Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulendo Wosaiwalika Wokaona Chigwa cha Ngorongoro

Ulendo Wosaiwalika Wokaona Chigwa cha Ngorongoro

Ulendo Wosaiwalika Wokaona Chigwa cha Ngorongoro

Yolembedwa ndi wolemba Galamukani! ku Tanzania

“ANGELO akanakhala kuti ankajambula zithunzi za m’Munda wa Edene, zithunzi zawo za zinthu zachilengedwe sizikanakhala zosiyana ndi zimene munthu angajambule ku chigwa cha Ngorongoro masiku ano.” Zimenezo n’zimene analemba Reinhard Künkel m’buku lake lofotokoza za malo ochititsa chidwi amenewa a ku Tanzania. Chigwa cha Ngorongoro ndi malo okongoladi kwambiri ndipo n’ngodzaza ndi zinyama zakutchire zambirimbiri. Tiyeni tikaonere limodzi zinthu zosangalatsazi!

Malo Okongola Kwabasi

Titayenda maola anayi pa misewu yafumbi, tikufika m’mphepete mwa chigwa cha Ngorongoro. Tikuyang’ana kukongola kwa malowo titakhala pakhonde pa hotela yathu. Malowo akuonekadi okongola mochititsa chidwi. Anthu ogwira ntchito zachilengedwe afika mpaka powatcha “chinthu chachieyiti pa zinthu zodabwitsa kwambiri padziko lonse lapansi,” ndipo tikutha kuona chifukwa chake anawapatsa dzina limenelo.

Kodi dzina loti Ngorongoro linachokera kuti? Palibe amene akudziwa bwinobwino. Malinga ndi bungwe loona zachilengedwe lotchedwa Conservation Corporation of East Africa, anthu ena amati Ngorongoro linali dzina la Mmasai winawake amene ankapanga mabelu oveka ng’ombe, amene ankakhala m’chigwamo. Ena amati dzinali linachokera ku gulu linalake la anthu ankhondo amphamvu otchedwa Adatogo amene anagonjetsedwa ndi Amasai atamenyana m’chigwamo zaka 150 zapitazo. Koma tikuyamba taiwala kaye nkhani ya komwe dzinalo linachokera chifukwa choti taona mbidzi zikudya udzu pafupi ndi pamalo oimika magalimoto. Pamene tikukwera galimoto yathu, tikuyandikana nazo kwambiri, koma zikuoneka ngati sizikutiona n’komwe. Tikuyendetsa galimotolo kulowera pakati pa chigwacho kuti tikaone zinyama zina.

Chigwacho chili pokwera mamita 2,236 pamwamba pa nyanja, ndipo ndi chigwa chachikulu kwambiri padziko lonse lapansi chopangika chifukwa cha kuphulika kwa phiri ndiponso chimene m’mphepete mwake monse muli mosagumuka. N’chachikulu makilomita 19.2 m’mimba mwake ndipo kukula kwa dera lake ndi masikweya kilomita 304. Tikuyendetsa galimotolo pang’onopang’ono kutsika mamita 610, uku titatulutsa mitu yathu kunja kwa galimotolo kuti tizijambula zithunzi. Pamene tinali m’mphepete mwa chigwacho m’mawa, mpweya wake unali wozizira. Koma tikudabwa kupeza kuti pakati pa chigwacho m’potentha.

Pamene dalaivala wathu akutiyendetsa pang’onopang’ono kuzungulira pansipo, tikudutsa nyanja yaing’ono yamchere yodzaza ndi mbalame zofiirira za mtundu wa flamingo. M’mphepete mwa chigwacho, mmene tsopano mukuonekera chakutali, mukuoneka bwino kwambiri chifukwa cha m’mlengalenga mopanda mitambo. Pamene tikumvetsera kulira kwa mbidzi ndi nyumbu kutaphatikizana ndi kulira kwa nyama zina zomwe sitikuzidziwa, zikutikhudza kwambiri mumtima. Zoonadi, kuno kuli ngati ku paradaiso!

Zinyama za M’chigwacho

M’chigwa cha Ngorongoro chino tikuyembekezera kuona njati, njovu, mbidzi, nyumbu, agwape, zipembere zakuda, ndi anyani, ndipo tikuzionadi nyama zonsezi. Kulinso nyama zodya zinzawo monga akakwiyo, afisi, nkhandwe, ndi mikango. Padziwe lina losazama kwambiri, pali mvuu zimene zikuziziritsa matupi awo. Zikuoneka kuti sizikudandaula pamene tikuzijambula zithunzi.

Mwadzidzidzi, dalaivala wathu akuimitsa galimotoyo. Akuloza chipembere chakuda chomwe chikuwoloka msewuwo pakamtunda kochepa chabe kuchoka pamene tili. Chipembere chakudacho chikuoneka kuti chimakhala mosangalala m’chigwachi, ndipo ndi mwayi wosowa kwambiri kuchiona pafupi choncho kutchire. Nyama zochititsa mantha zimenezi zatsala pang’ono kutha zonse, ndipo m’chigwachi akuti zilimo zosakwana 20. Anthu opha nyama popanda chilolezo agwidwapo kunoko chifukwa chopha zipembere kuti apeze nyanga zake, zomwe amazigulitsa mozembera boma. Anthu amagula nyangazi kuti azikapangira zigwiriro za zikwanje ndiponso mankhwala. Asilikali oteteza nyama amayendera derali nthawi zonse kuti azithamangitsa anthu opha nyama popanda chilolezo.

Munthu wokonda mbalame angaone mitundu yosiyanasiyana ya mbalame zokongola, monga nthiwatiwa, adokowe, ngalu, akakowa ndi mbalame zina zosiyanasiyana. M’chigwachi muli mitundu ya mbalame yopitirira 100 zomwe sizipezeka m’malo osunga zachilengedwe oyandikana nawo a Serengeti National Park. Kulinso anamgogomola ndi mbalame zina zimene zimabisala mu udzu utaliutali, ndiponso anthu ena anaonapo khwangwala winawake amene sapezeka kumadera ambiri.

Ngakhale kuti nyama zambiri sizingativutitse, tifunika kukhala m’galimoto mwathu. Komabe, Amasai, amene amakhala m’nyumba zadothi zofolera ndi udzu kunja kwa chigwacho amatha kumayendayenda m’chigwamo ndi ziweto zawo. Zikuoneka kuti zinyamazo zinawazolowera.

Kukongola ndi bata la ku chigwa cha Ngorongoro n’kochititsadi chidwi ndipo kwatisiya tili kakasi, kusowa chonena. Sitidzaiwala zomwe taona pa ulendo umenewu.

[Chithunzi patsamba 15]

Chipembere

[Chithunzi patsamba 15]

Abusa achimasai m’mphepete mwa chigwacho

[Chithunzi patsamba 15]

Mkazi wachimasai

[Chithunzi patsamba 16]

Akakwiyo

[Chithunzi patsamba 16]

Ngalu

[Chithunzi patsamba 16]

Mbalame zotchedwa “flamingo”

[Chithunzi patsamba 16]

Mvuu

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Chigwa cha Ngorongoro

[Chithunzi patsamba 17]

Mbidzi

[Chithunzi patsamba 17]

Njati

[Chithunzi patsamba 17]

Njovu

[Chithunzi patsamba 17]

Nyani