Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Udokotala uli ndi Tsogolo Lotani?

Kodi Udokotala uli ndi Tsogolo Lotani?

Kodi Udokotala uli ndi Tsogolo Lotani?

NTHAWI zambiri mukafunsa anthu za tsogolo la madokotala, amayamba kuganizira za momwe luso la sayansi lapitira patsogolo. Pamabukanso nkhani yoti kaya luso limeneli lidzathandiza madokotala kuti asamachite ntchito zing’onozing’ono zosavuta, m’malo mwake azitha nthawi yawo yambiri ali ndi odwala kuti aziwadziwa bwino. Ndipo n’zodziwikiratu kuti nkhani ya tsogolo la madokotala ikukhudzanso nkhani yokulirapo ya tsogolo la anthu onse. Mabuku awiri a m’Baibulo omwe amanenapo za m’tsogolo amafotokoza mbiri ya Yesu ndi atumwi ake. Mabuku awiri onsewo analembedwa ndi dokotala.

Kodi n’chifukwa chiyani kudziwa maganizo a dokotala pa nkhani zimenezo kuli kofunika? Kodi zikugwirizana bwanji ndi tsogolo la madokotala ndi anthu odwala? N’chifukwa chiyani madokotala ena akusangalala poyembekezera m’tsogolo momwe ntchito yawo sidzafunikanso?

Madokotala ambiri amayang’anitsitsa zinthu mwachidwi. Luka, amene amatchedwa “sing’anga wokondedwa,” ndi amene analemba mabuku awiri a m’Baibulo timanena aja, ndipo anafotokoza mwatsatanetsatane anthu ena odwala amene Yesu ndi atumwi anachiritsa. (Akolose 4:14) Choncho Luka akutithandiza kuganizira mafunso oti: Kodi zinthu zimenezi zinachitikadi? Ngati zinachitikadi, kodi zikutanthauza chiyani kwa madokotala ndi anthu odwala masiku ano?

Kufufuza Ngati Anachiritsidwadi

Luka anali ndi mwayi wofufuza ngati anthuwo anachiritsidwadi mozizwitsa mwa kufunsa anthu amene anaona zimenezo zikuchitika. Kuwonjezera apo, anayenda maulendo ambiri ndi mtumwi Paulo. Zikuoneka kuti Paulo anachiza anthu angapo Luka ali pomwepo. Pamene tikupenda nkhani ziwiri zimene dokotalayu analemba za anthu amene anachiritsidwa, taonani mmene anazilembera mwatsatanetsatane.

Luka anatchula nthawi, tsiku, ndi malo a chochitika chotsatirachi. Iye anati panali pakati pa usiku tsiku loyamba la sabata, ndipo gulu la Akristu linali m’chipinda chapamwamba pa nsanjika yachiwiri ku Trowa, m’chigawo cha Asiya cholamulidwa ndi Aroma. (Machitidwe 20:4-8) Timawerenga mwatsatanetsatane kuti: “Mnyamata dzina lake Utiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikulu; ndipo pakukhala chifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja pachiwiri, ndipo anam’tola wakufa.” Ndiyeno ndi mphamvu ya Mulungu, Paulo anachiza mnyamata wovulalayo ndipo anakhalanso wamoyo. Atatha kudya, “anadza naye mnyamata ali wamoyo, natonthozedwa kwakukulu.”—Machitidwe 20:9-12.

Luka ananenanso kuti anali ndi Paulo ku Melita. Iwo anali kucheza kunyumba kwa Popliyo, “mkulu” wa pa chisumbupo, pamene Paulo anachita chozizwitsa china. Ali kumeneko, munthu wina anadwala ndipo akanafa ndi matenda akewo chifukwa masiku amenewo kunalibe mankhwala amakono. Luka anafotokoza kuti: “Atate wake wa Popliyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, nam’chiritsa. Ndipo patachitika ichi, enanso a m’chisumbu, okhala nazo nthenda, anadza, nachiritsidwa.”—Machitidwe 28:7-9.

Kodi N’chifukwa Chiyani Dokotalayo Anakhulupirira Zimenezo?

Luka analemba nkhani zimenezi m’buku la Machitidwe pamene owerenga ake akanatha kufunsa anthu amene anaona zimenezi zikuchitika ngati zinalidi zoona. Ponena za zimene analemba m’buku la m’Baibulo lokhala ndi dzina lake, Luka analemba kuti: “Ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi . . . kuti udziwitse zoona zake.” (Luka 1:3, 4) Chifukwa cha zimene dokotala ameneyu anaona ndi kufufuza, anakhulupirira kuti zimene Yesu anali kuphunzitsa zinali zoona. Zimene anaphunzitsazo zinaphatikizapo kuchiritsa anthu mozizwitsa. Zimenezi zimatipatsa umboni wokhulupirira ulosi wa m’Baibulo woti Mulungu adzathetsa matenda onse. (Yesaya 35:5, 6) Pokhala dokotala wozolowera kuona anthu akuvutika, Luka ayenera kuti ankasangalala kwambiri akamaganizira nthawi imene ntchito yake sidzafunikanso. Kodi kuganizira za nthawi imeneyo kumakusangalatsani?

N’zosangalatsa kuti zimenezi n’zimene anthu amene amakonda Mulungu angayembekezere m’tsogolo muno, kaya akhale kuti padziko lapansi pano. Baibulo limalonjeza kuti mu Ufumu wa Mulungu, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Madokotala ambiri masiku ano aona kuti pali umboni wokwanira wokhulupirira malonjezo a m’Baibulo.

‘Zinandisangalatsa Kwambiri’

Dokotala winawake wa ku North America, Dr. Jon Schiller, anati: “Mofanana ndi anthu ambiri, ndinayamba ntchito ya udokotala kuti ndithandize anthu amene akuvutika ndi matenda. Chiyembekezo choti kudzakhala dziko lopanda matenda chinandisangalatsa kwambiri. Ndinayamba kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova nditaphunzira ku koleji mbiri ya chitukuko cha mayiko a Azungu. Maphunziro amenewo anasonyeza kuti zipembedzo n’zimene zinayambitsa mavuto ambiri, ndipo ndinaonanso kuti zimagwiritsa ntchito Baibulo mwachinyengo. Choncho ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi Baibulo limati chiyani kwenikweni?’

“Ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, chimene ndinakopeka nacho poyambirira chinali anthu ake ochezeka, amene anali osiyana ndi anzanga ambiri, ndipo zimenezi zinandisangalatsa. Mboni ina inandipempha kuti ibwere kwathu idzakambirane nane za m’Baibulo. Zimene ndinachita nazo chidwi kwambiri n’zoti kaya ndifunse funso lotani, ankandionetsa yankho lake m’Baibulo.

“Pamene ndikukula m’pamenenso ndikuyamikira kwambiri kuti ndine wa Mboni za Yehova. Ukamayamba kumene ntchito ya udokotala uli wachinyamata, umayembekezera kuti udzachita zinthu zinazake zaphindu. Koma nthawi zambiri ndimaona anthu okhumudwa amene amaona kuti palibe chaphindu chilichonse chomwe achita pamoyo wawo. Ndikuganiza kuti ubwino umodzi wokhala wa Mboni za Yehova ndi woti tili ndi chiyembekezo cha m’tsogolo ndiponso cholinga pamoyo wathu. Kaya tikhale madokotala, amakaniko, kapena ogwira ntchito yokolopa m’nyumba, timadziwa kuti zimene tikuchita pa utumiki wathu kwa Mulungu n’zaphindu. Tikuchita zinthu zosangalatsa Yehova, ndipo zimenezo zimatisangalatsa.”

“Kutsatira Mfundo za M’Baibulo Kunathandiza Banja Lathu”

Dr. Krister Renvall ndi dokotala wa ku Finland, ndipo nthawi zonse amasangalala kucheza ndi ana. Iye anati: “Tsiku lina ndinalankhula ndi mtsikana wa zaka 12 amene anali kudwala khansa yoti sachira nayo. Anandipatsa buku lakuti Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kuchokera ku Magwero Otani? * Ndinachita chidwi ndi zimene ankanena zosonyeza chikhulupiriro chake pamene anali kudwala matenda akewo, koma sindinapeze nthawi yowerenga bukulo. Ndipo panthawi imeneyo ndinali wotanganidwa kwambiri ndi ntchito imene ndinali kugwira pa chipatala chinachake ku Helsinki moti banja langa linayamba kusokonekera.

“Koma patapita nthawi mkazi wanga anatenga bukulo pa shelufu n’kuyamba kuliwerenga. Nthawi yomweyo anakhulupirira kuti zomwe anali kuwerengazo zinali zoonadi. Munthu wina wa Mboni za Yehova anabwera kudzaonana naye ndipo anayamba kuphunzira naye Baibulo. Poyamba mkazi wanga ankachita mantha kuti andiuze zimenezi. Koma atandiuza, ndinati, ‘Chilichonse chomwe chingathandize banja lathu n’chabwino.’ Ndinayamba kuchita nawo phunzirolo. Kutsatira mfundo za m’Baibulo kunathandiza banja lathu ndipo kunatithandiza kuyamba kuona moyo mosiyana ndi kale. Ndinasangalala kwambiri nditaphunzira za chiyembekezo cha dziko lopanda matenda. Ndinaganiza kuti m’pomveka kuti Mulungu akhale ndi cholinga choterocho kwa anthu. Posakhalitsa ine ndi mkazi wanga, ndipo kenaka banja lathu lonse, tinabatizidwa. Mtsikana wamng’ono amene analankhula nane koyamba uja anamwalira, koma tingati chikhulupiriro chake chikadali ndi moyo.”

Madokotala amakumana n’zovuta zambiri m’dziko lathu limene likusintha mofulumirali. Choncho zimene amachita podzipereka kuti athandize odwala n’zoyamikirika kwambiri. Koma kusintha kwakukulu kwambiri komwe kudzakhudze anthu kwatsala pang’ono kuchitika. Madokotala ambiri masiku ano amayembekezera ndi mtima wonse tsogolo limene Mawu a Mulungu amalonjeza, lomwe ndi dziko lopanda matenda! (Chivumbulutso 21:1-4) Imeneyi ndi nkhani yabwino yofunika kuifufuza panokha.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 24, 25]

“NDINAZINDIKIRA KUTI MOYO ULI N’CHOLINGA”

“Pamene ndinali kugwira ntchito yothandiza ana a sukulu olumala, ndinaona kuti makolo amene anali a Mboni za Yehova anali osiyana ndi makolo ena. Ankaoneka kuti zinthu zinali kuwayendera bwino ngakhale kuti anali ndi mwana wolumala kusiyana ndi makolo ena omwenso anali ndi ana olumala. Ndinaonanso kuti anali ophunzira bwino kusiyana ndi momwe munthu akanaganizira poona ntchito zomwe anali kugwira. Ndinasirira chikhulupiriro chawo. Chikhulupiriro changa chinali chitawonongeka chifukwa cha anthu amene amaphunzitsa kuti zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka kuchokera ku zinthu zina. Komabe, maphunziro anga a udokotala anandiyambitsa kuganizira kwambiri za moyo.

“Chapanthawi yomweyo, ndinazindikira kuti sindinkadziwa kulera ana anga. Sindinkadziwa kuti kodi ndiziwaletsa chiyani? Ndiziwalimbikitsa chiyani? Kodi ndingawapatse chiyani kuti chikhale cholinga chawo pamoyo? Ngakhale moyo wanga umene unali wopanda tanthauzo. Mpaka ndinapemphera kuti wina andithandize.

“Panthawi imeneyo m’pamene Mboni za Yehova zinandibweretsera magazini yonena za mmene tingawongolere ana ndi kuwadzudzula mwachikondi. Ndinaona kuti mfundo za m’Baibulo zimene magaziniyo inafotokoza zinali zothandiza kwambiri, choncho ndinavomera kuti aziphunzira nane Baibulo. Pamene ndinali kuphunzira chifukwa chimene Yehova analengera zinthu zamoyo ndi chifukwa chimene Yesu anafera, ndinazindikira kuti moyo uli n’cholinga. (Yohane 3:16; Aroma 5:12, 18, 19) Chiphunzitso chakuti zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka kuchokera ku zinthu zina chinapotoza maganizo anga. Ndinamva bwino kwambiri pamene ndinaphunzira kuti matenda ndi imfa sizinali mbali ya cholinga cha Mulungu pachiyambi! Masiku ano ntchito yophunzitsa anthu oona mtima za mmene Mulungu adzachiritsire matenda onse imandisangalatsabe.”

[Zithunzi]

Helena Bouwhuis anali dokotala wa ana asukulu ku Netherlands

[Zithunzi patsamba 23]

Luka, amene anali dokotala komanso wolemba Baibulo, anali kuyenda ndi Paulo pa maulendo ake pamene mtumwiyu anachiritsa bambo a Popliyo ndi kuukitsa Utiko

[Zithunzi patsamba 24]

Dr. Jon Schiller, ku United States

[Zithunzi patsamba 24]

Dr. Krister Renvall, ku Finland