Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kwalembedwa Kuti Ndidzawaonanso

Kwalembedwa Kuti Ndidzawaonanso

Kwalembedwa Kuti Ndidzawaonanso

Yosimbidwa ndi Rosalía Phillips

“Udzakhala munthu wotchuka kwambiri, chifukwa ndiwe munthu waluso kwabasi!” Mtsogoleri wa bandi yathu anandiuza mawu amenewo atakhala pa piyano yake kutangotsala timphindi tochepa kuti katani ya pabwalo lochitira masewero itsegulidwe ndipo ine ndiimepo. Anthu ena anayi a m’bandi mwathu anandilandira pabwalopo. Nditavala diresi yanga yofiira yokongola, ndinali munthu woimba mawu watsopano kwambiri kulowa nawo m’gululo. Ndinali ndi mantha aakulu. Aka kanali koyamba kuti ndiimbe pagulu, ndipo ndinali kumalo otchuka kwambiri ochitira masewero ku Mexico City. Kumeneku kunali kuyambika kwa ntchito yanga yausangalatsi! Munali mu March 1976 ndipo ndinali nditangotsala mwezi umodzi kuti ndikwanitse zaka 18.

BAMBO anga anali atamwalira zaka zitatu m’mbuyomo, ndipo ndinali kuwaganizirabe mumtima mwanga. Anthu ena analinso kuwakumbukira bwino. Anthu ankawakonda ndi kuwasirira poti anali mmodzi mwa anthu otchuka kwambiri ochita mafilimu oseketsa m’dzikomo, popeza anachita nawo mafilimu opitirira 120. Nthawi imene anachita mafilimu amenewo anthu ambiri amati inali nthawi yotsogola kwambiri pa nkhani ya makanema ku Mexico. Dzina lawo, Germán Valdés, kapena dzina limene ankatchuka nalo loti “Tin-Tán” linalembedwa pa makomo ambiri a malo ochitira masewero ku Central America ndi ku South America konse, kuphatikizaponso kumadera amene amalankhula Chisipanya ku United States ndi ku Ulaya. Ngakhale masiku ano, patatha zaka zopitirira 30 kuchoka pamene anamwalira, mafilimu awo amaonetsedwabe kambirimbiri pa TV.

Kuyambira ndili kamtsikana kakang’ono, kunyumba kwathu kunkakumana anthu otchuka ambirimbiri. Mayi anga ndi azing’ono awo anapanga gulu loimba la anthu atatu lotchedwa Las Hermanitas Julián (Ana Aakazi a a Julián). Mchimwene wawo Julio Julián anali woimba wotchuka wa tenala wa nyimbo za mtundu wa opera ku Ulaya, pamene mkazi wawo wachisipanya, Conchita Domínguez, ankaimba sapulano. Kuwonjezera apo, azichimwene awo a bambo anga, Manuel Valdés, amene ankatchuka ndi dzina loti “Loco” (wamisala), ndi Ramón Valdés, amene ankatchuka ndi dzina loti Don Ramón, (Bambo Ramón), anali anthu otchuka ochita masewero oseketsa pa TV.

Ine ndi mchimwene wanga Carlos tinazolowera kuona malo ojambulirako mafilimu, malo oonetserako masewero, ndi malo ojambulirako nyimbo chifukwa bambo anga nthawi zambiri ankatitenga kupita nawo limodzi kuntchito kwawo ndiponso pa maulendo okaonetsa masewero awo. Mmenemu ndi mmene anathandizira banja lathu kukhala logwirizana. Panali kusiyana kwakukulu pakati pa malo amenewo, amene kunkachitika zinthu zambiri zachiphamaso chabe, ndi kunyumba kwathu, kumene kunali mgwirizano ndi chikondi chenicheni. Ndikukumbukira kuti bambo anga anali munthu wachikondi kwambiri, wa nyonga zake, ndiponso wokonda kusangalala pamoyo. Anali opatsa kwambiri, mpaka kufika ponyanyira nthawi zina. Anandiphunzitsa kuti chimwemwe chimabwera chifukwa chopatsa osati chifukwa chokhala ndi zinthu.

Kusintha kwa Zinthu Kopweteka Kwambiri

Chakumapeto kwa chaka cha 1971, mayi anga anandiuza ine ndi mchimwene wanga nkhani yomvetsa chisoni kwambiri yoti bambo athu anawapeza ndi matenda osachiritsika. Kwa chaka chimodzi ndi theka, ndinawaona akuzunzika pamene thupi lawo linali kulimbana ndi mankhwala amphamvu kwambiri.

Ndikukumbukirabe tsiku limene ambulasi inabwera kunyumba kwathu kudzawatenga kupita nawo kuchipatala. Ndinadziwa kuti sabwerako. Sindingathe kufotokoza ululu umene ndinamva mumtima. Ndinaganiza kuti popeza bambo angawo anali kuvutika, inenso ndiyenera kuvutika. Ndinazimitsira ndudu m’manja mwanga n’kulira mosatonthozeka. Pa June 29, 1973, bambo anga anamwalira. Ndinayamba kudzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani munthu wabwino chonchi, amene anatibweretsera chimwemwe chachikulu, watisiya? Kodi panopa ali kuti? Kodi angandimve nditawalankhulitsa? Kodi tsopano moyo wanga uli ndi tanthauzo lanji popanda iwowo?’

Ntchito Yopanda Cholinga

Nditakhala nthawi kuti mtima wanga uzizireko, ndinayamba kuphunzira ntchito yokongoletsa m’nyumba. Koma ndinali wamakani, choncho ndinasiya kuchita maphunzirowo. Ine ndi mayi anga tinaganiza zoti tiyambe kucheza kwambiri ndi anthu. Tinkapita ku mapwando apamwamba kwambiri a asangalatsi. Nthawi zambiri yemwe wakonza phwandolo ankamaliza phwandolo ndi mawu oti, “Rosalía, tsopano tiimbire imodzi mwa nyimbo zako.” Anthu ankakonda nyimbo zanga ndi mmene ndinkaziimbira kuchokera pansi pa mtima, ndipo ankati ndinatengera luso la makolo anga.

Pa limodzi la mapwando amenewo, wolemba nyimbo ndi mtsogoleri wa bandi yotchedwa Arturo and His Castros 76 anandimva ndikuimba ndipo anandipempha kuti ndilowe nawo m’gulu lake. Poyamba sindinafune kuchita zimenezo. Ngakhale kuti ndinkakonda kuimba ndipo ndinakhala ndikulemba nyimbo ndi kuimba gitala kuyambira ndili ndi zaka 14, sindinkafuna kugwira ntchito yoimba. Koma mayi anga anandilimbikitsa kuvomera, ndipo banja lathu linkafunika ndalama, choncho pamapeto pake ndinavomera. Zimenezi n’zimene zinandichititsa kuti ndipezeke pa zochitika ndazifotokoza koyambirira zija.

Ndinkakhala ndi ntchito yokwanira yoti ndichite kuyambira pachiyambi penipeni pa ntchito yanga yausangalatsi. Gulu lathu linayendera dziko la Mexico, ndipo linkakhala ndi zionetsero ziwiri usiku uliwonse. Tinagwira ntchito ku Guatemala, Venezuela, New York, ndi ku Las Vegas. Ndinakhala ndi gululo kwa zaka ziwiri. Kenaka ndinapatsidwa mwayi wochita mafilimu. Ndinapatsidwa mbali ziwiri zazing’ono za m’mafilimu ndi mbali imodzi yokhala wochita sewero wamkulu mu filimu, imene inandipezetsa mphoto ziwiri zikuluzikulu.

Tsiku lina ndinalandira telefoni kuchokera ku kampani yaikulu kwambiri ya TV m’dziko mwathu. Anandiuza kuti akhoza kundilemba ntchito yoti ndikhale mmodzi mwa anthu awo ochita mbali zofunika kwambiri pa TV ndiponso kuti ndikhale ndi mbali yofunika kwambiri pa sewero linalake la pa TV loti likhale ndi dzina langa. Zimenezi zikanandichititsa kutchuka kwambiri pakati pa asangalatsi. Ndikanapatsidwa malipiro abwino kwambiri, ngakhale ndikanati ndisamagwire ntchitoyo nthawi zonse. Poona kuti sindinayenere kupatsidwa zinthu zonsezo ndiponso pofuna kukhalabe ndi ufulu, ndinakana ntchito imeneyo. Ndinavomera kuchita nawo sewero la pa TV lija, koma chifukwa chimene ndinavomerera chinali choti ndipitirizebe kuphunzira za masewero ku yunivesite. Komabe, sindinali wosangalala. Zinkandivutitsa maganizo kuona ochita mafilimu akuvutika kwa zaka zambiri asanapatsidwe mbali yaikulu pamene ine ndinapatsidwa mbali yofunika kwambiri, makamaka chifukwa choti ndinali mwana wa Tin-Tán.

Kenaka ndinayamba kujambulitsa nyimbo zanga. Yoyamba inali nyimbo yoyendera limodzi ndi sewero la pa TV lija, ndipo ineyo ndi amene ndinalemba mawu ndi maimbidwe ake. Kenaka ndinajambulitsa nyimbo zanga ku malo enaake otchuka ojambulitsira nyimbo ku London. Ndinajambulitsa nyimbo zowonjezereka, kuchita nawo mafilimu ena, ndi masewero ena a pa TV. Manyuzipepala anayamba kulemba nkhani zokhudza ineyo pa masamba oyambirira a chigawo cha asangalatsi, choncho tinganene kuti ndinali nditafika pachimake pa kutchuka. Komabe panali chinachake chimene ndinali kusowa. Ndinaona mmene asangalatsi analili onyada ndi opikisana, ndipo ankachita chiwerewere ndi chinyengo chambiri pakati pawo. Ndinasiya kukhulupirira anthu.

Kenaka m’nyengo yachilimwe ya mu 1980 ndinaonana ndi amalume anga a Julio banja lathu litakumana pamodzi. Anasiya kuimba nyimbo za opera ndipo ndinamvetsera pamene ankalankhula za paradaiso amene Mulungu analonjeza. Amalume a Julio anati kupanda chilungamo ndi chisoni zidzatha padziko lapansi ndipo m’malo mwake padzakhala chikondi chokhachokha. Ananenanso kuti dzina la Mulungu woona ndi Yehova. Chimene chinandisangalatsa kwambiri chinali kumva zoti m’Paradaiso, okondedwa athu amene anamwalira adzaukitsidwa. Kuganizira zodzawaonanso bambo anga kunandisangalatsa kwambiri. Sindinasiye kuwasowa ndi kufuna thandizo ndi chikondi chawo. Zikanakhala zosangalatsa kukhala nawonso limodzi! Koma mumtima mwangamu ndinkaganiza kuti zimenezo sizingatheke. Amalume a Julio anandipatsa Baibulo ndipo anapempha ine ndi amayi anga kuti tidzapite ku msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova umene unali kudzakhalapo patatha milungu yochepa. Tinawauza kuti mwina tidzapita.

Ndinaganiza Zosintha Moyo Wanga

Usiku winawake ndinali kusuta fodya ndili pabedi uku ndikuwerenga Baibulo limene amalume anga anandipatsa lija. Zimene ndinawerenga m’buku la Miyambo zinandichititsa kuzindikira kuti kuwala, kuzindikira, ndi moyo zinachokera kwa Mulungu pamene mdima, chisokonezo ndi imfa zinachokera kwina. Usiku womwewo ndinazimitsa nduduyo, imene inali yomaliza kusuta pamoyo wanga, ndipo ndinadikira kuti amayi abwere. Ndikulira, ndinawapempha kuti andithandize pa zinthu zinazake zikuluzikulu zimene ndimafuna kuchita. Kenaka ndinapita kumalo ochitira masewero kumene ndinali kuyeserera mbali ya Cordelia m’sewero la Shakespeare lotchedwa King Lear. Ndinasiya kuchita nawo sewerolo ndiponso ndinathetsa chibwenzi changa ndi mnyamata amene anali mmodzi mwa anthu amene anali ndi mbali zikuluzikulu m’sewerolo.

Koma ndinali ndisanaphunzire kutumikira Mulungu, choncho ndinalibe potsamira. Ndinadwala matenda aakulu ovutika maganizo. Ndinapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kuzindikira kuti ndingathe kukhala m’gulu linalake chifukwa cha khalidwe langa basi, osati chifukwa cha luso lotengera kwa makolo anga kapena chifukwa chokhala ndi dzina lotchuka. Ndinasiya kucheza ndi anzanga onse ndiponso kuchita zinthu zimene ndinkachita masiku onse.

Njira ya ku Moyo Wopambanadi

Ndili m’kati mosokonezeka choncho, ndinakumbukira kuti amalume anandipempha kuti ndidzapite ku msonkhano wachigawo. Ndinawaimbira telefoni ndipo anandipititsa ku bwalo la zamasewero kumene msonkhanowo unali kuchitikira. Zimene ndinaona kumeneko zinandikhudza kwambiri. Ndinaona anthu amtendere amene sankalankhula mawu otukwana kapena kusuta fodya ndipo sankayesera kugometsa munthu aliyense. Zimene ndinamva kuchokera m’Baibulo zinandikumbutsa zinthu zimene ndinawerenga m’buku laling’ono lotchedwa Is the Bible Really the Word of God? * lomwe ndinapeza m’nyumba mwanga bambo anga atangomwalira kumene.

Chapanthawi imeneyi ndinapatsidwanso ntchito ina yochita mbali yaikulu pa sewero la pa TV. Ndinasangalala nayo mbali yake, chifukwa inkaoneka kuti ikugwirizana ndi mfundo zokondweretsa Mulungu zimene ndinaphunzira pa msonkhano wachigawo uja. Poganizira zimenezo, ndinavomera ntchitoyo. Koma mawu a m’Baibulo otsatirawa ankangobwera m’maganizo mwanga, oti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti . . . kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?”—2 Akorinto 6:14.

Ndinayamba kufuna kwambiri kusangalatsa Mulungu. Ndinafuna kukasonkhana nawo ku Nyumba ya Ufumu ndi amalume ndi azakhali anga. Mpingo wawo unali pamtunda woyenda ola limodzi kuchoka kunyumba kwanga, koma ndinapita kukasonkhana nawo Lamlungu kwa milungu itatu yotsatizana. Amalume anga anaganiza zondipititsa ku mpingo wa m’dera lathu. Tinafika msonkhano ukutha, ndipo kumeneko ndinakumana ndi mtsikana wa msinkhu wanga dzina lake Isabel. Anali wodzichepetsa ndiponso wokoma mtima. Amalume anga atamuuza kuti dzina langa ndi Rosalía Valdés, sanatutumuke n’komwe ndi dzina langalo. Zimenezo zinandisangalatsa kwambiri. Isabel anandiuza kuti akhoza kumaphunzira nane Baibulo kunyumba kwanga.

Tinayamba kuphunzira pogwiritsa ntchito buku lotchedwa Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. * Isabel analolera kusintha pulogalamu yake kuti ifanane ndi yanga. Nthawi zina ankandidikirira mpaka usiku kwambiri kuti ndimalize kujambula sewero la pa TV lija. Ndinali woyamikira kwambiri kukumana ndi munthu amene anali nane chidwi chifukwa choti ndinkafuna kuphunzira choonadi cha m’Baibulo basi! Anali woona mtima ndiponso wotsungula, makhalidwe amene ndinkaganiza kuti munthu sangakhale nawo pokhapokha ataphunzira nzeru za anthu ndi zojambulajambula. Tinakonza zoti tiziphunzira kwa nthawi yaitali, nthawi zina kangapo pamlungu.

Poyamba zinali zovuta kuti ndisiye kukhulupirira maganizo anga olakwika, koma pang’ono ndi pang’ono mfundo za choonadi za m’Baibulo zinalowa m’malo mwa maganizo amenewo. Ndikukumbukira mmene ndinasangalalira ndi lonjezo la Mulungu loti: “Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:10, 11) Ndiponso panthawi imeneyi chiyembekezo chimene ndinali nacho chodzaonanso bambo anga m’Paradaiso chinayamba kukula. Nthawi zambiri ndinkaganizira mawu a Yesu oti: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo.”—Yohane 5:28, 29.

Ndinamaliza ntchito yanga pa sewero la pa TV lija ndipo ndinapatsidwa ntchito zina nthawi yomweyo. Ngakhale kuti ntchitozo zikananditchukitsa kwambiri, kuvomereza ntchitozo kukanatanthauza kuti ndikugwirizana ndi chiwerewere, kulambira mafano, ndi zikhulupiriro zina zabodza. Ndinali nditaphunzira kuti Satana ndi weniweni ndipo safuna kuti tizitumikira Yehova. Choncho ndinakana ntchitozo n’kuyamba kupita ku misonkhano yonse. Mosadabwitsa, mayi anga ndi mchimwene wanga sanamvetse chifukwa chimene ndinali kukanira ntchito ndi ndalama zambirimbiri. Panthawi yomweyo, ankaona kuti ndikusintha. Ndinali kusintha kuchoka pa munthu wosasangalala ndi wokhumudwa kukhala munthu wachimwemwe. Pomalizira pake, ndinapeza cholinga cha moyo wanga!

Ndinafuna kuuza ena zimene ndinali kuphunzira ndipo pasanapite nthawi yaitali ndinakhala wofalitsa wa uthenga wabwino kwambiri wa Ufumu wa Mulungu. Ndikamalalikira, nthawi zina zinali zovuta kuti mwininyumbayo azimvetsera zimene ndikunena chifukwa anthu ambiri ankazindikira kuti ndinali msangalatsi. Nthawi zingapo ine ndi mnzanga tinafika pamakomo pa anthu panthawi imene pa TV anali kusonyeza sewero limene ineyo ndinachita nawo. Eninyumbawo sankakhulupirira kuti ndinali nditaimiriradi pakhomo pawo!

Pa September 11, 1982, ndinabatizidwa posonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova. Moyo wanga tsopano unali ndi cholinga chenicheni, ndipo patsogolo panga panali ntchito yamtundu wina yoti ndichite. Khama limene Isabel anali nalo mu utumiki linandilimbikitsa. Iye anali mpainiya wokhazikika, dzina limene atumiki a nthawi zonse a Mboni za Yehova amatchedwa. Posakhalitsa ndinayamba kupita naye limodzi akamakaphunzira Baibulo ndi anthu ena. Isabel anakhala mnzanga wapamtima.

Ndinali nditasiya pafupifupi ntchito zanga zonse zausangalatsi choncho ine ndi mayi anga tinayamba kukhala moyo wotsikirapo. Panthawi imeneyo ndinalemba nyimbo za kaseti yanga yachinayi, zimene zinaphatikizapo nyimbo zokhudza zikhulupiriro zanga zatsopano. Ndinalemba nyimbo yonena za chiyembekezo champhamvu chomwe ndinali nacho choti bambo anga ndidzawaonanso. Ndinaitcha, “Kwalembedwa Kuti Ndidzawaonanso.” Pamene ndinawaimbira nyimboyo mayi anga koyamba, inawakhudza mtima kwambiri. Anatha kuona kuti ndinali kukhulupiriradi zimenezo ndi mtima wonse. Ndinasangalala kwambiri pamene ananena kuti akufuna kuphunzira Baibulo. Patatha zaka ziwiri anakhala mtumiki wa Yehova wobatizidwa. Mpaka pano amachitabe utumiki mwakhama.

Pamene nthawi inali kupita, sindinkavutikanso kukana ntchito. Ndipo ndikakumana ndi chiyeso, kuganizira za bambo anga ali limodzi nafe m’paradaiso wokongola kunkandilimbikitsa kuti ndipitirizebe kutumikira Yehova.

Tsiku lina ndinapemphedwa kuti ndichite nawo sewero la Sesame Street, lomwe anakonzera anthu a ku Latin America. Sewero limeneli inali pulogalamu ya ana ya pa TV. Ndinaganiza kuti sindingachite nawo sewerolo ndipo ndinauza bwana wanga kuti sindikanatha kulimbikitsa zinthu monga maholide ndi mapwando a tsiku lakubadwa chifukwa cha mfundo zomwe ndimayendera za m’Baibulo. Bwana wangayo anandiuza kuti ndikavomera ntchitoyo, adzalemekeza zikhulupiriro zanga ndipo tidzasainirana chipepala chosonyeza mwatsatanetsatane zinthu zoti ndichite. Choncho ndinavomera ndipo ndinachita nawo zigawo 200 za pulogalamuyo zimene zinajambulidwa. Imeneyo ndi ntchito yomaliza imene ndinagwira monga munthu wochita mafilimu.

Ndinali nditangotsala ndi ntchito imodzi yokha ndi kampani yojambula nyimbo ija, choncho ndinajambulitsa nyimbo zanga teni, kuphatikizapo nyimbo imene ndinalemba yokhudza bambo anga yonena za kuuka kwa akufa. Ndinakhala ndi mwayi woimba nyimbo imeneyo pa TV ndi pazionetsero, ndipo nthawi zonse ndinkatchulapo zikhulupiriro zanga. Komabe, kampani yojambula nyimbo ija inayamba kundikakamiza kuti ndizioneka mokopa amuna, choncho ndinasiya kugwira ntchitoyo.

Kupeza Madalitso Potumikira Mulungu

Mu December 1983, ine ndi Isabel tinakayendera likulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn, ku New York. Kumeneko ndinakumana ndi munthu amene anadzakhala mwamuna wanga, Russell Phillips. Tinalemberana makalata kwa zaka pafupifupi ziwiri. Ndimakumbukira bwino tsiku limene ndinayamba kuchita upainiya wokhazikika chifukwa Russel ananditumizira maluwa kuchokera komwe ku New York!

Kwa chaka chimodzi ndinachita upainiya ndi Isabel. Kenaka anaitanidwa kukatumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico. Zimene ankanena za utumiki wake watsopano zinandichititsa kuyamba kufuna kufutukula utumiki wanga, ndipo Yehova atalola, kutumikiranso pa Beteli.

Russel wakhala dalitso lina pamoyo wanga. Chifukwa cha mmene amakondera Yehova ndi gulu Lake, ndaphunzira kukonda kwambiri utumiki wa nthawi zonse. Ankakonda kutumikira pa Beteli, chifukwa anatumikira ku Beteli ya ku Brooklyn kwa zaka zitatu. Titakwatirana tinachitira limodzi upainiya ku Colorado, ku United States. Kenaka tinapemphedwa kugwira ntchito ya zomangamanga pa nthambi zatsopano m’mayiko ena. Tinadabwa kwambiri pamene anatipempha kuti tikatumikire ku Mexico. Mu April 1990, tinakhala ndi mwayi wapadera wokhala mbali ya banja la Beteli ku Mexico. Chitsanzo cha Russel chinandilimbikitsa kwambiri. Ndinasirira mtima wodzipereka umene anali nawo, umene unamuchititsa kusiya dziko lake ndi banja lake kukapititsa patsogolo zinthu za Ufumu ku Mexico.

Ine ndi Russel tinasangalala kwambiri ndi utumiki wathu pa nthambi ya Mexico. Koma zinthu zinasintha mwadzidzidzi pamene ndinakhala ndi pakati. Sitinkayembekezera n’komwe zimenezo. Ngakhale zinali choncho, nthawi zonse tinakhala tikusirira makolo amene amalera ana awo m’choonadi, ndipo tinalandira ntchito imeneyi ngati utumiki wathu watsopano. Mu October 1993, Evan anabadwa ndipo Gianna anabadwa patatha zaka ziwiri ndi theka. Ngakhale kuti kulera ana kumafuna kugwira ntchito mwakhama nthawi zonse, timaona kuti tadalitsidwa nthawi iliyonse imene mwana wathu wa zaka 11 ndi wa zaka 8 amanena za chikhulupiriro chawo akamachita utumiki.

Russel tsopano amagwira ntchito mu Komiti Yomanga Nyumba za Ufumu Yachigawo, ndipo ineyo posachedwapa ndinayambiranso kuchita utumiki wanthawi zonse monga mpainiya. Pa zaka 20 zapitazi, ndathandiza anthu 12 a m’banja mwanga, ndiponso anthu ena 8, kuphunzira choonadi cha m’Baibulo ndi kuyamba kutumikira Yehova.

Ana anga akandifunsa kuti, “Amama, kodi zinali zovuta kuti musiye ntchito yanu yausangalatsi?” Ndimawauza mawu a mtumwi Paulo, oti: “Ndimaziyesa zonse zotayidwa poyerekeza ndi kukula kopambana kwa kudziwa Khristu Yesu Ambuye wanga, amene pa chifukwa chake ndataya zinthu zonse. Ndimaziyesa zinyalala, kuti ndipindule Khristu.” (Afilipi 3:8, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Ndimayamikira kwambiri kuti Yehova anandipulumutsa ku moyo wachabechabe ndiponso wopanda cholinga n’kundilola kukhala mbali ya anthu ake abwino kwambiri. Sinditopa kumuthokoza chifukwa cha madalitso ambiri amene anatipatsa kudzera mwa Mwana wake, Yesu Kristu. Nthawi zambiri ndimaimba mosangalala nyimbo imene ndinalemba yokhudza bambo anga. Ndikukhulupirira kuti ndidzawaonanso.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 21 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano anasiya kulisindikiza.

^ ndime 24 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano anasiya kulisindikiza.

[Chithunzi patsamba 26]

Ndili ndi makolo anga ndi mchimwene wanga pamene ndinali ndi chaka chimodzi

[Chithunzi pamasamba 28, 29]

Kuimba ndi gulu la Arturo Castro and His Castros 76

[Mawu a Chithunzi]

Angel Otero

[Chithunzi patsamba 30]

Ndili ndi banja langa masiku ano

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

Activa, 1979