Buku la Achinyamata Limene Ambiri Amaliyamikira
Buku la Achinyamata Limene Ambiri Amaliyamikira
AHEDIMASITALA a pasukulu ya atsikana ya Tigoni Academy ku Limuru, ku Kenya, analemba kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko limenelo yopempha mabuku a Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Iwo anati: “Monga mukudziwa, kuchita zinthu ndi achinyamata nthawi zina kumakhala kovuta. Tili ndi mabuku anu amenewa awiri, amene athandiza kwambiri aphunzitsi ndi ana a sukulu. Bukuli limafotokoza zinthu zofunika zokwanira, ndipo limakwaniritsa zosowa za aphunzitsife ndi atsikanawo.”
A hedimasitalawo kenako anati: “Akuluakulu [a sukuluyi] akufuna kuti tizigwiritsa ntchito buku lothandizali pophunzitsa atsikana athu. Amalikonda kwambiri buku limeneli. Makolo a anawo amasangalala ndi zonse zomwe timachita pothandiza ana awo. Panopa tikuganiza kuti mabuku 25 angakhale okwanira.”
Buku la Achichepere Akufunsa limafotokoza bwino zinthu zimene achinyamata amaganiza. Limalimbikitsa kukambirana kwabwino pa nkhani ngati izi: “Kodi Ndingachititse Motani Makolo Anga Kundipatsa Ufulu Wowonjezereka?,” “Kodi Ndiyenera Kuchoka Panyumba?,” “Kodi Ndingapange Motani Mabwenzi Enieni?,” “Kodi Ndiyenera Kusankha Ntchito Yophunziridwa Yotani?,” “Bwanji Ponena za Kugonana Ukwati Usanachitike?,” ndi “Kodi Ndingadziŵe Motani Ngati Chiri Chikondi Chenicheni?”
Iyi ndi mitu yochepa chabe ya nkhani zomwe zili m’bukuli. M’mitu yake 39, bukuli limafotokozanso nkhani zina zambiri. Mungathe kuitanitsa buku limeneli polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.
□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.