Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mungachite Munthu Amene Mumakonda Akadwala Misala

Zimene Mungachite Munthu Amene Mumakonda Akadwala Misala

Zimene Mungachite Munthu Amene Mumakonda Akadwala Misala

TSIKU linalake linayamba bwinobwino ngati masiku onse m’banja la a Bwanali. * Anthu anayi onse a m’banjalo anali atadzuka ndiponso atavala kukonzekera zochita za tsikulo. A Najere anakumbutsa Yohane, mwana wawo wamwamuna wa zaka 14, kuti nthawi yokakwera basi yake ya kusukulu inali itapitirira. Zimene zinachitika kenaka zinali zosayembekezeka m’pang’onong’ono pomwe. Pasanathe mphindi 30, Yohane anapopera penti pa khoma lakuchipinda, anafuna kuyatsa galaja, ndiponso anafuna kudzipha m’chipinda cha pamwamba pa nyumbayo.

A Najere ndi amuna awo, a Bwanali, anatsatira ambulasi imene inatenga Yohane, ndipo sanali kumvetsa zimene zinali zitangochitikazo. Koma kumvetsa chisoni kwake n’koti ichi chinali chiyambi chabe. Yohane anachita zinthu zambiri zosonyeza kuti wazungulira mutu, zimene zinachititsa kuti akhale ndi moyo wosasangalatsa wa munthu wamisala. Pa zaka zisanu zimene anazunzika chonchi, Yohane anafuna kudzipha kangapo, anamangidwa kawiri, anagonekedwa m’zipatala zisanu ndi ziwiri za anthu amisala, ndipo anakumana kambirimbiri ndi madokotala a matenda a misala. Anzake ndi achibale ake, amene sankamvetsa zomwe zinali kuchitika, nthawi zambiri sankadziwa chonena kapena chochita.

Akuti mwina munthu mmodzi pa anthu anayi alionse padziko lonse lapansi adzadwala matenda enaake a misala panthawi ina pa moyo wawo. Poona kuchuluka kwa chiwerengero chimenechi, mwina n’kutheka kuti inuyo muli ndi kholo, mwana, mchimwene, mchemwali, kapena mnzanu amene ali ndi matenda enaake a ubongo. * Kodi mungatani ngati munthu amene mumakonda ali ndi vuto limeneli?

Muzidziwa zizindikiro zake. Nthawi zina munthu akhoza kukhala ndi matenda a misala koma anthu ena osadziwa. Anzake a munthuyo ndi anthu a m’banja mwake angamaone ngati zizindikiro zimene munthuyo akusonyeza n’chifukwa cha kusintha kwa timadzi tinatake ta m’thupi, matenda, kufooka kwa maganizo ake, kapena chifukwa cha mavuto amene akuchitika pa moyo wake. Mayi ake a Yohane anaona zizindikiro zosonyeza kuti iye sanali bwino. Komabe, makolo ake ankati kusasangalala kwakeko kunali chifukwa cha zochitika za paunyamata ndipo ankakhulupirira kuti pakapita nthawi kudzasiya. Komabe, kusintha kwambiri kwa magonedwe, kadyedwe, kapena khalidwe, kungasonyeze kuti chinachake sichili bwino. Koma wokondedwa wanuyo atakayezedwa ndi dokotala angathandizidwe ndiponso angathe kukhala ndi moyo wabwinopo.

Phunzirani za matendawo. Anthu amene akudwala misala nthawi zambiri sangathe kufufuza okha za matenda awowo. Choncho zimene mungafufuze m’mabuku odalirika aposachedwapa zingakuthandizeni kumvetsa zimene zikumuchitikira wokondedwa wanuyo. Zingakuthandizeninso kulankhula ndi ena momasuka ndiponso mosonyeza kuti mukudziwa zomwe mukunena. Mwachitsanzo, a Najere anapatsa agogo ake a Yohane timabuku tachipatala timene tinawathandiza kudziwa zambiri za matendawa ndiponso kutha kuthandizapo.

Pezani mankhwala. Ngakhale kuti matenda ena a misala amakhala nthawi yaitali, odwala ambiri angakhale ndi moyo wabwinobwino ndiponso waphindu pogwiritsa ntchito mankhwala oyenera. Koma n’zomvetsa chisoni kuti ambiri amavutika kwa zaka zambiri osapeza chithandizo. Monga momwe matenda aakulu a mtima amafunira dokotala wa mtima, matenda a misala amafunikanso anthu amene amadziwa bwino kuchiza matenda oterowo. Mwachitsanzo, akatswiri a matenda a maganizo angapereke mankhwala amene, ngati munthu awamwa motsatira ndondomeko yake, angamuthandize kuti asamakhumudwekhumudwe, angachepetse nkhawa, ndiponso angamuthandize kuyamba kuganiza molongosoka. *

Limbikitsani wodwalayo kuti apeze thandizo. Anthu amene akudwala misala sangazindikire kuti akufunikira thandizo. Mungawauze kuti akaonane ndi dokotala winawake, awerenge nkhani zinazake zothandiza zokhudza matenda awowo, kapena acheze ndi munthu wina amene analimbana bwinobwino ndi matenda amenewa. Mwina wokondedwa wanuyo sangamvere malangizo anuwo. Koma ngati munthu amene mukusamalira ali pangozi yoti akhoza kudzipweteka kapena kupweteka munthu wina, muyenera kuchitapo kanthu mosazengereza.

Pewani kumuimba mlandu. Asayansi sanadziwebe bwinobwino zinthu zovuta kuzimvetsa zokhudza mmene chibadwa, malo amene tikukhala ndi zochitika pamalopo, ndi anthu amene timacheza nawo, zingachititsire ubongo kusagwira bwino ntchito. Zinthu zosiyanasiyana zimene zingayambitse matenda a misala ndi monga kuvulala mu ubongo, kumwa kapena kusuta zinthu zimene zingawononge ubongo, zochitika zotopetsa kwambiri m’maganizo, kusagwira bwino ntchito kwa timadzi tinatake ta m’thupi, ndi zinthu zochita kutengera ku mtundu. Kuimba mlandu anthu kuti mwina anachita zinazake zimene zinawayambitsa matendawo sikuthandiza aliyense. M’malo mwake, ndi bwino kuthera mphamvu zanu pochita zinthu zothandiza ndi zolimbikitsa.

Musamayembekezere zinthu zoti sizingachitike. Ngati mukuyembekezera zambiri kwa munthu wodwala kuposa zomwe angathe kuchita, zingamukhumudwitse. Komanso, kumangokhalira kunena zolephera za wodwalayo kungamuchititse kudziona ngati sangathe kuchita chilichonse. Choncho muziyembekezera zinthu zimene zingachitikedi. N’zoona kuti simuyenera kusekerera zinthu zolakwa. Mofanana ndi munthu wina aliyense, anthu amene akudwala matenda a misala angaphunzire pa zotsatirapo za zochita zawo. Ngati wodwalayo akuchita zachiwawa mungafunike kudziwitsa oyendetsa malamulo a boma kapena kumuletsa kupita kwina ndi kwina kuti mumuteteze komanso kuti muteteze anthu ena.

Muzilankhulana bwino. Kulankhulana n’kofunika kwambiri, ngakhale kuti panthawi zina zingaoneke kuti sakukumvetsani bwino. N’zovuta kudziwiratu momwe munthu wodwala misala achitire zinthu, ndipo nthawi zina anganene zinthu zosadziwika komwe zikuchokera. Komabe, kukalipira wodwalayo chifukwa cha zimene wanena kungangomuchititsa kuti azidziimba mlandu powonjezera pa kuvutika maganizo kumene ali nako kale. Ngati zonena zanu sizikuthandiza, siyani kulankhulako ndipo khalani naye pansi wodwalayo n’kumvetsera zonena zake. Vomerezani maganizo ake ndi mmene akumvera popanda kumudzudzula. Yesetsani kukhala odekha. Inuyo ndi wokondedwa wanuyo mudzapindula ngati musonyeza bwino nthawi zonse kuti mumamukonda. Zimenezi n’zimene zinachitikira Yohane. Patapita zaka zingapo, anadzayamikira anthu amene anamuthandiza. Iye anati anthuwo “anali kundithandiza pamene sindinkafuna kuti munthu andithandize.”

Ganizirani zosowa za anthu ena m’banjamo. Panthawi imene banjalo likufunikira kuganizira kwambiri za munthu amene akudwalayo, anthu ena m’banjamo akhoza kunyalanyazidwa. Kwa kanthawi, mchemwali wake wa Yohane, Alinafe, anaona ngati “ankanyalanyazidwa chifukwa cha matenda a mchimwene wakeyo.” Iye anachepetsa zochita zake zabwino kuti asachititse anthu kuganizira za iyeyo. Koma panthawi yomweyo, zinkaoneka ngati kuti makolo ake ankafuna kuti azichita zambiri, ngati kuti ayeneranso kuchita zinthu zimene mchimwene wakeyo amalephera kuchita. Ana ena amene akunyalanyazidwa zinthu zikakhala chonchi amachita zinthu zoipa pofuna kuti anthu aziwaganizira. Mabanja amene ali pamavuto oterewa amafunika thandizo kuti akwaniritse zosowa za aliyense m’banjamo. Mwachitsanzo, pamene banja la a Bwanali linali lotanganidwa ndi mavuto a Yohane, anzawo a mu mpingo wa Mboni za Yehova anawathandiza posamalira kwambiri Alinafe.

Muzichita zinthu zimene zimathandiza munthu kukhala ndi maganizo abwino. Njira yabwino yothandizira kuti mukhale ndi maganizo abwino iyenera kuphatikizapo kadyedwe kabwino, kuchita zinthu zolimbitsa thupi, kugona mokwanira, ndi kuchita zinthu zosangulutsa. Kuchita zinthu zosangulutsa limodzi ndi kagulu kochepa ka anzanu nthawi zambiri kumakhala kosavuta. Chinanso, kumbukirani kuti zakumwa zoledzeretsa zingakulitse matendawo ndi kuchititsa kuti mankhwala asagwire bwino ntchito. Banja la a Bwanali tsopano limayesetsa kuchita zinthu zothandiza aliyense kukhala ndi maganizo abwino, makamaka Yohane.

Muzidzisamalira. Kutopa kumene kumakhalapo chifukwa chosamalira munthu wodwala misala kungawonongenso thanzi lanu inuyo. Choncho m’pofunika kuti muzisamalira thupi lanu, maganizo anu, ndi zosowa zanu zauzimu. Banja la a Bwanali ndi la Mboni za Yehova. A Najere akuganiza kuti chikhulupiriro chawo chinawathandiza kwambiri kulimbana ndi vuto limene banja lawo linakumana nalo. Iwo anati: “Misonkhano yachikristu inkanditsitsimula, chifukwa inkakhala nthawi yoti ndiiwaleko nkhawa zanga n’kuganizira zinthu zina zofunika kwambiri, ndiponso chiyembekezo chathu cha m’tsogolo choti mavuto onse adzatha. Nthawi zambiri ndinkapemphera kuti ndipezeko mpumulo, ndipo nthawi iliyonse chinachake chinkachitika n’kuchepetsako ululuwo. Mothandizidwa ndi Yehova Mulungu, ndinali ndi mtendere wa maganizo umene unali waukulu poyerekezera ndi mavuto amene tinali nawo.”

Yohane tsopano ndi mnyamata wachikulire ndipo wayamba kuona moyo mosiyana ndi kale. Iye anati: “Ndikuona kuti zimene zinandichitikira zandisandutsa munthu wabwino kuposa kale.” Mchemwali wake wa Yohane, Alinafe, nayenso akuona kuti zimene zinachitikazo zamuthandiza. Iye anati: “Masiku ano sindikhumudwa msanga ndi zochita za anthu ena. Munthu sungadziwe mavuto amene angagwere munthu wina. Ndi Yehova Mulungu yekha amene amadziwa.”

Ngati munthu amene mumakonda ali ndi matenda a misala, muzikumbukira nthawi zonse kuti kumumvetsera, kumuthandiza, ndi kusamuimba mlandu kungamuthandize kulimbana ndi vuto lakelo, ndipo mwina mpaka angathe kukhala ndi moyo wabwinobwino.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mayina asinthidwa.

^ ndime 4 Anthu ena amagwiritsa ntchito mawu oti “matenda a ubongo” chifukwa amamveka osachititsa manyazi ndiponso amasonyeza bwino kuti matendawa amayamba chifukwa cha kusokonezeka kwa ubongo kapena zinazake m’thupi.

^ ndime 7 Muyenera kuganizira phindu limene mankhwalawo angabweretse limodzi ndi mavuto ena amene angabweretsenso. Magazini ya Galamukani! silangiza anthu kuti atsatire njira yakutiyakuti ya chithandizo. Akristu ayenera kuonetsetsa kuti chithandizo chilichonse chimene akutsatira sichikutsutsana ndi mfundo za m’Baibulo.

[Bokosi patsamba 13]

Zizindikiro Zina Zimene Zingasonyeze Kuti Munthu Angadwale Matenda a Misala

Ngati munthu wina amene mumakonda ali ndi zizindikiro zilizonse mwa zizindikiro zotsatirazi, angafunike kukaonana ndi dokotala kuchipatala kapena kukaonana ndi dokotala wa maganizo:

• Kusasangalala kapena kusachedwa kupsa mtima, kwa nthawi yaitali

• Kusafuna kucheza ndi anthu

• Kusachedwa kusintha kuchoka pa kusangalala kufika pa kusasangalala

• Kukwiya kwambiri

• Kuchita zachiwawa

• Kumwa kapena kusuta zinthu zowononga ubongo

• Kuchita mantha kwambiri ndiponso kuda nkhawa monkitsa

• Kuopa kwambiri kunenepa

• Kusintha kwambiri kadyedwe kapena kagonedwe

• Kulota maloto oopsa nthawi zambiri

• Kusaganiza bwinobwino

• Kuona zideruderu

• Kuganizira za kufa kapena zodzipha

• Kulephera kuthana ndi mavuto kapena kulephera kuchita ntchito zatsiku ndi tsiku

• Kusavomereza kuti ali ndi mavuto, ngakhale kuti mavutowo angakhale oonekeratu kwa ena

• Kudwala matenda ambirimbiri osadziwika choyambitsa chake

[Chithunzi patsamba 14]

Ngati zonena zanu sizikuthandiza, siyani kulankhulako ndipo khalani naye pansi wodwalayo n’kumvetsera zonena zake