Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko Lathuli Likusakazidwa Kwabasi

Dziko Lathuli Likusakazidwa Kwabasi

Dziko Lathuli Likusakazidwa Kwabasi

MU 1805, Meriwether Lewis ndi William Clark, omwe anali anthu otchuka ofufuza malo anafika pa mtsinje wa Columbia m’boma limene masiku ano limatchedwa kuti Washington State, ku United States. * Koma chimene chinawachititsa chidwi kwambiri kuposa mtsinjewo chinali kuchuluka kwa nsomba zotchedwa salmon mumtsinjemo. M’buku lawo lolembamo zochitika za tsiku ndi tsiku iwo analemba kuti: “Mumtsinjemu muli nsomba zosasimbika za mtunduwu. Zimangoti nyomii, posambira motsata mtsinjewu ndipo madzi amazikankhira kumtunda, moti Amwenye a kunoko amakangozitola, kuzing’amba, n’kuziumika pa matabwa.” Inde, nsombazi zinaliko zambiri moti Amwenyewa ankazigwiritsa ntchito ngati nkhuni.

Masiku ano zinthu zinasintha kwambiri. Lipoti la magazini ya Newsweek linati: “Asayansi anadziwa zaka zoposa khumi zapitazo kuti anthu akuwedza nsomba zochuluka kwambiri m’nyanja kuposa nsomba zimene zikubadwanso.” Mwachitsanzo akuti m’dera la kumpoto kwa nyanja ya Atlantic, pa nsomba 10 zilizonse zomwe zinali m’nyanjayo kale pangotsala nsomba imodzi yokha.

Koma si nsomba zokha zimene zikutha. Zinthu zina zachilengedwe monga mafuta okumba pansi, miyala yamtengo wapatali, ndiponso zinthu zakutchire, zikusakazidwa mosaneneka. Bungwe la World Wildlife Fund linati kuchokera mu 1970 kudzafika mu 1995 pali zinthu zambiri zachilengedwe zimene zasakazidwa kwambiri. Ndipo vutoli lakula kwambiri chifukwa nthawi zambiri tikamagwiritsa ntchito zinthu zachilengedwe za padziko pano timakhalanso tikuwononga chilengedwecho.

Anthu ena amanena kuti popeza anthu ndi amene anayambitsa mavuto amenewa, angathenso kuwathetsa. Amapereka chitsanzo choti chaposachedwapa, m’mayiko ambiri otukuka vuto la kuwonongeka kwa mpweya mumlengalenga alichepetsako. Kodi nkhani zolimbitsa mtima ngati zimenezi zikutanthauza kuti anthu ayamba kuthana ndi vuto losakaza chilengedwe?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Lewis ndi Clark anachita kutumidwa kumeneku kuti akafufuze ndiponso kulemba mapu a chigawo chimene chinali chitangogulidwa kumene cha kumadzulo kwa mtsinje wa Mississippi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

© Kevin Schafer/CORBIS