Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mankhwala a Edzi Akufunika Kwambiri!

Mankhwala a Edzi Akufunika Kwambiri!

Mankhwala a Edzi Akufunika Kwambiri!

Kumsika waukulu wa ku Lilongwe, ku Malawi, Grace amagulitsa nsapato zokongola kwambiri. Akuoneka wosangalala ndiponso wathanzi. Koma ngakhale akumwetulira mwansangala, zimene zinachitika pamoyo wake n’zomvetsa chisoni kwambiri.

Mu 1993, Grace ndi mwamuna wake anasangalala kwambiri ndi kubadwa kwa mwana wawo wamkazi, Tiyanjane. Poyamba, Tiyanjane ankaoneka ngati ali ndi thanzi labwino. Koma pasanapite nthawi anasiya kunenepa ndipo anayamba kudwala matenda osiyanasiyana. Tiyanjane anamwalira ndi Edzi ali ndi zaka zitatu.

Patapita zaka zochepa, mwamuna wa Grace anayambanso kudwala. Tsiku lina anakomoka ndipo anamutengera kuchipatala. Madokotala analephera kumupulumutsa. Mwamuna wa Grace, amene anakhala naye pabanja kwa zaka eyiti, anamwalira chifukwa cha matenda oyamba chifukwa cha Edzi.

Tsopano Grace amakhala yekha m’nyumba ya chipinda chimodzi mu mzinda wa Lilongwe. Munthu angaganize kuti panopa, pamene Grace ali ndi zaka 30, angakhale akuganizira zokonzanso tsogolo lake. Koma iye akufotokoza kuti: “Ndili ndi HIV, choncho sindidzakwatiwanso kapena kuberekanso ana ena.” *

N’ZOMVETSA chisoni kuti nkhani ngati imeneyi si yachilendo ku Malawi, kumene anthu 15 pa anthu 100 alionse m’dzikomo akuti ali ndi kachilombo ka HIV. Kuchipatala china cha kumudzi, malinga ndi zimene nyuzipepala ya Globe and Mail inanena, “anthu ogonekedwa m’chipatalacho ndi ochuluka kwambiri kuposa nambala ya mabedi amene ali m’chipatalacho, ndipo ogwira ntchito pafupifupi theka m’chipatalamo anamwalira” chifukwa cha matenda a Edzi. Anthu amene ali ndi kachilombo ka HIV ndi ochuluka kuposa pamenepa m’mayiko ena a kum’mwera kwa Sahara ku Africa kuno. Mu 2002, bungwe la United Nations loona za HIV ndi Edzi lotchedwa Joint United Nations Programme on HIV/AIDS (UNAIDS), linati: “Kum’mwera kwa Sahara ku Africa, anthu panopa amayembekezeka kukhala ndi moyo zaka 47. Pakanapanda Edzi, bwenzi akumayembekezeka kukhala ndi moyo zaka 62.”

Koma mliri wa HIV ndi Edzi wafala kwambiri, ngakhalenso kumayiko ena kunja kwa Africa. Bungwe la UNAIDS likuyerekezera kuti anthu achikulire okwana mamiliyoni anayi ku India ali ndi kachilombo ka HIV, ndipo linati: “Poona anthu amene ali ndi matendawa panopa, chinthu chimene chidzaphe anthu ambiri achikulire kuposa chinthu china chilichonse pa zaka khumi zikubwerazi ndi HIV.” Mliriwu ukufalikira mofulumira kwambiri m’mayiko amene kale anali pansi pa ulamuliro wa dziko la Soviet Union amene anapanga bungwe lotchedwa Commonwealth of Independent States. Lipoti lina linati ku Uzbekistan, “mu 2002 mokha anthu ambiri anapezeka ndi kachilombo ka HIV kuposa anthu amene anapezeka ndi kachilomboka pa zaka khumi za m’mbuyomo.” Kachilombo ka HIV kakupitirirabe kupha anthu ambiri ku United States a zaka zapakati pa 25 ndi 44.

Magazini ya Galamukani! inafalitsa nkhani zonena za Edzi koyamba mu 1986. M’chaka chimenecho, Dr. H. Mahler, amene panthawiyo anali mkulu wa bungwe la World Health Organization, anachenjeza kuti n’kutheka kuti anthu okwana mamiliyoni khumi anali kale ndi kachilombo ka HIV. Pomatha zaka pafupifupi 20, anthu amene ali ndi kachilombo ka HIV padziko lonse awonjezeka kufika pa anthu pafupifupi mamiliyoni 42, ndipo awonjezeka kuwirikiza kakhumi mmene chiwerengero cha anthu padziko lonse chawonjezekera! Akatswiri akuti m’tsogolomu zinthu sizikuoneka ngati zisintha. Bungwe la UNAIDS linati: “M’mayiko 45 amene ali ndi anthu ambiri okhala ndi kachilomboka, tikuyembekezera kuti pakati pa chaka cha 2000 ndi 2020 anthu mamiliyoni 68 amene sanayenera kufa adzafa chifukwa cha Edzi.”

Poona mmene matendawa akufalikira mofulumira choncho, mankhwala a Edzi akufunika kwambiri panopa kuposa kale lonse. Choncho ochita kafukufuku wa zamankhwala akhala akugwira ntchito mwakhama kuti agonjetse HIV. Kodi pantchito yolimbana ndi mliri woopsawu pachitika zinthu zotani zolimbikitsa? Kodi tili ndi chifukwa chilichonse choyembekezera kuti Edzi idzatha?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 HIV ndi kachilombo kodziwika kuti kamayambitsa Edzi.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Padziko lonse lapansi, anthu pafupifupi mamiliyoni 42 ali ndi HIV kapena Edzi, ndipo mwa anthu amenewa anthu mamiliyoni awiri ndi theka ndi ana

[Chithunzi patsamba 4]

KU INDIA Anthu ongodzipereka ogwira ntchito kuchipatala akuphunzitsidwa za Edzi

[Mawu a Chithunzi]

© Peter Barker/Panos Pictures

[Chithunzi patsamba 4]

KU BRAZIL Wogwira ntchito ya boma yothandiza anthu akulimbikitsa mzimayi wodwala Edzi

[Mawu a Chithunzi]

© Sean Sprague/Panos Pictures

[Chithunzi patsamba 4]

KU THAILAND Munthu wogwira ntchito mongodzipereka akusamalira mwana amene anabadwa ndi kachilombo ka HIV

[Mawu a Chithunzi]

© Ian Teh/Panos Pictures