Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ntchito Yolemekezeka ya Amayi

Ntchito Yolemekezeka ya Amayi

Ntchito Yolemekezeka ya Amayi

NTCHITO ya amayi nthawi zambiri anthu saiyamikira ndipo nthawi zina amainyoza kumene. Zaka zingapo zapitazo, anthu ena anayamba kunyoza ntchito yosamalira ana. Maganizo awo anali oti ntchito imeneyi si yofunika ngati ntchito yolembedwa ndipo ena anafika mpaka ponena kuti kugwira ntchito imeneyi kuli ngati ukapolo. Ngakhale kuti anthu ambiri angaone kuti maganizo amenewo ndi onyanyira, zimene anthu ambiri amanena zimachititsa amayi kumva kuti kusamalira panyumba ndiponso kusamalira ana ndi ntchito yonyozeka. Ena mpaka amaganiza kuti mzimayi ayenera kupeza ntchito yolembedwa kuti athe kukwanitsa kuchita zonse zomwe angathe.

Komabe, amuna ndi ana ambiri amayamikira ntchito imene amayi amagwira pabanja. Carlo, amene amagwira ntchito pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Philippines, anafotokoza kuti: “Ndili kuno lero chifukwa cha zimene mayi anga anandiphunzitsa. Bambo anga anali ovuta ndipo ankatilanga msangamsanga, koma amayi ankatithandiza pokambirana nafe. Ndimayamikira kwambiri mmene anatiphunzitsira.”

Peter, wa ku South Africa, m’banja mwawo analipo ana sikisi ndipo analeredwa ndi amayi awo omwe anali osaphunzira mokwanira. Bambo awo anali atawathawa. Peter anati: “Mayi anga ankagwira ntchito m’nyumba za anthu ena ndipo sankalandira ndalama zambiri. Ankavutika kuti atilipirire sukulu tonsefe. Nthawi zambiri tinkagona ndi njala. Ankavutika kwambiri kuti apeze ndalama za lendi. Ngakhale anali ndi mavuto onsewa, amayi anachitabe khama. Anatiphunzitsa kuti tisamadziyerekezere ndi anthu ena. Akanakhala kuti sanali olimba mtima ndiponso akhama, zinthu sizikanatiyendera bwino chonchi pamoyo wathu.”

Mwamuna wina wa ku Nigeria dzina lake Ahmed anafotokoza momwe amaonera thandizo la mkazi wake polera ana awo. Iye anati: “Ndimayamikira ntchito imene mkazi wanga amachita. Ndikachokapo, sindida nkhawa chifukwa ndimadziwa kuti ana anga akusamalidwa bwino. M’malo moona ngati kuti mkazi wanga akuchita nane mpikisano, ndimamuthokoza ndipo ndimawauza anawo kuti ayenera kumulemekeza monga momwe amandilemekezera ineyo.”

Mwamuna wina wa ku Palestine nayenso amathokoza mkazi wake pa ntchito yake yabwino monga mayi. Iye anati: “Lina wachita zambiri polera mwana wathu wamkazi ndipo amathandiza kwambiri kuti banja lathu lizikonda zinthu zauzimu. Mmene ndikuonera, zinthu zamuyendera bwino chonchi chifukwa cha chipembedzo chake.” Lina ndi wa Mboni za Yehova ndipo amatsatira mfundo za m’Baibulo pophunzitsa mwana wake wamkazi.

Kodi zina mwa mfundo zimenezo n’zotani? Kodi Baibulo limati tiyenera kuwaona motani amayi? Kodi kale amayi ankalemekezedwa chifukwa cha ntchito yawo yophunzitsa ana?

Kuwaona Moyenera Amayi

Mkazi atalengedwa anapatsidwa ntchito yolemekezeka pa banja. Buku loyamba la m’Baibulo limati: “Yehova Mulungu ndipo anati, si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzam’pangira wom’thangatira iye.” (Genesis 2:18) Choncho mkazi woyamba, Hava, anali mnzake wa Adamu woti azimuthandiza. Analengedwa m’njira yabwino kwabasi yoti akanathadi kumuthandiza bwino kwambiri. Analengedwa kuti akwaniritse nawo cholinga cha Mulungu choti anthu abereke ana ndi kuwasamalira ndiponso asamalire dziko lapansi ndi zinyama zake. Anali munthu woti Adamu azicheza naye ndi kusanguluka naye ndiponso woti azimuthandiza monga mnzake weniweni. Adamu ayenera kuti anasangalala kwambiri atapatsidwa mphatso yabwino kwambiri imeneyi ndi Mlengi wake!—Genesis 1:26-28; 2:23.

Kenaka Mulungu anakhazikitsa malamulo ofotokoza momwe anthu ayenera kuonera akazi. Mwachitsanzo, amayi achiisrayeli anayenera kulemekezedwa, osati kuchitiridwa chipongwe. Ngati mwana wamwamuna ‘anatemberera atate wake kapena mayi wake,’ akanatha kuphedwa. Akristu achinyamata analimbikitsidwa ‘kumvera akuwabala.’—Levitiko 19:3; 20:9; Aefeso 6:1; Deuteronomo 5:16; 27:16; Miyambo 30:17.

Motsogozedwa ndi mwamuna wake, mayi anayenera kuphunzitsa ana ake aakazi ndi aamuna omwe. Ana aamuna analamulidwa kuti ‘asasiye malamulo a amayi awo.’ (Miyambo 6:20) Komanso, m’buku la Miyambo chaputala 31 muli “uthenga umene amake [a Mfumu Lemueli] anam’phunzitsa.” Iwo mwanzeru analangiza mwana wawo kuti apewe kumwa molakwika zakumwa zoledzeretsa ndipo anati: “Mafumu sayenera kumwa vinyo; akalonga sayenera kunena, chakumwa chaukali chili kuti? Kuti angamwe, naiwale malamulo, naweruze mokhota anthu onse osautsidwa.”—Miyambo 31:1, 4, 5.

Kuwonjezera apo, mnyamata aliyense amene akuganizira zokwatira angachite bwino kuganizira makhalidwe a “mkazi wangwiro” amene anafotokoza mayi a Mfumu Lemueli. Iwo anati: “Mtengo wake uposa ngale.” Kenaka, atafotokoza ntchito zaphindu zimene mkazi woteroyo amagwira pakhomo pake, mayi a mfumuwo anati: “Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.” (Miyambo 31:10-31) N’zachionekere kuti Mlengi wathu analenga amayi kuti akhale ndi udindo wolemekezeka m’banja.

Mumpingo wachikristunso, akazi ndi amayi amalemekezedwa ndi kuyamikiridwa. Lemba la Aefeso 5:25 limati: “Amuna inu, kondani akazi anu.” Timoteo, mnyamata amene mayi ake ndi agogo ake anamuphunzitsa kulemekeza “malembo opatulika,” anapatsidwa malangizo ouziridwa akuti: ‘Udandaulire . . . akazi aakulu ngati amayi.’ (2 Timoteo 3:15; 1 Timoteo 5:1, 2) Choncho mwamuna ayenera kulemekeza mkazi wachikulire ngati kuti ndi amayi ake. Zoonadi, Mulungu amaona kuti akazi ndi anthu ofunika ndipo amawalemekeza.

Muziwauza Kuti Mumawayamikira

Mwamuna wina amene anakulira kudera limene akazi ankaonedwa ngati anthu otsika anati: “Pamene ndinali kukula, ndinaphunzitsidwa kuti amuna ndiye anthu ofunika, ndipo ndaona kuti akazi amachitiridwa nkhaza ndipo salemekezedwa. Choncho ndinavutika kuti ndiyambe kuona akazi monga momwe Mlengi amawaonera, kuti akazi ndi anzathu otithandiza panyumba ndiponso ndi anthu oti tiziphunzitsira nawo limodzi ana athu. Ngakhale kuti zimandivuta kuuza mkazi wanga kuti ndimamuyamikira, ndikudziwa kuti ana anga ali ndi makhalidwe abwino chifukwa cha khama la mkazi wanga.”

Zoonadi, amayi amene amakwanitsa udindo wawo wophunzitsa ana ayenera kukondwera ndi ntchito yawo. Ndi ntchito yaphindu kwambiri. Ayenera kuyamikiridwa ndi kuuzidwa kuchokera pansi pa mtima kuti agwira ntchito yabwino. Timaphunzira zinthu zambiri kwa amayi athu. Timaphunzira zizolowezi zabwino zimene zimatithandiza moyo wathu wonse, makhalidwe abwino amene ali ofunika kwambiri kuti tikhale ndi ubwenzi wabwino ndi anthu ena, ndipo nthawi zambiri, amatiphunzitsanso makhalidwe abwino ndi zinthu zauzimu zimene zimathandiza achinyamata kuti asalowerere. Kodi mwauzako mayi anu posachedwapa kuti mumayamikira zonse zomwe akuchitirani?

[Chithunzi patsamba 17]

Mayi ake a Peter anamuphunzitsa kuchita khama

[Chithunzi patsamba 18]

Ahmed amayamikira kwambiri thandizo la mkazi wake polera ana awo

[Chithunzi patsamba 18]

Mwamuna wa Lina amati mwana wawo wamkazi ali ndi khalidwe labwino chifukwa cha chipembedzo cha mkazi wake