Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khoti la ku Ulaya Linalemekeza Ufulu wa Mayi

Khoti la ku Ulaya Linalemekeza Ufulu wa Mayi

Khoti la ku Ulaya Linalemekeza Ufulu wa Mayi

Yolembedwa ndi wolemba Galamukani! ku France

PA December 16, 2003, khoti la ufulu wachibadwidwe wa anthu la ku Ulaya lotchedwa European Court of Human Rights, lomwe lili ku Strasbourg, ku France, linapeza kuti makhoti a ku France anali olakwa pa mlandu wochita tsankho lachipembedzo kwa Séraphine Palau-Martínez, wa Mboni za Yehova.

Mu 1996, Séraphine analoledwa kusudzula mwamuna wake, amene anamuthawa zaka ziwiri m’mbuyomo. Séraphine anauzidwa kuti iyeyo ndi amene azikhala ndi ana awo awiri. Koma mu 1997, panthawi imene anawo anali atakhala ndi mayi awo kwa zaka pafupifupi zitatu, bambo wa anawo anakana kuwabwezera kwa mayi awo nthawi yoti acheze nawo itatha. Séraphine anafotokoza kuti: “Nditapita kukawatenga anawo kusukulu kuti ndipite nawo kunyumba, mkulu wa sukuluyo anaitana apolisi. Kuti ndilankhule ndi ana anga panafunika pakhale apolisi kuti aonetsetse kuti sindikulankhula nawo za chikhulupiriro changa. Zinkakhala ngati kuti ndine chigawenga. Anandiuza kuti, kuti ndiwatenge anawo ndinafunika kusaina chipepala chonena kuti sindilankhula nawo za Mulungu, Baibulo, kapena kuwapititsa ku misonkhano yachikristu.”

Séraphine anatengera nkhaniyo kukhoti. Komabe, mu 1998, khoti la apilo la ku Nîmes linanena kuti anawo azikhala ndi bambo awo. Podziikira kumbuyo, linanena kuti Mboni za Yehova zimaphunzitsa ana awo zinthu zoipa, ngakhale kuti mfundo zambirimbiri zimene anaperekazo zinalibe maziko alionse. Séraphine anafotokoza kuti: “Zinandipweteka kwambiri kuimbidwa mlandu woti ndinali kuwononga ana anga, pamene ndinali kuyesetsa kuwaphunzitsa zinthu zimene ndimakhulupirira kuti zinali zabwino kwambiri kwa iwo. Ndinali kuyesetsa kuwalera kuti akhale Akristu.”

Khoti la Cour de Cassation, limene lili khoti la apilo lalikulu ku France, litagwirizana ndi chigamulo cha khoti laling’ono lija, Séraphine anaganiza zotengera mlanduwo ku khoti la European Court of Human Rights. Pachigamulo chimene majaji 6 anagwirizana nacho ndipo jaji mmodzi yekha sanagwirizane nacho, khotilo linagamula kuti: “Khoti lino silikukayikira n’komwe kuti khoti la apilo [la ku France] linawachitira zinthu makolo awiriwo mosiyana chifukwa cha chipembedzo cha wodandaulayo. . . . Kuwachitira zinthu mosiyana koteroko ndi tsankho.” Khotilo linati, khoti la ku France lija popereka chigamulo chake silinayang’ane mfundo yoti Séraphine angathe kuyang’anira ana ake bwinobwino, mfundo imene palibe amene anaitsutsa, kapena kuyang’ana umboni weniweni, koma m’malo mwake linagwiritsa ntchito “zinthu zopanda maziko zimene anamva zokhudza Mboni za Yehova.” Chifukwa cha tsankho lachipembedzo limeneli ndiponso kumuphwanyira Séraphine ufulu wake, khotilo linalamula kuti dziko la France limupatse Séraphine ndalama za chipukuta misozi ndiponso limubwezere ndalama zonse zomwe anawononga pamlanduwo.

Chigamulo chimenechi n’chofanana ndi chigamulo china cha khoti la European Court of Human Rights cha mu June 1993, pa mlandu wofanana ndi womwewu pamene khotilo linalamula kuti dziko la Austria linasonyeza tsankho kwa Ingrid Hoffmann, wa Mboni za Yehova, chifukwa cha chipembedzo chake. * Magazini yofotokoza za malamulo ku France yotchedwa La Semaine juridique inati: “Mogwirizana ndi chigamulo cha mlandu wa Hoffmann, chigamulo chimenechi chikutsimikiza mfundo yoti ulamuliro umene makolo ali nawo pa ana awo suyenera kudalira makamaka chipembedzo cha makolowo.” Loya wa Séraphine anati: “Chigamulo chimenechi n’chofunika kwambiri, chifukwa chikusonyeza kuti makhoti akhala akugamula mofanana kuti makolo amene ali Mboni za Yehova ali ndi ufulu woweruzidwa mopanda tsankho.”

Séraphine, amene tsopano amakhala ku Spain atafunsidwa mmene akumvera chifukwa cha chigamulocho, anati: “Ndine wosangalala kwambiri ndiponso mtima wanga wakhala m’malo. Zinali zopweteka kwambiri kulandidwa ana anga ndiponso osawaona kwa zaka zisanu, koma Yehova anandithandiza nthawi yonseyo. Chiyembekezo changa n’choti chigamulo chimenechi chithandizenso anthu ena amene ali ndi mavuto ofanana ndi anga.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Onani nkhani yakuti “Mboni za Yehova Zilemekezedwa Pankhondo ya Kuyenera kwa Kusunga Ana,” mu Galamukani! ya October 8, 1993, tsamba 15.

[Chithunzi patsamba 18]

Séraphine