Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko Lathuli Lidzapulumuka

Dziko Lathuli Lidzapulumuka

Dziko Lathuli Lidzapulumuka

NKHANI zapitazo zasonyeza bwino kwambiri kuti ngati anthu apitirizabe kuwononga zinthu zapadziko lapansi monga mmene akuziwonongera panopa, zinthu sizingakhale bwino. N’zoona kuti atsogoleri a mayiko osiyanasiyana ayesetsa kuchepetsa kuwonongeka kwa mpweya, kupulula mitengo, ndi mavuto ena a zachilengedwe. Kuyambira pa msonkhano wa mayiko osiyanasiyana wotchedwa UN Conference on Human Environment umene unachitika mu 1972, ndi misonkhano ina imene yakhala ikuchitika nthawi ndi nthawi, mayiko okwana 163 akumana n’kugwirizana zimene ayenera kuchita kuti athetse mavuto amenewa. Koma kodi zotsatirapo zake zakhala zotani? David Hunter, mtsogoleri wa bungwe loona za malamulo oteteza zachilengedwe lotchedwa Center for International Environmental Law, anati: “N’zomvetsa chisoni kuti mapangano ndi zikalata zambirimbiri zonsezi sizinathetse kuwonongeka kwa zinthu zachilengedwe padziko lonse.” Ndipo Hunter anawonjezera kuti: “Pafupifupi mbali iliyonse ya zinthu zachilengedwe panopa ikusonyeza kuti zinthu zaipa kuposa mmene zinalili pamene ankachita msonkhano wa United Nations mu 1992.”

N’chifukwa chiyani zinthu sizinasinthe kwambiri patatha zaka zoposa 30 mayiko akukambirana mavuto a zachilengedwe? Chifukwa chimodzi ndicho kufunika koti chuma chizipita patsogolo. Chuma cha mayiko chimakula anthu akamagula katundu wambiri. Zimenezo zimafuna kuti makampani azipanga zinthu zambiri, zimenenso zimafuna kuti azigwiritsa ntchito zinthu zachilengedwe zambiri. Limeneli ndi vuto lovuta kulithetsa, ndipo pamapeto pake chilengedwe n’chimene chimawonongeka. Choncho kodi vutoli lingathe bwanji?

Kulephera Kuyendetsa Bwino Zinthu

Baibulo limafotokoza chifukwa chake anthu alephera kuyendetsa bwino zinthu. Mneneri Yeremiya anati: “Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Zomwe zachitika zasonyeza kuti mawu amenewo ndi oonadi.

Kodi munayamba mwapita kukaona malo enaake okongola? Timasangalala kwambiri kuona mitengo yambirimbiri, zitsamba, ndi maluwa okongola. Koma munda wamaluwa wolimidwa bwino sikuti umangopangika wokha. Anthu aluso odziwa za ulimi wamaluwa amatha maola ambiri akudulira mitengo, kutchetchera kapinga, ndi kukonza mabedi a maluwa kuti azioneka okongola. Tangoganizirani mmene dziko lathuli likanaonekera likanati lizisamalidwa mwachikondi ngati mmene munda wa maluwa woterowo umasamalidwira.

Mfundo n’njakuti, Mlengi wathu anafuna kuti dziko lathuli lizisamalidwa motero. Malinga ndi nkhani yonena za kulengedwa kwa zinthu yolembedwa m’Mawu a Mulungu ouziridwa, “Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m’munda wa Edene kuti aulime nauyang’anire.” (Genesis 2:15) Kuwonjezera apo, banja la anthu linapatsidwa udindo woti lisangosamalira munda wa Edene wokha, koma likulitsenso Paradaiso woyambirira ameneyo mpaka adzaze dziko lonse.—Genesis 1:28.

Koma n’zomvetsa chisoni kuti chifukwa cha kusamvera kwa Adamu ndi Hava, iwo anasanduka opanda ungwiro ndipo anataya mwayi wawo wosamalira ndi kukulitsa Paradaiso. (Genesis 3:1-6, 23) Popeza ndife ana a banja loyambirira limenelo, tinabadwa ndi uchimo ndi kupanda ungwiro. (Aroma 5:12) Kusakaza zinthu zachilengedwe padziko lapansi ndi chitsanzo chimodzi chokha cha mmene anthu alepherera kudzilamulira. N’zachionekere kuti anthu sangathe kuthetsa okha mavuto amene ali nawo. Akufunika kuthandizidwa ndi winawake wokhala ndi nzeru zoposa za anthu.

Kusintha kwa Zinthu

Pamene Yesu anali padziko lapansi, anauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Baibulo limaphunzitsa kuti mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu, dziko lapansi lidzasanduka paradaiso. (Salmo 37:10, 11) Panthawi imeneyo, mitengo ndi zomera zina zizidzabereka kwambiri padziko lapansi losawonongedwa. (Salmo 72:16) Motsogozedwa ndi Mulungu, dziko lapansi lidzayeretsedwa kuchotsa zonse zowononga chilengedwe ndipo anthu adzaphunzitsidwa kukhala bwinobwino osawononga chilengedwe. Kodi tingakhulupirire bwanji zimenezi?

Baibulo limati dziko lapansi “silidzagwedezeka ku nthawi yonse.” (Salmo 104:5) Panthawi yoikidwa ndi Mulungu, anthu onse amene adzakhalepo adzadalitsidwa mpaka muyaya, ndipo adzakhala ndi thanzi labwino, chakudya chokwanira, ndi nyumba zabwino. Kodi mungakonde kuphunzira zambiri zokhudza zolinga za Mulungu? Lankhulani ndi munthu aliyense wa Mboni za Yehova. Angakonde kukuthandizani kuona zomwe Baibulo limanena zoti dziko lapansili lidzapulumuka, ndiponso momwe lidzapulumukire.

[Zithunzi patsamba 10]

Motsogozedwa ndi Mulungu, anthu azidzakhala bwinobwino osawononga chilengedwe

[Mawu a Chithunzi]

Girl and farmer: © Jeremy Horner/Panos Pictures