Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mavuto Amene Amayi Amakumana Nawo

Mavuto Amene Amayi Amakumana Nawo

Mavuto Amene Amayi Amakumana Nawo

“Ntchito zofunika kwambiri pa moyo wa anthu ndi ntchito zapakhomo. . . . Ngati mayi atati asagwire ntchito yake, sipangakhale mbadwo wotsatira, kapena ukhoza kukhalapo koma ukhoza kukhala woipa kwambiri moti zingakhale bwino utati usakhalepo n’komwe.”—Anatero Theodore Roosevelt, pulezidenti wa nambala 26 wa ku United States.

N’ZACHIONEKERE kuti amayi ndi ofunika kwambiri pa moyo wa anthu. Iwo amagwira ntchito zosiyanasiyana, osati kubereka ana kokha. Ponena za udindo wa amayi m’madera ambiri a padziko lapansili masiku ano, wolemba wina anati: “Mayi ndi amene ali ndi udindo waukulu woyang’anira thanzi la mwana aliyense, maphunziro ake, nzeru zake, khalidwe lake, ndi mtima wake.”

Ntchito imodzi mwa ntchito zambiri za amayi ndi yophunzitsa ana awo. Mwana amaphunzira mawu ake oyambirira ndi kalankhulidwe kake kwa mayi ake. Mayi nthawi zambiri amakhala nthawi yambiri tsiku lililonse ali ndi ana ake kusiyana ndi mwamuna wake, choncho mayiyo ndi amene angakhale mphunzitsi ndiponso mlangizi wawo wamkulu. Choncho mwambi wa ku Mexico wakuti “Maphunziro timachita kuyamwira” umalemekeza udindo wofunika kwambiri umenewu wa amayi.

Mlengi wathu, Yehova Mulungu, nayenso amalemekeza amayi. Ndipo lamulo limodzi la Malamulo Khumi, olembedwa pa miyala ndi “chala cha Mulungu,” limalimbikitsa ana kuti: ‘Uzilemekeza atate wako ndi amako.’ (Eksodo 20:12; 31:18; Deuteronomo 9:10) Kuwonjezera apo, m’Baibulo muli mwambi umene umanena za “chilangizo cha amako.” (Miyambo 1:8) Kufunika kophunzitsa ana pa zaka zitatu zoyambirira za moyo wawo, pamene ambiri mwa iwo amakhala akusamalidwa ndi mayi awo nthawi zambiri, tsopano kwadziwika kwambiri.

Kodi Ena Mwa Mavutowa Ndi Otani?

Kwa amayi ambiri, vuto limodzi limene limawalepheretsa kuphunzitsa bwino ana awo pa zaka zoyambirira za moyo wawo, yomwe ili nthawi imene mwana amaphunzira zinthu zochuluka kwambiri, ndi vuto loti amafunika kugwira ntchito yolembedwa kuti athandize kupeza zosowa za banja lawo. A bungwe la United Nations anapeza kuti m’mayiko ambiri otukuka, azimayi opitirira theka la azimayi onse amene ali ndi ana a zaka zosakwana zitatu ali pantchito yolembedwa.

Kuwonjezera apo, nthawi zambiri amayi amafunika kulera okha ana awo chifukwa choti amuna awo anachoka panyumba kukafuna ntchito mumzinda wina kapena kudziko lina. Mwachitsanzo, kumadera ena a m’dziko la Armenia, akuti pafupifupi mwamuna mmodzi pa amuna atatu alionse a m’dzikomo anapita kunja kukafuna ntchito. Amayi ena amapezeka kuti akulera okha ana awo chifukwa choti amuna awo anawathawa kapena anamwalira.

M’mayiko ena, vuto lina limene amayi ambiri amakumana nalo n’loti amakhala osaphunzira. Bungwe la United Nations loona za chuma ndi chikhalidwe cha anthu lotchedwa Department of Economic and Social Affairs linati anthu osadziwa kulemba ndi kuwerenga padziko lonse lapansi alipo 876 miliyoni. Pa anthu amenewa, pafupifupi anthu awiri pa anthu atatu alionse ndi akazi. Ndipo lipoti lina la bungwe la UNESCO linati ku Africa kuno, kumayiko a Aluya, ndi kumayiko a kum’mawa ndi kummwera kwa Asia, akazi opitirira 60 pa akazi 100 alionse sadziwa kulemba ndi kuwerenga. Kuwonjezera apo, amuna ambiri amakhulupirira kuti kuphunzitsa akazi n’kosafunika kwenikweni ndiponso kuti kumawachititsa kuti asamagwire bwino ntchito yawo yobereka ana.

Magazini yotchedwa Outlook inati m’boma linalake la m’chigawo cha Kerala ku India, amuna safuna kukwatira mkazi wophunzira. Kudera limeneli, atsikana ambiri akamafika zaka 15 amakhala atabereka kale ana. M’dziko la kufupi ndi India la Pakistan, anthu amaona kuti ndi bwino kuphunzitsa ana aamuna, osati aakazi. Kuphunzitsa ana aamuna kumawathandiza kuti adzapeze ntchito zabwino kuti adzathe kusamalira makolo awo akadzakalamba. Koma malinga ndi zomwe linanena buku lotchedwa Women’s Education in Developing Countries, “makolo safuna kuwononga ndalama kuphunzitsa ana awo aakazi chifukwa sayembekezera kuti atsikanawo azidzapeza ndalama zoti akhoza kuthandizira mabanja awo.”

Vuto linanso limene amayi amakumana nalo n’lolimbana ndi miyambo ya kwawo. Mwachitsanzo, m’mayiko ena mayi amafunika kugwirizana ndi miyambo monga kugulitsa atsikana ang’onoang’ono kuti akwatiwe ndiponso kudula maliseche a akazi. Kumadera ena amaonanso kuti n’kulakwa kuti mayi aziphunzitsa ndi kulanga ana ake aamuna. Kodi mayi amafunika kutsatira miyambo yoteroyo n’kusiyira anthu ena ntchito yophunzitsa ana ake aamuna?

Mu nkhani zotsatirazi, tiona zimene amayi ena akuchita kuti athane ndi mavuto ngati amenewa. Nkhani zimenezi zitithandizanso kumvetsa bwino udindo umene amayi ali nawo ndi kuwayamikira kwambiri. Zitithandizanso kuona moyenera udindo wa amayi wophunzitsa ana awo.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 12]

“Mayi ndi wofunika kwambiri pa nkhani yolimbikitsa mwana kuganiza, ndiponso kumulimbikitsa kukhala ndi chidwi ndi zinthu zosiyanasiyana ndiponso kukhala ndi luso lotulukira zinthu zatsopano.”—Mawu amenewa ananenedwa pa msonkhano woona za ufulu wa ana wotchedwa Regional Summit on Children’s Rights, ku Burkina Faso, mu 1997.

[Zithunzi patsamba 11]

Amayi amathandiza kwambiri mwana aliyense pa thanzi lake, maphunziro ake, khalidwe lake, ndi maganizo ake