Kodi Ndiyenera Kutani Anthu Ena Akandiuza Mavuto Awo?
Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndiyenera Kutani Anthu Ena Akandiuza Mavuto Awo?
“Mtsikana winawake wa ku sukulu kwathu makolo ake anali pakati posudzulana, ndipo anayamba kulephera m’kalasi. Kenaka anayamba kundiuza za mavuto a m’banja mwawo.”—Anatero Jan, wa zaka 14.
“Mtsikana winawake ku sukulu kwathu anandiuza kuti anagona ndi mnyamata, ndipo anatenga mimba n’kuichotsa makolo ake osadziwa n’komwe.”—Anatero Mira, wa zaka 15.
TIYEREKEZERE kuti mukucheza ndi mnzanu kapena munthu wina wa kusukulu kwanu. Mwadzidzidzi, mnzanuyo akuyamba kukuuzani za vuto linalake limene akukumana nalo. Mwina akukumana ndi mavuto amene achinyamata ambiri amakumana nawo, monga okhudza zovala, ndalama, maonekedwe, anzawo, kapena kulephera ku sukulu. Koma n’kuthekanso kuti akhoza kukhala ndi mavuto aakulu.
Zimene zikuchitika ku United States zikusonyeza mavuto aakulu amene achinyamata angakumane nawo. Malinga ndi magazini ya Newsweek, “bungwe loona za matenda a maganizo lotchedwa National Institutes of Mental Health (NIMH) linati achinyamata pafupifupi 8 pa achinyamata 100 alionse ndiponso ana pafupifupi awiri pa ana 100 alionse (ena aang’ono kwambiri, monga a zaka 4) ali ndi zizindikiro zosonyeza kuti akudwala matenda ovutika maganizo.” Pa kafukufuku wina anapeza kuti: “Pafupifupi atsikana 97 pa atsikana 1,000 alionse a zaka zapakati pa 15 ndi 19, amene akuimira atsikana wani miliyoni a ku America, amatenga mimba chaka chilichonse. Ambiri mwa atsikana amene amatenga mimbawa, atsikana 78 pa atsikana 100 alionse, amakhala oti sakuzifuna mimbazo.” Ndiyeno palinso achinyamata ambirimbiri amene amakhala m’mabanja osowa mtendere. Ena ambirimbiri amachitiridwa nkhaza kapena kukakamizidwa kugonana ndi munthu wina. Ana a kusukulu za sekondale ku United States opitirira theka la ana onse amene ali m’makalasi omalizira a kusekondale analedzerapo ndi mowa. Palinso achinyamata ochuluka modetsa nkhawa amene akudwala matenda ovutika kudya.
Choncho n’zosadabwitsa kuti achinyamata ambiri amafunitsitsa kupeza munthu woti alankhule naye ndi kumuululira zakukhosi kwawo. Ndipo nthawi zambiri munthu amene amalankhula naye koyamba ndi mnzawo. Kodi muyenera 1 Timoteo 4:12; Afilipi 4:5) Choncho achinyamata ena, kuphatikizapo osakhulupirira, akhoza kufuna kukambirana nanu mavuto awo. Kodi muyenera kutani zikatero? Ndipo kodi muyenera kutani ngati mukuona kuti zomwe mwauzidwazo zakukulirani?
kutani mnzanu akafuna kulankhula nanu? Ngati ndinu Mkristu, musadabwe kuti akufuna kulankhula ndi inuyo. Baibulo limalamula Akristu kuti akhale “chitsanzo” chabwino posonyeza khalidwe labwino ndiponso kuti akhale ofatsa, kapena kuti omvetsa zinthu. (Kumvetsera Bwino Akamakulankhulani
Baibulo limati pali “mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.” (Mlaliki 3:7) Munthu wina akakhala kuti ali ndi vuto ndipo akufuna kulankhula nanu, chinthu chabwino kwambiri kuchita ndicho kumvetsera. Ndi bwino kutero chifukwa Baibulo limati si bwino kungokhala osachitapo kanthu “polira waumphawi.” (Miyambo 21:13) Mwina zinatenga nthawi yaitali kuti mnzanuyo alimbe mtima n’kulankhula nanu nkhani imeneyo. Mukakhala wofunitsitsa kumvetsera mungamulimbikitse mnzanuyo kulankhula nanu momasuka. Mnyamata wina wachikristu dzina lake Hiram anati: “Nthawi zambiri ndimangomusiya munthuyo kuti alankhule zonse zomwe akufuna. Ndimamulola kunena zimene zikumusowetsa mtendere, ndipo ndimayesetsa kumumvera chisoni.” Vincent nayenso anati: “Nthawi zina anthu amangofuna kulankhula ndi winawake basi.”
Choncho mnzanuyo akhoza kukhala kuti sakuyembekezera kuti muthetse mavuto akewo. Mwina akungofuna munthu woti amumvetsere basi. Choncho, mvetserani! Yesetsani kuti musadodometsedwe ndi zimene zikuchitika pamalo pamene mulipo kapena kumamudula mawu akamalankhula. Inuyo mukakhala pamenepo n’kumumvetsera zingamuthandize kwambiri. Zimasonyeza kuti mumamukondadi.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti simuyenera kunenapo chilichonse mukamva mavuto a mnzanuyo? Zingadalire makamaka vuto limene wakuuzanilo. Nthawi zambiri ndi bwino kunenapo mawu omulimbikitsa mnzanuyo. (Miyambo 25:11) Mwachitsanzo, ngati munthu wodziwana naye wagweredwa tsoka linalake, ndi bwino kumupepesa. (Aroma 12:15) Lemba la Miyambo 12:25 limati: “Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu; koma mawu abwino aukondweretsa.” Mwina akufunika kumulimbikitsa. Muuzeni kuti mukukhulupirira kuti akwanitsa kuthana ndi vuto lakelo bwinobwino. Kumuuza mawu ngati akuti “Ndikutha kuona chifukwa chake ukumva chonchi” kapena “Pepa kuti ukulimbana ndi vuto ngati limeneli” kungamusonyeze mnzanuyo kuti mukumvetsadi vuto lakelo ndipo mukufuna kumuthandiza.
Komabe, lemba la Miyambo 12:18 limachenjeza kuti: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga.” M’pofunika kwambiri kupewa kunena zinthu ngati “Limenelo si vuto kwenikweni,” “Ingoiwala zimenezo,” kapena “Usadandaule ndi zimenezo.” Pewaninso kuyesera kuchepetsa vutolo ponena nthabwala. Mnzanuyo akhoza kuona ngati simulemekeza mmene amamvera.—Miyambo 25:20.
Nanga bwanji ngati mukusowa chonena? Muuzeni chilungamo. Muuzeni mnzanuyo kuti simukudziwa choti munene koma mukufunabe kumuthandiza. M’funseni kuti, “Ndingachite chiyani kuti ndikuthandize?” Indedi, pakhoza kukhala zinthu zinazake zimene mungachite kuti mumuchepetsereko mavuto akewo.—Agalatiya 6:2.
Kumuthandizako Nzeru
Bwanji ngati mukuona kuti mnzanuyo akufunika kumuthandizako nzeru? N’zoona kuti pali zinthu zina zimene simukuzidziwabe popeza mukadali wamng’ono. (Miyambo 1:4) Choncho simungathe kuthandiza munthu pa mavuto onse omwe angakhale nawo. Komabe, Salmo 19:7 limati: “Mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.” Inde, ngakhale kuti ndinu ‘wopusa,’ kapena kuti wosadziwa zambiri, mukhoza kudziwa mfundo za m’Baibulo zoti zingathandize munthu wina. (Miyambo 27:9) Popanda kuoneka ngati mukumulalikira mnzanuyo, bwanji osamuuza mfundo zingapo za m’Baibulo? Ngati simukudziwa mfundo za m’Baibulo zoti zingagwirizane ndi vuto lakelo, chitani kafukufuku. Pa zaka zapitazi, nkhani zakuti “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . ” zopezeka m’magazini ino zafalitsa malangizo ambiri ochokera m’Baibulo onena za nkhani zosiyanasiyana. Buku lina limene lili ndi mfundo zothandiza ndi la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. *
Mwina zingamuthandizenso mutamuuza zimene zinakuchitikirani inuyo. Mwina mungakhale Miyambo 27:17) Koma kumbukirani kuti zochitika zimasiyanasiyana. Zimene zinakuthandizani inuyo sizingathandize anthu onse.
ndi malangizo ena othandiza. Popanda kumukakamiza munthuyo kutsatira maganizo anu, mungamufotokozere zimene zinakuthandizani inuyo. (Chenjezo
Musamathe nthawi yochuluka kumvetsera mavuto a achinyamata amene saopa Yehova kapena amene salemekeza mfundo zachikristu. Ambiri mwa mavuto awowo angabwere chifukwa chokhala ndi moyo wosemphana ndi zimene Baibulo limanena. Kuyesera kuthandiza anthu amene amanyoza malangizo a m’Baibulo kungangokhumudwitsa awiri nonsenu. (Miyambo 9:7) Mwinanso kungakuchititseni kumvetsera zinthu zopusa kapena zotukwana kumene. (Aefeso 5:3) Choncho mukaona kuti simukusangalala ndi nkhani imene mukukambiranayo, limbani mtima n’kumuuza munthu winayo kuti simungathe kumuthandiza kapena kuti simukufuna kukambirana nkhani imeneyo.
Ngati ndinu mnyamata, khalani wosamala mtsikana akafuna kukuululirani zakukhosi kwake, kapena mnyamata akafuna kutero ngati ndinu mtsikana. Baibulo limachenjeza kuti mtima ndi wonyenga. (Yeremiya 17:9) Kugwirizana kwambiri ndi munthu winayo kungakuchititseni kuyamba kumufuna kapena kuchita chiwerewere kumene.
Kuwonjezera apo, musalole kuti mnzanuyo akukakamizeni kulonjeza kuti simuuza aliyense nkhaniyo. Kudzichepetsa kungakuthandizeni kuzindikira kuti munthu amene akukulankhulaniyo angafunikire thandizo lambiri kuposa limene inuyo mungamupatse.—Miyambo 11:2.
Ngati Pakufunika Kuti Ena Athandizepo
Nthawi zambiri, chinthu chabwino kwambiri kuchita ndicho kupeza thandizo inuyo panokha. Mira, amene walembedwa koyambirira uja, anati: “Sindinadziwe mmene ndingamuthandizire mnzanga wa kusukulu uja. Choncho ndinalankhula ndi mkulu wa mu mpingo za nkhaniyo, ndipo anandipatsa malangizo abwino a mmene ndingamuthandizire.” Zoonadi, mu mpingo wachikristu wa Mboni za Yehova muli amuna odziwa zambiri amene angakuthandizeni. (Aefeso 4:11, 12) Mkuluyo anauza Mira kuti alimbikitse mnzakeyo kulankhula ndi makolo ake. Mtsikanayo anatsatira malangizo a Mira. Mira akuti: “Zinthu zayamba kumuyendera bwino. Tsopano akufuna kudziwa zambiri za m’Baibulo.”
Bwanji ngati Mkristu mnzanu wakuululirani zakukhosi? Mwachidziwikire mungafune kuchita zonse zomwe mungathe kuti mumuthandize. (Agalatiya 6:10) Ngati mukuona kuti wayamba kuchita zinthu zosemphana ndi mfundo za makhalidwe abwino za Yehova, musaope ‘kulankhula zoona.’ (Aefeso 4:25) Khalani oona mtima koma musalankhule ngati inuyo simulakwa. Kufunitsitsa kwanu kulankhula chilungamo n’chizindikiro choti ndinudi mnzake weniweni.—Salmo 141:5; Miyambo 27:6.
Mkristu mnzanu akakhala ndi vuto m’pofunikanso kuti mumulimbikitse kupeza thandizo, kaya kwa makolo ake, mkulu, kapena Mkristu wina wokhwima maganizo amene amamulemekeza. Ngati padutsa nthawi yokwanira koma sanalankhulebe ndi aliyense, inuyo mungafunike kukalankhula ndi munthu wina m’malo mwa mnzanuyo. (Yakobo 5:13-15) Mungafunike kulimba mtima kuti muchite zimenezo, koma zimasonyeza kuti mumamukondadi mnzanuyo ndipo mumam’funira zabwino.
N’zoona kuti Yehova sakuyembekezerani kuthetsa mavuto a anthu onse. Koma munthu wina akakuululirani zakukhosi, musamasowe chochita. Muzigwiritsa ntchito zinthu zomwe mwaphunzira monga Mkristu, ndipo muzisonyeza kuti ndinu “bwenzi” lenileni.—Miyambo 17:17.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 15 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 31]
Nthawi zina mungafunike kuuza munthu wina kuti athandize mnzanu amene ali pamavuto