Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndikanakonda Anthu Akanadziwa Zimenezi!”

“Ndikanakonda Anthu Akanadziwa Zimenezi!”

“Ndikanakonda Anthu Akanadziwa Zimenezi!”

ATAMALIZA sukulu ku sekondale, pamene achinyamata ambiri amaganiza zopanga chuma, David anali ndi maganizo ena. Mu September 2003, iye ndi mnzake anasamuka ku Illinois, ku United States, kupita ku Dominican Republic. * Davey, (dzina limene anzake ndi anthu a m’banja lake ankamuitanira) anaganiza zophunzira Chisipanya n’kulowa nawo Mpingo wa Navas wa Mboni za Yehova, kuti awathandize pantchito yawo yophunzitsa Baibulo. Mpingowo unamulandira ndi manja awiri. Juan, mkulu mmodzi yekhayo wa mu mpingomo, anati: “Davey ankachita chilichonse chomwe tamupempha kuchita. Nthawi zonse ankadzipereka kuthandiza anthu ena, ndipo abale anamukonda kwambiri.”

Davey anali kukonda kwambiri ntchito yake. Iye analembera mnzake amene anali ku United States kuti: “Ndikusangalala kwambiri kuno. Utumiki wake ndi wotsitsimula kwabasi. Timalankhula kwa mphindi pafupifupi 20 pakhomo lililonse chifukwa anthu amafuna kumva zonse zomwe ukufuna kuwauza. Panopa ndikuchititsa kale maphunziro a Baibulo sikisi, koma tikufunikabe thandizo. Pamsonkhano winawake wa mpingo, panabwera anthu 103 ngakhale kuti mpingo wathu uli ndi ofalitsa Ufumu 30 okha!”

Koma n’zomvetsa chisoni kuti pa April 24, 2004, Davey ndi mnyamata wina wa mumpingo womwewo anamwalira pangozi. Kufika mpaka imfa yake, Davey anali ndi changu kwambiri pa ntchito imene anali kuchita, ndipo ankalimbikitsa achinyamata ena kwawo kuti abwere adzachite nawo ntchitoyo. Iye anauza Mboni ina yachinyamata kuti: “Zidzakuchititsa kusintha mmene umaonera zinthu.”

Davey mwiniwakeyo anasintha mmene anali kuonera chuma. Bambo ake anati: “Atabwera kunyumba kudzacheza, Davey anaitanidwa kupita ku ulendo wokasewera pa chipale chofewa. Iye anafunsa kuti adzafunika kuwononga ndalama zingati. Atamuuza mtengo wake, Davey anati sangawononge ndalama zonsezo kusewera pa chipale chofewa pamene akanatha kugwiritsa ntchito ndalama zomwezo kwa miyezi ingapo ku Dominican Republic!”

Khama la Davey linakhudza anthu ena. Wachinyamata wina wa ku United States anati: “Nditamva zonse zimene Davey anali kuchita ndi mmene analili wosangalala, zinandithandiza kuzindikira kuti inenso bwenzi ndikuchita zinthu ngati zomwezo. Imfa ya Davey yandichititsa kuganizira zimene anthu anganene nditati ndamwalira ndiponso ngati ndingakhudze moyo wawo m’njira yabwino kwambiri choncho.”

Pokhala Mboni za Yehova, makolo a Davey, mkulu wake, ndiponso mchemwali wake, ali ndi chikhulupiriro chonse kuti Mulungu adzaukitsa Davey m’dziko latsopano la chilungamo lomwe likubwera posachedwapa. (Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:1-4) Koma panopa amalimbikitsidwa pozindikira kuti Davey anagwiritsa ntchito moyo wake m’njira yabwino kwambiri, yomwe ndi kutumikira Mlengi wake. (Mlaliki 12:1) Poganizira zimene anachita zokatumikira kumene kunali kufunika thandizo, Davey panthawi ina ananena kuti: “Ndingasangalale wachinyamata aliyense atachita zinthu ngati zimene ndikuchitazi n’kumva mmene ndikumveramu. Palibenso chinthu china chabwino kuposa kutumikira Yehova ndi mtima wonse. Ndikanakonda anthu akanadziwa zimenezi!”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mofanana ndi David, Mboni za Yehova zambiri zadzipereka kusamukira ku dera kumene kukufunika anthu ambiri olalikira za Ufumu, ndipo zina mwa izo zaphunzira chinenero chatsopano kuti ziphunzitse ena mfundo za choonadi zopezeka m’Mawu a Mulungu. Anthu odzipereka oterowo opitirira 400 panopa akutumikira ku Dominican Republic.