Kusowa Mtendere Chifukwa cha Moyo Wopanikizika
Kusowa Mtendere Chifukwa cha Moyo Wopanikizika
BUNGWE linalake la ku United States lofalitsa nkhani zokhudza moyo wopanikizika lotchedwa American Institute of Stress, linafalitsa nkhani imene inali ndi mutu wakuti: “Vuto Lalikulu Kwambiri Lokhudza Thanzi la Anthu ku America.” Nkhaniyo inati chinthu chimene chikudwalitsa kwambiri anthu masiku ano si khansa kapena Edzi. Nkhaniyo inati: “Pafupifupi anthu 75 mpaka 90 pa anthu 100 alionse amene amapita kukaonana ndi dokotala amatero chifukwa cha matenda oyamba chifukwa chokhala ndi moyo wopanikizika.”
Si kukokomeza kunena kuti masiku ano anthu akusowa mtendere chifukwa chokhala ndi moyo wopanikizika. Malinga ndi bungwe loimira ogwira ntchito ndi ogula malonda ku United States lotchedwa National Consumers League, “ntchito ndi imene imachititsa achikulire ambiri kukhala ndi moyo wopanikizika ndiponso wamavuto (anthu 39 pa anthu 100 alionse). Chachiwiri ndi mavuto a banja (anthu 30 pa anthu 100 alionse). Zinthu zina zimene zimachititsa anthu kukhala ndi moyo wopanikizika ndi thanzi lawo (anthu 10 pa anthu 100 alionse), kuda nkhawa ndi mmene chuma cha dziko chikuyendera (anthu 9 pa anthu 100 alionse), ndiponso kuda nkhawa ndi kuyambana kwa mayiko ndi uchigawenga (anthu 4 pa anthu 100 alionse).”
Komabe, sikuti ndi anthu a ku United States okha amene ali ndi moyo wopanikizika. Kafukufuku amene anachitika ku Britain mu 2002 anapeza kuti “anthu opitirira 500,000 ku Britain akukhulupirira kuti m’chaka cha 2001 ndi 2002 anali kupanikizika kwambiri ndi ntchito moti inali kuwadwalitsa.” Chifukwa cha “kupanikizika, kuvutika maganizo, ndi kuda nkhawa chifukwa cha ntchito,” pali “masiku mamiliyoni 13 ndi theka amene amawonongeka pa chaka chifukwa choti anthu sanapite ku ntchito ku Britain.”
Zinthu zaipanso chimodzimodzi kumayiko ena a ku Ulaya. Malinga n’zimene linanena bungwe lotchedwa European Agency for Safety and Health at Work, “pali umboni wosonyeza kuti anthu mamiliyoni ambiri ogwira ntchito zosiyanasiyana ku Ulaya konse akupanikizika ndi ntchito.” Pa kafukufuku winawake anapeza kuti pali “anthu pafupifupi 41 miliyoni ogwira ntchito m’mayiko a mu [European Union] amene amapanikizika ndi ntchito chaka chilichonse.”
Nanga bwanji ku Asia? Lipoti limene linatulutsidwa pa msonkhano wina ku Tokyo linati: “Kupanikizika ndi ntchito ndi vuto limene likudetsa nkhawa mayiko ambiri padziko lapansi, osatukuka ndi otukuka omwe.” Lipotilo linati “mayiko angapo kum’mawa kwa Asia, kuphatikizapo China, Korea, ndi Taiwan, atukuka mofulumira ndipo chuma chawo chapita patsogolo. Mayiko amenewa tsopano akuda nkhawa kwambiri ndi mmene anthu apantchito akupanikizikira ndiponso mmene thanzi lawo likuwonongekera.”
Komabe, simukuchita kufunikira kafukufuku winawake kuti mudziwe kuti anthu akukhala moyo wopanikizika. Mosakayikira, mwina inuyonso muli ndi moyo wopanikizika. Kodi kukhala ndi moyo wopanikizika kungapweteke bwanji inuyo ndi okondedwa anu? Kodi mabanja angachite chiyani kuti achepetse kupanikizika? Nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso amenewa.
[Chithunzi patsamba 3]
Anthu ambiri amakhala ndi moyo wopanikizika makamaka chifukwa cha ntchito yawo