Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Mphamvu za Magetsi Zili Zofunika Kwambiri pa Moyo Wathu?

N’chifukwa Chiyani Mphamvu za Magetsi Zili Zofunika Kwambiri pa Moyo Wathu?

N’chifukwa Chiyani Mphamvu za Magetsi Zili Zofunika Kwambiri pa Moyo Wathu?

MICAH anabadwa mu August m’chaka cha 2003. Galimoto imene inatenga mayi ake n’kuthamangira nawo ku chipatala inali yoyendera petulo. Magetsi amene ankaunika m’chipatala chimene anabadwiramo anali ochokera ku malo opanga magetsi pogwiritsa ntchito malasha. Makina otenthetsera m’nyumba amene anatenthetsa chipinda chomwe anabadwiramo anali oyendera gasi. Ngati njira iliyonse mwa njira zodziwika bwino zopangira mphamvu za magetsi zimenezi ikanati isagwire ntchito, moyo wa Micah ukanakhala pangozi.

Dziko lamakonoli, lomwe Micah anabadwiramo, limadalira kwambiri njira zosiyanasiyana zopangira magetsi pa ntchito zake zambiri. Tsiku lililonse timagwiritsa ntchito mafuta, malasha, kapena gasi m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, timagwiritsa ntchito zinthu zimenezi kuti tiyende kupita kuntchito, kuti tiphike zakudya zathu, kapena kuti tiunikire, titenthetse, ndiponso tiziziritse m’nyumba zathu. Bungwe loona za mphamvu zachilengedwe lotchedwa World Resources Institute linati mafuta, malasha, ndi gasi ndi zimene zimagwiritsidwa ntchito “kwambiri ndi makampani popanga zinthu zosiyanasiyana zamalonda padziko lonse lapansi.” Lipoti limene bungweli linafalitsa m’chaka cha 2000 linati: “Popanga mphamvu za magetsi, mafuta ndi amene amagwiritsidwa ntchito kwambiri padziko lonse lapansi, ndipo chinthu chachiwiri chimene chimagwiritsidwa ntchito kwambiri ndi malasha, pamene chachitatu ndi gasi.” *

Magazini yotchedwa Bioscience inati: “Munthu wa ku United States aliyense amagwiritsa ntchito . . . malita pafupifupi 8,000 a mafuta chaka chilichonse pochita zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo kuyendera, kuphikira, kutenthetsa m’nyumba, kuziziritsa m’nyumba, ndi kuziziritsa zinthu zosiyanasiyana.” Ku Australia, China, Poland, ndi ku South Africa, magetsi ambiri amene amagwiritsidwa ntchito kumeneko amapangidwa ndi majenereta oyendera malasha. Ku India amadalira kwambiri malasha popanga magetsi awo, pamene ku United States ndi ku Germany amagwiritsa ntchito malasha popanga magetsi opitirira theka la magetsi awo onse.

Jeremiah Creedon analemba mu nkhani yotchedwa “Mmene Moyo Ungakhalire Ngati Mafuta Atatha,” yomwe inatuluka m’magazini yotchedwa Utne Reader, kuti: “Anthu ambiri sadziwa kuti masiku ano zakudya zathu zimadalira kwambiri mafuta kuti zipangidwe. Mafuta ndi gasi n’zofunika kwambiri pa ulimi wamakono, kuyambira pa kupanga feteleza mpaka pa kunyamula zokolola kupita nazo kwina.” Koma kodi njira zosiyanasiyana zopangira mphamvu za magetsi zimenezi, zomwe dziko lamakonoli limadalira kwambiri, n’zodalirika motani? Kodi pali njira zina zopangira magetsi popanda kuwononga chilengedwe?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Kuti mumve tsatanetsatane wa mbiri yokumba mafuta, onani Galamukani! ya November 8, 2003, masamba 3-12.