Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kufatsa N’kupanda Mphamvu?

Kodi Kufatsa N’kupanda Mphamvu?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kufatsa N’kupanda Mphamvu?

“Mtumiki wa Ambuye sayenera kuchita ndewu, koma akhale wokomera mtima anthu onse.”—2 TIMOTEO 2:24, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono.

PATATSALA nthawi yaitali ndithu kuti tibadwe, khungu lathu, lomwe limakhala likupangikabe, limayamba kumva likakhudzidwa. Kuyambira tikangobadwa, timafunitsitsa kuti amayi athu azitisisita mwachikondi. Paubwana wathu, kusekerera kwathu, kutha kukhudzidwa mumtima bwinobwino, ndi kufuna kuphunzira luso la kulankhula, zimadalira kuchuluka kwa chikondi chimene makolo athu amatisonyeza.

Komabe, Baibulo linaneneratu kuti m’masiku otsiriza, anthu adzakhala “osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe.” Linaneneratunso kuti makhalidwe ogwirizana ndi kufatsa monga kukoma mtima ndi kumvera ena chisoni adzakhala osowa kwambiri, chifukwa anthu adzakhala “odzikonda okha” ndiponso “aukali, osakonda abwino.”—2 Timoteo 3:1-3.

Anthu ambiri masiku ano amaona kuti afunika kukhala ankhanza ndiponso ouma mtima. Amati kukhala wofatsa n’chizindikiro chakuti munthu alibe mphamvu. Koma kodi zimenezo n’zoona?

Ofatsa, Koma Amphamvu

Yehova Mulungu amafotokozedwa kuti “ndiye wankhondo.” (Eksodo 15:3) Iye ndiye Gwero la mphamvu zonse. (Salmo 62:11; Aroma 1:20) Komabe, mphamvu za Yehova sizinamulepheretse kukhala “wodzala chikondi, ndi wachifundo” podalitsa Yobu, mwamuna wokhulupirika. (Yakobo 5:11) Pofotokoza zochita zake ndi Aisrayeli, Yehova anasonyeza kuti anali kuwakonda ndi kuwamvera chifundo kwambiri. Iye anachita zimenezi mwa kuyerekezera mmene anali kumvera ndi mmene mayi woyamwitsa mwana amamvera chisoni “mwana wom’bala iye.”—Yesaya 49:15.

Yesu nayenso anali wamphamvu koma wofatsa. Iye anadzudzula mwamphamvu atsogoleri achipembedzo onyenga a mu nthawi yake. (Mateyu 23:1-33) Anathamangitsanso mwamphamvu anthu osintha ndalama adyera kuti achoke m’kachisi. (Mateyu 21:12, 13) Koma kodi chifukwa choti Yesu ankadana ndi katangale ndi dyera zinamuchititsa kukhala wouma mtima? Ayi ndithu! Yesu ankadziwika chifukwa cha kufatsa kwake pochita zinthu ndi ena. Ndipo mpaka anadziyerekezera ndi thadzi limene limasonkhanitsa “anapiye ake m’mapiko ake.”—Luka 13:34.

Kodi Tiyenera Kukhala Ouma Mtima Kapena Olimba Mtima?

Akristu oona amalimbikitsidwa kutsanzira Kristu povala “munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu.” (Aefeso 4:20-24) Timalimbikitsidwa ‘kuvula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,’ mofanana ndi nkhanu imene imavula chiganamba chake chakale kuti ithe kukula. (Akolose 3:9) Komabe, mosiyana ndi nkhanu imene thupi lake limalimbanso pasanapite nthawi yaitali itavula chiganamba chakale chija, ife tikulamulidwa kuti tiyenera kuvala mpaka kalekale “mtima wachifundo, kukoma mtima, . . . kuleza mtima.” (Akolose 3:12) Choncho tiyenera kudziwika monga anthu ofatsa.

Kudziveka makhalidwe ogwirizana ndi kufatsa si chizindikiro choti ndife opanda mphamvu. Mosiyana ndi zimenezo, kuchita zimenezo kumafuna kuti tikhale “ndi mphamvu mwa Mzimu wa [Yehova]” m’kati mwathu. (Aefeso 3:16) Mwachitsanzo, mwamuna wina dzina lake Lee anati: “Osati kale kwambiri ndinali munthu wouma mtima, woipa kwambiri. Ngakhale maonekedwe anga anali oopsa, chifukwa ndinaboola thupi langa n’kulikoloweka ndolo. Ndinkafunitsitsa kupanga ndalama zambiri ndipo sindinkazengereza kutukwana kapena kuchita chiwawa kuti ndipeze zomwe ndimafuna. Ndinalibe chisoni chilichonse.” Komabe, Lee anayamba kuphunzira Baibulo ndi mnzake wa kuntchito ndipo anadziwa Yehova Mulungu n’kuyamba kumukonda. Iye anavula umunthu wake wakale ndipo waphunzira kudziletsa. Masiku ano amasonyeza anthu kuti amawakonda podzipereka kugwiritsa ntchito nthawi yake kuwaphunzitsa Baibulo.

Panthawi inayake, mtumwi Paulo nayenso anali “wamwano” ndipo ankachita zachiwawa kuti akwanitse zolinga zake. (1 Timoteo 1:13; Machitidwe 9:1, 2) Komabe, Paulo ataphunzira za chifundo ndi chikondi chimene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu anamusonyeza, zinamukhudza kwambiri ndipo anayamba kuyesetsa kutsanzira makhalidwe amenewo. (1 Akorinto 11:1) Ngakhale kuti Paulo ankaima nganganga pa mfundo zachikristu, anaphunzira kukhala wofatsa pochita zinthu ndi anthu ena. Indedi, Paulo sankabisa chikondi chake kwa abale ake.—Machitidwe 20:31, 36-38; Filemoni 12.

Mmene Mungapezere Mphamvu Zokuthandizani Kukhala Ofatsa

Zimene zinachitikira Lee ndi Paulo zikusonyeza kuti kuphunzira kuchita zinthu mofatsa ndi anthu ena sikutanthauza kuti munthuyo ndi wofooka. M’malo mwake, munthu amafunika kukhala wamphamvu. Pamafunika mphamvu kuti munthu asinthe maganizo ake ndi zochita zake ndi kulimbana ndi chizolowezi chimene anthu amakhala nacho chofuna ‘kubwezera choipa chosinthana ndi choipa.’—Aroma 12:2, 17.

Nafenso tingaphunzire kukhala ofatsa ndi achikondi powerenga nthawi zonse Mawu a Mulungu ndi kusinkhasinkha za chikondi ndi chifundo chimene Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu atisonyeza kale. Tikatero, mphamvu ya Mawu a Mulungu idzatha kufewetsa mitima yathu. (2 Mbiri 34:26, 27; Ahebri 4:12) Kaya tikhale kuti tinachokera ku banja lotani ndiponso takumana ndi zotani pamoyo wathu, tikhoza kuphunzira kukhala ‘okomera mtima anthu onse.’—2 Timoteo 2:24.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri kapena kuti wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani Mboni za Yehova, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 5.

[Chithunzi patsamba 31]

Bambo wabwino amakhala wofatsa akamachita zinthu ndi ana ake