Mukuitanidwa ku Msonkhano Wofunika Kwambiri pa Chaka
Mukuitanidwa ku Msonkhano Wofunika Kwambiri pa Chaka
Lachinayi pa March 24, 2005, kudzakhala mwambo wosafunika kuuphonya. Limeneli ndi tsiku limene Mboni za Yehova zopitirira sikisi miliyoni padziko lonse lapansi limodzi ndi anzawo ambirimbiri adzasonkhane kumadera kwawo kukumbukira mgonero womaliza umene Yesu anadya ndi otsatira ake. Potsatira malangizo a Yesu, pa msonkhano uliwonse padzakhala mkate wopanda chotupitsa ndi vinyo wofiira, ndipo adzafotokoza tanthauzo la mwambo umenewu.—Marko 14:22-24.
Anthu ambiri mwambo umenewu amautcha Mgonero wa Ambuye. Mboni za Yehova zimautcha Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Ndi chikumbutso chofunika kwambiri cha nsembe imene Yesu Kristu anaperekera anthu ochimwa powafera. (Yohane 3:16; 1 Yohane 2:2) Atatha kudya mgonero womalizawu, Yesu anagwidwa ndipo kenaka anafera pamtengo ngati kuti anali chigawenga.—Yohane 19:17, 18.
Tidzakulandirani ndi manja awiri ku msonkhano wapadera umenewu, umene uli msonkhano wofunika kwambiri pa chaka kwa Mboni za Yehova. Kafunseni ku Nyumba ya Ufumu ya kwanu za nthawi yeniyeni ndi malo kumene mwambo umenewu udzachitikire m’dera lanulo.