‘Magazini Yochokera kwa Mulungu’
‘Magazini Yochokera kwa Mulungu’
MWAMUNA wina yemwe akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ku Nigeria anapita ku msonkhano womwe unakonzedwa ndi bungwe loona za amayi ndi ana lotchedwa Inter-African Committee on Women and Children. Popita ku msonkhanoko anatenga magazini awiri aposachedwapa a Galamukani!
Tsiku loyamba la msonkhanowo, mwamunayo anazindikira kuti wokamba nkhaniyo anali kugwiritsa ntchito mfundo za m’magazini imodzi mwa magazini omwe anabweretsa aja. Inali ndi nkhani zofotokoza za kukoma kwa moyo. (November 8, 2001, masamba 20 mpaka 29) Choncho iye anatulutsa magaziniyo n’kuyamba kutsatira wokamba nkhaniyo.
Pamapeto pa tsikulo, loya wina amene anali kudzakamba nkhani yake tsiku lotsatira anaona chikuto cha Galamukani! ina ija, yomwe wophunzira Baibuloyo anabweretsa, ya mutu wakuti “Kuthandiza Akazi Omenyedwa ndi Amuna Awo.” Loyayo anaibwereka. Usiku umenewo, anataya mfundo zomwe anali atakonzekera n’kukonza mfundo zina za nkhani yakeyo pogwiritsa ntchito nkhani za mu Galamukani! ija. Tsiku lotsatiralo, pamene loya uja anali kukamba nkhani yake, mzimayi wina amene anakhala mu mzere womwe wophunzira Baibulo uja anakhala anatulutsa magazini yake ya Galamukani! n’kuyamba kumatsatira wokamba nkhaniyo.
Wophunzira Baibuloyo anathanso kulankhulapo mfundo zaphindu pamsonkhanowo chifukwa chowerenga nkhani za mu Galamukani! Iye anati, ‘Sindikukayikira kuti magazini imeneyi ndi yochokera kwa Mulungu.’
Kodi mungakonde kuti munthu wina azikubweretserani magazini imeneyi kunyumba kwanu nthawi zonse? Bwanji osafunsa wa Mboni za Yehova aliyense kuti akuthandizeni?