Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukongola Kofunika Kwambiri

Kukongola Kofunika Kwambiri

Kukongola Kofunika Kwambiri

ANTHU amakopeka ndi anthu okongola m’maso mwawo. Koma kodi n’chiyani chimakupangitsani kukhaladi okongola? M’pofunika kudziwa zimenezi chifukwa pali zinthu zochepa chabe zimene mungathe kuchita kuti musinthe maonekedwe anu achibadwa popanda kudzivulaza. Kuwonjezera apo, kukongola kwa thupi n’kosakhalitsa chifukwa masiku ano palibe amene angapewe kuwonongeka kwa thupi kumene ukalamba ndi matenda zimabweretsa. Kodi pali kukongola kwa mtundu wina kumene kuli kofunika kwambiri, kokhalitsa, ndiponso kotheka kukhala nako?

Kukongola kwa Mumtima N’kofunika Kwambiri

Baibulo limatitsimikizira kuti Mlengi wathu, Yehova Mulungu, amaona kuti kukongola kwa mumtima n’kofunika kwambiri. Taganizirani zitsanzo zotsatirazi.

Yehova atauza mneneri Samueli kuti asankhe mfumu ya Israyeli pakati pa ana a Jese, mneneriyo anakopeka ndi Eliyabu chifukwa anali wokongola. Samueli anati: “Zoonadi, wodzozedwa wa Yehova ali pamaso pake.” Koma Yehova anauza Samueli kuti: “Usayang’ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza ine ndinam’kana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.”—1 Samueli 16:5-7.

Amene anasankhidwa kuti akhale mfumu anali Davide, mwana wamwamuna wamng’ono kwambiri m’banjamo. Ngakhale kuti anali “wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma,” Davide mwina sanali wooneka mogometsa ngati mmene analili azichimwene ake, amene anali achikulirepo. Koma “mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli.” Ngakhale anali wopanda ungwiro ndipo anachita machimo aakulu, anadziwika chifukwa chokhala munthu wa mtima wokondweretsa Mulungu ndi mtumiki wokhulupirika wa Mulungu mpaka pamapeto pa moyo wake. (1 Samueli 16:12, 13) Mosakayikira, iye anali wokongola kwa Mulungu makamaka chifukwa cha kukongola kwake kwa mumtima.

Mosiyana ndi zimenezi, taganizirani za Abisalomu, mmodzi mwa ana a Davide. Anadzakhala munthu woipa kwambiri ngakhale kuti anali wooneka bwino. Ponena za iye, Baibulo limati: “Ndipo m’Israyeli monse munalibe wina anthu anam’tama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pa mutu wake mwa iye munalibe chilema.” (2 Samueli 14:25) Komabe, mtima wa Abisalomu wofuna kukhala ndi udindo unamuchititsa kuukira bambo ake ndi kulanda ufumu wawo. Anafika mpaka pogona ndi akazi aang’ono a bambo ake. Chifukwa cha zimenezi, Abisalomu anakwiyitsa Mulungu ndipo anafa imfa yopweteka.—2 Samueli 15:10-14; 16:13-22; 17:14; 18:9, 15.

Kodi mumakopeka ndi Abisalomu? Ayi ndithu. Iye anali munthu wakhalidwe lonyansa. Kukongola kwake kogometsa sikunalungamitse kukula mtima ndi kusakhulupirika kwake, ndiponso sikunamuteteze kuti asawonongedwe. Koma m’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu anzeru ndiponso okopa amene sanatchulidwe maonekedwe awo. Mwachidziwikire, chimene chinali chofunika kwambiri chinali kukongola kwawo kwa mumtima.

Kukongola kwa Mumtima Kumakopa Ena

Kodi kukongola kwa mumtima kungakope ena? Georgina, amene wakhala pabanja kwa zaka pafupifupi khumi, anati: “Zaka zonsezi, ndakhala ndikukopeka ndi mwamuna wanga chifukwa cha kuona mtima kwake akamachita nane zinthu. Chinthu chofunika kwambiri pamoyo wake ndi kusangalatsa Mulungu. Zimenezi zamuchititsa kukhala munthu woganizira ena ndiponso wachikondi. Asanachite chinthu amayamba wandifunsa kaye maganizo anga ndipo amandichititsa kumva kuti amayamikira zimene ndimachita. Ndikudziwa kuti amandikondadi.”

Daniel, amene anakwatira mu 1987, anati: “Ndimaona kuti mkazi wanga ndi wokongola. Sikuti ndimangokopeka ndi maonekedwe ake okha, koma khalidwe lake limandichititsa kumukonda kwambiri. Nthawi zonse amaganizira anthu ena ndipo amayesetsa kuwachitira zinthu zabwino. Ali ndi makhalidwe abwino kwambiri achikristu. Zimenezi zachititsa kuti ndizisangalala kukhala naye.”

M’dziko lino limene anthu amangoona zakunja zokha, tiyenera kuona mtima wa munthu. Tiyenera kuzindikira kuti kukhala ndi thupi labwino kwambiri n’kovuta, mwinanso kosatheka kumene, ndipo kuli ndi phindu lochepa kwambiri. Komabe, n’zotheka kukhala ndi makhalidwe abwino amene amachititsa munthu kukhala wokongola mumtima. Baibulo limati: “Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.” Mosiyana ndi zimenezo, Malemba amachenjeza kuti: “Monga chipini chagolidi m’mphuno ya nkhumba, momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.”—Miyambo 11:22; 31:30.

Mawu a Mulungu amatithandiza kuyamikira “munthu wobisika wamtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.” (1 Petro 3:4) Zoonadi, kukongola kwa mumtima kumeneko n’kofunika kwambiri kuposa kukongola kwa thupi. Ndipo aliyense akhoza kukhala nako.

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Makhalidwe abwino angakukongoletseni kwambiri kuposa mankhwala kapena opaleshoni iliyonse