Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kunyanyira Kufuna Kukongola

Kunyanyira Kufuna Kukongola

Kunyanyira Kufuna Kukongola

MARIA * ndi mtsikana amene zinthu zikumuyendera bwino pamoyo wake ndipo amachokera ku banja labwino kwambiri. Komabe, iye si wosangalala. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti sasangalala ndi maonekedwe ake. Ngakhale kuti anthu a m’banja lake amayesetsa kumulimbikitsa, Maria amadziona kuti si wokongola, ndipo zimenezi zimamuvutitsa maganizo.

José amachokera ku banja lolemekezeka ndipo anayenera kukhala wosangalala. Koma iye amaganiza kuti sadzapeza munthu wokwatirana naye. Chifukwa chiyani? José amaganiza kuti si wooneka bwino, ndiponso kuti ndi wonyansa kumene. Amakhulupirira kuti palibe mkazi wabwinobwino amene angakopeke naye.

Luis, amene ali ndi zaka eyiti, amakonda kupita ku sukulu ndiponso ndi wochezeka. Amakonda kusewera ndi anzake a kusukulu, koma nthawi zambiri amalira chifukwa anzakewo amamuseka chifukwa cha maonekedwe ake. Amamunena kuti ndi wonenepa kwambiri.

Zimenezi sikuti zikungochitikira anthu okhawa ayi. Sitinganene kuti vuto la Maria, José, ndi Luis n’kudzikayikira basi. Zoona zake n’zakuti palibe amene amafuna kuti anthu ena azimusala chifukwa cha maonekedwe ake.

Komabe, anthu masiku ano amakokomeza kwambiri kufunika kwa maonekedwe abwino. Ndipo kuti zinthu zikuyendereni bwino, nthawi zambiri zimadalira maonekedwe anu. Mwachitsanzo, anthu okongola nthawi zambiri savutika kupeza ntchito. Pilar Muriedas, mmodzi wa atsogoleri a bungwe lotchedwa Latin-American and Caribbean Women’s Health Network, anati “kukhala ndi maonekedwe abwino ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri [kwa akazi] kuti zinthu ziwayendere bwino.” Ndipo malinga ndi Dr. Laura Martínez, akazi amadziwa bwino kuti kuposa china chilichonse, “maonekedwe ndi amene amachititsa kwambiri kuti munthu alembedwe ntchito kapena asalembedwe.”

Ndipo amuna ambiri nawonso ayamba kuda nkhawa kwambiri pofuna kukhala ndi thupi labwino kwambiri. Zoonadi, amuna ndi akazi ambiri amachita zinthu zosiyanasiyana pofuna kukhala okongola. Ena amalolera kupirira ndi njala kapena kuchitidwa maopaleshoni opweteka pofuna kukhala ndi nkhope kapena thupi labwino kwambiri. Kodi kufunafuna kukongola koteroko n’kwaphindudi? Kodi kuli ndi kuipa kwake?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mayina asinthidwa.

[Chithunzi patsamba 19]

Maonekedwe angachititse kuti munthu alembedwe ntchito inayake kapena asalembedwe