Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Aliyense Ayenera Kuwerenga Buku Limeneli”

“Aliyense Ayenera Kuwerenga Buku Limeneli”

“Aliyense Ayenera Kuwerenga Buku Limeneli”

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU POLAND

Kuyambira m’chilimwe cha chaka cha 2003, buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso linatulutsidwa m’zinenero zambiri pa misonkhano yachigawo padziko lonse lapansi. Mofanana ndi kumayiko kwina, ku Poland anthu atalandira buku lokhala ndi zithunzi zokongola limeneli anasangalala kwambiri. Ngakhale kuti kwenikweni bukuli analembera ana, makalata ochokera kwa achinyamata ndi achikulire asonyeza kuti bukuli limasangalatsa anthu a zaka zosiyanasiyana. M’munsimu muli mawu ena ochokera m’makalatawo.

“Dzina langa ndine Agata, ndipo ndili ndi zaka eyiti. Nditalandira bukuli, nthawi yomweyo ndinamva kuti Yehova amandikonda kwambiri. Mutu umene ndimakonda kwambiri ndi mutu 7, woti, ‘Kumvera Kudzakuteteza.’ Si nthawi zonse pamene ndakhala ndikumvera makolo anga, koma tsopano ndikudziwa kuti ndiyenera kusintha chifukwa Yehova amakonda ana omvera.”

Marlena, mtsikana wa zaka 13, pogoma nalo bukuli analemba motere: “Ndikudziwa kuti buku limeneli analembera ana aang’ono, koma ndikukhulupirira kuti limasangalatsa aliyense. Ndikaliwerenga chikhulupiriro changa mwa Yehova ndi Yesu chimalimba. Ngakhale zinthu zovuta anazifotokoza m’njira yosavuta kumva. Sindikufuna kusiya kuliwerenga. Ndipo zithunzi zake n’zokongola kwabasi! Mafunso amene ali pa zithunzizo adzachititsa chidwi ana aang’ono. Bukuli n’labwino kwambiri, choncho ndikuliwerenga mosamala. Zikomo kwambiri.”

Justyna, mtsikana wa zaka 15 akufotokoza mmene bukuli lamusangalatsira. Iye akuti: “Mitu imene ndawerenga yandichititsa chidwi kwambiri moti ndikufuna ndikuthokozeni kuchokera pansi pa mtima chifukwa cha mphatso yokongola ndi yophunzitsa imeneyi. Ndikuganiza kuti aliyense ayenera kuwerenga buku limeneli, ngakhale anthu achikulire. Zitsanzo zimene zili mmenemo n’zosavuta kumva, ndipo ndikuganiza kuti ngakhale mwana wa chaka chimodzi akhoza kuzimvetsa. Ndipo zithunzi zake pazokha n’zophunzitsa. Kungoti n’zovuta kuti ndifotokoze bwinobwino mmene ndimamvera ndikamawerenga buku limeneli.”

Eunika nayenso akuyamikira kwambiri buku limeneli. Ngakhale kuti ali ndi zaka 19, anawerenga buku latsopanoli mwachidwi kwambiri ndipo akuti anapeza kuti “n’lothandiza kwambiri achinyamata.” Iye analembanso kuti: “Lili ndi malangizo othandiza munthu tsiku ndi tsiku, kunyumba, kusukulu, ndi mumpingo. Zikomo kwambiri chifukwa cha mphatso imeneyi.”

Maria, mayi amene akusangalala kuti ali ndi mwana wa chaka chimodzi dzina lake Oliwia, ataona zomwe mwana wakeyo amachita akaona zithunzi zokongola za m’bukuli, anati: “Ndikufuna ndikuthokozeni kuchokera pansi pa mtima chifukwa cha thandizo lapadera limeneli lophunzitsira ana. Mwana wathu Oliwia safuna kulisiya bukuli. Amakhala pamiyendo pathu ndipo amafuna timufotokozere zomwe zili m’mitu yosiyanasiyana. Amakonda kwambiri chithunzi chimene chili pa tsamba 83, chosonyeza atsikana awiri a khungu losiyana atakolekana manja m’khosi. Zithunzi zina zimaoneka ngati zenizenidi moti amazikhudza, kuzikupatira, n’kuzisekerera.”

Maria akufotokozanso zinthu zothandiza zimene bukuli limaphunzitsa. Iye akuti: “Limafotokoza nkhani zofunika zokhudza kugonana (tsamba 58-60) ndi kugwiririra ana (tsamba 170-171). Ndi buku lothandiza kwambiri makolo amene akufuna kulera ana awo mwanzeru m’dziko loipa lamasiku anoli, limene lili ndi zoopsa zambirimbiri.”

Ofalitsa a buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso akufuna kuti bukuli lithandizenso inuyo ndi ana anu kuti mupindule ndi zinthu zimene Mphunzitsi Waluso, Yesu Kristu, anaphunzitsa anthu zaka pafupifupi 2,000 zapitazo.

[Chithunzi patsamba 15]

Agata

[Chithunzi patsamba 15]

Marlena

[Chithunzi patsamba 15]

Eunika

[Chithunzi patsamba 15]

Maria ndi Oliwia

[Chithunzi patsamba 15]

Justyna