Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Mnyamata Amene Ndimamufuna Akandikana?

Kodi Ndingatani Mnyamata Amene Ndimamufuna Akandikana?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingatani Mnyamata Amene Ndimamufuna Akandikana?

POYAMBA mnyamatayo anali mnzanu chabe. Koma kenaka anakusangalatsani mwa njira ina yake. Mwina khalidwe lake labwino kapena mmene anakusekererani pamene ankakulankhulani n’zimene zinakuchititsani kukopeka naye. Kaya chifukwa chake chinali chiyani, nthawi inadutsa ndipo sanachite chilichonse chosonyeza kuti amakufunani. Choncho munaganiza zomufunsa ngati akufuna kuti mukhale pachibwenzi. Komabe iye ananena motsindika koma mokoma mtima kuti sakufuna, zimene zinakukhumudwitsani kwambiri. *

Mwachidziwikire zakupwetekani kwambiri mumtima. Koma musakhumudwe nazo kwambiri. Yesani kuiona bwino nkhaniyo. N’zoona kuti mnyamatayo wanena kuti sakufuna kuchita nanu chibwenzi. Koma zindikirani kuti maganizo akewo sanachepetse kufunika kwanu monga munthu, kapena kusintha mfundo yoti anthu ena amakukondani ndi kukulemekezanibe. Ndipo zimene mnyamatayo wachitazo zingakhale chifukwa choti zolinga zake ndi zanu n’zosiyana, osati chifukwa cha inuyo.

Ngati ndinu Mkristu, mungakumbukirenso kuti “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” (Ahebri 6:10) Sonja * anafotokoza zimenezi motere: “Mukadali munthu wofunika. Ndinu aphindu kwa Yehova monga munthu wosakwatiwa.” Popeza Wam’mwambamwamba ndi anthu ena amakulemekezani, kodi pali chifukwa chanji choganizira kuti zimene zakuchitikiranizo zakuchotserani ulemu?

Mwina mungamvebe ngati ndinu munthu wolephera kapena kuganiza kuti palibe amene angafune kukukwatirani. Koma popeza zikuoneka kuti simunali womuyenerera mnyamatayo sizikutanthauza kuti simungakhale woyenerera kwambiri munthu wina. (Oweruza 14:3) Choncho m’malo moganiza kuti mwalephera kupeza mwamuna wabwino woti mungakwatiwe naye, zindikirani kuti kufufuza kwanuko kwakuphunzitsani chinthu chimodzi chabwino, chifukwa mwazindikira kuti mnyamata ameneyu si woyenera kuti mukwatiwe naye. N’chifukwa chiyani tikunena choncho?

Kodi Anali Wokuyenererani?

Baibulo limalamula amuna kuti “azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha.” (Aefeso 5:28) Limalamulanso amuna kuti ‘azichitira ulemu’ akazi awo. (1 Petro 3:7) Choncho n’zotheka kuti mnyamatayo amasangalala nanu monga mnzake. Koma mmene wanena kuti sakufuna kukhala nanu pachibwenzi wasonyeza kuti panopa sali wokonzeka kukukondani ndi kukulemekezani monga mkazi wake. Iye anali ndi ufulu wochita zimenezo. Taganizirani izi: Ngati mmenemo ndi mmene akuonera, kodi akanakhaladi mwamuna wokuyenererani? Tangoganizirani mmene mungakhalire wopanda chimwemwe ngati mutakwatiwa ndi munthu amene sakukondani ndi kukulemekezani monga momwe Malemba amanenera!

Zingakuthandizeninso mutati mumuyang’anenso kachiwiri mnyamatayo, popeza panopa mukudziwa kuti palibenso mwayi woti mungakhale naye pachibwenzi. Nthawi zina chikondi chongotengeka maganizo chingalepheretse munthu kuona zolakwika pa khalidwe kapena moyo wauzimu wa munthu wina, zomwe zingakhale zoonekeratu kwa anthu ena. Mwachitsanzo, kodi tinene kuti mnyamatayo sanadziwe kuti mwayamba kumukonda, kapena anadziwa koma mwadala analimbikitsa chikondi chanucho popitirizabe kucheza nanu? Ngati anakulimbikitsani mwadala, kodi zimenezi sizingasonyeze kuti sanakhwime maganizo mokwanira kuti akhale mwamuna wachikristu woganizira ena? Ngati ndi choncho, ndi bwino kuti mwazindikira zimenezi, ngakhale kuti zingakhale zopweteka.

Marcia anayamba kukonda mnyamata winawake pamene mnyamatayo anayamba kumuchitira zinthu zosonyeza kuti amamuganizira mwapadera. Atamufunsa cholinga chake, mnyamatayo anati samafuna kuti akhale naye pachibwenzi. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kupirira atakhumudwa choncho? Iye anati: “Kuganiza ndi ubongo wanga, osati mtima wanga, kwandithandiza kuthetsa maganizo anga achikondi.” Atakumbukira zimene Baibulo limafuna kuti amuna okwatira azichita, Marcia anazindikira kuti mnyamatayo samachita zimenezi. Zimenezi zinamuthandiza kuthana ndi chisoni chake.

Andrea nayenso anakumana ndi zinthu ngati zomwezo ndi mnyamata wina. Kenaka anadzazindikira kuti zimene mnyamatayo ankamuchitira zinasonyeza kuti sanali wokhwima maganizo. Anazindikira kuti mnyamatayo sanali wokonzeka kukwatira, ndipo akuyamikira kwambiri Yehova kuti anamuthandiza kuzindikira zimenezo. Iye anati: “Ndikukhulupirira kuti Yehova angakutetezeni ku zinthu zimene zingakupwetekeni, koma muyenera kumukhulupirira.” Komabe, nthawi zambiri mnyamata amakhala kuti wachita zinthu zabwinobwino ndipo wakana kukhala nanu pachibwenzi pa zifukwa zomveka. Mulimonse mmene zingakhaliremo, kodi mungatani kuti muyambenso kumva bwinobwino zimenezi zikachitika?

Zimene Mungachite Kuti Muyambirenso Kumva Bwino Mumtima

Mtima wanu ungafunike nthawi kuti uvomereze kuti mnyamatayo wakanadi. Chikondi chanu pa mnyamatayo chinatenga nthawi kuti chiyambe, ndipo kusintha zimenezi kumatenganso nthawi. Nthawi zambiri simungangosiya kukonda munthu wina mwadzidzidzi ngati mukuzimitsa magetsi. Nthawi zina mungamamve kuti chikondi chanu pa munthuyo chikusefukira! Koma dekhani. Nthawi ikamapita, chikondi chanucho chidzayambanso kuchepa. Koma ngati mukufuna kuti chikondi chanucho chithe msanga, pewani zinthu zimene zingachikolezere.

Mwachitsanzo, pewani kudzidzudzula poganiziranso liwu lililonse ndi chinthu chilichonse chomwe munachita pamene munkamuuza mnyamatayo kuti mumamukonda. Ngati simuthetsa maganizo oterowo, mungayambe kukhulupirira kuti sanakane kuchokera pansi pa mtima kapena kuti mutayesera njira ina akhoza kuvomera. Zindikirani kuti simungasinthe mmene iyeyo akumvera. Zoona zake n’zakuti ngakhale mukanati mumulankhule mwa njira ina iliyonseyo, akanakanabe basi.

Kuganizira zinthu zoti sizingachitike kungakhalenso msampha wina. Mwina m’mutu mwanu mumabwera chithunzi cha inuyo ndi mnyamatayo mutakwatirana, n’kumakhala mwachimwemwe mpaka kalekale. Maganizo oterowo mwina angachepetseko ululu wanu, koma si a zochitika zenizeni. Maganizowo akatha, mumazindikira kuti anakana basi ndipo mtima wanu umayambiranso kupweteka. Maganizo amenewa, omayamba ndi chisangalalo n’kutha ndi ululu, akhoza kupitirirabe kwa nthawi yaitali ngati simuyesetsa kuwathetsa.

Yesetsani kuti muchotse m’mutu mwanu maganizo a zinthu zomwe sizingachitike. Maganizowo akayamba, muziimirira n’kupita kokawongola miyendo. Gwirani ntchito inayake ndi manja anu, chilichonse chomwe chingakuyambitseni kuganizira zinthu zina. Muzilimbikira kuchita zinthu zimene zimakulimbikitsani, osati zimene zimakukhumudwitsani. (Afilipi 4:8) Zimenezi zingakhale zovuta poyamba, koma pakapita nthawi zinthu zingayambenso kukuyenderani bwino ndipo mungakhalenso ndi mtendere mumtima.

Anzanu apamtima akamakulimbikitsani akhozanso kukuthandizani. (Miyambo 17:17) Komabe Sonja anachenjeza kuti: “Si bwino kuti anzanu onse akhale osakwatiwa, a msinkhu umodzi, ndiponso ofuna kukwatiwa. Mumafunikiranso anzanu achikulire, amene angakuthandizeni kuganiza bwino.” Ndipo kumbukirani kuti pali winawake amene angakuthandizeni kwambiri kuposa anzanu kuti mtima wanu usiye kupweteka.

Yehova Ndi Bwenzi Limene Lingakuthandizeni

Kale, munthu wina wokhulupirika atakhumudwa, anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Iye analemba kuti: “Pondichulukira zolingalira zanga m’kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.” (Salmo 94:19) Yehova angakutonthozeni ndi kukulimbikitsaninso inuyo ngati mupemphera kwa iye ndi kumukhulupirira. Andrea anachita zimenezi. Iye anati: “Kupemphera n’kofunika kwambiri chifukwa kumakuthandizani kusiya kumva kupweteka mumtima n’kuyamba kuganizira zinthu zina.” Sonja nayenso ponena za kupemphera anati: “Kumakuthandizani kuona kuti ndinu munthu wa ulemu wake, umene sudalira kuti ena amakukondani kapena sakukondani.”

Palibe munthu amene angamvetsetse mmene mukumvera, koma Yehova amamvetsetsa. Iye analenga anthu ndi chilakolako chofuna kukhala pabanja ndi munthu wina n’kumakondana naye. Amadziwa mphamvu ya chikondi ndiponso amadziwa mmene mungachilamulire. Akhoza kukuthandizani kuthana ndi kupweteka kwakukulu kwa mumtima, chifukwa lemba la 1 Yohane 3:20 limati: “Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.”

Onani Zinthu Moyenera

Ukwati ukhoza kubweretsa chimwemwe chambiri, koma sikuti chimwemwe chimabwera chifukwa cha ukwati basi. Anthu onse amene akutumikira Yehova amakhala ndi chimwemwe, ndipo sikuti anthu okwatira ndi amene amakhala nacho chambiri. Mwanjira zina, anthu osakwatira ali pabwino kusiyana ndi okwatira. Savutika ndi “chisautso m’thupi” chotchulidwa pa 1 Akorinto 7:28. Chisautso chimenechi chikutanthauza mavuto ndi kusagwirizana maganizo kumene anthu onse okwatirana amakhala nako. Anthu osakwatira amakhalanso ndi ufulu wambiri ndipo angathe kugwiritsa ntchito moyo wawo kutumikira Yehova mosavuta. Choncho, Baibulo limaphunzitsa kuti: “Amenenso apereka unamwali wake mu ukwati achita bwino, koma amene saupereka mu ukwati adzachita bwino koposa.” (1 Akorinto 7:38, NW) Ngakhale ngati mukufuna kwambiri kukwatiwa, kusinkhasinkha ziphunzitso za m’Baibulo zimenezi kungakuthandizeni kuona zinthu moyenera ndi kusangalala ndi moyo wanu panopa.

Anzanu ena amene amakufunirani zabwino angakuuzeni kuti, “Osadandaula, tsiku lina udzapeza mwamuna wabwino kwambiri.” Ndipo n’zoona kuti kukanidwa kamodzi sikutanthauza kuti mudzakhala nokha mpaka kalekale. Komabe, Mkristu wina wachitsikana dzina lake Candace anati: “Ndimakhulupirira Yehova. Sikuti ndimayembekezera kuti ayenera kundipatsa mwamuna woti ndikwatiwe naye kuti ndikhale wachimwemwe. Koma ndikudziwa kuti adzandipatsa zimene ndikufunikira kuti ndikhale wachimwemwe.” Kuganiza bwino koteroko kunamuthandiza kuthana ndi kukhumudwa pamene anakanidwa ndi mnyamata.

Kuyesera kukhala pachibwenzi nthawi zambiri sikuyenda bwino m’dziko lino, koma maukwati ambirinso sayenda bwino. Ngati mukhulupirira Yehova n’kumvera malangizo ake, angakuthandizeni kusiya kukhala okhumudwa n’kukhala achimwemwe. Zinthu zingakuyendereni bwino ngati mmene zinamuyendera Mfumu Davide, amene analemba kuti: “Ambuye, chikhumbo changa chonse chili pamaso panu; ndipo kubuula kwanga sikubisika kwa Inu. Pakuti ndikuyembekezani Inu, Yehova; Inu mudzayankha, Ambuye Mulungu wanga.”—Salmo 38:9, 15.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Nkhani yakuti, “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi Mnyamata Ndingamuuze Bwanji Kuti Ndikumufuna?” (November 8, 2004) inafotokoza kuti m’mayiko ena zingakhale zosemphana ndi chikhalidwe chawo kuti mkazi auze mwamuna kuti akumufuna chibwenzi. Ngakhale kuti Baibulo sililetsa akazi kufunsira amuna, limalimbikitsa Akristu kupewa kukhumudwitsa anthu ena. Choncho atsikana amene akufuna kuti Mulungu awadalitse afunika kuganizira malangizo a m’Baibulo akamaganizira zoti achite pa nkhani imeneyi.—Mateyu 18:6; Aroma 14:13; 1 Akorinto 8:13.

^ ndime 5 Mayina ena asinthidwa.

[Zithunzi patsamba 14]

Gwiritsani ntchito thandizo limene Mulungu amapereka