Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupeza Gwero la Mphamvu Zonse

Kupeza Gwero la Mphamvu Zonse

Kupeza Gwero la Mphamvu Zonse

DZUWA ndiye chiyambi cha mphamvu zonse za padziko lapansi. Asayansi ambiri amakhulupirira kuti malasha ndi mafuta anapangika mitengo ndi zomera zina zomwe zinkapeza mphamvu zawo ku dzuwa zitawolerana. * Madzi amene amakathira m’madamu opanga magetsi amachoka m’nyanja za mchere pokokedwa ndi mphamvu ya dzuwa ndipo amanyamulidwa m’mitambo kudzafika kumtunda. Mphamvu yotentha ya dzuwa ndi imenenso imayambitsa mphepo imene imayendetsa majenereta opanga magetsi kuchokera ku mphepo. Komabe, akuti ndi kambali kochepa chabe ka mphamvu za dzuwa kamene kamafika padziko lapansi.

Ngakhale kuti nyenyezi imene timaitcha dzuwa ndi yamphamvu kwambiri, ndi imodzi yokha pa nyenyezi mabiliyoni ambiri zokhala ndi mphamvu zoterozo m’chilengedwe chonsechi. Kodi mphamvu zonsezi zinachokera kuti? Ponena za nyenyezi, wolemba Baibulo wina dzina lake Yesaya anati: “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziwerenga; azitcha zonse mayina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.”—Yesaya 40:26.

Tikamaganizira mphamvu zazikulu za nyenyezi timagoma, makamaka tikaganizira za Mlengi wa zinthu zonsezi. Komabe, Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Zoonadi, anthu amene amafunafuna Mlengi wa dziko lapansili ndi wa mphamvu zake zosiyanasiyana zambirimbiri, amenenso anatipatsa moyo, akhoza kumupeza.—Genesis 2:7; Salmo 36:9.

Anthu ena akaona dziko lapansili ndi zinthu zake zikuwonongedwa ndi kusagawidwa mwachilungamo, amavutika kukhulupirira kuti Mulungu ali ndi chidwi ndi dzikoli ndi anthu ake. Koma Baibulo limatilimbikitsa kuti zinthu zatsala pang’ono kusintha. Limati padzakhala kusintha kwakukulu pa mmene zinthu za m’dzikoli zimagawidwira ndi mmene dzikoli limalamulidwira. (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) Yehova Mulungu adzakhazikitsa boma limodzi lokha kuti lizilamulira dziko lonseli kuchokera kumwamba, lolamulidwa ndi Mwana wake, Kristu Yesu. Akadzatero ndiye kuti aliyense amene ali ndi moyo adzatha kugwiritsa nawo ntchito mokwanira zinthu zambirimbiri zimene zimapezeka padzikoli. (Mika 4:2-4) Yehova Mulungu adzawononganso “iwo akuwononga dziko,” kutanthauza anthu amene amawononga dzikoli, kaya mwauzimu kapena amene amawononga zachilengedwe.—Chivumbulutso 11:18.

Panthawi imeneyo, lonjezo lomwe linalembedwa pa Yesaya 40:29-31 lidzakwaniritsidwa mwauzimu ndiponso mwakuthupi. Lemba limenelo limati: “Iye alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu. Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu: koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.” Inunso mukhoza kuphunzira zambiri za Mulungu, amene ali Gwero la mphamvu zonse. Mukhozanso kuphunzira za mmene mavuto a kuperewera kwa mphamvu padziko lapansili adzathere. Mungathe kutero mutapatula nthawi kuti muphunzire Baibulo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Onani bokosi lakuti “Kodi Mafuta Anapangika Bwanji?” mu Galamukani! ya November 8, 2003.