Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ubwino Woŵerengera Ana

Ubwino Woŵerengera Ana

Ubwino Woŵerengera Ana

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU POLAND

Amene anakonza kampeni yapachaka yomwe mutu wake unali wakuti “Anthu Onse a ku Poland Aziŵerengera Ana” anati: “Kuŵerenga n’kofunika kwambiri kuti munthu adziŵe zinthu ndiponso kuti akhale wanzeru. . . . Munthu amatseguka mutu ndipo amadziŵa zimene ena anatulukira ndiponso zimene amadziŵa.” Ngati zimenezi zili zoona, n’chifukwa chiyani anthu ambiri, akuluakulu ndi ana omwe, amaona kuti kuŵerenga ndi ntchito yosasangalatsa yongofunika kuichita basi?

Amene anakonza kampeni imeneyi anati: “Chizoloŵezi choŵerenga ndi kukonda mabuku chiyenera kuyamba munthu ali mwana.” Iwo anauza makolo kuti: “Ngati mukufuna kuti ana anu adzakhale anzeru, azidzakhoza kusukulu, ndiponso zinthu zidzawayendere bwino pamoyo wawo, muziwaŵerengera motulutsa mawu kwa mphindi 20 tsiku lililonse.”

Iwo anauzanso makolo kuti asamachedwe kuyamba kuŵerengera ana awo koma kuti “aziyamba mwamsanga kwambiri.” Kodi aziyamba liti? Makolowo analimbikitsidwa kuti: “Tiziŵerengera mwana wakhanda, titamunyamula m’manja mwathu, tikumuyang’ana mwachikondi, ndipo mawu athu azidzutsa chidwi chake. Mwa njira imeneyi, mwanayo nthaŵi zonse adzaona kuti kuŵerenga n’kogwirizana ndi kutetezeka, kusangalala, ndiponso kukondedwa. Kuwonjezera apo, zimamulimbikitsa kuganiza.”

Amene anakonza kampeniwo ananenetsa kuti “kuŵerengera ana n’kofunika kwambiri masiku ano kuposa kale,” ndipo anatchulapo ubwino winanso woŵerengera ana. Kuŵerenga motulutsa mawu kumaphunzitsa ana kuganiza, “kumawathandiza kumvetsetsa anthu ena, kumvetsetsa dzikoli, ndiponso kudzimvetsetsa iwo eni, . . . kumadzutsa chidwi chawo, kumawaphunzitsa kuyerekezera zinthu, kumawathandiza kumva zinthu mumtima mwawo ndi kumvera ena chisoni, kumawaphunzitsa makhalidwe abwino, . . . ndiponso kumawathandiza kukhala odzidalira.” Mosakayikira, kuŵerengera ana “kumawathandiza kupeŵa kutengera zinthu zambiri zoipa. . . zimene zingawononge maganizo ndi mitima yawo,” anamaliza motero atsogoleri a kampeniyo.

Kuti kuŵerengako kukhale kwaphindu kwambiri, muyenera kugwiritsa ntchito mabuku amene amalimbikitsa ana kukonda kwambiri Mlengi wawo wakumwamba. Baibulo ndilo buku labwino kwambiri limene lingatithandize kukonda kwambiri Mulungu. Baibulo limati “kuyambira ukhanda,” mnyamata wina dzina lake Timoteo anaphunzitsidwa “malembo opatulika.” (2 Timoteo 3:15) Poŵerengera ana awo motulutsa mawu, makolo angagwiritsenso ntchito mabuku ofotokoza za m’Baibulo monga Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndi Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, amene makamaka ndi mabuku a ana, ndipo amafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.