Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Edzi Idzatha Liti?

Kodi Edzi Idzatha Liti?

Kodi Edzi Idzatha Liti?

Kuyambira ali aang’ono, achinyamata amaona mauthenga ambirimbiri okhudza kugonana amene amalimbikitsa munthu kuchita zachiwerewere. Kugwiritsa ntchito masingano podzibaya jakisoni, imene ili njira inanso yaikulu yotengera Edzi, kwafalanso kwambiri. Poona momwe khalidwe lotayirira lafalira masiku ano, mwina mungakayikire zoti Edzi idzatha.

MADOKOTALA osiyanasiyana amanena mosapita m’mbali kuti kusintha khalidwe ndiyo njira yofunika kwambiri yolimbanirana ndi Edzi. Lipoti la bungwe la Centers for Disease Control and Prevention linati: “Mbadwo uliwonse wa achinyamata uyenera kuphunzitsidwa kwambiri ndiponso mosalekeza zinthu zokhudza thanzi lawo ndi zimene angachite kuti athe kupewa khalidwe limene lingawachititse kutenga HIV. Maphunziro oterowo ayenera kuphatikizaponso makolo ndi aphunzitsi.”

N’zachionekere kuti makolo ayenera kuphunzitsa ana awo za zinthu zoopsa zimenezi anawo asanamve zinthu zina zabodza kwa anzawo kapena anthu ena. Kuchita zimenezi sikuti kumakhala kophweka nthawi zonse. Koma kungapulumutse moyo wa mwana wanu. Kuphunzitsa ana za kugonana ndi mankhwala osokoneza bongo sikuti n’kuwalaulira. M’malo mwake kungawathandize kuti akhale odzisunga.

N’zofunika Kwambiri Kuti Makolo Aziphunzitsa Ana Awo

Pakati pa anthu akale a Mulungu, makolo ankayenera kuphunzitsa ana awo za kugonana ndi mmene angatetezere thanzi lawo. N’zochititsa chidwi kuti malamulo a Aisrayeli akale anaphatikizapo malamulo omveka bwino onena za khalidwe loyenera ndi losayenera, komanso khalidwe limene likanawateteza ku matenda. (Levitiko 18:22, 23; 19:29; Deuteronomo 23:12, 13) Kodi anthuwo ankaphunzitsidwa bwanji malamulo amenewa? Yehova Mulungu anauza Aisrayeliwo kuti: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu.” Choyamba, makolo anayenera kumvetsa phindu lotsatira malamulo amenewa ndi zotsatirapo zophwanya malamulowo. Kenaka anauzidwa kuti: “Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.”—Deuteronomo 6:6, 7.

Mawu a Chihebri amene anawamasulira kuti ‘kuphunzitsa mwachangu’ amatanthauza ‘kubwereza,’ ‘kunena zomwezomwezo nthawi zambiri,’ kapena ‘kutsindika.’ N’zachionekere kuti kuchita zimenezi kumafuna nthawi. Makolo amene amapatula nthawi kuti aphunzitse ana awo za kuopsa kogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndi kuchita chiwerewere angawathandize kwambiri anawo kupewa khalidwe limene lingawachititse kutenga HIV ndi matenda ena. *

Kulimbikitsa Anthu Amene Ali ndi HIV Kapena Edzi

Ntchito yothandiza kupewa Edzi singathandize anthu mamiliyoni ambiri amene ali kale ndi HIV kapena Edzi. Kuwonjezera pa kuvutika ndi nthendayo, nthawi zambiri anthu amenewa amasalidwa chifukwa cha matenda awowo. Chifukwa chiyani? Pali chikhulupiriro chofala, koma cholakwika, choti munthu angatenge matendawa pongokhudzana chabe ndi munthu wina amene ali ndi HIV kapena Edzi. N’zomveka kuti anthu amaopa kuti angatenge HIV kapena Edzi, chifukwa ndi nthenda yopatsirana ndiponso yakupha. Anthu ena alola kuti mantha awo a nthendayi aziwachititsa kuopa anthu odwala nthendayi popanda chifukwa chilichonse. Anthu odwala nthendayi akanizidwapo mankhwala, kuchotsedwa mu mpingo, ngakhale kumenyedwa kumene.

Anthu ena amanena kuti Edzi ndi temberero la Mulungu pa anthu oipa. N’zoona kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo pankhani ya kugonana, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, ndi magazi, kukanateteza odwala ambiri kuti asatenge nthendayi. (Machitidwe 15:28, 29; 2 Akorinto 7:1) Ngakhale zili choncho, Malemba amasonyeza kuti kudwala si umboni woti munthu akulangidwa ndi Mulungu chifukwa choti wachita tchimo linalake. Mosiyana ndi zimenezo, Baibulo limati: “Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” (Yakobo 1:13; Yohane 9:1-3) Munthu amene ali ndi HIV kapena Edzi chifukwa chosatsatira mfundo za m’Malemba, koma amene wasintha khalidwe lake, adziwe kuti Mulungu sanamutaye.

Chifundo ndi chikondi cha Mulungu pa anthu odwala matenda osachiritsika chinaoneka pamene Mwana wake, Yesu, anabwera padziko lapansi. Atakumana ndi munthu wakhate paulendo wake wina, Yesu “anagwidwa chifundo, natansa dzanja nam’khudza iye.” Yesu anagwiritsa ntchito mphamvu zake zodabwitsa ndipo anamuchiritsa wakhateyo. (Marko 1:40-42) Yesu sananyoze anthu odwala. Chikondi chimene anawasonyeza chimasonyeza bwino kwambiri chikondi chimene Atate ake akumwamba ali nacho.—Luka 10:22.

Edzi Idzatha Posachedwapa!

Kuchiritsa kwa Yesu kodabwitsa kumatisonyeza zambiri osati chikondi cha Mulungu chokha. Baibulo limatiuza kuti panopa Yesu Kristu akulamulira monga Mfumu kumwamba. (Chivumbulutso 11:15) Utumiki wake wapadziko lapansi unasonyeza kuti ali ndi mphamvu yotha kuchiza nthenda iliyonse imene anthu amadwala ndiponso kuti amafunitsitsa kuchita zimenezi. Ndipo zimenezo n’zomwe adzachite.

Ulosi wa m’Baibulo umatitsimikizira kuti posachedwapa, “wokhalamo [m’dziko] sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Ngakhale kuti anthu alephera kuletsa kufalikira kwa Edzi kapena kupeza mankhwala ochiza anthu onse amene ali ndi nthendayi, tingakhulupirire kuti Edzi idzatha. Mfumu Davide inati: ‘Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi: Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse.’Salmo 103:2, 3.

Kodi zimenezi zidzachitika liti? Kodi Mulungu amafuna kuti anthu amene akufuna kudzasangalala ndi madalitso amenewo azichita chiyani? Tikukulimbikitsani kuti mulankhulane ndi Mboni za Yehova kuti mudziwe zambiri zokhudza lonjezo losangalatsa kwambiri limeneli la m’Baibulo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Makolo ambiri aona kuti buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, n’lothandiza kwambiri pophunzitsa ana aang’ono za kugonana ndi mfundo zofunika za makhalidwe abwino pang’onopang’ono.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Ulosi wa m’Baibulo umatitsimikizira kuti posachedwapa, “wokhalamo [m’dziko] sadzanena, Ine ndidwala”

[Chithunzi patsamba 10]

Kuphunzitsa ana anu za kugonana ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kungawateteze

[Chithunzi patsamba 10]

Mphamvu za Yesu zotha kuchiza odwala ndi kufunitsitsa kwake kuchita zimenezo zinasonyeza zomwe adzachite m’tsogolo