Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupatsa Ana Chisamaliro Chimene Amafunikira

Kupatsa Ana Chisamaliro Chimene Amafunikira

Zimene Baibulo Limanena

Kupatsa Ana Chisamaliro Chimene Amafunikira

KODI Mwana wa Mulungu anali ndi nthawi yocheza ndi ana? Ophunzira ake ena anaganiza kuti analibe. Panthawi ina, anafuna kuletsa ana aang’ono kuti asafike pafupi ndi Yesu. Iye ataona zimenezi anati: “Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse.” Kenaka mwachikondi analola kuti anawo abwere pamene iye anali ndipo analankhula nawo. (Marko 10:13-16) Pamenepa Yesu anasonyeza kuti ankafuna kucheza ndi ana. Kodi makolo masiku ano angatsatire bwanji chitsanzo chake? Angatero mwa kuphunzitsa bwino ana awo ndi kucheza nawo.

N’zoona kuti makolo amene sanyalanyaza udindo wawo amayesetsa kusamalira ana awo ndipo sawazunza. Ndipo tinganene kuti “mwachibadwa” makolo amafuna kulemekeza ndi kuganizira ana awo. Koma Baibulo limachenjeza kuti anthu ambiri m’masiku athu ano adzakhala “opanda chikondi chachibadwidwe.” (2 Timoteo 3:1-3) Ndipo ngakhale anthu amene amayesetsa kusamalira ana awo mwachikondi angaphunzirebe zinthu zina zatsopano zokhudza mmene angalerere bwino ana awo. Choncho mfundo za m’Baibulo zotsatirazi ndi zikumbutso zabwino kwa makolo amene amafunira ana awo zabwino.

Kuphunzitsa Ana Popanda Kuwakwiyitsa

Dr. Robert Coles, mphunzitsi wodziwika bwino ndiponso katswiri wofufuza za maganizo, nthawi ina ananenapo kuti: “Mwana aliyense akamakula amafuna azizindikira chabwino ndi choipa. Ndikuganiza kuti ndi mmene Mulungu anawalengera, kuti amafuna munthu wina aziwathandiza kudziwa chabwino ndi choipa.” Kodi ndani angawathandize kudziwa zabwino ndi zoipa monga momwe amafunira?

Pa Aefeso 6:4, Malemba amalimbikitsa atate kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” Kodi mwaona kuti lemba limeneli limasonyeza kuti ndi udindo wa atate makamaka kuphunzitsa ana awo kukonda Mulungu ndi kulemekeza kwambiri mfundo zake? Mu vesi 1 la Aefeso chaputala 6, mtumwi Paulo anatchula atate ndi amayi omwe pamene anauza ana ‘kumvera akuwabala.’ *

Koma ngati abambo palibe, amayi ayenera kutenga udindo umenewu. Amayi ambiri olera okha ana alera ana awo bwino m’maleredwe ndi m’chilangizo cha Yehova Mulungu. Komabe, ngati mayiyo akwatiwanso, mwamuna wachikristu ndiye ayenera kutsogolera. Amayi ayenera kutsatira zomwe abambo akutsogolerazo pophunzitsa ndi kulangiza ana awo.

Kodi mungalangize kapena kuphunzitsa bwanji ana anu popanda ‘kuwakwiyitsa’? Sikuti pali njira imodzi yokha yophunzitsira ana, chifukwa mwana aliyense ndi wosiyana ndi mnzake. Koma makolo ayenera kuganizira mosamala mmene amalangizira ana awo, ndipo ayenera kuwakonda anawo ndi kuwalemekeza nthawi zonse. N’zochititsa chidwi kuti nkhani yosakwiyitsa ana anuyi inabwerezedwanso m’Malemba pa Akolose 3:21. Pa lemba limenelo atate akulangizidwanso kuti: “Musaputa ana anu, kuti angataye mtima.”

Makolo ena amakalipira ana awo mokuwa. Mosakayikira zimenezi zimaputa anawo. Koma Baibulo limatilimbikitsa kuti: ‘Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu.’ (Aefeso 4:31) Baibulo limanenanso kuti “kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse.”—2 Timoteo 2:24.

Pezani Nthawi Yocheza Nawo

Kupatsa ana chisamaliro chimene amafunikira kumatanthauzanso kuti mukhale okonzeka kupatulapo nthawi imene mumachita zinthu zosangalatsa inuyo kuti musamalire ana anu bwino. Baibulo limati: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.”—Deuteronomo 6:6, 7.

Masiku ano, ndi makolo ochepa chabe amene amakhala tsiku lonse lathunthu ali limodzi ndi ana awo chifukwa choyesayesa kupeza ndalama zokwanira zosamalira mabanja awo. Komabe, lemba la Deuteronomo limeneli limatsindika kuti makolo ayenera kupeza nthawi yocheza ndi ana awo. Kuchita zimenezo kumafuna dongosolo labwino ndiponso kudzimana. Komabe, ana amafunikira chisamaliro choterocho.

Taonani zotsatira za kafukufuku winawake wokhudza achinyamata opitirira 12,000. Ochita kafukufukuwo pomaliza anati: “Ngati wachinyamata akugwirizana kwambiri ndi kholo lake, chimenechi n’chizindikiro chabwino kwambiri chimene chingakutsimikizireni kuti wachinyamatayo adzakhala ndi thanzi labwino ndipo adzatha kupewa khalidwe loipa limene lingamubweretsere mavuto.” Indedi, ana amafuna kwambiri kuti makolo awo azicheza nawo. Mayi wina anafunsapo ana ake kuti, “Pa zinthu zonse, n’chiyani chomwe mungafune kwambiri kukhala nacho?” Ana anayi onse anayankha kuti, “Tingafune nthawi yambiri yocheza ndi amama ndi ababa.”

Choncho, kukwaniritsa udindo wanu monga kholo kumatanthauza kuti muyenera kuonetsetsa kuti ana anu akupeza zimene amafunikira. Zimenezi zikuphatikizapo kuwaphunzitsa anawo zinthu zauzimu ndiponso kuwathandiza kukhala ndi ubwenzi wabwino kwambiri ndi inuyo monga makolo awo. Kumatanthauzanso kuthandiza ana kuti akadzakula adzakhale odziwa zinthu, aulemu, ndiponso oona mtima, okomera mtima anzawo ndi kulemekeza Mlengi wawo. (1 Samueli 2:26) Zoonadi, makolo akamaphunzitsa ndi kulangiza ana awo motsatira zimene Mulungu amanena ndiye kuti akukwanitsa udindo wawo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Pamenepa Paulo anagwiritsa ntchito liwu la Chigiriki lakuti go·neuʹsin, lochokera ku liwu lakuti go·neusʹ, lotanthauza “kholo.” Koma mu vesi 4 anagwiritsa ntchito liwu la Chigiriki lakuti pa·teʹres, lotanthauza “atate.”

[Chithunzi patsamba 13]

Kukalipira mwana mokuwa kungamusokoneze maganizo

[Chithunzi patsamba 13]

Muzicheza ndi ana anu