Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kodi Akaidi Angatheke Kuwasintha?”

“Kodi Akaidi Angatheke Kuwasintha?”

“Kodi Akaidi Angatheke Kuwasintha?”

Limenelo ndi funso lomwe linalembedwa pa chikuto cha magazini ya “Galamukani!” ya May 8, 2001. Anthu ambiri amene anawerenga nkhani za m’magazini imeneyo ananena kuti anasangalala nazo kwambiri. Mu nkhanizo munalinso lipoti la ntchito yophunzitsa anthu Baibulo yomwe Mboni za Yehova zikuchita pa ndende ya ku Atlanta, m’chigawo cha Georgia, m’dziko la United States. M’munsimu muli mawu ena ochokera m’makalata ambirimbiri amene talandira.

▪ “Popeza ndakhala mkaidi kwa zaka eyiti zapitazi, ndaona kuti ntchito yophunzitsa Baibulo imene Mboni za Yehova zimagwira m’ndende ndi imene imathandizadi akaidi. Pamene ndinali m’ndende ku Atlanta, ndinali ndi mwayi wogwira ntchito ndi anthu asanu amene anatchulidwa mu nkhani yanu. Ndinayamikira kwambiri chikondi ndi thandizo lawo. Ndimathokoza abale ngati amenewa, amene amatikonda anthu ngati ife omwe tinachita zinthu zolakwika koma tikuyesetsa kusintha kuti tikhalenso anthu abwino.”—R. J.

▪ “Panopa ndili m’ndende, ndipo abale amene amasonkhana m’Nyumba ya Ufumu yapafupi ndi kuno anayambitsa maphunziro abwino kwambiri kunoko. Chifukwa cha zimenezo, mkaidi mnzanga wabatizidwa, ndipo ineyo, ngakhale kuti ndinali wochotsedwa mu mpingo wachikristu, tsopano ndabwezeretsedwa. Enanso ambiri akuphunzira Baibulo. N’zolimbikitsa kuona kuti tikugwira ntchito yophunzitsa anthu yomwe ikuchitikanso padziko lonse lapansi. N’zosangalatsa kwambiri kutumikira Yehova, kulikonse komwe tingakhale!”—J. M.

▪ “M’chaka cha 1970, ndinaikidwa m’ndende ngakhale kuti sindilakwe. Ndinakhala m’ndende kwa zaka 14. Ndili m’ndende, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ndinakhudzidwa kwambiri ndi kuona mtima kwawo ndiponso nkhawa yomwe anali nayo pa anthu ena. Nditatulutsidwa, ndinapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo ndinabatizidwa patangotha nthawi yochepa. Nthawi zina mtima wanga umandipwetekabe chifukwa cha kupanda chilungamo kumene ndinavutika nako. Koma ndimakumbukira kuti posachedwapa, Yehova adzathetsa kupanda chilungamo ndi kuvutika konse. Akaidi akhoza kusintha atatsatira malangizo opezeka m’Baibulo. Akhozanso kuyamikira khama la abale athu amene amapatula nthawi yawo kuwathandiza. Ineyo ndine mmodzi mwa anthu amene amawayamikira kwambiri!”—R. S.

▪ “M’mene ndinkabwera kundende kuno ndinkasuta fodya, ndinkagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, ndinkatukwana, ndipo sindinkamvera malamulo alionse. Ndinalinso m’gulu la zigawenga. Kuwonjezera apo, ndinali nditachotsedwa mu mpingo wachikristu. Panopa ndabwezeretsedwa, ndipo ndikupita patsogolo bwino. Chifukwa cha choonadi, ndimaona ngati ndamasulidwa kale!”I. G.