulu a boma ankanena poyera kuti: “Mboni za Yehova sitikuzifuna m’dziko la Chikomyunizimu.” Komabe, tinkasangalala poona kuti mawu a Yesu onena za otsatira ake anali kukwaniritsidwa pa ife, oti: “Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi.”—Yohane 17:16.

Mavuto Enanso

Mu 1959, mwana wathu wamkazi, Valentina, anabadwa. Patangopita kanthaŵi kochepa, kunayambika chizunzo chatsopano. Buku la Encyclopædia Britannica limati: “Kuyambira mu 1959 mpaka 1964, Nduna Yaikulu, Nikita Khrushchev inayamba kuzunza anthu achipembedzo.” Apolisi a gulu la KGB anatiuza kuti cholinga cha boma la Soviet chinali kuthetsa zipembedzo zonse, makamaka chipembedzo cha Mboni za Yehova.

Pamene Valentina anali ndi chaka pafupifupi chimodzi, anandiitana kuti ndipite kunkhondo. Nditakana kupita, ndinaŵeruzidwa kuti ndikhale zaka zisanu m’ndende chifukwa chokana kutenga nawo mbali m’nkhondo. Tsiku lina Lidiya atabwera kudzandiona, wapolisi wa KGB anamuuza kuti: “Tauzidwa ndi boma la Russia kuti pomatha zaka ziŵiri, m’dziko la Soviet Union simudzakhalanso munthu wa Mboni za Yehova ngakhale mmodzi.” Ndiyeno anamuchenjeza kuti: “Usiye chipembedzo chako, apo ayi udzaikidwa m’ndende.” Wapolisiyo ankaganiza kuti kuopseza koteroko kudzawachititsa mantha azimayiwo, ndipo anati: “Azimayi ameneŵa ndi anthu ofooka.”

Pasanapite nthaŵi yaitali, amuna ambiri a Mboni anaikidwa m’ndende wamba ndi m’ndende zozunzirako anthu. Komabe, azimayi achikristu olimba mtima anapitiriza ntchito yolalikira. Ndipo ankabisa mabuku n’kumawapereka kwa anthu amene anali m’ndendezo, ngakhale kuti kuchita zimenezi kunali kuika miyoyo yawo pangozi. Lidiya anakumana ndi mavuto oterowo, ndiponso nthaŵi zambiri ankavutitsidwa ndi amuna amene ankapezerapo mwayi poona kuti ine kulibe. Kuwonjezera apo, anauzidwa kuti ineyo sindidzamasulidwa. Koma ndinamasulidwa!

Ndinamasulidwa N’kusamukira ku Kazakhstan

Mlandu wanga anayambanso kuuweruza mu 1963, ndipo kenaka ndinamasulidwa, nditakhala zaka zitatu m’ndende. Koma tinalephera kupeza chikalata chotiloleza kukhala kulikonse m’dzikolo, choncho sindinathe kupeza ntchito. Lamulo la m’dzikolo linanena kuti: “Wopanda chilolezo chokhalira m’dziko muno saloledwa kugwira ntchito.” Tinachonderera Yehova m’pemphero kuti atithandize. Kenaka tinaganiza zosamukira ku Petropavl kumpoto kwa Kazakhstan. Koma akuluakulu a boma kumeneko anali atauzidwa kale za ife ndipo anakana kutiloleza kukhala kumeneko kapena kugwirako ntchito. Mboni zina pafupifupi 50 mu mzinda umenewu zinavutikanso chimodzimodzi.

Limodzi ndi banja lina la Mboni, tinasamukira kum’mwera, ku tauni yaing’ono ya Shchuchinsk. Kumeneko kunalibe Mboni zina, ndipo akuluakulu a boma kumeneko sankadziŵa chilichonse chokhudza ntchito yathu yolalikira. Kwa mlungu umodzi ine ndi mwamuna mnzangayo Ivan tinkafuna ntchito pamene azikazi athu ankakhala pa siteshoni ya sitima, pamene tinali kugona madzulo. Kenaka tinapeza ntchito pa fakitale yopanga magalasi. Tinachita lendi chipinda chaching’ono choti tonsefe tizikhalamo chimene munkangokwanira mabedi aŵiri ndi zinthu zina zochepa basi, koma tinakhutira nacho.

Ine ndi Ivan tinkagwira ntchito yathu mwakhama kwambiri, ndipo mabwana athu ankasangalala nafe. Panthaŵi imene ndinadzaitanidwanso kuti ndipite kunkhondo, abwana a fakitaleyo anali atadziŵa kuti chikumbumtima changa chophunzitsidwa Baibulo sichikanandilola kupita ku nkhondo. Modabwitsa, analankhulana ndi mkulu wa asilikali n’kumuuza kuti ine ndi Ivan tinali antchito aluso kwambiri ndipo fakitaleyo sikanayenda popanda ifeyo. Choncho tinaloledwa kukhala.

Kulera Ana Ndiponso Kutumikira Anthu Ena

Mwana wathu wamkazi wachiŵiri, Lilya, anabadwa mu 1966. Chaka chotsatira tinasamukira ku Belyye Vody, kum’mwera kwa Kazakhstan kufupi ndi malire a dziko la Uzbekistan, kumene kunali kagulu kochepa ka Mboni. Kenaka kunapangidwa mpingo ndipo ine ndinaikidwa kukhala woyang’anira wotsogolera. Mu 1969, tinakhala ndi mwana wamwamuna, Oleg, ndipo zaka ziŵiri pambuyo pake tinakhala ndi mwana wathu wamkazi womaliza, Natasha. Ine ndi Lidiya nthaŵi zonse tinkakumbukira kuti ana ndi cholandira chochokera kwa Yehova. (Salmo 127:3) Tinkakambirana zimene tinayenera kuchita kuti tiwalere mowathandiza kukonda Yehova.

Ngakhale m’zaka za m’ma 1970, amuna ambiri a Mboni anali adakali m’ndende zozunzirako anthu. Mipingo yambiri inkafunikira anthu okhwima mwauzimu kuti aziiyang’anira ndi kuitsogolera. Choncho ndinayamba kutumikira monga woyang’anira woyendayenda, pamene Lidiya ankagwira ntchito yaikulu yolera ana athu, nthaŵi zina kumagwira ntchito ya mayi ndi bambo yemwe. Ndinkayendera mipingo ku Kazakhstan, ndiponso mayiko oyandikana nafe a Tajikistan, Turkmenistan, ndi Uzbekistan amene anali kulamulidwa ndi boma la Soviet. Panthaŵi imodzimodziyo ndinkagwiranso ntchito kuti banja lathu lizipeza zofunika pamoyo, ndipo Lidiya ndi anawo anachita zinthu mogwirizana nane.

Ngakhale kuti nthaŵi zina ndinkachokapo kwa milungu ingapo, ndinayesetsa kuwakonda anawo monga atate wawo ndi kuwathandiza kukula mwauzimu. Ine ndi Lidiya tinkapemphera limodzi kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima kuti athandize ana athu, ndipo tinkakambirana nawo zimene angachite kuti asamaope anthu ndi kuti akhale ndi ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Pakanapanda thandizo lachikondi la mkazi wanga, sindikanakwanitsa udindo wanga monga woyang’anira woyendayenda. Lidiya ndi alongo athu ena sanali “anthu ofooka” ngati mmene wapolisi uja ananenera. Anali olimba, amphamvudi mwauzimu!—Afilipi 4:13.

Mu 1988, ana onse atakula, ndinaikidwa kukhala woyang’anira woyendayenda wokhazikika. Dera langa linaphatikizapo mayiko ambiri a pakati pa Asia. Ntchito ya Mboni za Yehova itavomerezedwa ndi boma m’dziko limene kale linali Soviet Union mu 1991, amuna ena oyeneretsedwa, okhwima mwauzimu anayamba kutumikira m’mayiko a ku Asia, amene kale anali kulamulidwa ndi dziko la Soviet Union. Masiku ano, m’mayiko ameneŵa muli oyang’anira oyendayenda okwana 14, ndipo chaka chatha anthu opitirira 50,000 anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu!

Kuitanidwa Mosayembekezera

Kumayambiriro kwa 1998, ndinalandira telefoni yosayembekezera kuchokera ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Russia. Anandifunsa kuti: “Anatoly, kodi iwe ndi Lidiya munaganizirapo zochita utumiki wa nthaŵi zonse?” N’zoona kuti tinaganizirapo zoti ana athu angachite utumiki woterowo. Ndipo mwana wathu wamwamuna, Oleg, n’kuti atatha pafupifupi zaka zisanu akutumikira pa ofesi ya nthambi ya ku Russia.

Nditamuuza Lidiya zimene anatipemphazo, anandifunsa kuti: “Nanga nyumba yathuyi, munda wathu, katundu wathu, titani nazo?” Titapemphera ndi kukambirana, tinaganiza zoti tivomere. Kenaka tinapemphedwa kukatumikira pa likulu la Mboni za Yehova ku Issyk, ku Kazakhstan, pafupi ndi mzinda waukulu wa Alma-Ata. Kunoko n’kumene amagwira ntchito yomasulira mabuku athu ofotokoza za m’Baibulo kuti akhale m’zinenero zimene zimalankhulidwa m’dera limeneli.

Banja Lathu Masiku Ano

Tikuthokoza kwambiri Mulungu potithandiza kuphunzitsa ana athu choonadi cha m’Baibulo! Mwana wathu wamkazi woyamba, Valentina, anakwatiwa ndipo anasamukira ku Ingelheim, ku Germany, ndi mwamuna wake mu 1993. Ali ndi ana atatu, ndipo onsewo ndi Mboni zobatizidwa za Yehova.

Lilya, mwana wathu wamkazi wachiŵiri, nayenso ali ndi banja lake. Iye ndi mwamuna wake, amene ali mkulu mu mpingo wa Belyye Vody, akulera ana awo aŵiri m’njira yowathandiza kukonda Mulungu. Oleg anakwatira Natasha, mlongo wa ku Moscow, ndipo akutumikira limodzi pa ofesi ya nthambi ya ku Russia pafupi ndi mzinda wa St. Petersburg. Mwana wathu wamkazi womaliza, Natasha, anakwatiwa mu 1995, ndipo akutumikira limodzi ndi mwamuna wake mu mpingo wa chinenero cha Chilasha ku Germany.

Nthaŵi zina banja lathu lonse limakumana pamodzi. Ana athu amauza ana awo mmene “Amama” ndi “Ababa” awo anamvera Yehova ndi kulera ana awo m’njira yowathandiza kukonda ndi kutumikira Mulungu woona, Yehova. Ndimaona kuti kukambirana zinthu zimenezi kumathandiza zidzukulu zanga kukula mwauzimu. Chidzukulu chathu chachimuna chomaliza chimafanana ndi ineyo mmene ndinali msinkhu wake. Nthaŵi zina amakwera pamwendo panga ndipo amandipempha kuti ndimuuze nkhani ya m’Baibulo. M’maso mwanga mumalengeza misozi chifukwa cha chisangalalo ndikakumbukira nthaŵi zambiri zimene ndinkakhala pamwendo pa Agogo aamuna ndi mmene anandithandizira kukonda Mlengi wathu Wamkulu ndi kumutumikira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Dzina limene dzikoli limadziŵika nalo masiku ano, loti Moldova, n’limene tigwiritse ntchito mu nkhani yonseyi m’malo mwa mayina akale oti Moldavia kapena Soviet Republic of Moldavia.

[Chithunzi patsamba 21]

Ndili ndi makolo anga panja pa nyumba yathu ku Moldova, Bambo atatsala pang’ono kumangidwa

[Chithunzi patsamba 22]

Ndili ndi Lidiya mu 1959, tikadali ku dziko limene tinasamutsidwirako

[Chithunzi patsamba 23]

Lidiya ali ndi mwana wathu Valentina ine ndili m’ndende

[Chithunzi patsamba 25]

Ine ndi Lidiya masiku ano

[Chithunzi patsamba 25]

Tili ndi ana athu ndi zidzukulu zathu, ndipo tonsefe tikutumikira Yehova!