Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amayi Akuthana ndi Mavutowa

Amayi Akuthana ndi Mavutowa

Amayi Akuthana ndi Mavutowa

VUTO lalikulu limene amayi ambiri amakumana nalo masiku ano n’loti amafunika kugwira ntchito yolembedwa kuti athandizeko kupeza zosowa za mabanja awo. Kuwonjezera apo, ena a iwo amafunikanso kulera okha ana awo popanda wina wowathandiza pa zifukwa zosiyanasiyana.

Margarita amakhala ku Mexico ndipo akulera yekha ana ake awiri. Iye anati: “Zakhala zondivuta kuti ndiwaphunzitse makhalidwe abwino ndiponso zinthu zauzimu. M’mbuyomu, mwana wanga wachinyamata anabwera kunyumba ataledzera kuchokera ku phwando. Ndinamuuza kuti akadzachitanso zimenezo, sindidzamutsegulira pakhomo. Choncho ulendo wotsatira womwe anachita zimenezo, ndinamutsekera panja, ngakhale kuti mtima wanga unapweteka kwambiri. Koma ubwino wake ndi woti sanachitenso zimenezo.”

Pasanapite nthawi yaitali Margarita anayamba kuphunzira Baibulo, lomwe linamuthandiza kuphunzitsa ana ake makhalidwe abwino. Panopa ana awiri onsewo ndi atumiki a nthawi zonse a Mboni za Yehova.

Amuna Akapita Kunja

Amuna ambiri m’mayiko osauka amapita kukagwira ntchito ku mayiko olemera, ndipo amasiya akazi awo kuti azilera okha ana. Laxmi, mayi wa ku Nepal, anati: “Mwamuna wanga watha zaka seveni tsopano ali kunja. Ana athu sandimvera kwenikweni kusiyana ndi bambo awo. Akanakhala kuti bambo awo amakhalapo nthawi zonse kuti azitsogolera banja lathu, bwenzi zinthu zili bwinoko.”

Ngakhale Laxmi ali ndi mavuto amenewa, zinthu zikumuyendera bwino. Popeza sanaphunzire mokwanira, anakonza zoti aphunzitsi azibwera kunyumba kwawo kudzathandiza ana ake osinkhukirapo pa maphunziro awo a kusukulu. Koma iye amachita chidwi kwambiri ndi maphunziro awo auzimu ndipo amachita nawo phunziro la Baibulo mlungu uliwonse. Amakambirana nawo lemba la m’Baibulo tsiku lililonse ndiponso amapita nawo limodzi ku misonkhano yachikristu nthawi zonse.

Amayi Osaphunzira Mokwanira

M’mayiko ena, vuto lina n’loti azimayi ambiri amakhala osadziwa kulemba ndi kuwerenga. Posonyeza kuipa kokhala mayi wosaphunzira, Aurelia wa ku Mexico, amene ali ndi ana sikisi, anafotokoza kuti: “Mayi anga nthawi zonse ankanena kuti atsikana safunika kuphunzira. Choncho sindinaphunzire kuwerenga ndipo sindinkatha kuthandiza ana anga kuchita homuweki yawo. Zimenezo zinkandipweteka kwambiri. Koma popeza sindinkafuna kuti anawo adzavutike ngati momwe ndinavutikira ineyo, ndinachita khama kuti aphunzire.”

Ngakhale akhale wophunzira pang’ono chabe, mayi akhoza kuthandiza kwambiri ana ake. Mawu oti, “Mukaphunzitsa akazi ndiye kuti mwaphunzitsa anthu odzaphunzitsa amuna” ndi oona. Bishnu wa ku Nepal, mayi wa ana aamuna atatu, kale sankadziwa kulemba ndi kuwerenga. Koma chifukwa choti ankafunitsitsa kuphunzira Baibulo ndi kuphunzitsanso ana ake, anachita khama kuti aphunzire kulemba ndi kuwerenga. Ankaonetsetsa kuti ana ake achita homuweki yawo ndiponso ankapitapita ku masukulu awo kukakambirana ndi aziphunzitsi awo za momwe ana ake akuchitira pa maphunziro awo.

Pa nkhani yophunzitsa ana ake makhalidwe abwino ndi zinthu zauzimu, mwana wamwamuna wa Bishnu dzina lake Silash akufotokoza kuti: “Chinthu chimene chinkandisangalatsa kwambiri pa kaphunzitsidwe ka mayi anga n’choti tikalakwa, ankatisonyeza zitsanzo za m’Baibulo potiwongolera. Njira yophunzitsira imeneyo inali yabwino kwambiri ndipo inandithandiza kumvetsa bwino ndi kugwiritsa ntchito malangizo awo.” Bishnu waphunzitsa bwino ana ake aamuna, ndipo atatu onsewo tsopano ndi anyamata oopa Mulungu.

Antonia wa ku Mexico, mayi amene akulera ana awiri, anati: “Ndinaphunzira sukulu ya pulayimale yokha basi. Tinkakhala kumudzi wakutali ndipo sukulu ya sekondale yapafupi nafe inali kutali kwambiri. Koma ndinkafuna kuti ana anga aphunzire kwambiri kuposa ineyo, choncho ndinkatha nthawi yambiri ndili nawo limodzi. Ndinawaphunzitsa kuwerenga, kulemba, ndi manambala. Mwana wanga wamkazi ankatha kulemba dzina lake ndi kulemba zilembo zonse za mu alifabeti asanayambe sukulu. Mwana wanga wamwamuna ankatha kuwerenga bwinobwino pamene anali kuyamba sukulu ya mkaka.”

Atam’funsa zomwe anachita kuti aphunzitse ana ake makhalidwe abwino ndi zinthu zauzimu, Antonia anafotokoza kuti: “Ndinawaphunzitsa nkhani za m’Baibulo. Mwana wanga wamkazi asanayambe kulankhula, ankatha kufotokoza nkhani za m’Baibulo ndi manja ake. Mwana wanga wamwamuna anawerenga Baibulo koyamba pa msonkhano wathu wachikristu ali ndi zaka zinayi.” Amayi ambiri osaphunzira mokwanira akukwanitsa ntchito yophunzitsa ana awo.

Kukana Kutsatira Miyambo Yoipa

Anthu achitsotsilu a ku Mexico ali ndi mwambo wogulitsa atsikana kuti akwatiwe ali ndi zaka 12 kapena 13. Nthawi zambiri atsikana amagulitsidwa kwa mwamuna wachikulire amene akufuna mkazi wachiwiri kapena wachitatu. Ngati mwamunayo sanakhutitsidwe ndi mtsikanayo, amatha kumubweza kwa makolo ake ndipo makolowo amam’bwezera ndalama zake. Petrona anafunika kulimbana ndi mwambo umenewu ali mwana. Mayi ake anagulitsidwa kuti akwatiwe, anabereka mwana, ndipo anasudzulidwa, ndipo zonsezi zinachitika asanakwanitse zaka 13! Mwana woyambayo anamwalira, ndipo mayi ake a Petrona anagulitsidwanso kawiri zimenezi zitachitika. Ana onse amene anabereka anakwana eyiti.

Petrona sankafuna kukhala ndi moyo woterowo ndipo akufotokoza zomwe anachita. Iye akuti: “Nditamaliza sukulu ya pulayimale, ndinauza mayi anga kuti sindikufuna kukwatiwa koma ndikufuna kupitiriza sukulu. Mayi anga anandiuza kuti sakanatha kuchitapo chilichonse pa nkhani imeneyo ndipo anati ndilankhule ndi bambo anga.”

Bambo anandiuza kuti: “Ndikupezera mwamuna kuti ukwatiwe. Umatha kulankhula Chisipanya. Umatha kuwerenga. Nanga ukufunanso chiyani? Ngati ukufuna kupitiriza sukulu, uzidzilipirira wekha.”

“Choncho ndinayambadi kudzilipirira ndekha,” akufotokoza Petrona. “Ndinkapeta nsalu kuti ndipeze ndalama zodzithandizira.” Mmenemo ndi mmene anapulumukira kuti asagulitsidwe. Petrona atakula, mayi ake anayamba kuphunzira Baibulo ndipo zimenezi zinawathandiza kulimba mtima n’kuyamba kuphunzitsa mfundo zabwino za m’Baibulo kwa azibale ake aang’ono a Petrona. Poona zinthu zomwe zinawachitikira iwowo, mayi a Petrona anatha kuwaphunzitsa kuipa kwa mwambo wogulitsa atsikana ang’onoang’ono kuti akwatiwe.

Mwambo wina wofala pakati pa anthu ambiri ndi woti bambo okha ndi amene amaloledwa kulanga ana aamuna m’banja. Petrona akufotokoza kuti: “Akazi achitsotsilu amaphunzitsidwa kuti ndi otsika poyerekezera ndi amuna. Amuna amakhala opondereza kwambiri. Anyamata ang’onoang’ono amatsanzira abambo awo, ndipo amauza amayi awo kuti: ‘Simungandiuze chochita. Ngati bambo anga sandiuza kuti ndichite zimenezo, sindingakumvereni.’ Choncho amayi sangaphunzitse ana awo aamuna. Koma panopa popeza mayi anga aphunzira Baibulo, atha kuphunzitsa bwinobwino azichimwene anga. Azichimwene angawo analoweza pamtima lemba la Aefeso 6:1, 2 limene limati: ‘Ananu, mverani akukubalani . . . Lemekeza atate wako ndi amako.’”

Mary, mayi wa ku Nigeria nayenso anati: “Kumene ndinakulira, mwambo wathu sulola mayi kuphunzitsa kapena kulanga anyamata. Koma potsatira chitsanzo cha m’Baibulo cha Loisi ndi Yunike, agogo ndi amayi a Timoteo, ndinatsimikiza mtima kuti sindilola miyambo yakwathu kundiletsa kuphunzitsa ana anga.”—2 Timoteo 1:5.

Mwambo wina wofala m’mayiko ena ndi umene amautcha “mdulidwe wa akazi,” umene tsopano nthawi zambiri amautcha kudula maliseche a akazi. Pochita zimenezi amadula pang’ono kapena kudula mbali yaikulu ya maliseche a mtsikana. Kuipa kwa mwambo umenewu kunafalitsidwa poyera ndi Waris Dirie, mtsikana wotchuka wogwira ntchito yojambulitsa zithunzi zotsatsira malonda ndiponso nthumwi yapadera ya bungwe la United Nations Population Fund. Potsatira miyambo ya ku Somalia, iye ali mwana mayi ake anakam’dulitsa maliseche. Malinga ndi lipoti lina, azimayi ndi atsikana pafupifupi eyiti miliyoni mpaka teni miliyoni ku Middle East ndi ku Africa kuno ali pangozi yoti akhoza kudulidwa maliseche. Ngakhale ku United States, atsikana pafupifupi 10,000 ali pangozi imeneyi.

Kodi ndi zikhulupiriro zotani zimene zinayambitsa mwambo umenewu? Ena amaganiza kuti maliseche a akazi ndi oipa ndipo amadetsa atsikana moti sangakwatiwe. Kuwonjezera apo, kudula maliseche amaona ngati kumathandiza kuti mwanayo adzakhalabe namwali mpaka kukwatiwa ndiponso kuti akadzakwatiwa adzakhala wokhulupirika kwa mwamuna wake. Mayi akakana kutsatira mwambo umenewu, mwamuna wake ndi anthu a mderalo angamukwiyire kwambiri.

Koma amayi ambiri azindikira kuti palibe chifukwa chilichonse chabwino, kaya cha chipembedzo, mankhwala, kapena ukhondo chochitira zinthu zopwetekazi. Buku la ku Nigeria lotchedwa Repudiating Repugnant Customs limati amayi ambiri alimba mtima n’kukana kuti ana awo asachitidwe zimenezi.

Zoonadi, amayi padziko lonse lapansi akuteteza ndi kuphunzitsa bwinobwino ana awo ngakhale kuti amakumana ndi mavuto ambiri. Kodi anthu amayamikiradi ntchito imene amayi amagwira?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 13]

“Kafukufuku wosiyanasiyana wasonyeza kuti palibe njira iliyonse yobweretsera chitukuko yomwe imayenda bwino ngati amayi satengapo mbali. Amayi akakhala kuti akutenga nawo mbali kwambiri, zotsatira zake zimaoneka nthawi yomweyo. Mabanja amadya bwino ndipo amakhala athanzi, ndipo ndalama zimene amapeza, kugwiritsa ntchito, ndi kusunga zimawonjezeka. Ndipo zimene zimachitikira mabanjazi zimachitikiranso magulu a anthu, ndipo pakapita nthawi, mayiko athunthu.”—Anatero mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations, Kofi Annan, pa March 8, 2003.

[Mawu a Chithunzi]

UN/DPI photo by Milton Grant

[Bokosi/Zithunzi patsamba 16]

Amayi Athu Anadzipereka Kuti Atithandize

Mnyamata wina wa ku Brazil, dzina lake Juliano anati: “Pamene ndinali ndi zaka zisanu, mayi anga anali pa ntchito yabwino kwambiri. Koma mchemwali wanga atabadwa, anasiya ntchitoyo kuti atilere bwino. Alangizi a kuntchito kwawo anayesera kuwanyengerera kuti asasiye ntchitoyo. Anawauza kuti ana awo akadzakwatira n’kuchoka panyumba, zonse zomwe anawachitira zidzatayika, choncho zomwe anali kufuna kuchitazo zinali zopanda phindu. Koma zimenezo sizinali zoona. Sindidzaiwala chikondi chomwe anatisonyeza.”

[Zithunzi]

Mayi a Juliano ndi ana awo. Kumanzere: Juliano ali ndi zaka zisanu

[Zithunzi patsamba 14]

Bishnu anaphunzira kulemba ndi kuwerenga, kenaka anathandiza ana ake aamuna kukhala ophunzira bwino

[Zithunzi patsamba 15]

Mwana wamwamuna wamng’ono wa Antonia amawerenga Baibulo pa misonkhano yachikristu

[Zithunzi patsamba 15]

Petrona amagwira ntchito mongodzipereka pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico. Mayi ake, amene anakhala a Mboni, akuphunzitsa azibale ake aang’ono

[Chithunzi patsamba 16]

Waris Dirie ndi munthu mmodzi wotchuka amene amanena poyera za kuipa kodula maliseche a akazi

[Mawu a Chithunzi]

Photo by Sean Gallup/ Getty Images