Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndine Wokonzeka Kuthandiza Ena

Ndine Wokonzeka Kuthandiza Ena

Ndine Wokonzeka Kuthandiza Ena

YOSIMBIDWA NDI CLAIRE VAVY

CHILUMBA cha Madagascar, chomwe chili pa mtunda wa makilomita pafupifupi 400 kuchokera ku dziko la kum’mawa kwa Africa la Mozambique, chili ndi mapiri ambiri ndi nkhalango zowirira. Ine ndinabadwa kum’mawa kwa chilumbachi m’mudzi waung’ono wotchedwa Betoko II. M’chaka cha 1987, pamene ndinali ndi zaka 15, ndinasamukira ku tauni ya kugombe la nyanja ya Manahoro kuti ndizikaphunzira sukulu kumeneko.

Ku Manahoro ndinkakhala ndi mchimwene wanga wamkulu Celestin, amene anali atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Patatha zaka ziwiri ndinakhala Mboni. Ndinafunitsitsa kutumikira Yehova Mulungu ndi mtima wanga wonse.

Kuyesetsa Kukwanitsa Zolinga Zanga

Cholinga changa chimodzi choyambirira chinali choti ndithandize anthu a m’banja mwathu kumudzi kwathu ku Betoko II, ndipo ndinkapemphera nthawi zonse kwa Yehova za nkhani imeneyi. Koma ndinkapita kumudzi kwathuko patchuthi pokha. Ndinkayenda ulendo wovuta kwambiri wa makilomita 100. Makilomita 40 oyambirirawo ndinkatha kuyenda pa galimoto, koma makilomita 60 otsalawo kanjira kake kanali kakang’ono kodutsa m’mapiri ndipo kuyenda kwake kunali kwapansi basi.

Ndinkakwera mitunda yambiri ya m’mapiri, ndipo njirayi m’malo mwina inali yopapatiza kwambiri moti m’lifupi mwake munali mofanana ndi kutalika kwa phazi langa. Ndikayamba kuyenda m’mawa kwambiri n’kuyenda mpaka madzulo, nthawi zambiri ndinkayenda ulendo wa makilomita 40. Ndinkanyamula katundu wambiri wolemera makilogalamu opitirira 15. Wina ndinkamusenza pamutu, wina kumuberekera kumbuyo, ndipo wotsalayo ndinkamunyamula m’manja. Nthawi zambiri ndinkanyamula mabuku ofotokoza za m’Baibulo, amene ndinkapatsa azibale anga ndi anthu ena achidwi. Anthu amene ankandiona m’njiramo anandipatsa dzina loti “wonyamula katundu wambiri uja.”

Poyamba anthu a m’banja mwanga sanafune kundimvetsera ndikamawauza za chikhulupiriro changa chatsopanocho ngakhale kuti ndinali wofunitsitsa kuwaphunzitsa. Koma pasanapite nthawi yaitali anasintha ndipo ankafunsa mafunso ambiri moti nthawi zina tinkagona 2 koloko m’mawa.

Ulendo Wosaiwalika

Pa December 24, 1990, ndinafika kumudzi kwathu ku Betoko II patchuthi. Anthu a m’banja mwanga anasangalala kundiona, poganiza kuti ndabwera kudzakondwerera nawo limodzi Khirisimasi. Koma anakhumudwa nditawafotokozera chifukwa chomwe sindikanakondwerera nawo limodzi Khirisimasiyo. Ankachita manyazi kuti auze anthu ena a m’mudzimo nkhani imeneyi, chifukwa anthu ake anali ogwirizana kwambiri. Choncho ndinaona kuti ndifunika kuwafotokozera ndekha anthu a m’mudzimo. Koma kodi ndikanachita bwanji zimenezi?

Sindinadziwe chochita, makamaka chifukwa choti ndinali wamng’ono kwambiri. Ndinaganiza zoti mwina zingakhale bwino nditafotokozera zikhulupiriro zanga anthu a m’mudzimo akasonkhana kutchalitchi tsiku lotsatira. Ndinapemphera pemphero lalitali lochokera pansi pa mtima kwa Yehova, kumupempha kuti anditsogolere. Kenaka ndinafunsa mchimwene wanga wamkulu Paul, amene anali mphunzitsi wa kutchalitchiko, kuti, “Kodi mukuganiza kuti zingakhale bwino nditafotokozera anthu amene abwere kutchalitchi mawa chifukwa chomwe sindikondwerera Khirisimasi?” Anafunsa kaye anthu ena, kenaka anavomera.

Tsiku lotsatira anandiitana kuti ndipite ku tchalitchiko mapemphero atatha. Ndinapempheranso kwa Yehova ndipo ndinanyamula mabuku osiyanasiyana ofotokoza za m’Baibulo n’kupita ku tchalitchiko. Nditatha kulankhula mawu a malonje, ndinathokoza anthu onsewo chifukwa cha zomwe anachita pondithandiza kuti ndizilemekeza kwambiri Baibulo. Ndinafotokoza kuti nditapita ku tauni ndinapitirizabe kuphunzira Baibulo. Ndinawauza kuti ndinaphunzira mfundo zambiri za m’Baibulo zomwe sitinaphunzitsidwe m’mbuyomu.

Ndinagwiritsa ntchito mpata umenewu kufotokoza chiyembekezo cha m’Baibulo choti tidzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. (Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4) Ndinafotokozanso chifukwa chomwe anthu okhulupirika ochepa adzatengedwe padziko lapansili kupita kumwamba. (Yohane 14:2, 3; Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3) Ndinawauzanso zimene Baibulo limaphunzitsa zoti anthu akufa sadziwa chilichonse ndipo amakhala ngati ali m’tulo choncho sangakhale akuvutika. (Mlaliki 9:5, 10; Yohane 11:11-14, 38-44) Ndinawasonyezanso kuti Akristu oyambirira sankakondwerera Khirisimasi ndiponso kuti chikondwerero chimenechi chinachokera ku chikunja.

Nditamaliza kulankhula, anthu ambiri amene anali pamenepo anavomereza kuti ndimanenadi zoona. Ena mpaka anafunsa mafunso ena owonjezereka. Kenaka ndinawaonetsa mabuku amene ndinabweretsa aja n’kuwafotokozera kuti amenewa anali mabuku othandiza pophunzira Baibulo ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Ndinawauza kuti ndinali wokonzeka kuthandiza aliyense amene angafune kuphunzira Baibulo. Ambiri analandira mabuku ofotokoza Baibulowo.

Kupeza Zimene Sindinayembekezere

Mzimayi wina amene ndinali ndisanakumanepo naye anabwera kwa ine n’kundiuza kuti: “Mng’ono wanga, amene amakhala m’mudzi wina, ndi wa chipembedzo chanu.” Ndinadabwa, ndipo ndinamufunsa kuti, “Amakhala mudzi uti?”

Iye anayankha kuti, “Ku Andranomafana.” Mudzi umenewu uli pa mtunda wa makilomita pafupifupi 30 kuchokera ku Betoko II.

Ndinauza mzimayiyo kuti mng’ono wakeyo mwina ali mpingo wina chifukwa a Mboni onse m’deralo amadziwana. Koma mzimayiyo analimbikirabe, ndipo anati mng’ono wakeyo anamuphunzitsa zinthu zofanana ndi zimene ndinafotokoza m’tchalitchi zija. Ndinamuuza kuti andiuze dzina la mng’ono wakeyo ndi kumene amakhala, chifukwa ndinali wokonzeka kunyamuka nthawi yomweyo kupita kumeneko. Koma amayi anandiuza kuti ndidikire kaye tsiku limodzi kapena masiku angapo, chifukwa ulendo wake unali wovuta, ndiponso wapansi. Patatha masiku awiri ine ndi mchimwene wanga Charles tinanyamuka kupita ku Andranomafana.

Titangofika tinafunsa anthu ena a m’mudzimo kuti, “Kodi kuno kuli Mboni za Yehova?” Ndinakhumudwa pamene anayankha kuti, “M’mudzi uno muli matchalitchi a Katolika, Pentekoste, ndi Indipendenti basi.”

Kenaka mzimayi wina analankhulapo, ndipo anati, “Ngati mukufuna Mboni za Yehova, ndiye kuti mwina mukufuna Marceline ndi banja lake.” Limenelo linali dzina lomwe ndinapatsidwa lija!

Munthu wina anapita kukaitana Marceline. Anabwera pasanapite nthawi yaitali koma ankaoneka wamantha. Anthu onse a m’mudzimo anabwera n’kutizungulira, poti ankaganiza kuti tinali anthu ogwira ntchito ku boma ndipo tabwera kudzamufunsa zinazake. Kenaka ndinadzazindikira kuti Marceline ndi banja lake anazunzidwa m’mudzimo chifukwa chokhala ‘m’chipembedzo chachilendo.’

Marceline anatitengera pambali kuchoka pamene panali gulu la anthu paja, pomwe tikanatha kulankhula momasuka. Nditamufunsa ngati anali wa Mboni za Yehova, anavomera. Atatero, anapita kukatenga buku la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, limene Mboni za Yehova zinkagwiritsa ntchito kale pophunzitsa anthu Baibulo, limodzi ndi magazini akale a Nsanja ya Olonda. Mabuku onsewa anali akale ndiponso ong’ambika. Ndinamufunsa kuti, “Lamlungu lapitali munaphunzira magazini iti?”

Iye anayankha kuti, “Magazini amene tili nawo ndi okhawa basi, ndipo timawaphunzira mobwerezabwereza.” Atatero m’pamene ndinamuuza Marceline kuti inenso ndine Mboni. Anasangalala kwambiri! Nditamuuza kuti ndimafuna kukumana ndi mwamuna amene amachititsa misonkhano yawo, anandifotokozera kuti amakhala kudera lina, kutali ndi kumene tinaliko.

Zinthu Zinanso Zosangalatsa

Tsiku lotsatira ine ndi Marceline tinanyamuka kupita kunyumba kwa mwamuna uja. Titafika, anadabwa komanso anasangalala kutiona. Tinamva kuti analidi wa Mboni amene anabwera kuchokera ku tauni ya Toamasina ya kugombe la nyanja, yomwe inali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 200 kumpoto chakum’mawa. Iye ndi banja lake anakakamizika kubwera kuno zaka zingapo m’mbuyomu, ntchito itamuthera mwadzidzidzi. Atabwera, anayamba kulalikira, kuchititsa maphunziro a Baibulo, ndi kuchititsa misonkhano.

Mboniyo ndi banja lake anasangalala kwambiri ataona magazini atsopano a Nsanja ya Olonda omwe ndinabweretsa. Ndinawaonetsanso buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, limene tinali kugwiritsa ntchito panthawi imeneyo pochititsa maphunziro a Baibulo. Aka kanali koyamba kuti alione. Lamlungu lotsatira ndinapitanso ku Andranomafana kukasonkhana nawo limodzi. Ndinawalimbikitsa kuti alembere ofesi ya nthambi ya Mboni ku likulu la dziko lathu ku Antananarivo, chifukwa anthu a ku nthambiwo sankadziwa za kagulu kameneka.

Kuyambira mu January 1991, ndinkapita ku Andranomafana kuchokera ku Mahanoro mwezi uliwonse, ndipo ndinkawabweretsera magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi mabuku ena. Unali ulendo wa makilomita pafupifupi 130, ndipo kwa makilomita opitirira 88 ndinkayenda pansi. Ndinkakwera ndi kutsika mapiri a miyala, kudutsa m’nkhalango zowirira, ndipo kukagwa mvula, ndinkayenda m’matope akhathikhathi oterera kwambiri.

Katundu amene ndinkanyamula anayamba kulemera kwambiri chifukwa choti anthu amene ankafuna mabuku ndi magazini anayamba kuchuluka. Koma pamapeto pa ulendo uliwonse, ndinkakhala wosangalala kwambiri moti ndinkaiwala za kutopa ndi kupweteka kwa thupi langa. Ndinkasangalala kwambiri kuona anthuwo akukondwera kwambiri kulandira buku lililonse latsopano ndi kuona momwe ankasangalalira ndi choonadi cha m’Baibulo.

Kuyamba Utumiki wa Nthawi Zonse

Pa September 1, 1992, ndinaikidwa kukhala mpainiya, dzina limene Mboni zimatcha anthu ochita utumiki wa nthawi zonse. Ndinkachita upainiya ku Mahanoro koma ndinkalemberanabe makalata ndi azibale anga ku Betoko II. Patapita nthawi anayamba kuphunzira nane Baibulo kudzera m’makalata, ndipo anandipempha ngati ndingapite kumudzi kukawathandiza. Ndinali wokonzeka kuchita zimenezo, koma choyamba ndinafuna kuona ngati anatsimikizadi zoti akufuna kuphunzira Baibulo ndi kupita patsogolo mwauzimu. Choncho kwa kanthawi, ndinakhalabe ku Mahanoro n’kumachita upainiya.

Chakumapeto kwa 1993, ndinali ndi mwayi wophunzira nawo sukulu ya milungu iwiri ya apainiya ku Antananarivo. Kenaka anandipempha kuti ndilembetse upainiya wapadera, zomwe zikanatanthauza kuti akanatha kunditumiza kulikonse m’dzikomo. Koma sindinafune kaye kuyamba kuchita upainiya wapadera panthawi imeneyo, chifukwa choyamba ndimafuna kuthandiza azibale anga ku Betoko II, amene ankakhala kutali ndi mpingo uliwonse. Choncho ndinabwerera ku Mahanoro kukapitiriza kuchita upainiya.

Kenaka, woyang’anira woyendayenda wa Mboni za Yehova atabwera kudzatiyendera, ndinamufunsa ngati ndingathe kubwerera kumudzi kwathu kukathandiza abale anga. Panthawi imeneyo n’kuti ku Andranomafana kutapangidwa mpingo, choncho anandiuza kuti zingakhale bwino nditapita kumeneko kuti ndikakhale limodzi ndi mpingowo n’kumakalalikira m’dera la Betoko II. Ndinayamba kuchita zimenezi pa September 1, 1994. Mwezi womwewo, mchimwene wanga Paul, amene anali mphunzitsi wa ku tchalitchi, anapita nane limodzi ku msonkhano wachigawo. Pasanapite nthawi yaitali anthu 30 anayamba kulalikira ku Andranomafana, ndipo Lamlungu anthu pafupifupi 65 ankabwera pa misonkhano yathu.

Sindinasiye Kuyenda

Patapita nthawi yochepa nditabwerera ku Betoko II, achimwene ndi achemwali anga anayi anavomerezedwa kuyamba kulalikira limodzi ndi Mboni za Yehova, ndipo pasanapite nthawi yaitali anabatizidwa. Nditabwerera ku Betoko II, nthawi zambiri ndinkapita ku Anosibe An’ala kukatenga mabuku, womwe unali ulendo wa makilomita pafupifupi 50. Ngakhale unali ulendo wotopetsa, chimwemwe chomwe ndinali nacho poona ntchito yauzimu ikupita patsogolo m’derali chinandipangitsa kuti ndisamadandaule nawo.

Masiku ano ku Betoko II kuli mpingo wolimba, ndipo Lamlungu lililonse pamsonkhano pamabwera anthu pafupifupi 45. Azibale anga onse a m’derali tsopano ndi Mboni, ndipo ambiri mwa iwo ndi apainiya okhazikika. Mchimwene wanga wamng’ono ndi mpainiya wapadera. Pa November 1, 2001, nanenso ndinaikidwa kukhala mpainiya wapadera ndipo ndinatumizidwa ku mudzi wa Antanambao-Manampotsy. Koma ndinachoka ku Betoko II ndili wosangalala kwambiri.

Pamene ndinayamba kuphunzira choonadi cha m’Baibulo mu 1987, ku Madagascar kunali Mboni zosakwana 3,000. Tsopano zilipo zopitirira 14,000. Mofanana ndi zambiri mwa Mboni zimenezi, ndine wosangalala kuti ndakhala ndi mwayi wogwiritsa ntchito mphamvu zanga pothandiza ena. Ndipo ndikuthokoza Yehova kuti wadalitsa khama langa pa ntchito imeneyi.

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Nthawi zambiri ndinkanyamula katundu wolemera makilogalamu oposa 15 kwa mtunda wa makilomita 60 kupita naye kumudzi kwathu

[Chithunzi patsamba 25]

Mchimwene wanga wamkulu Paul

[Chithunzi patsamba 26]

Mchimwene wanga Charles

[Chithunzi patsamba 26]

Ndili ndi anthu ena a m’banja mwathu. Onsewa tsopano ndi Mboni za Yehova