Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Ali Paliponse?

Kodi Mulungu Ali Paliponse?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mulungu Ali Paliponse?

MULUNGU amafotokozedwa molondola kuti ndi wamphamvuyonse ndiponso wodziwa zonse. Koma pofuna kupitiriza kufotokoza ukulu wa Mulungu, anthu ena amanenanso kuti Mulungu amakhala paliponse, ndipo amatha kukhala malo osiyanasiyana nthawi yomweyomweyo.

Malemba amagwirizana ndi zoti Mulungu ndi wamphamvuyonse ndiponso amadziwa zonse. (Genesis 17:1; Ahebri 4:13; Chivumbulutso 11:17) Zoonadi Mulungu ndi wamphamvuyonse ndipo amadziwa zonse m’lingaliro lakuti palibe chimene chingabisike kwa iye. Koma kodi Mulungu ali paliponse, kapena kodi ali ndi malo ake amene amakhala?

Kodi Mulungu Amakhala Kuti?

Mavesi angapo a m’Baibulo amanena kuti, “m’Mwamba” ndiye m’malo “mokhala” Mulungu. (1 Mafumu 8:39, 43, 49; 2 Mbiri 6:33, 39) Komabe, nkhani ina ya m’Baibulo imafotokoza ukulu wa Yehova Mulungu motere: “Kodi n’zoona kuti Mulungu akhala ndi anthu padziko lapansi? Taonani, thambo, inde m’mwambamwamba, sizifikira inu.”—2 Mbiri 6:18.

Baibulo limati, “Mulungu ndiye mzimu.” (Yohane 4:24) Choncho amakhala kumalo a mizimu, kutali ndi thambo timalionali. Baibulo likamanena kuti “m’Mwamba” ndiye mmene Mulungu amakhala, limakhala likunena za kukwezeka kwa malo amene amakhala poyerekezera ndi chilengedwe chomwe ifeyo timapezekamo. Choncho Baibulo limaphunzitsa kuti kumene Mulungu amakhala n’kosiyana kwambiri ndi chilengedwechi koma ndi kumalo kwenikweni ndithu.—Yobu 2:1, 2.

Mulungu Ali ndi Thupi

Yesu anafotokoza za kumene Yehova amakhala pamene anauza ophunzira ake kuti: “M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. . . . Ndipita kukukonzerani inu malo.” (Yohane 14:2) Kodi Yesu anapita kuti? Pomalizira pake analowa “m’Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.” (Ahebri 9:24) Lemba limeneli likutiphunzitsa zinthu ziwiri zofunika kwambiri zokhudza Yehova Mulungu. Choyamba, kuti ali ndi malo ake amene amakhala, ndipo chachiwiri, kuti ali ndi thupi, ndiponso kuti iye si mphamvu chabe imene imakhala paliponse.

N’chifukwa chake Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera chonchi: “Atate wathu wa Kumwamba,” kutanthauza kuti azipemphera kwa Yehova, yemwe ali ndi thupi, ndiponso amene amakhala kumalo kwinakwake, komwe ndi kumwamba kwauzimu. (Mateyu 6:9; 12:50) Zimene Yesu anaphunzitsazi zinali zogwirizana ndi zimene anthu a Mulungu anaphunzitsidwa kwa zaka zoposa 1,500 za momwe ayenera kupempherera. Malemba akale kwambiri omwe Mulungu anauzira ali ndi pemphero lotsatirali: ‘Penyani muli mokhalamo mwanu mopatulika, m’mwamba, ndipo dalitsani anthu anu.’—Deuteronomo 26:15.

Mzimu Woyera wa Mulungu Womwe Umatha Kufika Paliponse

Ngakhale kuti Baibulo nthawi zonse likamanena za Mulungu limasonyeza kuti ali ndi malo ake amene amakhala, nthawi zambiri likamanena za mzimu woyera limasonyeza kuti umatha kupezeka paliponse. Wamasalmo Davide anafunsa kuti: “Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu? Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu?” (Salmo 139:7) Anthu ena asokonezeka ndi mawu ngati amenewa ndipo amaganiza kuti Mulungu amakhala paliponse. Koma tikaonetsetsa mawu a patsogolo ndi pambuyo pa lemba limeneli ndi malemba ena, timatha kuona bwinobwino kuti mzimu woyera wa Yehova, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito, umatha kuchoka ku malo kumene Yehova amakhala n’kufika kulikonse m’chilengedwe chonsechi.

Mofanana ndi dzanja la bambo limene walitambasulira pansi kuti atonthoze ndi kulimbikitsa ana ake, dzanja la Yehova, kapena kuti mzimu woyera, ukhoza kufika ku mbali iliyonse ya dziko la mizimu kapena ya chilengedwe chooneka ndi maso kuti ukwaniritse zolinga za Yehova. Choncho wamasalmo akanatha kunena kuti: “Ndikadzitengera mapiko a mbanda kucha, ndi kukhala kumalekezero a nyanja; kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.”—Salmo 139:9, 10.

Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu

Yehova Mulungu modzichepetsa ndiponso mwachikondi walola kuti iyeyo ndi kumene amakhala zifotokozedwe m’mawu amene anthu angamve, ofotokoza bwino kwambiri mmene iye alili ndi komwe amakhala. Pankhani imeneyi ndi pankhani zina, zimakhala ngati kuti ‘wadzichepetsa kuti apenye zam’mwamba ndi za pa dziko lapansi.’ (Salmo 113:6) Komabe, anthufe sitingathe kumvetsetsa mmene Mulungu alilidi.

Yehova ndi wochititsa chidwi kwambiri, wamphamvu kwambiri, ndi wodabwitsa kwambiri moti sangatheke kufotokozeka m’mawu oti anthufe tingathe kumumvetsa bwinobwino. Choncho ngakhale kuti Malemba akamafotokoza za malo ake okhala a kumwamba amasonyeza kuti ndi malo enieni, anthu sangathe kumvetsa bwinobwino za malo auzimu oterowo.—Salmo 139:6.

Komabe, timayamikira kwambiri kuti timamvetsa pang’ono za mmene Yehova alilidi. Timadziwa kuti iye si mphamvu chabe yomwe imapezeka paliponse m’chilengedwe. M’malo mwake, iye ali ndi thupi ndipo ali ndi malo enieni omwe amakhalako ndiponso ali ndi khalidwe lakelake, lodziwika ndi chikondi ndi chifundo chake. Kudziwa zimenezi kumatithandiza kukhala ndi mwayi wapadera kwambiri womwe munthu aliyense angakhale nawo. Umenewu ndi mwayi wotha kukhala paubwenzi wapadera kwambiri ndiponso kwamoyo wathu wonse ndi Mulungu Wamphamvuyonse, Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse.—Yakobo 4:8.